Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 1/8 tsamba 5-7
  • Ana Opanda Kokhala—Kodi Nchifukwa Ninji Kuli Kovuta Kuthandiza?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ana Opanda Kokhala—Kodi Nchifukwa Ninji Kuli Kovuta Kuthandiza?
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Ena Angathandizidwire
  • Mmene Ena Apambanira
  • Chifukwa Chimene Kuyesayesa kwa Munthu Kumalephera
  • Ana Opanda Kokhala—Kodi Pali Yankho?
    Galamukani!—1990
  • Ana Opanda Kokhala—Kodi Ndani Ali ndi Liŵongo?
    Galamukani!—1990
  • Kodi N’chiyani Chimayambitsa Vuto la Kusowa Pokhala?
    Galamukani!—2005
  • Kufunafuna Njira Zothetsera Mavuto a Ana Kukupitirizabe
    Galamukani!—2000
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 1/8 tsamba 5-7

Ana Opanda Kokhala—Kodi Nchifukwa Ninji Kuli Kovuta Kuthandiza?

PA OCTOBER 14, 1987, Jessica McClure wachichepere anatsekeredwa mamita 6.7 kunsi kwa chitsime chamadzi chosagwiritsiridwa ntchito mu United States. Kwa maola 58 ovutikira, antchito yopulumutsa anakumba kupyola thanthwe lolimba kuti apeze njira yofikira mtsikanayo wa miyezi 18 yakubadwa. Chochitikacho chinadzala m’masamba akutsogolo a manyuzipepala ndi mitima ya amdziko lonselo, ndipo kuwonetsera kwa pawailesi yakanema kunasunga openyerera ake ali odera nkhaŵa kufikira Jessica anatulutsidwa kuchoka m’dzenje lakudalo ali wamoyo.

Koma Jessica anali ndi kokhala. Ngakhale ndi tero, mwachilendo, kusauka kwa ana opanda kokhala sikumadzutsa nkhaŵa yofananayo mpang’ono pomwe. Kodi chifukwa chingakhale chakuti mkhalidwe wawo ndiwogwirizanitsidwa ndi umphaŵi? Akumasanthula m’khalidwe wa osowa, mlembi wa World Health, magazine ya World Health Organization, analengeza kuti: “Amphaŵi m’mizinda sali nzika zenizeni za dziko lawo, popeza kuti alibe kuyenera kwa ndale zadziko, mayanjano, kapena kwa zachuma. Amphaŵi amakalamba mofulumira ndi kufa adakali achichepere.” Chotero, masinthidwe akuya m’njira imene maboma ndi anthu amawonera amphaŵi amafunikira pamene chuma chadziko chisanapereke zakudya zokwanira, zovala ndi nyumba kaamba ka iwo.

Mmene Ena Angathandizidwire

Mfundo zolongosoledwa mu Chilengezo cha UN cha Zoyenerera Mwana ziridi zabwinopo, koma kodi nchifukwa ninji zimawonekera kukhala zosafikirika? (Onani bokosi.) Mwachisawawa, anthu amakonda ana ndipo amawafunira zabwino koposa. Pambali pa icho, ana ndi ofunika kaamba ka ubwino wa kutsogolo wa dziko. Mu Latin America Daily Post, James Grant wa UNICEF akunena kuti: “Ndiiko nkomwe, ali ana amene potsirizira pake ayenera kutsogolera maiko awo kuchoka m’kutekeseka kwa zachuma.” Ripoti limasonyeza, akupitiriza tero Grant, “kuti kuwonongera pa chisamaliro chachikulu chaumoyo ndi maphunziro oyambirira kungatsogolere ku ziwonjezeko zowonekera mu uchikumbe ndi kuchuruka kwa chuma.” Maiko onga ngati Brazil amadziŵa monenetsa za chithunzi choipa choperekedwa ndi mkhalidwe wa ana m’makwalala ndi chiwawa chogwirizana ndi ichi. Mwamwaŵi, mu Brazil kuyesayesa kukupangidwa kuthetsa vutolo kupyolera m’zaufulu, nyumba za opanda makolo, kosungira ana amasiye, ndi malo a kukonzanso.

Maboma ena akuwona phindu la kuchilikiza kumanga manyumba kodziyambira kwa mabanja aumphaŵi ndi zitaganya mmalo mwa kungowamangira manyumba. Mwanjirayi, amphaŵi enieniwo amakhala magwero osintha.

Chotero, pambali polandira thandizo kuchokera ku ochilikiza osiyanasiyana, mabanja aumphaŵi ayenera kukhala ofunitsitsa kuchita mbali yawo. Banja limachita zochurukira m’zachuma ndi m’zamayanjano pamene ligwirizana pamodzi ndi kuthetsa mavuto ake. Ndithudi, ziwalo zonse zothekera zingathandizire ku ndalama zolinganizidwa zabanja.

Mmene Ena Apambanira

Ana ena opanda kokhala akhala okhoza kuchoka mumkhalidwe umenewo. Lingalirani chitsanzo cha Guillermo. Asanabadwe, banja lawo linkakhala m’mudzi waung’ono koma chifukwa cha mkhalidwe waumphaŵi m’zachuma anasamukira ku likulu la dziko. Pamene Guillermo anali ndi miyezi itatu yakubadwa, atate wake anaphedwa; kenaka, zaka zoŵerengeka pambuyo pake, amai wake anamwalira, akumasiya anawo kwa agogo awo aakazi. Chotero, kuchiyambiyambi m’moyo, Guillermo anakhala mwana wa m’khwalala. Tsiku ndi tsiku, kwa zaka zisanu, iye ankayendayenda m’maresitilanti ndi m’mabawa, akumapemphapempha zakudya ndi ndalama kuti asamalire zosowa za banja lake, kuyendayenda m’makwalala mochedwerako usiku. Anthu achifundo amene anamudziŵa m’makwalala anam’phunzitsa mfundo za udongo waumwini ndi kakhalidwe. Pambuyo pake, anatengedwa ali m’khwalala ndi othandiza aboma ndi kuikidwa mosungira ana, kumene analandira zakudya ndi maphunziro. Mboni za Yehova zinamuthandiza kuwona kuti Mlengi anali wokondweretsedwa ndi iye monga munthu payekha, ndipo anasamalira zosowa zake zauzimu. Atasangalatsidwa ndi kuwona mtima ndi ubwenzi wa Mbonizo, Guillermo pambuyo pake ananena kuti: “Kodi ndani amene angathandize wachichepere yemwe m’chenicheni adakula popanda chitsogozo ndi chilangizo? Kokha abale achikondi anandipatsa ine thandizo loterolo, pambali pa thandizo la ndalama.” Guillermo anabatizidwa pa msinkhu wa zaka 18 zakubadwa. Tsopano iye akutumikira monga chiwalo cha ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society m’dziko lawo.

Kenaka pali João, amene pamene adali wamng’ono anathamangitsidwa panyumba ndi atate wake chidakwa limodzi ndi abale ake. Koma kampani yamasitolo inamulowetsa ntchito João. Pokhala wakhama, João anapambana ndipo mofulumira anapeza kudaliridwa ndi antchito anzake ndi ena. Tsopano iye ali munthu wachimwemwe wokhala ndi banja lake. Lingaliraninso Roberto wa zaka 12 zakubadwa. Nayenso anathamangitsidwa ndi banja lake. Iye anapita m’ntchito yoyeretsa nsapato ndi kugulitsa maswiti, ndipo pambuyo pake anagwira ntchito monga wopaka utoto. Kufunitsitsa kuphunzira ndi kugwira ntchito kunathandiza ponse paŵiri João ndi Roberto kulaka zopinga zambiri. Iwo amakumbukira nthaŵi za kuda nkhaŵa ndi kupanda chisungiko monga ana opanda kokhala, koma analimbitsidwa ndi kuphunzira kwawo Baibulo ndi Mboni za Yehova. Zitsanzo zochepera zimenezi zimasonyeza kuti ana mwachibadwa amapola msanga ndipo, atakhala ndi thandizo labwino, potsirizira pake angalake mikhalidwe yoipitsitsa, ngakhale kutaidwa.

Kuwonjezerapo, pamene achichepere alandira chitsogozo chaukholo mogwirizana ndi Mawu a Mulungu, mabanja okhazikika amaturukapo, ndipo mavuto onga ngati kutaidwa ndi kuipsya ana samachitika.

Chifukwa Chimene Kuyesayesa kwa Munthu Kumalephera

Mosasamala kanthu za chimenecho, kukhalapo kwa mamiliyoni a ana opnda kokhala kumawunikira kulephera kwa anthu kuthetsa vuto lokulira limeneli. Mtsogoleri wa gulu lothandizira kakhalidwe kabwino ka ana anagwidwa mawu mu Time kukhala akunena kuti: “Munthu wosokonezeka maganizo ndi kupenga, munthu wodwala—chiwerengero cha anthu odwala, osalimba—sichingachite ngati othandizira chitukuko.” Magazine imodzimodziyo inaneneratu kuti monga choturukapo cha chimenechi, dziko limodzi la mu Latin-America “likatopetsedwa ndi mamiliyoni a achikulire osadyetsedwa mokwana, opanda ukatswiri wantchito ndi osaphunzira kotero kuti adzakhala chothodwetsa ku mtundu uliwonse wa dongosolo lotsungula.”

Mutalingalira pa zomwe zakambidwazo, kodi mukuganiza kuti ziyambukiro za kudya mopereŵera, kuipsyidwa kwa kugonana, ndi chiwawa zingathetsedwe kwakukulukulu ndi zothetsera za anthu? Kodi mulingalira kuti programu iriyonse yopangidwa ndi munthu ingachotse ana onse omwe ali m’makwalala pambuyo pa kulimbikira kwao kukhala ndi moyo m’makwalala pakati pa anthu ankhalwe, osalamulirika? Kodi mungaganizire za programu iriyonse yophunzitsira makolo kuchita mwathayo kulinga kwa ana awo? Mwachisoni, kuyesayesa kwa anthu, mosasamala kanthu za kuwona mtima kwake, sikungathetseretu mavuto a ana opanda kokhala.

Chifukwa ninji? Winawake kapena chinachake chikuchinga kuti vutoli lisathetsedwe. Mosangalatsa, Yesu anazindikira munthu, yemwe anamutcha “wolamulira wadziko.” (Yohane 14:30) Iye ali Satana Mdyerekezi. (Onani tsamba 12.) Chisonkhezero chake cha machenjera olikwira mtundu wa anthu ndicho chochinga chokulira choletsa kuthetsa mavuto amenewa ndi kuchifikira chimwemwe chowona. (2 Akorinto 4:4) Chotero, kuchotsedwa kwa zolengedwa zauzimu zimenezo kuli koyenerera ngati mikhalidwe yolungama kaamba ka ana onse opanda kokhala ndi anthu opanda mwaŵi iti ifikiridwe. Chotero, pamenepa, kodi tingaganizire za dziko lopanda ana a m’makwalala ndi achisoni? Kodi pali chiyembekezo chenicheni, chosatha kaamba ka ana opanda kokhala?

[Mawu Otsindika patsamba 6]

‘Kodi ndani yemwe angakonde kuthandiza wachichepere yemwe adakula popanda chitsogozo ndi chilangizo?’

[Bokosi patsamba 7]

Chilengezo cha UN cha Zoyenerera Mwana:

◼ Kuyenerera kukhala ndi dzina ndi mtundu.

◼ Kuyenerera kufunidwa, kukondedwa, ndi kumvetsetsedwa ndi chisungiko cha zinthu za kuthupi.

◼ Kuyenerera kukhala ndi kadyedwe kokwana, nyumba, ndi mautumiki a mankhwala.

◼ Kuyenerera kupatsidwa chisamaliro chapadera ngati ndiwopunduka, kaya kukhale kwakuthupi, kwa maganizo, kapena mayanjano.

◼ Kuyenerera kukhala pakati pa oyamba kulandira chitetezero ndi thandizo m’mikhalidwe yonse.

◼ Kuyenerera kutetezeredwa molimbana ndi mitundu yonse ya kunyalanyaza, nkhanza, ndi kudyerana masuku pamutu.

◼ Kuyenerera kukhala ndi mwaŵi wokwana wa kuseŵera ndi zosangulutsa ndi mwaŵi wofanana ku maphunziro aulere ndi osasankha, kutheketsa mwana kukulitsa kuthekera kwake kwaumwini ndi kukhala chiwalo chaphindu cha chitaganya.

◼ Kuyenerera kukulitsa kuthekera kwake konse m’zochita zaufulu ndi ulemu.

◼ Kuyenerera kuleredwa mumkhalidwe wolingaliridwa wopirira, waubwenzi pakati pa anthu, mtendere, ndi ubale wa ponseponse.

◼ Kuyenerera kusangalala ndi kuyenera kumeneku mosasamala kanthu za fuko, khungu, mwamuna kapena mkazi, chipembedzo, malingaliro a ndale zadziko kapena ena ake, kokhala kapena chiyambi cha mayanjano, ndi chuma, kubadwa, kapena zinthu zina.

Chidule chozikidwa pa Everyman’s United Nations

[Mawu a Chithunzi patsamba 5]

Reuters/Bettmann Newsphotos

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena