Mkangano Wakalekale wa Apongozi
“SINDIKUFUNA kuwonanso nkhope yanu!” Fujiko anazazira motero apongozi ake, a Tomiko. Fujiko anatopa ndikutumidwatumidwa. Ngakhale kuti anayesa kuwonekera kukhala wodekha pamaso, mkati mwake ankavutika maganizo. “Ndinaipidwa nazo,” iye akutero. “Sindinamve bwino. Sindinafunedi kukhala mwanjirayo tsiku lirilonse.”
Ntchemberembaya ina yokhala yokha m’Japan ikunena kuti: “Ndinanyanyalidwa ndi mwana wanga wamwamuna ndi mkazi wake. Tsopano sindifunikira kudera nkhaŵa ndi enawo, ndipo ndimachita zimene ndikonda, koma ndimamva kukhala wosungulumwa dzuŵa litaloŵa.”
Mkangano wakalekale wa mpongozi ndi mkazi wa mwana wake ngwapadziko lonse. “Mwachisoni,” akutero Dulcie Boling, mlembi wa magazine mu Australia, “akazi ena nthaŵi zonse amakhala odukidwa ndi akazi a ana awo. . . . Nzochepera zimene mungachite kusiyapo kumwetulira ndi kupirira.” M’maiko Akum’maŵa, kuli ngakhale miyambi yonena za kunyanyalidwa kwa ntchemberembaya kusiidwa m’mapiri, zochitika zosonkhezeredwa ndi akazi a ana awo.
Lerolino, mkangano umenewu ngwocholowanadi mowonjezereka kuposa ndi kalelonse. Mogwirizana ndi ziŵerengero, zaka za moyo zikuwonjezereka, mabanja akukhala ochepachepa, ndipo mpata wa zaka zamoyo pakati pa amuna ndi akazi ukutakata. Kodi chotulukapo chakhala chiyani? Pamene akazi ochurukirapo akukhala ndi moyo zaka zawo za m’ma 70 ndi m’ma 80, mkangano wa amai ndi akazi a ana awo wakhala wa nyengo yaitali, mmalo mokhala wa nyengo yaifupi chabe.
Kodi Okalamba Amafuna Chiyani?
Mosasamala kanthu za mkanganowo, kodi makolo okalamba amafuna kusamaliridwa motani ngati anati asankhe? “M’zaka zoposa makumi aŵiri zapitazo,” akutero Jacob S. Siegel ndi Cynthia M. Taeuber, ofufuza tsatanetsatane wa mkhalidwe wa anthu, “onse aŵiri akazi ndi amuna anali ndi chikhoterero chochepera cha kukhala ndi anthu ena ngati iwo adalibe mnzawo wa muukwati.” Elaine M. Brody, amene kale anali mtsogoleri wa Dipatimenti ya Mautumiki a Anthu, akuwonjezera kuti mu United States, “kukhala molekana ndi achibale ndiko kakonzedwe koyanjidwa pakati pa okalamba.” Kaŵirikaŵiri, ana awo amakhala pafupi, kuwachezera, ndi kuwasamalira.
Akum’maŵa amakonda kuchitira mwina. Mogwirizana ndi kupenda kwa m’mitundu yonse kochitidwa ndi gulu la Management and Coordination Agency mu Japan, unyinji wa okalamba mu Japan ndi Thailand amafuna kukhala ndi achibale. Kupendako kunapeza kuti 61 peresent ya okalamba mu Thailand ndi 51 peresent mu Japan amachitadi tero.
Ndithudi, chosankhachi nchofalikiranso m’maiko Akummadzulo. Kaŵirikaŵiri makolo okalamba kwenikweni kapena obindikiritsidwa kaŵirikaŵiri amakhala ndi ana awo. Mu Faransa kuli kowanda kwa amsinkhu wa zaka zoposa 75 amene aferedwa anzawo amuukwati kukhala ndi mmodzi wa ana awo.
Kumvetsetsa Zoyanja ndi Zosayanja
Ndithudi, pamene mibadwo iŵiri kapena itatu isankhapo kukhala m’nyumba imodzi, pamakhaladi ubwino winawake. Okalamba amadziwona kukhala osungika kwenikweni ndi kusungulumwa kocheperapo. Mbadwo wachicheperewo ungaphunzire kuchokera ku zokumana nazo za okalambawo, ndipo pamakhalanso mapindu azachuma.
Kumbali ina, kukhala pamodzi kungawonjezere kuipa kwa unansi wachipongozi wosokonekera kale. Mwachitsanzo, mu Japan, kumene monga mwa mwambo makolo okalamba anakhala ndi mwana wachisamba ndi banja lake, kukangana kwa maiyo ndi apongozi ake nkofalikira.
Ngati muyang’anizana ndi mkhalidwewo, kodi mungachitenji? M’bukhu lake America’s Older Population, Paul E. Zopf, Jr., profesala wa maphunziro a makhalidwe a anthu pa Koleji ya Guilford, akuti: “Banja limayambitsanso kukangana ndi mwaŵi wa kulamulira kukanganako. Mphamvu ya kulamulira kukangana ndi kusonkhezera mwachiyanjo ndi ziŵalo zokalamba popanda kuputa mkwiyo kungakhale luso limene lingayambukirenso m’mabanja ena.”
Chotero khalani ndi lingaliro lotsimikizirika la nkhaniyo. Ngati muphunzira kuthetsa mikangano ya m’banja, mwinamwake mudzakhala waluso kwambiri pothetsa mikhalidwe ina yovutanso. Ivomerezeni kukhala chitokoso, ndipo mudzachita bwino m’zimenezo. Tiyeni tipende mavuto a kukhala ndi azipongozi ndikuwona mmene mavuto ameneŵa angasamalidwire mwachipambano. Ndipo ngakhale ngati pakali pano simukukhala pansi pakakonzedwe kotero, inu mungapindulebe ndi kupenda malamulo a makhalidwe abwino ophatikizidwamo.
[Bokosi patsamba 20]
Makolo Ochuluka Kuposa Ana
Tsopano, kwa nthaŵi yoyamba m’mbiri, mogwirizana ndi katswiri wa makhalidwe ndi chiŵerengero cha anthu Samuel Preston, okwatirana wamba ali ndi makolo ambiri kuposa ana. Nkhani yoyang’anizana ndi okwatirana ambiri lerolino ndi yonena za mmene angalinganizire mathayo awo a kusamalira magulu aŵiri a makolowo.