Kodi Zonsezi Zidzatha Liti?
KUDZILOŴETSA m’maseŵera akuthupi odzetsa mpumulo n’kosangalatsa ndi kwaumoyo. Koma mwatsoka, kukhala otengamo mbali kapena openyerera okha pa chochitika cha maseŵera kaŵirikaŵiri kumatanthauza kuloŵetsedwa m’chiwawa chopambanitsa, ndipo nthaŵi zambiri dziko lodzazidwa ndi kugwiritsira ntchito mankhwala.
Maseŵera amakono ali kokha chisonyezero cha dziko lachiwawa. Polankhula za zochitika mu Belgium mu 1985 zomwe zinapangitsa imfa ya anthu 39 m’masitandi a bwalo la maseŵera la mpira, wanthanthi Emanuele Severino adanena kuti: “Chikuvomerezedwa mwachisawawa kuti zochitika zonga zomwe zidachitika mu Brussels zimawoneka chifukwa chakuti anthu alibe chikhulupiriro m’makhalidwe aakulu a chitaganya chathu.” Kenaka iye adawonjezera kuti: “Chiwawa cha nthaŵi zathu sichimatulukapo chifukwa cha kusoŵeka kwa makhalidwe koma chifukwa cha kukhalapo kwa makhalidwe atsopano.”
Makhalidwe Atsopano m’Maseŵera
Kodi makhalidwe atsopano ameneŵa omwe akutchulidwa ndi Profesa Severino ngwotani? Ena ali kudzikonda kwa othamanga komwe kumapangitsa ngwazizo kukhala “onga milungu.”
Kenaka pali utundu ndi chotulukapo cha kuloŵereramo kwa ndale zadziko. Magazine otchedwa L’Espresso analongosola kuti: “Maseŵera akhala choyendetsera chachikulu chopititsira patsogolo mayanjano. Kuchulukira kwa zilakiko zomwe amapambana, kumakhalanso kukulira kumene mtunduwo umalingaliridwa.”
Ndalamanso ziri umodzi wa makhalidwe atsopano omwe akhala mbali ya dziko lamaseŵera. Ndalama zochulukira ndi ziwongola dzanja za malonda—kuyenera kwa kuwulutsa pa wailesi ya kanema, kufalitsa, malotale, ndi kuchirikiza—zimatsimikizira “mpikisano wosalamulirika,” ngakhale pakati pa oseŵera enieniwo. Yemwe kale anali woseŵera mpira ananena kuti mpila “sulinso seŵero. Iwo uli bizinezi.”
Lamulo la makhalidwe abwino lomwe liripo n’lakuti chipambano pa muyezo uliwonse, ndipo mogwirizana ndi makhalidwe atsopano a lerolino, izi zimatanthauza zirizonse—kuyambira pa chiwawa ponse paŵiri m’bwalo loseŵerera ndi m’masitandi kufikira ku chiwawa choyambitsidwa ndi ochemerera seŵerolo lisanayambike ndi pamapeto pake, kutemera mangolomera ndi zotulukapo zake zakupha kufika ku kuchitira moipa ndi kusalamulirika. Mzimu wa maseŵera, wotchedwa kuseŵera kwabwino, ukuwoneka kukhala chinthu chakale. Kodi iwo udzabwereranso? Polingalira zomwe zanenedwa, anthu amayembekezera choncho, koma nsongazo nzosalimbikitsa.
Mankhwala ndi Chiwawa—Kodi Zidzatha Konse?
Monga mmene Profesa Severino akuvomerezera, chiwawa m’maseŵera chiri kokha mbali imodzi ya chiwawa chachisawawa chomwe chikuzunza chitaganya chamakono. Kodi nchiyani chimene chiri choyambitsa cha chiwawa chochulukira choterocho? Ulosi wa Baibulo umatithandiza kumvetsetsa vutolo. Polankhula za masiku otsiriza a dongosolo iri la zinthu loipa, mtumwi Paulo anandandalitsa zikhotero zotsatirazi: ‘Anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, osayera mtima, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliwuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu.’ Ndipo anawonjezera kuti: “Koma anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire.”—2 Timoteo 3:1-5, 13.
Baibulo likulongosola kuti dziko liripoli, “ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Satana Mdyerekezi ndiye “woipayo” yemwe akuwononga zinthu zabwino, zonga ngati machitachita omangirira a maseŵera. Ndiye ali ndi thayo la mzimu wachiwawa. Amayambitsanso utundu, kudzikonda, ndi dyera lomwe lawononga chitaganya ndi maseŵera.
Koma monga munthu aliyense payekha, sitiyenera kugonjera ku mzimu wauchiwanda. Kupyolera m’kugwiritsa ntchito malamulo a makhalidwe abwino a Baibulo, tingakhoze “kuvula” umunthu wathu wakale ndi machitachita ake olakwa, kuphatikizapo makhalidwe achiwawa, ndi kuvala “umunthu watsopano,” womwe umatulutsa zipatso za mtendere.—Akolose 3:9, 10, NW; Agalatiya 5:22, 23.
Komabe, kodi padzakhaladi mapeto ku chiwawa ndi kutemera mangolomera m’maseŵera? Motsimikizirikadi! Liti? Pamene chiwawa ndi kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala m’chitaganya zidzatha. Kuwonjezeka komwe kulipo m’zoipa kumasonyeza kuti nthaŵiyo yayandikira!—Salmo 92:7.