Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g89 8/8 tsamba 25-27
  • Nchiyani Chomwe Ndingachite Ponena za Ovutitsa ku Sukulu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nchiyani Chomwe Ndingachite Ponena za Ovutitsa ku Sukulu?
  • Galamukani!—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Nchiyani Chomwe Chimapanga Wovutitsa?
  • Ndandanda ya M’nkhole
  • Otsimikiza, Osati Aukali
  • Auzeni Makolo Anu!
  • Miyezo Yoletsera
  • Kuthana ndi Khalidwe Lopezerera Ena
    Galamukani!—2003
  • Kodi Ndingatani Anthu Ena Akamandivutitsa?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Kodi Ndingatani Anthu Ena Akamandivutitsa Kusukulu?
    Mayankho a Mafunso 10 Omwe Achinyamata Amadzifunsa
  • Muzidalira Yehova Anzanu Akamakuvutitsani
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
Onani Zambiri
Galamukani!—1989
g89 8/8 tsamba 25-27

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Nchiyani Chomwe Ndingachite Ponena za Ovutitsa ku Sukulu?

RYAN ankapezeka ku sukulu yaing’ono ya kumudzi kumene chiwawa chinali chosamvedwa. Koma kenaka iye anasamukira ku sukulu yapamwamba yokulirapo ndi yovutirapo—ndipo mwamsanga anakhala chandamale cha ovutitsa ku sukulu. Ryan akusimba kuti: ‘Ulendo wa pa basi wa mphindi 15 unakhala chizunzo chomwe chinawoneka kutha kwa maora angapo pamene ondizunza anapitiriza kuchokera ku kuchitira molakwa kwa pakamwa kufikira ku kuvutitsa kwakuthupi. Iwo anapinda chogwirira mapepala kukhala swastika, kuchitentha icho ndi choyatsira ndudu, ndipo kenaka kuzemba ndi kunditentha nacho ine pa dzanja. Ndinalefulidwa ndi kulira.’

Elizabeth anamaliza sukulu zaka zingapo zapitazo. Koma misozi imagwabe kuchokera m’maso mwake pamene iye akumbukira masiku ake a kusukulu. “Ndinawoneka wosiyana ndi ana ena,” iye akulongosola kuti, “chifukwa mayi wanga anali a fuko lina. Chotero kuyambira mu giredi lachiŵiri mpaka ku sukulu yapamwamba, ndinali kuvutitsidwa ndi kukanidwa mokhazikika. Panawoneka kukhala panali gulu la ‘Ndimadana Naye Elizabeth’, ndipo ngakhale m’zaka za pambuyo pake, ndinapeŵa kupita ku zimbudzi za ku sukulu kotero kuti ndisakhale chandamale cha ziwopsyezo za atsikana ena za kuika mitu ya adani awo m’chimbudzi. Ndinalingalira kuti ndinali woyenerera woyambirira.”

Chiwopsyezo cha ku sukulu chiri chokumana nacho cha tsiku ndi tsiku cha peresenti yokulira yochititsa mantha ya achichepere a msinkhu wa ku sukulu omwe mokhazikika amalandira ziwopsyezo za pakamwa ndi zolembedwa, omwe amavutitsidwa m’zipinda zazing’ono za ku sukulu, kuwopsyezedwa m’kupereka ndalama zawo zodyera chakudya cha masana mokhazikika—ngakhale kukakamizidwa kukhala ndi unansi wa kugonana—ndi ovutitsa ku sukulu.a Ndipo ngati inu munali mmodzi wa minkholeyo, iri lingakhale vuto lalikulu chotero m’moyo wanu kotero kuti simungathe kusumika maganizo pa china chirichonse! Mwachimwemwe, chinachake chingachitidwe ponena za icho! Koma choyamba muyenera kumvetsetsa vutolo.

Nchiyani Chomwe Chimapanga Wovutitsa?

Ofufuza mwachisawawa amavomereza kuti palibe aliyense amene amabadwa wovutitsa. “Wovutitsa ku sukulu amakhala m’nkhole kunyumba,” akudzinenera tero katswiri wa maphunziro a za maganizo Nathaniel Floyd. Wovutitsayo mwakutero angakhale akupereka kuchitiridwa moipa komwe amalandira kunyumba.—Yerekezani ndi Mlaliki 7:7.

Akatswiri ena amasonyeza “kupenyerera chiwawa chochuluka koposa pa wailesi ya kanema” ndi “chikondi chochepera ndi chisamaliro ndi ufulu wochulukira mu ubwana” monga nsonga zina zothandizirako. Ngakhale achichepere omwe mwachibadwa sali aukali nthaŵi zina amakokedwera kukhala ovutitsa kokha chifukwa cha chikhumbo chofuna kukhala mbali ya gulu kapena kuchotsa chisamaliro cha iwo eni.

Ndandanda ya M’nkhole

Chirichonse chomwe chimalingaliridwa kukhala chosiyana, monga ngati kawonekedwe kakuthupi kachilendo kapena chophophonya, kapena kokha kukhala watsopano ku sukulu, kungasonkhezere kuwukira kwa wovutitsayo. Ngakhale kuli tero, chikhoterero chimodzi chapadera chikupezeka mwa minkhole yambiri ya ovutitsa. Elizabeth, wogwidwa mawu poyambirirapo, akulozera ku icho kuti: “Nthaŵi zonse ndinali kulira mosavuta, kotero kuti ena anakhoza kudziŵa pa nthaŵi yomweyo kuti ndinavulazidwa kapena kuchita mantha.”

Magazini ya Parents inandandalitsa mikhalidwe yotsatirayi yofala ku minkhole ya ovutitsa: “kudera nkhaŵa, manyazi, kuchenjera, kuzindikira, kudzilemekeza kwaumwini kochepera,” ndi “chizoloŵezi cha kulira kapena kuthaŵa pamene wawukiridwa”! (Kanyenye ngwathu.) Ayi, minkhole siyenera kupatsidwa mlandu chifukwa cha kuvutika kwawo. Mosasamala kanthu za icho, kudziŵa kuti ovutitsa amakokedwa ku kusoŵa thandizo kungakuthandizeni inu kusamalira iwo.

Otsimikiza, Osati Aukali

Choyamba, musayesere kubwezera wovutitsa. ‘Kubwezera choipa pa choipa’ sikuli kokha kolakwa koma kungakuloŵetseni m’vuto lomwe simuliyenerera, ndipo iko kungangokulitsa vutolo. (Aroma 12:17) Koma pamene kukhala waukali sikuli kwanzeru, kukhala wotsimikiza kungatsimikizire kukhala kothandiza. “Mwa kungomuwuza wovutitsayo kuleka,” ikuyamikira tero magazini ya Parents, “kulongosola kuti iye samakonda chimene wovutitsayo akuchita, ndipo kenaka kuchokapo, mnkholeyo amachepetsako mokulira mwaŵi wa kukhala wovutitsidwa mtsogolo.” Kapena monga mmene katswiri wa maphunziro a za maganizo wina akuikira icho, ‘chilimikani ndipo khalani ndi ulemu.’

Kufikira kwina (pa nthaŵi yoyenerera ndi malo) kuli kuyesera kulingalira modekha ndi wovutitsayo. ‘Kulingalira—ndi iye?’ inu mungafunse tero. Inde, nchotheka kuti pamakhala kusamvetsetsa kwina ku mbali yake, kuti mosafuna mwachita chinachake kudzutsa kukukwiyirani. Pa mwaŵi uliwonse, kufikira wovutitsayo modekha ndi molimba mtima kudzatumiza uthenga wakuti mukukana kukhala m’nkhole wopanda thandizo. Akulongosola tero Dr. Kenneth Dodge kuti: “Ovutitsa amayang’ana kaamba ka kulandira kosakaniza, kaamba ka misozi. Mwana amene samayankha molingana ndi zomwe zikufunidwa motsimikizirika sangasankhidwe monga chandamale kachiŵirinso.” Mwambiwo umanena bwino kuti: “Kuwopa anthu kutchera msampha.”—Miyambo 29:25.

Auzeni Makolo Anu!

Bwanji ngati kuvutitsako sikuleka? Ophunzitsa ndi ofufuza mozizwitsa akuvomereza kuti muyenera kuwuza makolo anu ponena za vutolo. Zowona, mungadzimve kuti makolo anu sadzamvetsetsa. Ndipo mungakhale munawopsyezedwa ndi kuchitiridwa koipirapo ngati munanenezera wovutitsayo. Koma makolo anu ali ndi kuyenera kwa kudziŵa chomwe chikuchitika kwa inu m’sukulu, kodi si tero?

Ichi sichitanthauza kwenikweni kuti makolo anu ayenera kulankhula mwachindunji ndi wovutitsayo. Koma iwo angakupatseni chilimbikitso ndipo mwakutero kumangirira chidaliro chanu chaumwini chomanyonyotsoka ndi chikhutiritso cha kukhala ndi moyo ndi maprinsipulo aumulungu. Iwo angakupatseninso uphungu wothandiza. Iwo, mwachitsanzo, angalingalire kuti mulankhule kwa akuluakulu a kusukulu ponena za kuvutitsidwako. Mphunzitsi wa ku sukulu Gerald Hoff akulingalira kuti: “Choyamba yesani kupita kwa phungu wopereka chitsogozo, makamaka pamene muli ndi chirikizo la makolo anu, koma popanda kulola ophunzira ena kudziŵa kuti mukuchita tero, ngati nkotheka. Phunguyo ali wophunzitsidwa kudziŵa mmene angalankhulire bwino kwa wovutitsayo, koma ngati zinthu ziipirako, iri ntchito yake kudziŵitsa mkulu wa pa sukulu.”

Nthaŵi zina makolo amagamulapo kulankhula kwa akuluakulu a ku sukulu m’malo mwanu. Momvetsetseka, inu mungakhale osinkhasinkha kukhala nawo akuloŵereramo mwa njira imeneyi. Ryan, wotchulidwa poyambirirapo, akukumbukira kuti: “Ndinapempha amayi ndi atate anga kusadziloŵetsamo chifukwa ndinawopa kachitidwe ka gulu molimbana nane, ndiponso ndinayembekeza kuti tsiku lirilonse zinthu zikakhalako bwino.” Koma pambuyo pa chochitika chowotchedwacho, atate wake anawumirira pa kulankhula ndi akuluakulu a ku sukulu. Chotulukapo chake? Masitepi anzeru anatengedwa m’malomwake. “Popanda kundivutitsa ine koposa moyenerera,” akukumbukira tero Ryan, “magawo okhala osamalitsa anapangidwa, ndipo ophunzira olakwirawo anayang’aniridwa mwathithithi.”

Ngati mpumulo sukubwerabe, makolo anu angagamulepo kuti miyezo yokulirapo ingatengedwe molimbana ndi wolakwayo.

Miyezo Yoletsera

Chiri chabwino koposa, ngakhale ndi tero, kupeŵa kukhala wovutitsidwa pa malo oyamba. Motani? Choyamba cha zonse, mwa kungokhala wolankhuzana ndi ena mkati ndi kunja kwa kalasi kungathandize kuchotsa chithunzi cha wosungulumwa chimene ovutitsa amawoneka kukhala okokedwerako. Kukhala waubwenzi ndi aphunzitsi ndi oyendetsa basi, ngakhale kungowamwetulira iwo ndi kuwapatsa moni wachisangalalo, motsimikizirika kudzakupatsani inu chisamaliro chawo chokulira cha chiyanjo, chotero kukhala muyezo wa chitetezero. Mungayeserenso kupeŵa nthaŵi kapena malo kumene mavuto ali otsimikizirika kuwoneka.—Miyambo 22:3.

Gwirirani ntchito pa kusonyeza mkhalidwe wa mpumulo kwenikweni ndi wabwino. Ichinso chidzakupangani kukhala chandamale chochepera cha ovutitsa. Baibulo limanena kuti: “Pakuti Mulungu sanatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.” (2 Timoteo 1:7) Mungalimbikitse chidaliro cha mzimu chimenecho mwa kusinkhasinkha pa nsonga iyi: “Koma ngati wina akonda Mulungu, yemweyo adziŵika ndi Iye.” (1 Akorinto 8:3) Kudziŵa kuti Mulungu ali wozindikira za vuto lanu ndipo kuti amasamaladi kungachite zambiri kukuthandizani kuchita ndi ilo.

Ryan akukumbukira kuti: “Ndinapemphera kwambiri mkati mwa nthaŵi yonseyi, ndipo ndimadzimva woyandikira kwa Yehova monga chotulukapo chake. Ndapeza kudziletsa kokulira. Koposa zina zirizonse, ndapeza chikhulupiriro chambiri mwa Yehova pamene iye akunena kuti ‘sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza.’” (1 Akorinto 10:13) Mulungu angakuthandizeni inunso kuchita ndi mavuto anu—ngakhale lovuta monga wovutitsa wa mantha.

[Mawu a M’munsi]

a Mu phunziro lina, 25 peresenti ya ophunzira m’makalasi oyambirira a ku sukulu yapamwamba a mu U.S. anandandalitsa “ovutitsa ndi mkhalidwe wosokoneza” monga chodetsa nkhaŵa chachikulu. Mu Great Britain ndi West Germany, ophunzitsa mofananamo alongosola kudera nkhaŵa kuti kuvutitsa kwawonjezeka m’kuchitika ndi kuipa.

[Chithunzi patsamba 26]

Ovutitsa amakondwera kutenga olimbana nawo aang’ono, ofooka

[Chithunzi patsamba 27]

Ngati mkhalidwewo uli wokulira kwambiri kuchita nawo, uzani makolo anu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena