Makolo Omwe Achita Ntchito Yawo ya Kunyumba
MAKOLO omwe amachita ntchito yawo ya kunyumba amapereka kwa ana awo zinthu zimene iwo ndithudi akusowa. Motsimikizirika, ichi chimaphatikizapo zoposa kokha kulipira ndalama zowonongedwa. Makolo oterowo amathandizanso ana awo kukulitsa mapindu olondola ndi zonulirapo m’moyo, ndipo amawapatsa iwo nthaŵi yochulukira ndi kudera nkhaŵa kwachikondi.
“Pamene ana anali achichepere, tinakwawa pansi ndi iwo, kugunda mapoto, kuvala zivindikiro za miphika monga zisote, ndi kuwopsyezana ndi zipande wina ndi mnzake kuchita monga zitsanzo zofala za m’Baibulo m’zochitika za m’mbiri,” walongosola tero Wayne, atate wa ana anayi. “Achicheperewo anachikonda icho.”
Pamene ana anakula, Wayne ndi mkazi wake, Joanne, anasintha njira zawo zophunzitsira; komabe anapitiriza kudzutsa lingaliro la ana awo ndi chikhumbo cha kuphunzira. Iwo chotero anachita ndi malamulo abwino kwambiri a kuphunzitsa. Julie M. Jensen, prezidenti wa U.S. National Council of Teachers of English, amakhulupirira kuti mphunzitsi wabwino samaiwala nkomwe kusangalatsa kwake kwa ukhanda pamene anali kuphunzira, ndipo amawunikira chimenechi kwa ana ake a kusukulu.
Kufunika kwa Kuthokoza
Wayne ndi Joanne anakulitsa dongosolo la kuthandiza ana awo ndi ntchito yawo ya kusukulu. Pali dengu loikamo “zinthu zobwera” mu kichini kumene ana amaika mapepala awo ochongedwa pofika kunyumba kuchokera ku sukulu. Joanne amabwereramo m’mapepalawo pamene ana akuseŵera kapena akuchita ntchito yawo ya kunyumba, ndipo pa chakudya chamadzulo banja kaŵirikaŵiri limakambitsirana izo. Abwino kwambiri amasonyezedwa pa chiwiya choziziritsira zakudya ndi pa makoma a mu kichini, omwe amafanana ndi malo oikapo zithunzithunzi.
“Iri njira yathu yoperekera chithokozo kwa ana,” akutero Joanne, “ndipo amanyadira pa icho.” M’chipinda chochezera, banja liri ndi dengu la “zinthu zotuluka” kunja kumene ntchito ya kunyumba imapita nthaŵi yogona isanadze. “Mwa njira imeneyi,” akulongosola tero Joanne, “sitimazifunafuna izo m’mawa pamene anawo akuthamangira ku sukulu.”
Beatrice, mayi wa atsikana aŵiri, amakometseranso kichini yake ndi ntchito ya kusukulu ya ana ake. Iye akunena kuti: “Ndimachita tero chifukwa chakuti ndiri wonyadira ponena za ana anga ndipo ndimafuna kuti iwo adziŵe ponena za icho.”
Akumazindikira mlingo wokulira wa kuthokoza, Independent School District ya ku Dallas, Texas, imalimbikitsa aphunzitsi ake aufulu kupanga kugwiritsira ntchito kuwoloŵa manja kwa kalongosoledwe kolimbikitsa, konga ngati: Yabwino kwambiri! Yabwinoko. Limbikira! Chiri chabwino kaamba ka iwe. Uku ndi kuchenjera. Wachita bwino ndendende. Yomangirira kwambiri. Kuganiza kwabwino. Ntchito yopambana. Tsopano wachita bwino. Ndimayamikira njira imene ukuyesera.
Ngati muli kholo, kodi mungapereke chilimbikitso mwa kaŵirikaŵiri kwambiri?
Kupereka Chirikizo mwa Njira Zina
Kuwonjezera ku kuthokoza zoyesayesa za ana awo, makolo omwe amachita ntchito yawo ya kunyumba amalimirira mkhalidwe wa panyumba womwe uli wabwino kwambiri m’kuphunzira. Iwo amapangitsa ana awo kukondweretsedwa m’kuŵerenga ndi kuphunzira ponena za dziko lowazungulira.
“Makolo anga anandichirikiza ine,” akulongosola tero Julie, “mwa kuika mpanda mozungulira nthaŵi yanga ya kuphunzira. Ndinali ndi malo achindunji m’nyumba akuchitira ntchito yanga yochitira kunyumba, ndipo sindikachita chirichonse ku banja lonselo kufikira itachitidwa. Mkati mwa nthaŵi yanga ya kuphunzira, sindinafunidwe kuchita ntchito yaing’ono iriyonse. Kusokoneza malo obindikiritsidwa anga chotero kunapewedwa.”
Mark akulongosola mmene makolo ake anamuchirikizira iye ndi alongo ake: “Iwo anatsimikizira kuti tinali ndi dikishonale ndi mabukhu ena otithandiza ife m’kuphunzira kwathu. Anatilimbikitsa ife kupanga malaibulale aumwini mwa kutilola ife kugula mabukhu omwe tinasangalala nawo popanda kulipira kaamba ka iwo ndi ndalama zathu.”
“Tinayamba programu yathu yoŵerenga ndi ana pamene iwo anali chifupifupi miyezi itatu ya kubadwa,” analongosola tero Althea, mayi wa ana anayi. “Chinali chovuta kusungilira chifukwa chakuti, mofanana ndi akazi ambiri lerolino, ndinafunikira kugwira ntchito. Kuti ndilole kaamba ka icho, ndinafunikira kuwombola nthaŵi kuchokera ku zochitachita zina. Ana anali ndi mabukhu oposa 300—onena za ku nasale, mabukhu a sayansi, amitundu yonse. Ankabweretsa kwa ine omwe anakonda koposa kuti ndiwaŵerengere. Nthaŵi ina ndinkadumpha gawo kuyesera kufupikitsa nkhanizo, koma chimenecho sichinagwire ntchito. Anawo nthaŵi zonse anadziŵa mbali yosoweka ndipo ankandikumbutsa ine mwa kuidzaza iyo kuchokera mu chikumbumtima!”
Johan kuchokera ku Finland akunena kuti makolo ake anakhoza kuŵerenga kwa iye mphindi 10 kufika ku 15 usiku uliwonse asanapite kukagona. “Ndinakhoza kutenga nkhaniyo,” Johan akulongosola tero. “Amayi ankaseŵera mbali mu nkhaniyo. Mlongo wanga ndi ine tinakokedwa kwambiri ku makonzedwewo kotero kuti ngakhale pamene makolo anga analibe nthaŵi, tinkatenga bukhu ndi kuyesera pa tokha. Ichi chinatithandiza ife kukulitsa chizolowezi chabwino kwambiri cha kuŵerenga. Icho chapangitsa ntchito yathu ya kusukulu kukhala yopepuka ndi kufutukula dziko lathu.”
Ravindira kuchokera ku Sri Lanka anakonda kukhala ndi atate ake akumugoneka iye chifukwa cha mkhalidwe wawo wa kuŵerenga. “Nthano yanga ya madzulo yokondeka inali Mmene Ngamila Inapezera Chinunda Chake. Atate ankaliza zala, kudumpha, kuseka, ndi kuchita chirichonse mkati mwa kuŵerengako. Chimenecho chinachitidwa ndi cholinga chondigonetsa ine, koma chinangopitirizabe m’kundisunga ine wogalamuka ndi kufuna zowonjezereka. Iwo anachita ngati kuti sakudziŵa chimenechi, koma anadziŵa kwenikweni chimene iwo anali kuchita. Pambuyo pake, pamene ndinakula, iwo ankandilola ine kunyamula mabukhu kuwabwezera mu laibulale. Chimenecho chinandipangitsa ine kudzimva kukhala wofunika ndipo chinandilimbikitsanso ine kusangalala ndi kuŵerenga.”
Akulongosola mmene atate ake anamthandizira iye, Susan wanena kuti: “Atate anakonda maulendo a kumunda. Iwo ankanditenga ine kulikonse—kosungira zithunzithunzi zakale, kumalo osungira mbalame, malaibulale, kutchola mpoza wa kutchire mthengo. Nthaŵi zina tinkayendera kokha malo a nkhalango osadziŵika. Tinkabwerera kunyumba okwalawulidwa, koma chinali chosangalatsa. Maulendo amenewo anapereka chifuno ku maphunziro anga a kusukulu.”
Emilo kuchokera ku Puerto Rico akukumbukira: “Mayi wanga anafuna kuti tidziŵe kuti nthaŵi zonse tinali kuphunzira. Pamene ndinabwerera kunyumba kuchokera ku sukulu, iwo ankafunsa kuti, ‘Chotero, nchiyani chomwe mwaphunzira lero?’ Ngati ndinanena kuti, ‘Oo, palibe’ iwo ankafunsanso kuti, ‘Ukutanthauza chiyani, pamene ukuti palibe? Ufunikira kukhala utaphunzira chinachake.’ Iwo ankapitiriza kufunsa kufikira nditanena chimene ndinaphunzira. Iwo anachita chinthu chofananacho ndi abale anga aŵiri. Iwo anafuna kuti tidziŵe kuti tinali ofunika kwambiri kwa iwo ndi kuti iwo anasamalira kaamba ka ife. Chimenechi chinatipanga ife kukhala banja logwirizana mwathithithi.”
Kulimilira Unansi Wathithithi wa Banja
Mabanja opita patsogolo amakhala pamodzi bwino lomwe, koma ichi chimafunikira kuyesayesa. Chotero makolo omwe amachita ntchito yawo ya kunyumba amafunafuna kulimirira mzimu wa banja wogwirizana.
“Timakambitsirana nkhani za banja mowona mtima ndipo chifupifupi pa maziko a tsiku lirilonse,” akunena tero Carol, kholo limodzi la ana akazi a zaka zapakati pa 13 ndi 19. “Nthaŵi zina atsikanawo amabisa mavuto awo chifukwa chakuti amadzimva kuti ndiri ndi okwanira a inemwini. Ndimakhoza kudziŵa pamene atero, popeza kuti amakangana pa zinthu zachabechabe. Ndimafunikira kuwakumbutsa iwo kuti makonzedwe a banja amagwira ntchito bwino lomwe pamene tikambitsirana mavuto athu wina ndi mnzake mowona mtima.”
Ndalama ziri magwero a mavuto m’mabanja ambiri, koma Carol akunena kuti kukhala kwake wotseguka ndi atsikana ponena za mkhalidwe wa ndalama wa banja kwadzetsa chichirikizo chawo. Iye akulongosola kuti: “Ndimawalimbikitsa iwo kupeza ntchito kulandira ndalama zawozawo kaamba ka zinthu zowonjezereka zomwe angakonde. Ndimawalemekeza iwo kaamba ka kuzilandira izo ndi kuwalola iwo kudziŵa kuti ziri ndalama zawo.”
Makolo ena amagwiritsira ntchito mkhalidwe wa chuma wa banja lawo kuphunzitsa ana awo kupeza zofunikira kugulidwa, kusunga, ndi maluso a masamu. “Phunziro lina limene takhala okhoza kuliphunzitsa kupyolera mu kakonzedweka,” wawona tero Henry, tate wa anyamata atatu ndi mtsikana, “liri kugwirizana m’zochitachita za banja kupyolera m’kutengamo mbali.”
Koma kodi ndi kuti kumene makolo angapeze nthaŵi kaamba ka ntchito ya kunyumba yoteroyo? Audrey, mayi wa ana aŵiri, wanena kuti chifukwa cha ndandanda yake yolimbitsa, iye amaitana ana ake kutsagana naye pamene aperekera makalata. Iwo amampangitsa iye kulankhula pochita tero.
Kuchita ndi Mavuto
M’malo mochita ntchito yawo ya kunyumba bwino lomwe, makolo afunikira kuphunzira kumvetsera mosamalitsa kwa ana awo. Monga mmene mwambo wa Baibulo umanenera: “Kuti wanzeru amve nawonjezere kuphunzira.” (Miyambo 1:5) Kumvetsera kosamalitsa kumamangirira chikhulupiriro, ndipo ichi chiri chofunika kwambiri m’kuchita ndi mavuto mwachipambano.
Mwachitsanzo, pamene Leon ndi Carolyn anaphunzira kuti mwana wawo wamkazi wamkulu, Nikki, ankaphonya ku sukulu ndi kulephera makosi ena, kuyankha koyamba kwa Carolyn kunali kupatsa mlandu chiyambukiro choipa cha mabwenzi a kusukulu. Komabe, Leon analongosola kuti: “Ndinalingalira kuti tiyembekeze kupereka chiweruzo kufikira titakhala ndi nsonga zonse.”
“Koma ngakhale pamenepo,” Leon anadziŵa tero, “chinatenga milungu ya kuleza mtima, kufufuza kosamalitsa ndi kumvetsera tisanafikire magwero a vuto la Nikki. Chimenecho chinali chozizwitsa chotani nanga kwa ife! Nikki anadzimva kuti sitinali okondweretsedwa mwa iye, popeza kuti tinali otanganitsidwa kwambiri ndi zochitachita zathu! Carolyn ndi ine tinapanga masinthidwe, ndipo Nikki anayankha mwakukhala wogalamuka kwambiri ku thayo lake mozungulira nyumba ndi kusukulu.”
Dan ndi Dorothy ali ndi ana asanu ndi atatu. Awa amathera ora limodzi ndi theka pa basi ya kusukulu tsiku lirilonse, ndipo vuto lalikulu lakhala kuipirako kwa mikhalidwe kumeneko. “Pamene achikulire anali kusukulu, inali nkhani yopepuka kugwiritsira ntchito nthaŵi m’basimo kuchita ntchito ya kunyumba kapena kusatsalira kumbuyo m’kuŵerenga,” anadziŵitsa tero Dan. “Mu kokha zaka 12 zapitazo, ngakhale ndi tero, zonsezo zasintha. Tsopano pali zocheutsa zambiri zosakhala zabwino—chinenero choipa, nyimbo za rock zaphokoso, ndi utsi wochokera ku ndudu ndi mbanje, nthaŵi zambiri cha kumbuyo kwa basi.”
Dan analongosola kuti anathetsa vuto limeneli ndi anawo. “Malingaliro aŵiri anawonekera,” iye anadziŵitsa tero. “Kukhala pafupi kwambiri ndi woyendetsa basi monga mmene kungathekere, ndi kukonzekeretsa mwana aliyense ndi zokwezera mawu za m’makutu zolumikizidwa ku wailesi ya kaseti yaumwini ya AM/FM. Tsopano anawo ali okhoza kudzilekanitsa iwo eni ku mavutowa, kusangalala ndi kumvetsera kwabwino kwa nyimbo pamene akuŵerenga kapena kuchita ntchito yochitira kunyumba yopepuka. Chothetseracho chikuwoneka kukhala chosavuta, koma chagwira ntchito!”
Kugwira Ntchito ndi Dongosolo la Sukulu
Mkati mwa chaka cha sukulu, ana a sukulu amatsiriza chifupifupi maora asanu ndi limodzi pa tsiku pansi pa chisonkhezero chachindunji cha aphunzitsi. Makolo omwe amayamikira chimene icho chimatanthauza ponena za kuthekera kwa kuphunzira kaamba ka ana awo adzafuna kuwona ku icho kuti nthaŵi imeneyi ikuwonongedwa bwino. Mayi wa ana atatu analongosola mmene iye ndi mwamuna wake anatsimikizirira kuti zinali tero.
“Pamene John ndi ine tinali osakhutiritsidwa ndi imodzi ya makalasi a ana athu,” iye akulongosola tero, “tinkapita ku sukuluko ndi kugwirira ntchito pa masinthidwe oyenerera ndi phungu wotsogoza, mphunzitsi, kapena mkulu wa sukulu. Tinakhala olowetsedwa mozama m’maphunziro oyambirira a ana athu kuyambira pa chiyambi kufika ku mapeto. Tsopano popeza chimenecho chatha, tiri okhutiritsidwa kuti anapeza zabwino za chimene chinalipo kwa iwo.”
Ana angafune thandizo ndi ntchito yawo ya kusukulu, ndipo mbali ya ntchito ya kunyumba ya makolo ifunikira kukhala olowetsedwamo. Komabe, kholo mwanzeru limagwirizana ndi dongosolo la sukulu. “Chinthu chimodzi chimene ndimakumbukira ponena za makolo anga,” akutero Wesley, “chiri chakuti iwo sanakhoze mpang’ono pomwe kusokoneza ndi zochitachita za aphunzitsi a m’kalasi. Iwo anazindikira kuti tsatanetsatane wa kuphunzitsa angasinthesinthe.
“Mwachitsanzo, pamene ndinasokonezedwa ndi kachitidwe komwe kakanandipereka ku yankho la vuto la masamu, Atate anakhoza kundipatsa ine yankho ndi kundilola ine kulimbana ndi dongosololo kufikira nditalipeza. Ndinadziŵa kuti ndinalipeza ilo pamene yankho langa linafanana ndi la Atate.”
Si Ntchito Yopepuka
Mwana aliyense adzakuuzani inu kuti magawo ena a ntchito zochitira kunyumba ali olimba kwambiri kuposa ena. Koma ntchito ya kunyumba imene inu makolo muli nayo iri yovuta kwambiri kuposa iriyonse imene munakhala nayo mu sukulu. Ndithudi, kulera ana mwachipambano iri ntchito yovuta, ya nthaŵi yaitali. Ena aitcha iyo kukhala ntchito ya zaka 20.
Mfungulo ku kupambana imaphatikizapo kukhala womvetsera, waubwenzi, kholo lomvetsetsa, mmodzi amene amadziŵa ana bwino lomwe ndi kuyankha kwa iwo monga aliyense payekha. Kumbukirani, chimene achichepere anu akufunikira chiri chisamaliro chaumwini chomwe chimasonyezedwa ndi kudera nkhaŵa kwa chifundo kaamba ka mkhalidwe wawo wabwino. Pangani mwa iwo chilakolako kaamba ka kuphunzira, ndi kuwathandiza iwo kupanga kupeza chidziŵitso kukhala chokumana nacho chosangalatsa.
Kuyesayesa Konse Kuli Kophulapo Kanthu
Inu makolo amene mumachita ntchito yanu ya kunyumba mukudzipereka nsembe, osati kudzipambanitsa mwini. Muli okonzekera kupanga masinthidwe. Inu mumazindikira kuti kuti muthandize ana anu, inu mufunikira ‘kukhala kumeneko,’ ndi kuti muyenera kudziikizako inu eni mwa kupereka nthaŵi, chikondi, ndi kudera nkhaŵa zimene ana anu amazifunikiradi.
Pamene muchita ntchito yanu ya kunyumba, zotulukapo zingakhale zoyerekeza ku kututa kwa mlimi yemwe amakonzekera nthaka ndipo kenaka kuwoka, kulimirira, ndi kuthirira mbewu zake. Inu mungafupidwe ndi zotuta zosangalatsa. Chiri monga mmene Baibulo limanenera kuti: “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo ngakhale pamene iye atakalamba sadzachokamo.”—Miyambo 22:6.
[Bokosi patsamba 11]
Nchiyani Chinanso Chimene Makolo Angachite?
M’chitaganya chamakono, aphunzitsi ndi masukulu ali ofunika ku kukula kwachipambano kwa ana. Chimenecho sichimatanthauza kuti iwo angakwaniritse mbali ya makolo, koma angakhale achithandizo choposa m’kulera ana mwachipambano. Chotero gawo lina la ntchito yochitira kunyumba limene inu makolo muli nalo liri kugwirizana mokwanira kumene kuli kothekera ndi dongosolo la sukulu kumene ana anu alembetsedwako.
Bwanji, kenaka, ngati pali kagwiridwe ka ntchito kachindunji kapena programu pa sukulu? Mwachitsanzo, pa sukulu mu Massachusetts, panali programu ya Kupatsa Mphatso Yakufikapo kwa Wophunzira. “Ndinapita chifukwa chakuti ndinafuna kuti ana anga adziŵe kuti ndinali wonyadira ponena za iwo,” analongosola tero Joanne, mayi wa anyamata anayi. Ophunzira makumi aŵiri analandira mphatso zapadera za kufikapo tsiku limenelo, komabe ochulukira a makolo sanapezekeko. Kodi muganiza kuti kusapezekapo kwawo kunalimbikitsa ana awo kuchita zoposerapo pa sukulu? Kutalitali!
Lingaliraninso aphunzitsi. Masukulu kaŵirikaŵiri amaika pambali madzulo kusonyeza ntchito ya ophunzira ndi kubwereramo m’kupita kwawo patsogolo ndi makolo, ndipo aphunzitsi ambiri amataya nthaŵi yawo yaumwini kukonzekera kaamba ka zochitika zimenezi. Mphunzitsi mmodzi anawona kuti: “Tiri ndi mabanja athu enieni ndi miyoyo yathunso yeniyeni yakukhala nayo. Chimakhala chokhumudwitsa pamene muwononga nthaŵi yochulukira tero kukonzekera kaamba ka zochitika zapadera ndi kuwona kokha kholo limodzi, aŵiri, kapena atatu madzulo onsewo.”
Monga makolo, inu nthaŵi zina mungayembekezere masukulu ndi aphunzitsi kupanga masinthidwe kukumaniza zosowa zapadera za ana anu. Kodi simuyenera kukhala ofunitsitsa kupanga kudzipereka kofananako kuchirikiza kuyesayesa kwa dongosolo la sukulu, makamaka popeza kuti ikuyesera kuthandiza ana anu kukula kukhala achikulire achipambano?
Broshuwa yakuti “School and Jehovah’s Witnesses,” yofalitsidwa kuchirikiza kumvetsetsa ndi kugwirizana pakati pa makolo ndi aphunzitsi, yandandalitsa ntchito yochitira kunyumba yotsatirayi kaamba ka Mboni za Yehova zomwe ziri makolo: “Chiri chofunika kuti makolo akhale ozoloŵerana ndi aphunzitsi a ana awo—kupanga makonzedwe a kukumana ndi kulankhula ndi iwo. . . .
“M’kukumana koteroko tate yemwe ali Mboniyo kapena mayi ayenera kulola mphunzitsi kudziŵa kuti makolowo amayembekezera mkhalidwe wabwino Wachikristu kwa ana awo, ndi kuti ngati ana sadzisamalira bwino, ayenera kudziŵitsidwa. Makolo ayeneranso kupatsa chitsimikiziro chakuti adzachirikiza mphunzitsi m’chilango chirichonse choyenera chomwe chidzaperekedwa, ngakhale kuchichirikiza icho kunyumba.
“Njira zina zimene makolo angathandizire: Tsimikizirani kuti ana akhala ndi chakudya cham’mawa chabwino asanachoke kupita ku sukulu. Onani kuti ntchito yawo yochitira kunyumba yatha ndi kuti ali ndi mabukhu awo onse. Nthaŵi zonse sonyezani ulemu kaamba ka malamulo a ku sukulu ndipo yembekezerani ana kulemekeza amenewanso. Pangitsani ana kulankhula panyumba ponena za zochitachita za ku sukulu ndi mavuto aliwonse omwe angakumanizane nawo kumeneko.”
Kodi simukuvomereza kuti awa ndi malingaliro abwino? Kodi inu monga makolo mukuwagwiritsira ntchito iwo? Mbali ya ntchito yanu ya kunyumba iri kuchita tero.
[Bokosi patsamba 12]
Mafunso kaamba ka Kudzisanthula kwa Ukholo Kwaumwini
1. Kodi ndimatenga chikondwerero chenicheni m’kuphunzira kwa ana anga?
2. Kodi ndimadziŵa aphunzitsi awo?
3. Kodi aphunzitsi amadziŵa kuti ndimayamikira kuyesayesa kwawo?
4. Kodi ndimatsimikizira kuti ana anga amatenga ntchito yawo ya kusukulu mosamalitsa?
5. Kodi ndimawona ku icho kuti ntchito yawo ya kunyumba ikuchitidwa bwino ndipo pa nthaŵi yake?
6. Kodi mkhalidwe wanga kulinga ku chidziŵitso ndi kuphunzira uli weniweni?
7. Kodi ana anga amandiwona ine ndikuphunzira?
[Chithunzi patsamba 7]
Kuŵerenga kumadzutsa chilakolako cha ana ndi kulingalira
[Chithunzi patsamba 8]
Makolo omwe amathera nthaŵi kuŵerengera ana awo amalimbitsa chomangira cha banja
[Chithunzi patsamba 9]
Maulendo a banja ku malo osungira zinthu zamakedzana kapena mu dziko angakhale chosangalatsa chenicheni cha banja—ndi chokumana nacho chophunzira
[Chithunzi patsamba 10]
Achichepere anu amafunikira chisamaliro chaumwini