Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g89 12/8 tsamba 27-31
  • Gawo 23: 1945 Kupita Mtsogolo—Nthaŵi Yoŵerengera Yayandikira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Gawo 23: 1945 Kupita Mtsogolo—Nthaŵi Yoŵerengera Yayandikira
  • Galamukani!—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Baibulo Limanenanji?
  • “Mliri Wofuna Mtendere”
  • Atsogoleri Achipembedzo Akugwira Ntchito Molimba—Kaamba ka Chiyani?
  • Musataye Nthaŵi Iriyonse—Thawani kaamba ka Moyo Wanu!
  • Mtendere Weniweni—Kodi Udzachokera Kuti?
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Lolani “Mtendere wa Mulungu” Uchinjirize Mtima Wanu
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Palibe Mtendere kwa Amithenga Onyenga!
    Nsanja ya Olonda—1997
  • “Mphindi ya Mtendere” Ili Pafupi!
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Galamukani!—1989
g89 12/8 tsamba 27-31

Mtsogolo mwa Chipembedzo M’chiyang’aniro cha Nthaŵi Yake ya Kumbuyo

Gawo 23: 1945 Kupita Mtsogolo—Nthaŵi Yoŵerengera Yayandikira

“Chiyeneretso choyamba kaamba ka chimwemwe cha anthu chiri kuchotsedwa kwa chipembedzo.”—Karl Marx, katswiri wa zakakhalidwe ka anthu ndi wa zachuma wa ku Germany wa m’zaka za zana la 19

MOSASAMALA kanthu za kukhala ndi makolo achirabi Achiyuda ambirimbiri ku mbali zonse ziŵiri za banja lake, Karl Marx anabatizidwa monga Mprotesitanti pa msinkhu wa zaka zisanu ndi chimodzi zakubadwa. Koma pa msinkhu wake wachichepere, iye anagwiritsidwa mwala ndi chipembedzo ndi ndale zadziko. Iye anatsutsa kuti ngati mtundu wa anthu udati upeze chimwemwe, ziŵirizo zikafunikira kusinthidwa mokulira.

Baibulo limavomerezana ndi chimenechi. Komabe, pamene kuli kwakuti masinthidwe aakulu olingaliridwa ndi Marx sanabweretse kuwongokera kwenikweni, komwe kunanenedweratu ndi Baibulo kuchitika mu mbadwo wathu uno kudzalemekezedwa ndi chipambano chosatha. Sipangakhale chikaikiro chirichonse ku zimenezi.

Makamaka chiyambire 1914, liwongo lamwazi la chipembedzo chonyenga lafika pa mlingo wapamwamba kwenikweni. Chiyambire nthaŵiyo chipembedzo chonyenga chakanthidwanso ndi kusakondwereredwa ndi kuzimiririka kwa kuchirikiza kofala. (Onani nkhani ziŵiri zapita mu mpambo umenewu.) Mosemphana kotheratu, chipembedzo chowona chafutukuka mowonekera kwambiri chaka ndi chaka.

Koma kodi nchiyani chikubwerabe? Tsopano kuposa ndi kalelonse, kuli koyenerera kufunsa kuti, Kodi nchiyani chimene chiri mtsogolo mwa chipembedzo poyerekezera ndi nthaŵi yake yapita?

Kodi Baibulo Limanenanji?

Zochitika za m’zaka za zana loyamba za Nyengo Yathu ino zimapereka chiwunikiro pa nkhaniyo. Chifukwa chotengera chipembedzo chonyenga chachilendo, Israyeli anayang’anizana ndi mtsogolo monenedweratu kuthera m’chiweruzo cha Mulungu motsutsana ndi mtunduwo. Koma makonzedwe anapangidwa kwa awo ochita chipembedzo chowona kuthaŵa chiwonongeko cha dongosolo Lachiyuda. Yesu anawuza ophunzira ake kuti: “Koma pamene paliponse mudzawona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti chipululutso chake chayandikira. Pamenepo iwo ali m’Yudeya athaŵire kumapiri, ndi iwo ali mkati mwa uwo atuluke.”—Luka 21:20, 21.

Mu 66 C.E., magulu ankhondo Achiroma anazinga Yerusalemu. Mzindawo unawoneka kukhala utaukiridwa. Koma mwadzidzidzi magulu ankhondowo anabwerera, kupereka mwaŵi kwa Akristu wa kuthaŵira ku chisungiko. Komabe, lingaliro lirilonse lakuti Israyeli wampatuko anapulumuka chilango, linathetsedwa zaka zinayi pambuyo pake pamene Aroma anabweranso, kachiŵirinso anamangira tsasa mzindawo, ndipo pomalizira pake anautenga mwa kusakaza miyoyo kochititsa mantha kwa amene anali mkati. Masada, linga Lachiyuda lolimba lomalizira, linagwa zaka zitatu pambuyo pake. Komabe, chipembedzo chowona, monga chinachitidwira ndi Akristu okhulupirika, chinapulumuka.

Tsopano, mu mbadwo wathu, ulamuliro wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga ukuyang’anizana ndi ngozi mwachindunji. Kachiŵirinso “magulu ankhondo olalira” akukonzekera kupereka chiweruzo chaumulungu. Mofanana ndi magulu ankhondo Achiroma a m’zaka za zana loyamba omwe analinganizidwa kusunga Pax Romana (Mtendere Wachiroma), magulu ankhondo olalira a lerolino alinso chiŵiya chosunga mtendere. Ulosi wa Baibulo umasonyeza kuti magulu ankhondo pakati pa ziŵalo za mitundu ya UN adzakhala chiŵiya cha Yehova m’kuŵerengera komalizira ndi Yerusalemu wamakono, Dziko Lachikristu, limodzinso ndi Babulo Wamkulu yense.—Chibvumbulutso 17:7, 16.

Kodi zimenezi zidzachitika liti? Atesalonika Woyamba 5:3 akuyankha kuti: “Pamene angonena, mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo chiwonongeko chobukapo chidzawagwera, monga zowawa mkazi wapakati; ndipo sadzapulumuka konse.”

“Mliri Wofuna Mtendere”

Mkati mwa 1988 yemwe kale anali mlembi wa boma wa U.S. George Schultz ananena kuti “mtendere ukumveka kulikonse.” Katswiri wa lamulo lakunja kwa dziko analankhula za “mliri wofuna mtendere.” Nyuzipepala yotchuka ya mlungu ndi mlungu ya ku Germany Die Zeit inafunsa kuti: “Kodi zingakhale tero kuti, m’zaka za zana lodzala chotero ndi masoka, zaka zake khumi zomalizira zingazindikiritse mapeto a chiwonongeko ndi chiyambi cha nyengo ya kumanga kwamtendere?” Ndipo magazine a Time ananena kuti: “Mtendere ukuwopsyeza mu Iran-Iraq, Kampuchea, Afghanistan, kum’mwera kwa Africa ndiponso Central America.”

Chaka cha 1989, tsopano choyandikira mapeto ake, chakhalanso chodzala ndi nkhani za mtendere. Mu February nyuzipepala ya ku Germany Süddeutsche Zeitung inanena kuti: “Chiyambire chifupifupi 1985 tikukhala m’nyengo imene maiko amphamvu achita zoposa pa kukhala chete. . . . Lerolino pali kokha malo ochepera padziko lapansi kumene mphamvu ziŵiri zadziko sizikukumanira. . . . Pa mlingo uliwonse, palibe ndi kalelonse pamene zonenedweratu zawo zakhala zoyanjidwa chotero, mbali zonse ziŵiri zakhala zotsimikiza kwenikweni, ndipo masitepi ambiri atengedwa pa nthaŵi imodzimodzi m’njira yolondola.”

Posachedwapa zaka zisanu ndi chimodzi zapita, zinthu sizinawoneke kukhala zowala kwambiri. Mtola nkhani Roy Larson ananena kuti “mu 1983 yonse atsogoleri achipembedzo kuzungulira dziko anafuula ‘mtendere, mtendere,’ koma panalibe mtendere.” Kodi zochitika za dziko zodabwitsa chiyambire nthaŵiyo ziri kukwaniritsidwa kwa 1 Atesalonika 5:3? Sitinganene. Mosasamala kanthu za izo, chiri chotsimikizirika kuti lerolino, mu December 1989, “mtendere ndi chisungiko” zayandikira kukwaniritsidwa kuposa ndi kalelonse.

Atsogoleri Achipembedzo Akugwira Ntchito Molimba—Kaamba ka Chiyani?

Monga mmene Larson akusonyezera, atsogoleri achipembedzo sanakhale osakangalika m’kufunafuna mtendere. Mwakupitirizabe kutamanda kwake 1983, iye akutchula “ulendo wachipembedzo wofuna mtendere” wopita ku Central America ndi Caribbean umene John Paul II anawupanga. Ndiponso mkati mwa chaka chimenecho, Msonkhano Wadziko wa ku U.S. wa Abishopu Achikatolika unavomereza kalata ya upasitala yokhala ndi mutu wakuti “Chitokoso cha Mtendere.” Nthaŵi yochepa pambuyo pake, oimira a matchalitchi oposa 300 ochokera ku maiko 100 anakumana pa Msonkhano Waukulu wa chisanu ndi chimodzi wa World Council of Churches ndipo anavomereza chigamulo chofananacho. Alaliki ambiri Achiprotesitanti nawonso analoŵetsedwa m’chimene Larson anachitcha “kutanganitsidwa ndi mtendere kwa dziko lonse.”

Pamene inayambitsidwa mu 1948 ndi pa msonkhano wake wa 1966, World Council of Churches inatsutsa mwamphamvu kugwiritsira ntchito zida zamakono zakupha. Moyenerera, unyinji wa atsogoleri achipembedzo ndi akatswiri a maphunziro a zaumulungu atenga zida za mtendere, amuna onga ngati katswiri wa maphunziro a zaumulungu Wachiprotesitanti wa ku Germany Helmut Gollwitzer. Ku chiyambi kwa chaka chino, pa chochitika chokumbukira tsiku lake lakubadwa la zaka 80, iye anatamandidwa ndi nyuzipepala Yachiprotesitanti ya ku Switzerland ya mlungu ndi mlungu kukhala “katswiri wa maphunziro a zaumulungu wachangu m’zandale zadziko, nthaŵi zonse wokalamira mtendere,” amene “mogwiritsira ntchito chiphunzitso chake ndi ntchito yake ya ndale zadziko wasonkhezera mwamphamvu akatswiri ambiri a maphunziro a zaumulungu ndiponso bungwe lochirikiza mtendere m’tchalitchicho.”

Chotero, nzosadabwitsa kuti Babulo Wamkulu mokangalika anachilikiza Chaka cha Mtendere wa Mitundu Yonse cha 1986, cholinganizidwa motero ndi gulu la Mitundu Yogwirizana, limene tchata chake chimaitanira pa “kuchirikiza mtendere ndi chisungiko cha dziko lonse.” Mkati mwa chaka chimenecho, papa Wachikatolika, Akibishopu wa Anglican wa ku Canterbury, ndi atsogoleri achipembedzo ena 700, kuphatikizapo odzinenera kukhala Akristu, Abuda, Ahindu, Asilamu, okhulupirira mizimu ya akufa a mu Africa, nzika za ku America (Amwenye), Ayuda, Asikh, Azoroastria, Ashinto, ndi Ajain, anakumana pamodzi pa Assisi, pafupi ndi Rome, kukapempherera mtendere.

Posachedwapa kwenikweni, mu January 1989, Sunday Telegraph ya ku Sydney, Australia, inalemba kuti ziŵalo za “chikhulupiriro Chachibuda, Chikristu, Chihindu, Chiyuda, Chisilamu, Chisikh, Chiunitarian, Chibaha’i, Chikonfyushani, Chijain, Chishinto, Chitao, Chiraja Yoga ndi Chizoroastria” zinakumana mu Melbourne kaamba ka Msonkhano wachisanu wa Dziko Lonse pa Chipembedzo ndi Mtendere. Mowonekeradi, “nthumwi zoposa 600 zochokera m’maiko 85 . . . zinavomereza kuti mikangano yochititsidwa ndi kusamvana kwachipembedzo inagwiritsiridwa molakwa kwa nthaŵi yaitali kukhala chimodzi cha zochititsa nkhondo.”

Kudziloŵetsa kwa chipembedzo m’kufunafuna mtendere kumatsimikizira chimene Dag Hammarskjöld, yemwe kale anali mlembi wamkulu wa Mitundu Yogwirizana, ananena nthaŵi ina kuti: “Gulu la [UN] ndi matchalitchi akuimirira pheŵa ndi pheŵa monga otengamo mbali m’kuyesayesa kwa anthu onse okoma mtima, mosasamala kanthu za chiphunzitso chawo kapena mtundu wa kulambira, kukhazikitsa mtendere pa dziko lapansi.”

Komabe, ndawala zotsutsa za Babulo Wamkulu, ziwonetsero zake zapoyera, ndi mitundu ina ya machenjera ake owonjezereka a kudziloŵetsa kwachipembedzo m’zochitika za ndale zadziko zidzatsogolera ku kulephera kwake.a Iye wachititsa kale mkangano waukulu, monga mmene Albert Nolan, friar wa ku Dominican wochokera ku South Africa, posachedwapa anavomerezera, akumati: “Njira yokha yokhutiritsa yopezera mtendere m’chigwirizano ndi chifuno cha Mulungu ndiyo kudziloŵetsa m’kumenyana. . . . Kuti tifikire kuchepetsa zida zankhondo, kukangana kwa maboma kuli chifupifupi kosapeŵeka.”

Mlekeni Babulo Wamkulu apitirizebe kufuulira mtendere. Mlekeni papa apitirizebe kupereka dalitso lake lamwambo la Urbi et orbi (ku mzinda [Rome] ndi dziko) pa Krisimasi ndi Isitala. Mlekeni apitirizebe kuyerekezera—monga mmene anachitira May watha—kuti chitonthozo cha nthaŵi ino cha mikangano ya ndale zadziko chiri yankho la Mulungu ku mapemphero “Achikristu.” Kulankhula mawu a mtendere ndi kulozeretsa kwa iyemwini madalitso a Mulungu sikungachotsere Babulo Wamkulu nthaŵi yake yapita yokhetsa mwazi. Iko kumamuika chizindikiro kukhala wotsekereza mtendere pakati pa mtundu wa anthu, ndiponso pakati pa anthu ndi Mulungu, komwe kwakhalapo nthaŵi zonse. Mwachindunji kapena mosakhala mwachindunji, vuto lirilonse la mtundu wa anthu lingatsatiridwe mpaka kukafika pakhomo pake!

Nchoseketsa chotani nanga kuti chipembedzo chonyenga chikupitirizabe kumenyera, mogwirizana ndi UN, kubweretsa “mtendere ndi chisungiko” zimene kwenikweni zidzayambitsa chiwonongeko chake! Mapeto a chipembedzo chonyenga adzalemekeza Mulungu wa chipembedzo chowona, amene akuti: “Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.”—Agalatiya 6:7.

Musataye Nthaŵi Iriyonse—Thawani kaamba ka Moyo Wanu!

Nthaŵi ya kuŵerengera ya chipembedzo chonyenga yayandikira! Njira yokha yopeŵera kutaya moyo ndiyo kuchithaŵa popanda kuchedwa. (Chibvumbulutso 18:4) Kuŵerenga chafutambuyo kofika pa chiwonongeko kwayamba kale.

Pambuyo pakuti dziko lapansi la Mulungu lokongola lachotsedwera chipembedzo chonama ndi chipembedzo cha chiphamaso chochilikiza utundu, chipembedzo chowona chokha pansi pa boma laumulungu chidzakhalabe. Ndi mawonekedwe okopa mtima chotani nanga kwa anthu opulumuka masinthidwe aakulu ameneŵa! Kodi mudzakhala pakati pawo? Kodi mungakonde kusangalala kosatha mu “Kukongola Kwamuyaya kwa Chipembedzo Chowona”? Ngati nditero, phunzirani mmene mungachitire mwa kuŵerenga nkhani yomalizira mu mpambo uno mu Galamukani! ya January 8, 1990.

[Mawu a M’munsi]

a Bukhu la Revelation—Its Grand Climax At Hand! lofalitsidwa mu 1988 ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., limalongosola mmene chimenechi chidzachitikira.

[Chithunzi patsamba 29]

Malikulu a UN mu New York ndi chifano choumba cha mtendere wa dziko—munthu akusula lupanga kukhala cholimira

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena