Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g89 7/8 tsamba 13-15
  • Kusuta—Kawonedwe Kachikristu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kusuta—Kawonedwe Kachikristu
  • Galamukani!—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chikondi cha Mulungu ndi Mnansi
  • Nchifukwa Ninji Iwo Analeka?
  • Kodi Chiridi Kanthu?
  • Kodi Mawu a Mulungu Amati Chiyani pa Nkhani ya Kusuta Fodya?
    Nsanja ya Olonda—2014
  • N’kusiyiranji Kusuta?
    Galamukani!—2000
  • Ogulitsa Imfa—Kodi Ndinu Wogula?
    Galamukani!—1989
  • Ndudu za Fodya Kodi Mumazikana?
    Galamukani!—1996
Onani Zambiri
Galamukani!—1989
g89 7/8 tsamba 13-15

Kusuta—Kawonedwe Kachikristu

MWACHIDZIŴIKIRE, Baibulo silimatchula fodya kapena kusuta, popeza kuti zinali zosadziŵika mu Middle East wakale. Chifukwa chopepuka chiri chakuti chomera cha fodya chinali chomera cha ku South America, Mexico, ndi West Indies ndipo sichinaperekedwe ku mbali zina zotsala zadziko kufikira pakati pa zana la 16.

Kodi chimenechi chimatanthauza kuti Baibulo silimanena chirichonse choyenera kulinga ku kusuta? Kutalitali. Ilo momvekera limalongosola maprinsipulo amene ali ndi kugwira ntchito kwa chilengedwe chaponseponse ndipo ali zitsogozo kaamba ka mkhalidwe wathu. Kodi ndi ati amene ali ena a maprinsipulo aakulu amenewa?

Chikondi cha Mulungu ndi Mnansi

Magwero a lamulo osonkhezera kaamba ka Mkristu ayenera kukhala aja omwe Yesu analongosola kuti: “Udzikonda [Yehova, NW] Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu yako yonse, ndi nzeru zako zonse ndi mnansi wako monga iwe mwini.”—Luka 10:27.

Kodi ndimotani mmene wina angaperekere chikondi kwa Mulungu ndi mtima wake wonse, moyo, maganizo, ndi mphamvu ngati iye mwadala akuipitsa nzeru zake mwa kudziloŵetsa m’chizoloŵezi, chikhoterero choipa, chomwe chimatsogolera ku matenda ndi imfa ya mwamsanga? Ndimotani mmene wina asonyezera chiyamikiro kaamba ka mphatso ya Mulungu ya moyo pamene akusuta nam’goneka omwerekeretsa monga chikonga? Mulungu anapatsa “zonse moyo ndi mpweya.” (Machitidwe 17:24, 25) Kodi tifunikira kuipitsa mpweya wopatsidwa ndi Mulungu umenewo? Kuchokera ku kawonedwe ka Mulungu iko kulidi chikhoterero choipa, “choipa, chonyonyotsoka, kapena kachitidwe ka mkhalidwe woipa kapena chizoloŵezi.”—The American Heritage Dictionary of the English Language.

Kodi ndimotani mmene kusuta kumasonyezera chikondi kaamba ka mnansi, pamene mpweya woipa wa wosuta ndi utsi zimaipitsa zovala ndi mpweya wozungulira? Bwanji ponena za anansi oyandikana kwambiri a wosuta, mkazi wake ndi ana? Kodi chiri chikondi kulondola njira yomwe ingatsogolere ku imfa ya mwamsanga, ya pang’onopang’ono, ndi yowawitsa imene iwo adzapenyerera? Kodi kumasonyeza kulingalira Kwachikristu kaamba ka anthu ena kuwapangitsa iwo kukhala osuta apambali, akumakoka mpweya wa ululu wotulutsidwa ndi wosuta? Nchosadabwitsa kuti munda wa zomera mu Blanes, Spain, uli ndi chomera cha fodya m’chigawo chake cha zomera zaululu!

Bwanji ponena za chikondi chaumwini? Chiri chokwanira kudzikonda mwini ku mlingo wa kusamalira kaamba ka umoyo wa mwini yekha wa kuthupi, maganizo, ndi wauzimu. Mtumwi Paulo analongosola kuti “munthu sanadana nalo thupi lake ndi kale lonse; komatu alilera nalisunga.” Kodi kumasonyeza chikondi chaumwini kudziloŵetsa m’chizoloŵezi chimene pang’onopang’ono chimavulaza umoyo wa wina?—Aefeso 5:28, 29.

Yehova Mulungu walonjeza kuti padzakhala ‘miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano m’zimene chilungamo chidzakhala.’ (2 Petro 3:13) Limenelo lidzakhala dziko latsopano laudongo, lopanda kuipitsa kwa mtundu uliwonse. Kusuta sikudzaloledwa kapena ngakhale kukhumbidwa nthaŵiyo, chotero kusutiranji tsopano? Mwanzeru, uphungu wa Paulo umagwira ntchito pano: “Pokhala nawo tsono malonjezano amenewa, okondedwa, tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m’kuwopa Mulungu.” (2 Akorinto 7:1) Chikonga chimadetsa thupi m’lingaliro lenileni. Kusuta kumachipangitsa kukhala chosatheka kwa Mkristu kupereka thupi lake kwa Mulungu “nsembe ya moyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.” (Aroma 12:1) Mphamvu ya kulingalira imasonyeza kuti kusuta kuli kovulaza ndi kotsutsana ndi maprinsipulo Achikristu. Chimenecho, kenaka, chiri chisonkhezero choyambirira cha kuleka kusuta ngati wina amafuna kukondweretsa Mulungu.

Nchifukwa Ninji Iwo Analeka?

Mamiliyoni a anthu kuzungulira dziko aleka kusuta. Icho chingachitidwe. Koma motani? Kodi chofunikira nchiyani? Chisonkhezero champhamvu. Kwa ambiri chiri umoyo, ulemu waumwini, ndi chikondi kaamba ka banja. Koma ena nawonso ali ndi chisonkhezero cha chipembedzo—chikhumbo cha kukondweretsa Mulungu.

Chotero, bwanji ponena za Ray, Bill, Amy, ndi Harley, otchulidwa m’nkhani yathu yachiŵiri? Nchifukwa ninji iwo analeka kusuta?

Bill, yemwe kale anali wandevu, wa luso lamanja watsitsi lalitali, anaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Chinatsatira nchiyani? “Ndinagamulapo kuti ndinafuna kukondweretsa Mulungu ndi kumutumikira iye ndi thupi laudongo ndi maganizo. Ndinaleka popanda chothandizira chirichonse. Osati kusiya kwa pang’onopang’ono. Pa January 1, 1975, ndinatenga ndudu yanga yothera ndipo kenaka kutaya thumba lokhalamo ndudu. Chiyambire pamenepo umoyo wanga wawongokera. Ndikali chikhalirebe ndi emphysema. Koma ngakhale kuwona kwanga mitundumitundu kunawongokera pambuyo poleka kusuta.”

Amy, namwino wotumbula, akulongosola mmene iye analekera. “Ine ndinathandizira m’kutumbula kotsegula mtima, ndipo ndawona mtundu uliwonse wa mapapo—ofiirira ndi aumoyo, akuda ndi oipitsidwa ndi ululu. Ngakhale kuti ndinawona mapapo amenewo odwala moipitsitsa, owoneka ngati anadzazidwa ndi tsabola wakuda, sindinasiyebe kusuta. Ndinadzinyenga inemwini, ndikumati, ‘Ukali wachicheperebe. Chimenecho sichidzachitika kwa iwe.’

“Kenaka mu 1982 ndinachimva chifuno cha kuwongolera moyo wanga, ndipo ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni. Ngakhale kuti ndinakhala ndi Mboni yachikazi mnyumba yake, ndinali kuzemba kutulukira pa denga kuti ndikasute! Chotero ndinafunikira kudziletsa inemwini. Ndinapemphera molimba ndipo motalikira. Koma pamene ndinapanga chigamulocho, chinali chosavuta. Masiku aŵiri oyambirira anali chiyeso, koma pemphero losalekeza linali mfungulo kaamba ka ine.”

Harley, yemwe kale anali woyendetsa ndege wa Navy, anali ndi nthaŵi yovuta kuchotsa chizoloŵezi cha chikonga. “Ndinayesera kuleka kusuta kwanga mwapang’onopang’ono, koma sichinagwire ntchito. Kenaka pamene ndinagamulapo kuti ndinafuna kubatizidwa monga mmodzi wa Mboni za Yehova, ndinaleka popanda chothandizira chirichonse. Ndinapyola masiku aŵiri kapena atatu a kuvutika. Ndinali wonjenjemera, wokwinjika, ndi womangika. Mmene ndinafunira ndudu! Kenaka Mboni inandithandiza ine ndi uphungu wabwino. ‘Pamene iwe ufuna kutenga ndudu, ndi pamene ufunikira kupemphera kwa Yehova kaamba ka thandizo.’ Chinagwira ntchito kaamba ka ine. Lingaliro lina lomwe linandikondweretsa linali lakuti, ‘Kodi ndingalingalire Yesu ali ndi ndudu mkamwa mwake?’ Chinali chosalingalirika. Koma ndimazindikira kuti wosuta amafunikira chisonkhezero champhamvu kuti aleke. Ndinkawuza amayi kuti, ‘Ndikungodzivulaza inemwini, Amayi.’ M’chenicheni ndinali kuvulaza iwo nawonso, m’njira zambiri kuposa imodzi.”

Ray, yemwe kale anali nduna yopereka zovala ndi chakudya mu Navy, nayenso sanachipeze kukhala chopepuka kuleka kusuta. “Ndinayesera nthaŵi zambiri ndisanakumane ndi Mboni za Yehova, koma sichinagwire ntchito konse. Nthaŵi zonse ndinali kusakanizana ndi anthu osuta, ndipo chinali chovuta kukana ndudu yoperekedwa. Koma pamene ndinadziŵa chowonadi chochokera m’Baibulo, ndinafuna kutumikira Yehova, mongadi mmene Kristu anachitira. Chotero ndinaleka m’tsiku limodzi. Chinali chowopsya kwa milungu iŵiri. Thupi langa linali kulakalaka chikonga. Koma ndi kusintha kotani nanga komwe ilo linakupanga! Mwadzidzidzi ndinakhalanso ndi nyonga yopanda malire. Ndinadzimva bwino ponena za inemwini. Ndinali wamphamvu kachiŵirinso.”

Kodi Chiridi Kanthu?

Kulingalira kofala kumasonyeza kuti kachitidwe kovulaza kalikonse kayenera kulekedwa. Koma ndi kusuta sitikungolankhula za kuvulaza. Iko kuli kwakupha, kodzetsa imfa. Kuli kwaululu. Monga mmene Patrick Reynolds, woloŵa m’malo wa mwaŵi wa kampani ya fodya, analongosola mu umboni wake ku komiti yaing’ono ya Msonkhano wa Nthumwi za ku U.S. kuti: “Ndikhulupirira kuti kusatsa malonda kwa ndudu kuli kuchirikiza zotulutsidwa zaululu ndikuti kuli mkhalidwe woyenera, wolondola ndi wabwino kuchotsa kusatsa malonda konse kwa ndudu.”

Kwa Akristu okhumba kukondweretsa Mulungu, chiri motsimikizirika mkhalidwe woyenera, wolondola, ndi wabwino kuchotsa, osati kokha kusatsa malonda a fodya, koma zopangidwa za fodya zonse m’miyoyo yawo. Ndudu zogula (“zachisungiko” ndi zopanda chisungiko), ndudu zokulunga, fodya ya kaliwo, ndi yamphuno—zonsezi zimachokera ku chomera cha fodya chaululu chimodzimodzicho, chotulutsa chikonga. Ndipo inu simufunikira icho kuti mutsimikizire kuti ‘wachokera pa ulendo wautali, bwanawe’ kapena kukhala ndi kusangalala ndi kulaŵa kwabwino m’moyo wanu. Kukhala wotchuka sikumawonetsedwa mwa kudziipsya ndi ululu inumwini, mosasamala kanthu za chimene ogulitsa nthenda ndi imfa akuyesera kukuwuzani!

[Bokosi patsamba 15]

Opatuka Kuchoka ku Malonda a Kusuta

Mu 1875 R. J. Reynolds anakhazikitsa kampani yopanga fodya yotafuna mu North Carolina. Mu 1913 iwo anapanga ndudu yawo yoyamba—Camel brand. Kuchokera pamenepo malondawo apita patsogolo nakhala achiŵiri kokha ku Philip Morris m’kugulitsa ndudu ndi gulu la opeza ndalama koposa mu United States. Mwana wamwamuna wa mdzukulu wa woyambitsayo ali Patrick Reynolds, yemwe tsopano ali m’zaka zake zoyambirira za m’ma 40. Kale wosuta kwa zaka 15, iye anadabwitsa dziko la fodya.

Mu 1986 iye anawonekera pamaso pa komiti yaing’ono ya msonkhano wa nthumwi kudzachitira umboni motsutsana ndi kusuta! Chiyambire pamenepo iye wakhala wochita ndawala wokhazikika motsutsana ndi kugwiritsira ntchito fodya. Kodi nchiyani chomwe chinayambitsa kuda kwake chopangidwa chomwe chinapanga mwaŵi wa banja lake? Kukumbukira akuyang’ana monga mnyamata wachichepere pamene atate ake, wosuta wamphamvu, anafa pang’onopang’ono ndi emphysema. Patrick analongosola kuti: “Zikumbukiro zanga za atate anga ziri zonse za mwamuna wopereŵera mpweya nthaŵi zonse, ndi kuŵerenga nthaŵi yomwe anatsala nayo ya kukhalabe ndi moyo.”

Patrick anagamulapo kuchita chinachake chabwino ndi moyo wake. “Ndinawona kuti ndikakhoza kupanga kusiyana ndi kuchita chinachake ndi moyo wanga.” Iye ananena kuti kupitirizabe kuchirikiza “akupha otsimikiziridwa” kukakhala “mwapoyera mkhalidwe woipa.”

“Ngati dzanja lomwe pa nthaŵi ina linandidyetsa ine liri indastri ya fodya, kenaka dzanja limodzimodzilo lapha mamiliyoni a anthu ndipo lidzapitirizabe kupha mamiliyoni owonjezereka pokhapo ngati anthu agalamuka ku ngozi za ndudu.”—The New York Times, October 25, 1986.

David Goerlitz ali chitsanzo yemwe anali wotchuka kaamba ka kukhala Winston pa kusatsa malonda kwa ndudu za Winston. Iye waleka kusatsa malonda a ndudu kwake ndipo tsopano wakhala wolankhulira wa American Cancer Society. Kodi nchiyani chomwe chinampangitsa iye kusintha? M’kufunsidwa kwa pa TV, December 29, 1988, iye ananena kuti: ‘Ine ndinachezera mbale wanga m’chipinda cha odwala kansa ku chipatala mu Boston. Chinandibweretsa ine nkhope ndi nkhope ndi ziyambukiro za ntchito yanga—odwala kansa omwe anali kuvutika chifukwa cha kusuta. Ndinawona ziyambukiro zosakaza kwa minkhole yosuta ndi minkhole ya minkholeyo, mabanja awo. Ndinawona amuna m’zaka zawo za m’ma 40 opanda tsitsi, mapaipi pa mmero pawo ndi m’mimba. Ndinadzimva wa liwongo ndi kugamulapo kuleka kusatsa malonda a fodya.’

[Chithunzi patsamba 14]

“Ine ndinathandizira m’kutumbula kotsegula mtima, ndipo ndawona mtundu uliwonse wa mapapo”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena