Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Bwanji Ponena za Ntchito Zowonetsa Masitayelo ndi Mipikisano ya Kukongola?
“PAMENE tinali paulendo wopita ku New York chaka chatha,” akukumbukira tero Amy wa zaka 12 zakubadwa, “mwamuna wina mwini hotela anauza amayi anga kuti, ‘Muyenera kuloŵetsa msungwana wanu mu sukulu yowonetsa masitayelo. . . . Iye ngokongola.’”
Achichepere ambiri okongola akhala ndi zokumana nazo zofanana. Racine wa zaka khumi ndi zisanu zakubadwa analandira foni kuchokera kwa mwamuna yemwe anayesera kunyengerera iye ndi mlongo wake wamng’ono kuloŵa ntchito yowonetsa masitayelo. Mkazi wachichepere wa ku South Africa anapemphedwa kutengamo mbali mu mpikisano wa kukongola. Ndipo zopereka zimenezo zodzetsa ndalama sizimalekezera kwa atsikana okha. Jonathan wachichepere anapatsidwa ntchito monga mwamuna wowonetsa masitayelo.
Inde, kuzungulira dziko lonse, amuna ndi akazi achichepere ndipo ana a misinkhu yonse akuloŵetsedwa ntchito zowonetsa masitayelo, ziwonetsero zosonyeza kukongola, ndi zina zofananako. Mu United States mokha, zimachitiridwa ripoti kuti zikwi mazana za mipikisano ya kukongola imachitidwa chaka chirichonse. Opambana amalandira zikwi za ndalama za madola, mphotho, ndi maphunziro. Kwa owerengeka, kupambana pa chiwonetsero cha kukongola kwatulukapo zosangulutsa zodzetsa ndalama ndi ntchito zowonetsa masitayelo.
Mkazi wina wachichepere akunena kuti: “M’moyo wanga wonse ndakhala ndikufuna kukhala wowonetsa mafashoni—kuwonetsa masitayelo a zovala kaamba ka magazine akumaloko ndi pa ziwonetsero za mafashoni. Malipiro amakwera kuchokera pa $25 kufika ku $100 pa ola.” Ngakhale ndi tero, zasimbidwa kuti, owonetsa mafashoni ena otchuka amapeza malipiro ochuluka kufika ku $2,500 pa tsiku! Chotero, nzosadabwitsa kuti, Akristu achichepere ena okongola akhumbira kupezera ndalama pa mawonekedwe awo abwino. Kodi mungachite motani mutapatsidwa mwaŵi wokhumbirika woterowo?
Kukongola Kungakhale Kopindulitsa
Ponena za namwali Wachiyuda Estere kunanenedwa kuti iye anali “wamawonekedwe okoma, ndi wokongola.” (Estere 2:7) M’chenicheni, inu munganenedi kuti iye mosadzifunira anatengamo mbali mu mpikisano winawake wa kukongola. Kodi zochitikazo zinali zotani? Mkazi wamkulu wa ku Perisiya wotchedwa Vasiti adachotsedwa pa malo ake kaamba ka kupanda chigonjero. Kuti apeze woloŵa malo woyenera, Mfumu Ahaswero anasokhanitsa pamodzi anamwali onse okongola a m’dziko lake. Iye anakonza kuti, akazi achicheperewo apatsidwe chakudya chapadera ndi kumalandira mauthenga mokhazikika limodzi ndi kuwapatsa mafuta onukhira ndi mafuta a mure kwa nyengo ya miyezi 12. Kenaka mkazi aliyense anakhala ndi nthaŵi ya kuyesedwa. Ndipo pamene nthaŵi ya Estere inafika, iye anasankhidwa kukhala mkazi wamkulu!—Estere 1:12–2:17.
Ngakhle kuli tero, kodi nchifukwa ninji Estere anatengamo mbali? Kodi iye anali wofunafuna ulemelero mopanda pake? Ayi, Estere ankatsatira chitsogozo cha Yehova, chimene anafunafuna mobwerezabwereza kupyolera mwa msuwani ndi msungi wake waumulungu, Moredekai. (Estere 4:5-17) Mwamuna woipa wotchedwa Hamani ankakonza chiwembu cha kuwononga anthu a Mulungu, mtundu wa Israyeli. ‘Mpikisano wa kukongolawo’ unalola Yehova kuchititsa Estere kuloŵa malo apamwamba omwe akamkhozetsa kulepheretsa chiwembuchi. Chotero mawonekedwe okongola a Estere anatsimikizira kukhala dalitso kwa anthu a Mulungu onse!
Bwanji ponena za lerolino? Ndithudi mawonekedwe a munthu sindiwo chinthu chofunika koposa m’moyo.a Mosasamala kanthu za chimenecho, atatsagana ndi kudekha ndi kudzichepetsa, mawonekedwe okongola angakhale chuma. Komabe, kodi izi zikutanthauza kuti kuwonetsa masitayelo kapena kutengamo mbali m’ziwonetsero za kukongola kuli njira yanzeru ya kugwiritsira ntchito chuma chimenechi? Kapena kodi pali mbali zina zofunika kulingalira zimene ziri kumbuyo kwa ubwino wa kutchuka, ulemelero, kapena chuma?
Kumbuyo kwa Ubwinowo
Kuwonetsa mafashoni kuli ndi maubwino ake. Zovala zabwino, zokometsa zamtengo, malipiro abwino, ziyembekezo zakuyenda maulendo ndi kuwonekera pa wailesi ya kanema—zonsezi ziridi zokhumbirika. Kuwonjezerapo, maphunziro a kuwonetsa masitayelo kwathandiza amuna ndi atsikana achichepere ambiri kuyenda modekha ndi kulankhula ndi chidaliro ndi chifatso. Koma kumbuyo kwa ukomawo, ubwino, ndi kukongola konseku kungabisale ngozi zenizeni kaamba ka Mkristu.
Sikuti kuwonetsa masitayelo nkoipa mwa iko kokha. Kuwonetsa masitayelo kwina kumatumikira chifuno chabwino: kuchititsa chinthu chopangidwacho kuwoneka chokhumbirika. Nchifukwa chimodzi chimene manja okongola amagwiritsiridwa ntchito kuwonetsa polishi ya zikhadabo m’zithunzi za m’magazine ndi m’ziwonetsero zamalonda za pa TV. Mofananamo, amuna ndi akazi a thupi loyima bwino amagwiritsiridwa ntchito kuwonetsera zovala. Malinga ngati chovalacho chiri chodekha, sipangakhale choletsa kwa Mkristu kulipiridwa kuti achivale kuwoneta sitayeloyo.
Ngakhale kuli tero, pali mavuto ambiri okhala m’kuwonetsa masitayelo amene nthaŵizonse ali ovuta kuwapewa. Mwachitsanzo, kodi mukachita motani, ngati munayitanidwa kukavala chinachake chosakhala chachikatikati kapena chosayenera Mkristu? Kapena ngati wokopa zithunzi anakukakamizani mwamachenjera kuti muyime mwanjira yokhumbirika, yodzutsa chilakolako? Kuwonjezerapo, wina sangakhale wotsimikiza nthaŵi zonse mmene zithunzizo zidzagwiritsiridwa ntchito. Mwachitsanzo, zithunzizo zingawonekere m’zisonyezero zochirikiza matchuti a chipembedzo chonyenga kapena zamakhalidwe achisembwere.
Kenaka pali chiyambukiro chimene ntchito yoteroyo ingakhale nacho pa umunthu wa munthu, kuchirikiza kukula kwa zikhoterero zoipa. Chigogomezero chopitirizabe pa mawonekedwe akunja m’malo mwa “munthu wobisika wamtima” chachititsa owonetsa masitayelo kukhaladi osaphula kanthu. (1 Petro 3:4) Ndiponso, kuchita ndi zovala zodula kwambiri, zokometsera zamtengo ndi zina zofananako, kungachititse malingaliro a kukondetsa zakuthupi kuyamba kuzika mizu.—1 Timoteo 6:10.
Ntchito yowonetsa mafashoni irinso yoipa kaamba ka kuwunikira wina kwa anthu osiyanasiyana, amuna ndi akazi, omwe amaumilira pa mayanjano akugonana mosinthanitsana ndi kupita patsogolo m’ntchito. Monga mmene wina yemwe kale anali wowonetsa masitayelo anadziŵitsira kuti: “Kunena mosabisa, uyenera kugonjera [m’zakugonana] kuti upite patsogolo.” Ena amanena kuti kugonana kwa ofanana ziwalo nkofala pakati pa amuna owonetsa masitayelo. Ngakhale kuti izi sizingakhale zowona, mungakhale mavuto ambiri m’kusonyeza masitayelo kuposa ndi m’ntchito zina.
Ziwonetsero za Kukongola
Zambiri zomwe zakambidwazo zinganenedwenso ponena za ziwonetsero za kukongola. Komabe, kuwonjezerapo, palinso chididikizo cha mpikisano wokulira. Zimenezi zachititsa opikisana ena kuchitira upandu opikisana anzawo mwadala. Mogwirizana ndi ripoti lina, “opikisana ena ali ofunitsitsa chilakiko m’chakuti amafikira pa kupaka lipstick (mafuta a kumilomo) ku zovala zosambira za opikisana nawo kapena ‘mwangozi’ kukhathamiritsa zovala zawo zogona nazo ndi Coke.”
Ndiponso, eniŵake a ziwonetsero za kukongola amafuna atsikana awo kudzipereka kotheratu monga oyimira malonda awo ndi ochirikiza unansi wawo kwa anthu. Kaŵirikaŵiri izi zimafuna wina kudziyanjanitsa ndi anthu kufikira mbandakucha. Mkazi wachichepere wina anauzidwa kuti: “Wokondedwa, suyenera kutopa konse. Tangokumbukira chimenecho. Uyenera kukhala woyamba kufika pa phwando ndipo uyenera kukhala wotsirizira kuchoka.” Pansongayo, izi zingawunikire Mkristu wachichepere ku mayanjano oyipa ndipo kungamtsogoleredi kulowa m’chikondi ndi wosakhulupiria.—2 Akorinto 6:14.
Chomalizira, pali nsonga yakuti mipikisano ya kukongola imanyalanyaza lamulo la makhalidwe abwino la Baibulo la pa Aroma 1:25, limene limatsutsa awo ‘olemekeza ndi kupereka utumiki wopatulika ku chilengedwe m’malo mwa Yemwe adalenga.’ (Yerekezani ndi Machitidwe 12:21-23.) Pa maziko amenewo okha, Mkristu wachichepere akachita bwino kukana kutengamo mbali mumpikisano wa kukongola ngakhale ngati unali pa mlingo waung’ono pa sukulu.
Kukongola Kwenikweni
Achichepere otchulidwa poyambapo anayesa nsongazi popanga zosankha zawo. Ngakhale kuti kukhala ndi ntchito yowonetsa masitayelo sikungakhale kolakwa mwa iko kokha, Amy ndi Racine anasankha kusatero. Jonathan mofananamo anakana ntchito monga mwamuna wowonetsa masitayelo ndipo tsopano akutumikira pa malikulu a dziko lonse a Mboni za Yehova, akuchita ntchito ya utumiki wa nthaŵi zonse. Koma mtsikana wina wokongola anatengamo mbali ndi kupambana mipikisano ya kukongola iŵiri. Lerolino, iye sakupezekanso ku misonkhano Yachikrstu. Ngowona chotani nanga mwambi wakuti: “Chikomekome cha nkhuyu m’kati muli nyerere; kukongoladi nkwabwino ndi mkati momwe.”
Tikukumbutsidwanso za Estere. Chifukwa cha kukongola kwake kwakuthupi, iye anaphatikizidwa pa mzere wa mfumu wosankhapo mkazi. Komabe, kunali kudeka kwake, chigonjero, chimvero, ndi kupanda dyera zimene zidampangadi kukhala wokongola. (Estere 2:13, 15-17) Iye anachitira chitsanzo mawu a Petro akuti: “Kukometsera kwanu kusakhale kwa kunja, kuluka tsitsi ndi kubvala za golidi, kapena kubvala chobvala; koma kukhale munthu wobisika wamtima, m’chobvala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu.” (1 Petro 3:3, 4) M’kupita kwa nthaŵi, kukulitsa mikhalidwe Yachikristu imeneyi kudzakhala kwaphindu lokulira kuposa mphotho zosakhalitsa za kukongola kwakuthupi.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yakuti “Kodi Mawonekedwe Ali Ofunika Kwambiri Chotani?” yowonekera m’kope la Galamukani! ya November 8, 1986.
[Chithunzi patsamba 18]
Mikhalidwe Yachikristu iri yaphindu lokulira kuposa mphotho zosakhalitsa za kukongola kwakuthupi