Chiwawa—Kodi Tikuchifikira Chitokosocho?
WOCHULUKIRA wa upandu wa mu Britain umachitidwa ndi achichepere a msinkhu wa ku sukulu. Mphunzitsi wina wamkazi mu Sheffield, England, ananena kuti iye anali ataphunzitsa kalasi la ana ophunzira 15 mu sukulu limene kokha 3 analibe cholembera cha upandu. M’chenicheni, ngakhale ana a kusukulu ya nasale akuloŵetsedwa m’chiwawa cha m’chipinda cha kalasi.
“Ogwira ntchito pa masukulu a nasale akuvulazidwa mowopsya ndi ana awo ophunzira, ndipo mungalingalire mantha m’mitima ya ana ena,” anatero mphunzitsi wina wamkazi wa mu Yorkshire. Iye anawonjezera kuti: “Ngati mwana wa sukulu loyambirira angachite chivulazo cha mtundu umenewu, kodi adzakhala otani ku sekondale ngati sitichitapo kanthu ponena za icho?”
Koma nchifukwa ninji ana ali okhoterera chotero kukhala achiwawa?
Ntchito ya TV ndi Makanema
Ana owonjezereka akuwonerera maprogramu achiwawa ndi achisoni a pa wailesi ya kanema ndi makanema, ndipo maulamuliro ambiri akunena kuti chimenechi chiri chochititsa m’kuwonjezeka kwa chiwawa. Mu Australia, mwachitsanzo, kufufuza kunachitidwa kwa zizoloŵezi za kuwonerera kwa ana chifupifupi 1,500 a zaka zakubadwa 10 ndi 11. Bungwe lobwereramo m’zamakanena la Australia linaŵerengera theka la mafilimu onse omwe ana anawonerera kukhala osayenera. Komabe, mbali imodzi mwa zitatu ya ana ananena kuti iwo anasangalala mwapadera ndi zochitika za chiwawa.
Mmodzi analongosola kuti: “Ndinakonda mbali mu imene mtsikana anadula mutu wa atate wake ndi kuwudya monga keke ya pa phwando la tsiku la kubadwa.” Ponena za kanema ina, mwana wina ananena kuti: “Ndinaikonda iyo pamene mlendo anadya mutu wa mkazi ndi kumapitirizabe kugeya.” Chikhalirechobe mwana wina ananena kuti: “Ndinakonda pamene anaduladula mkazi ndipo zonse za mkati mwake zinatulukira kunja.”
Ofufuzawo anamaliza kuti monga chotulukapo cha kuwonerera zinthu za mtundu umenewu, ponse paŵiri ana ndi achikulire akukulitsa chilakolako kaamba ka chiwawa. Iwo ananenanso kuti makolo akhala akuwopsyezedwa kapena kukakamizidwa ndi zididikizo zamphamvu za mayanjano zobwera kupyolera mwa ana awo kulola ana awo kuwonerera mafilimu oterowo.
Independent Broadcasting Authority ya ku Britain (Ulamuliro Wowulutsa Wodziimira Pawakha) inachititsa phunziro la chiyambukiro cha kuwonerera maprogramu owonetsa chiwawa. Owonerera mamiliyoni aŵiri, kapena 6 peresenti ya gulu lonse, ananena kuti pambuyo pa kuwonerera maprogramu achiwawa, iwo nthaŵi zina anadzimva “kukhala achiwawa.” The Times ya ku London, mu ripoti lake la zopezedwa, inanena kuti ana amalephera kumvetsetsa kuti chiwawa cha pa chowonetsera sichiri chenicheni ndipo ali ndi kawonedwe kakuti kupha kuli “kachitidwe ka tsiku ndi tsiku.” Kodi nchodabwitsa kuti ana ambiri chotero azoloŵetsedwa ku chiwawa ndipo ali ndi mantha ochepera ponena za kuchichita icho iwo eni?
Masukulu ndi Makolo
Ena agwirizanitsa wokulira wa mlanduwo kaamba ka kuwonjezeka kwa chiwawa ku kulephera kwa masukulu kuphunzitsa mapindu a makhalidwe abwino. Ponena za kulephera kumeneku, ripoti lokonzedwa mu Britain ndi aphunzitsi aŵiri a mkati mwa mzinda likunena kuti: “Uwu uli mkhalidwe wa ngozi ndipo umodzi umene umapita kutali kulinga ku kulongosola chiwawa chowonjezereka m’chitaganya chathu.” Koma kodi kuli kuchita bwino kupatsa mlandu aphunzitsi kaamba ka kulephera kuika mapindu a makhalidwe abwino mwa ana?
Ripoti lopangidwa ndi British National Association of Head Teachers (Bungwe la Dziko la Britain la Aphunzitsi Aakulu) Lalikuyankha kuti: “Miyezo ya makhalidwe mu sukulu ndi m’chitaganya ikunyonyotsoka koma chisonkhezero chimene masukulu angakhale nacho pa chitaganya kupitira mwa achichepere sichiyenera kugogomezeredwa mopambanitsa.” Popeza kuti mkhalidwe wa maganizo wa mwana uli wopangidwa kale nthaŵi yaitali iye asanapite ku sukulu, ripotilo linanena kuti: ‘Ndi zochepera zimene mphunzitsi angachite kusintha chimenecho.’
Roy Mudd, wachiŵiri kwa mphunzitsi wamkulu pa Sukulu la Anyamata mu Mzinda wa Portsmouth, mofananamo akugogomezera kuti aphunzitsi omwe amawona ana awo ophunzira kokha kwa maora oŵerengeka pa tsiku ‘sangachite chirichonse kuikako muyezo wowonjezereka wa makhalidwe abwino m’zopereka zasukulu pokhapo ngati ana aphunzitsidwa kusiyana kwa pakati pa chabwino ndi choipa ndi makolo awo.’
Palibe chikaikiro ponena za icho, maziko kaamba ka makhalidwe abwino ayenera kuyalidwa m’moyo poyambirira ndi makolo. Iwo, m’malo mwa masukulu, ayenera choyambirira kudziloŵetsa m’kuphunzitsa ana awo mapindu a makhalidwe abwino ngati kutembenuka kwa chiwawa chomakula kuti kuchitike. Komabe, palibe makolo kapena masukulu akuchifikira chitokoso cha chiwawa, kapena siokwanira a iwo omwe akutero.
Bwanji Ponena za Kukakamizidwa kwa Lamulo?
Kodi akuluakulu okakamiza lamulo akuchifikira chitokosocho? Mu Colombia, South America, oweruza 62 asimbidwa kukhala anaphedwa chifukwa chakuti anakana kulandira ziphuphu kuchokera kwa opititsa cocaine. Mofananamo, m’gawo la Los Angeles, U.S.A., kukakamiza lamulo sikunakhoze kuletsa kupha 387 kochitidwa ndi magulu a anam’goneka mu 1987. Maulamuliro okakamiza lamulo m’malo ambiri oterowo akuzindikira kuti makamaka chifukwa cha anam’goneka, iwo akuyang’anizana ndi vuto losalamulirika. Koma nchifukwa ninji iwo sangachifikire chitokoso?
Chiri chifukwa cha kunyonyotsoka m’lamulo ndi dongosolo m’dziko lonse. Mu Great Britain, m’polisi wamkulu wa ku Surrey, Brian Hayes, akulongosola kuti: “Zaka zapita m’polisi ankauza gulu kusuntha ndipo iwo ankatero. Lerolino m’polisi akawukiridwa.” The Sunday Times ya ku London ikunena kuti chitaganya kaŵirikaŵiri “chachepetsa mapindu, pamene apolisi akuwonedwa kukhala aupandu ndipo akuswa lamulo akuwonedwa kukhala ngwazi.”
Richard Kinsey, mphunzitsi m’phunziro la upandu pa Yunivesite ya Edinburgh, akunena kuti: “Mu Scotland timatumiza anthu owonjezereka m’ndende kuposa m’dziko lirilonse mu Europe ndipo nthaŵi ziŵiri ndi theka kuposa kum’mwera kwa [England].” Ndi chotulukapo chotani? Mu 1988 polisi ya Strathclyde ya ku Glasgow inachitira ripoti chiwonjezeko cha 20 peresenti m’maupandu a chiwawa pa nyengo ya miyezi 12. M’mawu opyoza, Kinsey akumaliza kuti: “Ife mu Scotland tawona [kuti] mfungulo ya chitseko cha ndende yatsimikizira kukhala yopanda pake.”
Chitokoso Chosafikiridwa
Kuchitira fanizo kulephera kufikira chitokoso cha chiwawa linali danga mu Nursing Times ya ku Britain. Ilo linanena kuti: “Palibe yemwe amachenjeza ophunzira unamwino kuti iwo akuloŵa mu ntchito ya ngozi—mwinamwake afunikira kutero.” Zopezedwa za Health and Safety Commission (Bungwe la Umoyo ndi Chisungiko), dangalo likupitiriza tero, ziri zakuti anamwino akuyang’anizana ndi “mlingo wa chiwawa ndi chiwopsyezo nthaŵi zambiri zokulira kuposa anthu onsewo.”
Pakati pa malo a ngozi koposa kaamba ka namwino kugwiriramo ntchito ali mu A&E (Accident and Emergency), monga mmene amatchedwera mu Britain. Awa angakhale mwapadera malo achiwawa pakutha kwa milungu pamene madipartimenti a chipatala a nthaŵi zonse amatsekedwa. Galamukani! inafunsa amene kale anali namwino yemwe analongosola ntchito mu A&E ya ku London.
“Chipatalacho chinali m’malo kumene kunali omwerekera ndi anam’goneka ambiri, ndipo tinali ndi malo apadera a dipartimenti yochiritsira ovulazidwa opatulidwa kaamba ka iwo. Kumeneko ankasiidwa kugona kufikira ziyambukiro za kumwa kwawo mankhwala mopambanitsa zitatha, ali kutali ndi odwala ena. Pa nthaŵi zina, pamene ankabwera, iwo ankakhala achiwawa kwambiri. Chinali chokumana nacho chowopsya.
“Ndawona anthu akugonekedwa m’chipatala ovulazidwa moipitsitsa m’kumenyana kwa m’gulu ndipo omwe anapitiriza kumenyana kwawo mu A&E. Mwa kaŵirikaŵiri chotero chiwawa chingadzutsidwe popanda chenjezo kwa ogwira ntchito ya unamwino. Pamene ndinaloŵa ntchito ya unamwino, yuniformu ya namwino inawoneka kukhala ikupereka mtundu wa chitetezero—koma osati tero lerolino.”
Chiwawa chaika tonsefe pa kudzichinjiriza. Ndemanga zonga ngati, “Tsopano palibe wosungika” ndipo, “Chikuwoneka kuti siuli wa chisungiko kulikonse,” ziri zofala mowonjezerekawonjezereka. Makolo akuyang’anira pa ana awo, kuwopa kuwalola iwo kuchoka pamaso pawo. Akazi akukhala m’mantha a kumenyedwa ndi kugwiriridwa chigololo. Anthu achikulire amadzibindikiritsa m’nyumba zawo. Kuchokera ku mbali iriyonse, ndi chithunzi cha chisoni.
Chimenechi chimatibweretsa ku funso lofunika kwambiri, Kodi nchiyani chimene tingachite pamene tiyang’anizana ndi chiwawa?
[Chithunzi patsamba 26]
Chiwawa cha pa wailesi ya kanema chingapititse patsogolo chiwawa cha moyo weniweni