Lingaliro la Baibulo
Kugonana kwa Ofanana Ziŵalo—Kodi Nchiyani Chimene Chiri Thayo la Atsogoleri Achipembedzo?
OGONANA ofanana ziŵalo amene mowona mtima amafuna kutumikira Mulungu amadzipeza iwo eni m’vuto. Monga mmene mmodzi wa iwo ananenera kuti: “Ngati uli wodzipereka ku tchalitchi ndipo wangopeza kuti ulinso wogonana wa chiŵalo chofanana, kodi ndi zosankha zenizeni zotani zomwe uli nazo?”
Kuti aphunzire chomwe chiri chofunikira kuti akhale okondweretsa kwa Mulungu, ogonana ofanana ziŵalo ambiri mwanzeru atembenukira kwa atsogoleri achipembedzo awo. Kodi “amuna achipembedzo” amenewa akupereka chitsogozo cholondola? Kodi thayo lawo n’lotani ku chitaganya cha ogonana ofanana ziŵalo? Kodi ntchito yawo yaikulu njotani kwa anthu onse?
Ansembe Ali Ndi Thayo la Kuchirikiza Miyezo ya Mulungu
Baibulo limachiika icho mosavuta pamene limanena za ansembe akale kuti iwo “amaikika chifukwa cha anthu m’zinthu za kwa Mulungu.” (Ahebri 5:1) Pamene Abrahamu wakale anatumikira banja lake m’njira imeneyi, iye anawathandiza iwo kuti “asunge njira yake ya Yehova.”—Genesis 18:19.
Mofananamo, unsembe mu Israyeli wakale unachita mbali yokulira kuchirikiza miyezo ya Mulungu. Ansembe anali ndi thayo la kuthandiza mtunduwo kupitirizabe kukhala “anthu a Yehova.” (2 Mbiri 23:16) Lerolino, monga chinaliri panthaŵiyo, oimira a Mulungu ali ndi thayo la kuthandiza nkhosa ‘kupitirizabe kukhala anthu a Mulungu,’ ndi ‘kusunga njira ya Mulungu.’
Kuti achite chimenechi, iwo afunikira kuphunzitsa gulu la nkhosa Mawu a Mulungu. (Malaki 2:7) Kodi atsogoleri achipembedzo atsimikizira kukhala ‘athenga a Mulungu,’ kuthandiza anthu ‘kusunga njira ya Mulungu’? Mwachisawawa ayi. Ndipo chimenechi chiri chowonekeradi m’nkhani ya kugonana kwa ofanana ziŵalo.
Athenga Olakwika, Chitsogozo Changozi
Kunena molunjika, Baibulo limatsutsa kugonana kwa ofanana ziŵalo. Palibe unyinji wa mawu a machenjera womwe ungapangitse malemba onga Levitiko 18:22 ndi Aroma 1:26, 27 kuzimiririka. (Onani bokosi.) Koma mochirikiza zikhoterero zamakono zotsutsana ndi Baibulo, wansembe wa Chijesuit ananena za maunansi a kugonana kwa ofanana ziŵalo kuti: “Iwo ali thandizo lokha lothekera kwa unyinji wa anthu kutsogoza moyo wachimwemwe ndi watanthauzo.” Kutsatira kalingaliridwe kofananako, bishopu wina wa Episcopal anatcha kugonana kwa ofanana ziŵalo “chinachake pa chimene [ogonana ofanana ziŵalo] alibe ulamuliro.” Koma Baibulo limanena za amene kale anali ogonana ofanana ziŵalo m’zana loyamba kuti: “Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa.”—1 Akorinto 6:9-11.
Ena amakhululukira kutsutsa kwawo miyezo ya Baibulo pamaziko a chikondi. Wansembe wina ananena kuti: “Chikondi, makamaka chikondi cha wakunja ndi wokanidwa, chiri chiyeso chofunikira cha moyo wathu wauzimu.” Iye kenaka anamaliza kuti, “Kugonana kwa ofanana ziŵalo sikukanakhala konse nkhani kwa Kristu. Nkhani kwa iye ikanakhala yakuti: Kodi anthu amenewa amakhalirira m’miyoyo yawo, mosasamala kanthu ndi zimene iwo ali, m’njira yachikondidi?”
Koma Baibulo silimasokoneza chikondi ndi kukhudzidwa kwa maganizo. Chikondi cha Mulungu chimalinganizidwa ndi chilungamo ndipo chimaphatikizapo kudana ndi choipa. Baibulo mwamphamvu limalangiza kuti, “Inu okonda Yehova, danani nacho choipa.” (Salmo 97:10) Chikondi chowona chimaphatikizaponso chilango, popeza kuti “iye amene [Yehova, NW] amkonda amlanga.” (Ahebri 12:6) Chotero, atumiki ali ndi thayo ponse paŵiri “kuchenjeza m’chiphunzitso cholamitsa, ndi kutsutsa otsutsana naye.” (Tito 1:9) Ndipo kumbukirirani ichi: Pamene wansembe wakale akachita ntchito zake mokhulupirika, “[a]nabweza ambiri aleke mphulupulu.”—Malaki 2:5, 6.
Kunyalanyaza Miyezo ya Baibulo
Koma mwachisawawa, atsogoleri achipembedzo lerolino ali ngati makolo olekerera: amantha kupanda ana awo chifukwa ‘kutero sikukakhala kuwakonda.’ Kwa zaka makumi angapo atsogoleri achipembedzo mwakutero anyalanyaza miyezo ya Baibulo. Chotulukapo? “Popeza sambwezera choipa chake posachedwa atamtsutsa munthu, ana a anthu atsimikizadi mitima yawo kuchita zoipa.” (Mlaliki 8:11) Mwachitsanzo, ngakhale kuti kaimidwe ka lamulo ka Tchalitchi Chachikatolika kali kotsutsana ndi mayanjano a kugonana kwa ofanana ziŵalo, masankho ena anasonyeza kuti 55 peresenti ya Akatolika onse a mu U.S. anakhulupirira kuti winawake yemwe adziloŵetsa m’mayanjano a kugonana kwa ofanana ziŵalo angakhalebe Mkatolika wabwino.
Chinachake chofananako chinachitika kwa Aisrayeli akale pamene ansembe sanachirikize miyezo ya Mulungu. Iye ananena za iwo kuti: “Andichokera kunka kutali . . . Osati, Ali kuti Yehova?” Ndipo nchifukwa ninji? Chifukwa “ansembe sanati, Ali kuti Yehova? ndi iwo amene agwira malamulo sandidziŵa ine.” (Yeremiya 2:5-8) Mneneri Zefaniya ananena kuti: “Wosalungama sadziŵa manyazi” chifukwa chakuti “ansembe awo anaipsya malo opatulika, napotoza chilamulo.”—Zefaniya 3:1-5.
“Kanani Chisapembedzo”
Oganana ofanana ziŵalo omwe afuna kutumikira Mulungu ayenera kuchita tero pa miyezo yake—miyezo imene yasonyezedwa momvekera bwino m’Baibulo. Lerolino, monga mmene chinaliri m’zana loyamba, pali ogonana ofanana ziŵalo omwe athandizidwa ‘kufetsa ziŵalo za thupi lawo kulinga ku dama, chidetso, ndi chilakolako choipa.’ (Akolose 3:5) Mosakaikira, chimenechi sichinakhale chopepuka kwa ena, koma iwo aphunzira kufetsa zikhumbo zawo zachisembwere monga mmene ogonana osiyana ziŵalo ambiri anafunikira kufetsa zikhumbo zawo zolakwa kaamba ka wina wosiyana chiŵalo. Magulu onse aŵiri athandizidwanso mwa kuyanjana kokhazikika ndi mpingo wowona Wachikristu, umene ungawachirikize iwo m’chonulirapo chawo ‘kukana chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi kuti akhale ndi chilungamo ndi kudzipereka kwaumulungu.’—Tito 2:12.
Atsogoleri achipembedzo omwe amafooketsa miyezo ya Baibulo ndi kulola chimo sakuchitira ogonana ofanana ziŵalo ubwino uliwonse. Iwo ‘anganyenyetse makutu,’ koma samakhala ndi moyo mogwirizana ndi thayo lawo la “kulalika mawu.” Limeneli ndilo thayo lawo kwa ogonana ofanana ziŵalo—ndi kwa anthu onse.—2 Timoteo 4:1-5.
[Bokosi patsamba 31]
“Usamagonana ndi mwamuna, monga amagonana ndi mkazi; chonyansa ichi.”—Levitiko 18:22
“Chifukwa cha ichi Mulungu anawapereka iwo ku zilakolako za manyazi: pakuti angakhale akazi awo anasandutsa machitidwe awo achibadwidwe akhale machitidwe osalingana ndi chibadwidwe: ndipo chimodzimodzinso amuna anasiya machitidwe a chibadwidwe cha akazi, natenthetsana ndi chilakolako chawo wina ndi mnzake amuna okha okha anachitirana chamanyazi, ndipo analandira mwa iwo okha mphotho yakuyenera kulakwa kwawo.”—Aroma 1:26, 27