Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g89 5/8 tsamba 3-4
  • Kukwera kwa Mitengo—Mtengo wa Munthu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukwera kwa Mitengo—Mtengo wa Munthu
  • Galamukani!—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kusakhazikika Kochititsidwa ndi Vuto la Zachuma
  • Ndani Ayenera Kupatsidwa Mlandu?
  • Kukwera Mitengo Kwa Zinthu Padziko Lonse—Kodi Baibulo Limanena Zotani?
    Nkhani Zina
  • Nchifukwa Ninji Pali Vuto la Mtengo wa Kakhalidwe?
    Galamukani!—1989
  • Gawo 1a: Kukhupuka ndi Kugwa kwa Dongosolo Lamalonda
    Galamukani!—1992
  • Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Kaamba ka Kubwezeretsa Chuma?
    Galamukani!—1989
Galamukani!—1989
g89 5/8 tsamba 3-4

Kukwera kwa Mitengo—Mtengo wa Munthu

Ndi mlembi wa Galamukani! mu Spain

“Ife talekeratu kudya matimati chifukwa chakuti ali odula kwambiri. Ndipo ponena za zipatso, sindingathe kukumbukira nthaŵi yomalizira pamene ndinagulapo zina,” anausa moyo tero mkazi wa panyumba mu India.

“Ife sitingathe kugula nsapato kapena zovala,” akuchitira chisoni tero wogwira ntchito mu fakitale yopanga nsalu wa ku Mexico, akumayesa kuchirikiza banja la asanu. “Zaka zinayi zapita, tinali ndi ndalama zochepera, koma chirichonse chinali chotsika mtengo. Tsopano ndalama ziribe ubwino kaamba ka chinthu chirichonse.” M’dziko lake mphamvu yogulira ya ndalama ya peso inagwa ndi 35.4 peresenti pakati pa 1982 ndi 1986.

Muhammed el-Ghani ali mlonda wausiku mu Cairo, Igupto, kumene mitengo ya zinthu zina zofunika inawonjezereka kaŵiri m’kokha nyengo imodzi ya miyezi 12. “Ife timakhalapo ndi moyo tsiku ndi tsiku,” iye akulongosola tero, “ndipo pali masiku ena amene ife sitingakhoze kudya.”

Mu Brazil m’nkhole wosowa mwaŵi wa ngozi ya pa njanji anafunikira kuyembekeza kwa zaka 20 funso lake la kubwezeredwa lisanagamulidwe ndi mabwalo a milandu. Iye potsirizira pake anafupidwa kubwezeredwa kwa pamwezi ndi mwezi kolingana ndi theka la amene anali malipiro aang’ono a mtunduwo nthaŵi imene ngoziyo inachitika. Chifukwa cha kukwera kwa mtengo wa zinthu, ngakhale kuli tero, ndalama zimenezi mwinamwake sizinakhoze ngakhale kukwaniritsa malipiro a basi pamene anapita kukazitenga.

Bala wa ku Nigeria, wokhala kale tate wa atatu, anasweka mtima pamene anamva mbiri yakuti mkazi wake anali atangobala ana atatu. Mosasamala kanthu za kukhala kwake ndi ntchito ziŵiri, ndalama za banja sizinali zokwanira mpang’ono pomwe kaamba ka zinthu zofunika, ndipo mitengo ya chakudya yapitirizabe kukwera. Iye akudziŵa kuti chidzakhala chosatheka kupereka ngakhale zinthu zofunika kaamba ka ana ake. Iye anali wokonzekera kupereka makanda ake kaamba ka kuleredwa ndi winawake.

Tsatanetsatane angasiyane, koma nkhaniyo iri yofanana kuzungulira dziko lonse. Mtengo wa kakhalidwe ukukwera mosabwerera m’mbuyo. Kwa ambiri, mkate ndi mkaka zakhala zosangalatsa, ndipo kudya katatu pa tsiku kwakhala kwa apa ndi apo. Ripoti lochokera ku Nigeria likunena kuti: “Mkate, pakali pano chakudya chachikulu cha anthu ambiri koposa a ku Nigeria, ukudyedwa kokha ndi anthu achuma. Mpunga ukudyedwa kokha pa zochitika za phwando.”

Ena amathetsa vutolo mwa kugwira ntchito maora ochulukirapo, koma ena amapeza ntchito kukhala yovuta kapena ngakhale yosatheka kuipeza. Iwo amakakamizidwa kupereka tsiku lirilonse ku ntchito yosatha ndipo kaŵirikaŵiri yosaphula kanthu ya kufunafuna zakudya. Kwa iwo, siliri kokha funso la kuchita ndi mtengo wa kakhalidwe koma, m’malomwake, nkhani ya kulimbana ndi kufikira mtengo wa kupulumuka.

Chochititsa m’nkhani zambiri koposa chiri kukwera kwa mtengo wa zinthu, kapena kukwera kwa mitengo. Malipiro nawonso angawonjezeredwe, koma si nthaŵi zonse pamene amayendera limodzi ndi kukwera kwa mitengo. Okanthidwa molimba mwachindunji ali aja a malipiro osasintha, onga ngati otenga penshoni kapena osalembedwa ntchito. Mu ambiri a maiko otukuka pang’ono a dziko, pakhala kugwa kozindikiritsidwa mu muyezo wa kakhalidwe m’zaka zaposachedwapa. Pa mlingo wa dziko lonse chinganenedwe mowonadi kuti ngakhale kuti olemera angakhale akulemererakobe, osauka motsimikizirika akusaukirakobe. Kodi umenewo ndiwo mkhalidwe m’dziko lanu?

Kusakhazikika Kochititsidwa ndi Vuto la Zachuma

Mosadabwitsa, ambiri amakweza mawu awo m’kutsutsa. Mwachitsanzo, aphunzitsi osauka kuchokera ku madera a Chiapas ndi Oaxaca akumanga mahema m’malo aakulu apakati a Mzinda wa Mexico m’chiyembekezo chakuti kachitidwe kawo koteroko kakabweretsa chilungamo cha zachuma. “Anthu akudyeredwa masuku pamutu,” mmodzi wa iwo akutsimikizira tero. M’maiko ena ziwawa zaulika pamene mitengo yakwera mowopsya.

Upandu, wolongosoledwa ndi ena kukhala kusintha kwakachetechete koma kowopsya kwa osauka motsutsana ndi olemera, ukuwonjezeka nawonso. Msonkhano wa apolisi unagwirizanitsa funde la kupulupudza la mitundu yonse ku tsoka la zachuma losowa nalo chochita la nzika zambiri. Kukhumudwitsidwa kwa zachuma nthaŵi zina kumatenga kutembenuka koipitsitsa. Mu 1987 m’midzi iŵiri ya ku India anthu 50 a gulu logawidwa lapamwamba anaphedwa ndi mazana a osauka osowa chakudya omwe analingalira kuti iwo anali kudyeredwa masuku pamutu ndi eni malo olamulira a m’gulu logawidwa lapamwamba.

Ndani Ayenera Kupatsidwa Mlandu?

M’zana la 20, chuma chowonjezereka chapangidwa kuposa ndi kale lonse. Koma modabwitsa, pamene zana lino likuyandikira mapeto, mamiliyoni owonjezereka akugwera m’kusauka kopitirizabe. Malonjezo a mtsogolo mwabwinopo, kuwongokera m’zachuma, malipiro abwino kaamba ka onse, zonse kaŵirikaŵiri zimakhala maloto otsimikizirika a ndale zadziko.

Kodi ndani kapena nchiyani chomwe chiyenera kupatsidwa mlandu? Ambiri amapatsa mlandu maboma awo. Maboma ku mbali yawo angapatse mlandu malamulo a zachuma a maiko ena. Dongosolo la zachuma la dziko nalonso lasulizidwa mwamphamvu. Mwachiwonekere, mavutowo ali ocholoŵanacholoŵana ndipo mayankho ali osatsimikizirika. M’nkhani yotsatira, tidzalingalira kokha zina za zochititsa zazikulu za vuto la mtengo wa kakhalidwe ndi chifukwa chimene izo ziri zovuta kwenikweni kuzithetsa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena