Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 8/8 tsamba 20-23
  • Chipani cha Akazi—Nchiyani Chimene Chachitika ku Icho?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chipani cha Akazi—Nchiyani Chimene Chachitika ku Icho?
  • Galamukani!—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mkangano wa Chizindikiritso
  • Malo a Zachuma
  • Kodi Chidzakhalitsa?
  • Mbali Yowongoleredwa ya Akazi Dalitso Losakanizika?
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Mbali Yowongoleredwa ya Akazi mu Nthawi Zamakono
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kodi Mulungu Amaona Kuti Akazi Ndi Otsika?
    Nsanja ya Olonda—2012
  • ‘Akazi Amene Agwiritsa Ntchito mwa Ambuye’
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Galamukani!—1988
g88 8/8 tsamba 20-23

Chipani cha Akazi—Nchiyani Chimene Chachitika ku Icho?

CHISONKHEZERO kaamba ka ufulu wa akazi sichinakhale chopanda malipiro ake, makamaka ku umodzi wa banja. Akazi omwe analabadira ku chiitano cha kuthaŵa “ukapolo” wa umodzi wa banja agawirako ku liŵiro lokulira la kusudzulana, limene m’maiko ena liri pamwamba kufika ku 50 peresenti ya maukwati onse atsopano. Kuwonjezera ku kukwinjika kuli kuwonjezereka kwa chiŵerengero cha amayi omwe akugwirizana ndi gulu logwira ntchito nthaŵi zonse, kokha kudzipeza iwo eni akuvutika pansi pa katundu wa ntchito ziŵiri—imodzi ku ntchito ndi inayo kunyumba.

Phunziro la ku U.S. linapeza kuti pamene kuli kwakuti mu 1960 kota imodzi ya akazi okhala ndi ana anali m’gulu la ogwira ntchito, podzafika mu 1986 chiŵerengerocho chinali choposa theka. “Koma pamene kuli kwakuti amayi ambiri amagwira ntchito, masinthidwe panyumba sanapangidwe,” linadziŵitsa tero ripoti limodzi. “Iwo amapitiriza kuchita yokulira ya ntchito ya m’nyumba ndipo ziwiya za chisamaliro cha mkati mwa tsiku kaamba ka ana awo kaŵirikaŵiri ziri zosakwanira kapena zoletsa mwa mtengo.”

Opititsa patsogolo zikondwerero za akazi amanena kuti kuti akhaledi omasuka mowona mkazi ayenera kukhala ndi ulamuliro wotheratu pa thupi lake, kuphatikizapo kuyenera kwa kuchotsa mimba zosafunika. Chikhumbochi kaamba ka ‘kufanana kwa kubala’ ndi amuna chathandizira ku chiŵerengero chomawonjezereka cha kutaya mimba—chiŵerengero choyerekeza cha 55 miliyoni pa dziko lonse chaka chirichonse.

Ngakhale Baibulo silinapulumuke mkwiyo wa opititsa patsogolo zikondwerero za akazi. “Khulupirirani Mulungu. Iye [wamkazi] adzagawira,” amatero opititsa patsogolo zikondwerero za akazi, akumanyodola Baibulo monga latsankho la pakati pa amuna ndi akazi m’kusonyeza kwake Mulungu wa “mwamuna.” “Ena [opititsa patsogolo zikondwerero za akazi] . . . amapatsa mlandu Baibulo wa kukhalabe chida champhamvu mkusungilira akazi ‘m’malo awo’ ndipo amakaikira kaya ngati chinachake chogwiritsira ntchito moterocho chingakhale mawu a Mulungu,” inasimba tero The United Church Observer ya ku Canada. Matchalitchi ena agonjera ku chididikizo chochokera ku ziwalo zopititsa patsogolo zikondwerero za akazi ku kusinthira ku chinenero “chophatikiza” m’kulambira kwawo, kulowa m’malo mawu a umuna kaamba ka Mulungu ndi maina onga ngati Wochirikiza ndi Msungi.

Pa nthaŵi imodzimodziyo, chipani cha akazi icho cheni chalowa m’chimene wopeza gulu la opititsa patsogolo zikondwerero za akazi mayi Betty Friedan wachitcha “kuleka kugwira ntchito kotheratu.” Mphamvu za opititsa patsogolo zikondwerero za akazi ziri zogawanika m’chiŵerengero ndithu cha malo apamwamba—kumenyera kaamba ka kuyenera kofanana pansi pa lamulo, malipiro olingana, malamulo omasuka mokulirapo a kuchotsa mimba, kuyenera kwa Kugonana kwa Akazi Okhaokha, tchuthi cha lamulo cha kuyembekezera kubala mwana, ndi chisamaliro cha pa tsiku chabwinopo, limodzinso ndi kumenyera molimbana ndi zithunzithunzi za maliseke.

Mkangano wa Chizindikiritso

Kupititsa patsogolo zikondwerero za akazi kukupita kupyola mu mkangano wa kuzindikiridwa, magazini ya Newsweek ikusimba tero. “Mavuto a kukhazikitsa ntchito, kukulitsa maunansi athithithi ndi kusamalira kaamba ka ana zatsimikizira kukhala zovuta kwambiri kuposa mmene wina aliyense analingalirira m’masiku oyambirira a kupititsa patsogolo zikondwerero za akazi.”

Mu Woman on a Seesaw, mlembi Hilary Cosell akulemba kulira kwa mkazi wogwira ntchito mmodzi wovutitsidwa maganizo yemwe anayesera kulowa ‘m’malo a Mkazi Wapamwamba’: “Ndawonderatu tsopano, sindikulingalira kuti pali china chirichosne chotsalira cha ine kuchipereka ku china chirichonse. Ndiri katswiri wa ntchito wogwira ntchito mopambanitsa, mayi wotopa mopambanitsa, bwenzi la pa nthaŵi yabwino yokha, ndi mkazi wa kanthaŵi kochepa. Mkazi Wapamwamba, ee? Chimveka kwenikweni ngati Mkazi Wosungulumwa.”

Akazi omwe apereka mwaŵi kaamba ka ukwati ndi kukhala ndi ana ndi cholinga chofuna kulondola ntchito kaŵirikaŵiri amazunzidwa ndi zokhumudwitsa. Wofunsako wa bungwe lotsogoza ntchito wa zaka 38 zakubadwa anawuza magazini ya ku Canada Chatelaine kuti: “Pali mbadwo wonse wa akazi onga ine omwe adzapita kumanda awo osakwatiwa . . . Mosasamala kanthu za chipambano chathu timatsogoza miyoyo yopanda kanthu kwenikweni.” Newsweek inasimba ponena za kudera nkhaŵa kwa wachiŵiri kwa prezidenti wa kampani yopanga nsapato wa zaka 39 zakubadwa kuti: “Ntchito yanga iri yosangalatsa ndi yoyamikirika koma ndiri wochititsidwa mantha ndi kuwopa kuti ndikusoweka mbali ya tanthauzo koposa ya moyo mwa kusakhala ndi ana. Pa nthaŵi zina ndimadzilingalira inemwini kuti ngati ndifa tsopano mwala wanga wa pa manda udzaŵerengedwa kuti: ‘Pano pagona . . . Iye anaŵerenga magazini ochulukira.’”

Ngakhale opititsa patsogolo zikondwerero za akazi otchuka amawoneka kukhala ndi malingaliro achiŵiri ponena za makhalidwe abwino a za kugonana mwaufulu. Wolemba wa ku Australia Germaine Greer, m’bukhu lake la 1970 The Female Eunuch, analongosola ukwati kukhala “ntchito yaufulu yopangidwa pa lamulo la wolemba ntchito wokhala ndi pangano la ntchito kaamba ka moyo wonse, lopangidwa m’chiyanjo chake.” Chikhumbo cha mkazi cha kuwongolera mkhalidwe wake “choyamba chingakhale chinayenera kusonkhezeredwa ndi ‘mkhalidwe wa chisembwere wosalamulirika,’” iye analingalira tero. Pamene kuli kwakuti Greer anawonedwa ndi ambiri monga wotsogolera wodzipereka wa masinthidwe a za kugonana, mu bukhu lake la 1984 iye anadzidzimutsa opititsa patsogolo zikondwerero za akazi mwa kuyambitsa chiyero ndi kutsutsa kulolera.

Malo a Zachuma

Chipani cha opititsa patsogolo zikondwerero za akazi chasiya akazi mu mkhalidwe woipirapo m’njira zina, akutero mkonzi wa U.S. Sylvia Ann Hewlett. Mwa kugogomezera ufulu wa kudzilamulira ndi kulingana m’malo mwa kukalamira kaamba ka kusintha kuthandiza amayi ogwira ntchito, chipani cha akazi chachita zochepera kuwongolera mkhalidwe wa zachuma wa akazi ambiri, iye akutsutsa tero. “Kudzikhalira pa okha koyambitsidwako kwa omasulidwa ndi osudzulidwa kaŵirikaŵiri kunatembenuka kutanthauza kusungulumwa ndi umphaŵi [umphaŵi woipitsitsa].”

Phunziro limodzi la U.S. linapeza kuti maboma amene anapereka ndi malamulo a chisudzulo chopanda cholakwika, poyambirirapo ochirikizidwa ndi opititsa patsogolo zikondwerero za akazi, akazi osudzulidwa ndi ana awo anavutika ndi kutsika kwa mwamsanga kwa 73 peresenti mu mkhalidwe wawo wa moyo, pamene amuna awo akalewo anasangalala ndi kukwera kwa 42 peresenti. Kutalitali ndi kuwongokera kaamba ka akazi!

M’chenicheni, malipiro a mkazi mu United States akali kokha chifupifupi 64 peresenti ya malipiro a mwamuna—chifupifupi mlingo wofananawo zaka 50 zapitazo. M’maiko a ku Europe kumene opititssa patsogolo zikondwerero za akazi alunjikitsa pa kupeza tchuthi chabwino cha kuyembekezera kubala ndi madongosolo osamalira ana, malipiro a akazi anakwera kuchoka pa 71 peresenti ya malipiro a amuna mu 1970 kufika ku 81 peresenti zaka khumi pambuyo pake.

Opititsa patsogolo zikondwerero za akazi tsopano amadzipeza iwo ogawanika mozama pa funso limodzi: Kodi nchiyani kwenikweni chimene chiri kufanana? Betty Friedan akuloza kuti akazi sali zikope za amuna. Iye akulongosola kuti: “Nthaŵi yafika yovomereza kuti akazi ali osiyana ndi amuna. Payenera kukhala lingaliro la kufanana lomwe limaŵerengera kuti akazi ali amene amakhala ndi makanda.” Opititsa patsogolo zikondwerero za akazi ena amatsutsa kuti ngati akazi amavomereza malamulo omwe amawapatsa iwo chisamaliro chapadera chomwe sichimapezeka kwa amuna—monga ngati lamulo la tchuthi cha kuyembekezera kubala—iwo tsopano akuvomereza kuti sali ofanana ndi amuna, ndipo chimenecho chingatsegule njira kaamba ka kusiyanitsa.

“Tsoka la kupititsa patsogolo zikondwerero za akazi,” molingana ndi wophunzira mmodzi, liri kaya kusiyana m’kawonekedwe ndi zikhumbo pakati pa osiyana ziwalo kuli kwachibadwa kapena chotulukapo cha kusinthidwira ku mayanjano. Akazi ambiri sali a nkhalwe kapena opikisana mokwanira kaamba ka ntchito zina za malonda, olemba ntchito atero. “Akazi anazolowera kukhala osalankhula kwambiri,” akutsutsa tero Jody, wotsogolera wa gulu lofufuza za mayanjano opititsa patsogolo zikondwerero za akazi. “Mbali ya ntchito yathu monga osamalira iri kudzizindikiritsa iwemwini m’chigwirizano ndi ena ndi kusafunsa kaamba ka inu eni,” iye analongosola tero kwa Galamukani! Ambiri amene amapititsa patsogolo zikondwerero za akazi amakhulupirira kuti kokha kasinthidwe m’njira imene akazi amaizoloŵera mwa kuleledwa kwawo kudzabweretsa kufanana kwenikweni kwa mwaŵi.

Ena amatsutsa kuti akazi angafikire bwino koposa kulingana mwa kuzindikira kuti iwo ali osiyana ndi amuna. Betty Friedan waitanira kaamba ka ‘chiwonetsero chachiŵiri’ cha kupititsa patsogolo zikondwerero za akazi. “Kulingalira kwatsopano kwa kupititsa patsogolo zikondwerero za akazi kuli kofunikira ngati . . . akazi akafunikira kupitiriza kupita patsogolo m’dziko la amuna, . . . ndipo komabe ‘osakhala ngati amuna’” iye watero. Ena amaseka kafikiridwe kofewa kameneka ndipo amalankhula za ‘kubweza m’makwalala,’ kupititsa patsogolo zikondwerero za akazi kuipidwa kwa lamulo ndi kuyenda mumsewu kaamba ka malamulo owonjezereka omasuka a kuchotsa mimba ndi masinthidwe ena.

Kodi Chidzakhalitsa?

Pakali pano, opititsa patsogolo zikondwerero za akazi amadabwa amene adzanyamula zowunikira za mtsogolo. “Atsikana achichepere amadzimva ochititsidwa mantha ndi icho [kupititsa patsogolo zikondwerero za akazi] kuposa kukokeredwa ku icho,” inasimba tero The Toronto Star. Akazi ena achichepereko amawopa ufulu umene kufanana kokulira kwabweretsa. “Akazi ambiri lerolino akunena kuti akhala ndi zokwanira,” anatero wopititsa patsogolo zikondwerero za akazi wa ku France Benoite Groult. “Iwo akufuna kusamaliridwa kachiŵirinso; iwo akufuna kuchinjirizidwa ndi amuna.”

M’maiko ena opititsa patsogolo zikondwerero za akazi alowa m’kutsutsana kowopsya kuchokera ku magulu ena a akazi ogamulapo kulimbana ndi chimene iwo akuchiwona monga chiwukiro pa banja ndi mapindu ena “a mwambo”. Gulu limodzi lotero mu Canada, REAL Women (Realistic, Equal, Active for Life), linadzilongosola ilo lokha kukhala “lolinganizidwa ndi lokonzekera kaamba ka nkhondo.”

Kwina kulikonse chipani cha akazi chikuwoneka kukhala chikuzimiririka. Mu West Germany, wolemba Peter H. Merkl akunena kuti akazi asiya kupititsa patsogolo zikondwerero za akazi ku mlingo wokulira. “Umayi wochotsedwa mwalamulo wabwereranso mu dongosolo. Akazi ogwira ntchito ndi olembedwa ntchito akuthaŵa kubwerera m’zomangira za banja . . . , pamene opititsa patsogolo zikondwerero za akazi oyambirira abwerera m’gulu lochepera la mwambo lopatulidwa.”

Zopeza zatsopano za sayansi pa chibadwa cha ubongo wa munthu zingayambukire kulingalira kwa mtsogolo ponena za mbali ya ziwalo. Katswiri wa za minyewa Richard Restak ananena kuti: “Umboni ukusonyeza kuti kusiyana kwambiri kwa mkhalidwe pakati pa amuna ndi akazi kuli kozikidwa pa kusiyana m’kugwira ntchito kwa ubongo komwe kuli kwa cholowa mwa chipangidwe cha zolengedwa ndipo kosathekera kusinthidwa ndi zochititsa za mwambo zokha.” Ayi, akazi sali chithunzi cha amuna koma anapangidwa kaamba ka zifukwa zosiyana kwenikweni ndi zikhumbo zosiyana ndi zofunika m’moyo.

Koma kodi zopeza zimenezi zingabwere monga chodabwitsa? Sayansi yapeza chowonadi chonenedwa kalekale mu mbiri ya Baibulo ya chilengedwe cha mkazi woyamba, Hava. Genesis 2:18 imalemba chifuno cha Mlengi: “Si kwabwino kuti munthu akhale yekha, ndidzampangira womthangatira iye.” Chotero amuna ndi akazi aliyense akakhala ndi mikhalidwe yomwe ikathangatira wina ndi mnzake. Iwo sanapangidwe kuti akhale olimbana wina ndi mnzake. Aliyense akakhala woyenerera m’mbali ina yake yapadera, yothangatira.

Ndipo “kupeza” kwakuti akazi sali chithunzi cha amuna—kuti akazi ali ndithudi ‘osiyana kuchokera kwa amuna,’ kuti akazi ‘amabala ana’—kodi chimenecho chiridi chatsopano? Kachiŵirinso, Baibulo linachimveketsa icho kuyambira pa chiyambi kuti Mulungu anawalenga iwo osiyana, “mwamuna ndi mkazi anawalenga iwo,” ndipo kuti mkazi anakonzedwa mwapadera kubala ana.—Genesis 1:27, 28; 2:21-23.

Koma kusiyana sikumatanthauza kukhala wotsika. Palibe kulungamitsidwa kaamba ka kuchitira ndi mtundu wa akazi m’njira yolamulira. Iye ali “wochokera kwa mwamuna,” ndipo chotero mu mpingo Wachikristu, mwamuna amakonda mkazi wake “monga iyemwini.” M’mikhalidwe yoteroyo iye amapeza ulemu, chikondi, ndi lingaliro la chisungiko.—Aefeso 5:28-33; 1 Timoteo 5:2, 3.

Amuna ndi akazi ali osiyana, koma iwo sali opikisana. Wina amathangatira mnzake; mmodzi amakwaniritsa wina. M’makonzedwe a Yehova a ukwati, aŵiriwo amakhala mmodzi. Mamiliyoni a akazi Achikristu owona lerolino akupeza ufulu weniweni m’kukwaniritsa mbali yawo yolongosoledwa m’Baibulo.

[Zithunzi patsamba 22]

Moyo wa mkazi wogwira ntchito uli wotopetsa ndi wosweka

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena