Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g89 12/8 tsamba 5-6
  • Kodi Umoyo Nchiyani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Umoyo Nchiyani?
  • Galamukani!—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Umoyo ndi Njira Yamoyo
  • Sungirirani Chikhulupiriro Chanu ndi Umoyo Wauzimu
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Umoyo Wabwino—Kodi Mungachitenji Ponena za Iwo?
    Galamukani!—1989
  • Kodi Ndife Aumoyo Motani?
    Galamukani!—1989
  • Samalirani Thanzi Lanu M’njira Yogwirizana ndi Malemba
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Galamukani!—1989
g89 12/8 tsamba 5-6

Kodi Umoyo Nchiyani?

KODI munthu amakhaladi waumoyo wabwino kokha chifukwa chakuti samadzimva wodwala? Chabwino, kodi ndi mwakaŵirikaŵiri chotani pamene inu mwamva za anthu amene ankawoneka odzinzana bwino koma mwadzidzidzi anafa ndi chinthu chosayembekezereka? Maripoti amasonyeza kuti chifupifupi mmodzi mwa asanu a awo amene anafa ndi matenda a mtima chaka chirichonse sanasonyezepo chizindikiro n’ching’ono chomwe chakuti chinachake chinalakwika ndi iwo. Ndithudi, kudzimva bwino kapena wathanzi sikuli chitsimikiziro chakuti winawake ali ndi umoyo wabwino.

Mwachitsanzo, ganizirani za woseŵera mpira wa basketball wa zaka 22 zakubadwa wa kukoleji. Pa miyezo ya kusanthula kwa nthaŵi zonse, iye akalingaliridwa kukhala munthu waumoyo mu msinkhu wake. Koma usiku wina anafa—mwadzidzidzi. Kufufuza kunavumbula kuti chochititsa imfayo chinali kumwa kopambanitsa kwa mankhwala ogodomalitsa. Ngakhale kuti mwakuthupi anali wakawonekedwe kodzinzana, kodi iye ankakhala ndi moyo waumoyo? Kutalitali.

Pamenepa, m’chenicheni, umoyo uli woposadi pa kukhala wosadwala. Ndithudi, zopatsiridwa m’mitsempha ndi malo otizinga zimachita mbali yawo, koma pansi pa mikhalidwe yabwino, njira yathu yamoyo mwinamwake iri chochititsa chimodzi chofunika koposa cholamulira umoyo wathu. Zimene timadya ndi kumwa, mmene timakhalira achangu, kuchulukira kwa kupuma kumene timakhala nako, mmene timachitira ndi kupsinjika, ndi unyinji wa zizoloŵezi zina zaumwini mwinamwake zidzawongolera umoyo wathu kapena kuwuvulaza. Chotero, umoyo wathu umadalira ku mlingo wokulira pa zimene timachita ku uwo. Lamulo lamakhalidwe abwino Labaibulo lakuti, “Chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta,” limagwiranso ntchito mofananamo mu umoyo wathu wakuthupi.—Agalatiya 6:7.

Umoyo ndi Njira Yamoyo

Mwachitsanzo, nchodziŵika bwino lomwe kuti m’makampani aakulu ambiri a ku Japan, ogwira ntchito amapita m’chizolowezi cha maseŵera olimbitsa thupi akuya tsiku lirilonse. Chotulukapo chake? “Pali unyinji wa umboni wa chiŵerengero chokwanira chimene chimachilikiza lingaliro lakuti antchito a ku Japan ali anthu aumoyo koposa m’dziko,” akutero magazine a nkhani a Asiaweek. Kumbali ina, ripotilo likusonyeza kuti mu Japan “kansa iri mwinamwake chochititsa cha imfa imodzi mwa zinayi; kulephera kwa mtima ndi kuwundana kwa mwazi m’thupi chimodzi n’chimodzi cha izi chimapha munthu m’modzi mwa asanu, ndipo matenda a mopita mpweya amapha m’modzi mwa khumi ndi aŵiri. Mwamuna mmodzi mwa 52 aliwonse amadzipha yekha (kwa akazi, kudzipha kuli m’modzi mwa 70).”

Kodi ndemanga zimenezi zikumveka zosagwirizana kapena zotsutsana? Osati kwenikweni, pamene tisanthula nsonga. Pokhala ndi 40 peresenti ya achikulire onse osuta ndudu mamiliyoni zikwi 300 pachaka, Japan ndiyachiŵiri padziko lonse (yotsatiradi Greece) m’kusuta ndudu pa unyinji wonse. Kuwonjezerapo, chaka chirichonse amuna a ku Japan amamwa mamiliyoni zikwi 8 a mabotolo a mowa ndi mamiliyoni zikwi 1.5 a malita a sake (mowa waukali wakwawoko). Ichi chiri chofanana ndi kumwa kwa munthu mmodzi chifupifupi theka la lita la mowa weniweni pa mlungu. Chikakhaladi chodabwitsa ngati machitachita ovulaza oterowo sanakhale ndi chiyambukiro chowonekera paumoyo wa anthu.

Ngakhale kuti chinganenedwe kuti anthu a ku Japan ali ndi utali wokulira wa moyo wa anthu aliwonse ndikuti mlingo wa kusuta fodya ndi kumwa kwawo zakumwa zoledzeretsa uli wochepera kuposa ena, kuyerekeza koteroko kuli kopanda tanthauzo kotheratu. Chenicheni chiri chakuti anthu akufa adakali achichepere ndipo mosayenerera. Iwo angawoneke kukhala aumoyo kwenikweni kuposa ena, koma kodi alidi aumoyo?

Pamenepa, momvekeradi, umoyo wathu umatanthauza chiwonkhetso chonse cha njira yathu ya moyo ndi zizoloŵezi zathu za tsiku ndi tsiku. Umoyo wabwino umaphatikiza njira yolinganizika ya moyo yomwe imatulukapo thanzi lathu lakuthupi, maganizo, malingaliro, ndi mayanjano, kutitheketsa ife kuchita ndi malo otizinga ndi kutengamo chisangalalo chokwanira ndi chikhutiritso m’zochita zathu za tsiku ndi tsiku. Kodi tingachitenji kuti tikwaniritse zimenezo?

[Mawu Otsindika patsamba 6]

Zopatsiridwa m’mitsempha ndi malo otizinga zimachita mbali yawo, koma njira yathu yamoyo mwinamwake iri chochititsa chimodzi chofunika koposa cholamulira umoyo wathu

[Chithunzi patsamba 5]

Mawonekedwe a umoyo wabwino angakhale onyenga

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena