Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndine Wokonzeka Kubatizidwa?
Wokondedwa Watchtower Society:
Dzina langa ndine Sharon ndipo ndine wazaka 13 zakubadwa. Ndakhala ndikukaikira ngati ndiri wokonzeka kaamba ka ubatizo. Ndilingalira kuti ndiri tero, komabe sindiri wotsimikiza. Ndiri wotsimikiza kuti achichepere Achikristu ena nawonso ali ndi zimenezi m’maganizo. Chonde kodi mungalembe nkhani yondiwongolera?
SHARON ngolondola. Ubatizo ulidi m’maganizo mwa achichepere ambiri owopa Mulungu. Pakati pa Mboni za Yehova, achichepere amazindikira kuti ayenera kupanga chosankha chawo kutumikira Mulungu, kuti makolo awo sangawapangire chosankhacho. Iwo amadziŵanso kuti Yesu Kristu analamula atsatiri ake kuzindikiritsa kudzipatulira kwawo kwa Mulungu mwa ubatizo wa m’madzi.—Mateyu 28:19, 20.
Kupanga chilengezo chapoyera monga mtumiki wa Mulungu wodzipatulira kuli thayo lalikulu. Ndithudi inu simungafune kuthamangira kungofuna kukondweretsa anzanu kapena makolo anu. Ndiponso, palibe amene ayenera kukukakamizirani ubatizo. (Salmo 110:3) Komabe, Yesu analangiza onse “[ku]ŵerengera mtengo wake” wa kukhala wophunzira wake. (Luka 14:28) Ichi sichikutanthauza kuti muyenera kudzipima kupeza kaya mukufuna kukhala wophunzira wa Kristu kapena ayi. Momvekera bwino, ichi ndichinthu cholondola kuchichita. Komabe, muyenera kukhala wodziŵa bwino lomwe zimene kukhala Mboni ya Yehova kumaloŵetsamo.a Chotsatira, muyenera kudzitsimikizira kaya mulidi wokonzeka kunyamula thayoli.—Yerekezerani ndi Miyambo 20:25.
‘Kodi Ndine Wamkulu Wofikapo?’
Pamene azaka zapakati pa 13 ndi 19 akukulirako, kaŵirikaŵiri amalingalira kuti ali ndi kuyenera kwa kusangalala ndi mwaŵi winawake ndi mathayo. Iwo amakhala ofulumira kuwumirira pa kuyendetsa galimoto la banja, kuchonderera kaamba ka chilolezo cha kugwira ntchito za pambuyo pa sukulu, akumafuna ndalama zawozawo zodziwonongera. Koma tiyeni tinene za ubatizo, achichepere ambiri amadzikhululukira kukhala aang’ono kwambiri kapena osakonzekera kunyamula thayolo. Wachichepere wotchedwa Andre akupereka ndemanga yakuti: “Achichepere ambiri amayembekeza kufikira atafika zaka 17 kapena 18 kuti abatizidwe, kumene kuli kuchedwako pang’ono.” Nchifukwa ninji? “Chifukwa chakuti adakali kutali ndi kufika pa msinkhuwu amakhala aakulu mofikapo kupanga zosankha zina zawozawo.”
Inde, kukhala wazaka zapakati pa 13 ndi 19 mwa iko kokha sikuli chodzikhululukira chokhalira ‘wokayikakayika,’ kapena sichiri chifukwa chomveka cholekera kutenga kaimidwe kanu monga Mkristu. (1 Mafumu 18:21) “Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako,” limalangiza tero Baibulo. (Mlaliki 12:1) Mneneri Samueli anayamba kutumikira Yehova pa msinkhu wachichepere kwambiri. (1 Samueli 3:1-18; 12:2) Wamasalmo Davide mofananamo anakhoza kunena kuti: “Pakuti Inu ndinu chiyembekezo changa, Ambuye Yehova; Mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga.”—Salmo 71:5.
Mofananamo, achichepere Achikristu zikwizikwi lerolino—kuphatikizapo osafikira zaka zapakati pa 13 ndi 19—adzitsimikizira iwo okha kukhala athayo mokwanira kupanga kudzipatulira kutumikira Mulungu. Kusapita m’mbali, azaka zapakati pa 13 ndi 19 ena alibe kulama kwa maganizo ndipo ali osasamala kwenikweni ndi osafikapo mwamalingaliro kupanga chosankha chapatali chonga ubatizo. (Miyambo 22:15) Koma kodi zimenezi ziri zowona kwa inu? (Mosakaikira makolo anu adzakhala ndi zokambapo zambiri pa zimenezi.) Mulungu sakuyembekezera mpang’ono ponse wazaka zapakati pa 13 ndi 19 kukhala ndi uchikulire wa munthu wa zaka 40. Iye amadziŵa bwino lomwe kuti inu muli nkhole ku “zilakolako za unyamata.” (2 Timoteo 2:22) Koma ngati ndinu wamkulu wofikapo kukhala wolama m’maganizo ndi wathayo, mwachiwonekere muyenera kukhala wamkulu mofikapo kulingalira za kudzipatulira. Komabe, pali mafunso ena amene muyenera kudzifunsa.
‘Kodi Ndiri ndi Chidziŵitso Chokwanira?’
Bukhu lakuti The Adolescent, lolembedwa ndi F. Philip Rice, limanena kuti “maganizo achipembedzo osazama, ongokhalapo mwachibadwa kaŵirikaŵiri samakhoza kulimbana ndi kuwukiridwa kapena chiyeso.” Inde, Mr. Rice akudziŵitsa kuti: “Pali zisonyezero zakuti achichepere a lerolino mwatsoka ali osadziŵitsidwa. Phunziro pa chidziŵitso Chabaibulo cha ophunzira a pa yunivesite a m’chaka chawo chachiŵiri Achiprotesitanti ndi Achiyuda linavumbula umbuli weniweni wa Chipangano Chakale ndi Chatsopano.”
Siziyenera kukhala tero kwa amene akubatizidwa. Munthu ayenera choyamba ‘kupeza chidziŵitso’ kuti akhale wophunzira, kapena wophunzitsidwa. (Yohane 17:3; Mateyu 28:19) Chotero kodi sichikakhala chanzeru kuyembekezera kuti musanabatizidwe, muyenera kudziŵa “zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu”? (Ahebri 5:12) Izo zikaphatikizapo kudziŵa zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani zonga moyo, mkhalidwe wa akufa, kuyeretsedwa kwa dzina la Mulungu, Ufumu, ndi dipo.
Zowonadi, inu mungakhale munaphunzira chinachake ponena za Baibulo mwakungotsagana ndi makolo anu ku misonkhano Yachikristu. Koma chidziŵitso chopezedwa mwanjirayo chingakhale chapamwamba ndipo sikwenikweni kuti “chingalimbane ndi chiwukiro kapena chiyeso.” Muyenera kukhala wokhoza kuwapatsa ena “chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chiri mwa inu.”—1 Petro 3:15.
Terry akunena kuti anakhulupirira zowonadi za Baibulo. Komabe akuwulula kuti: “Sindinadzikhutiritsepo ndekha mwakudzifunsa mafunso kenaka nkuwayankha. Posachedwapa, ndinayamba kuchita zimenezi.” Chotulukapo cha programu ya phunziro la Baibulo loterolo? “Chikhulupiriro changa chikukula, ndipo tsopano ndipeza kuti ndikhoza kulankhula kwa anthu ndi chikhutiritso chenicheni. Ndikuuza achichepere onse okhala Mboni kuti asachite mantha kudzifunsa ngati ichi ndicho chowonadi. Pezani zenizeni! Fufuzani, phunzirani. ‘Tsimikizirani zinthu zonse.’ Ndiyeno mudzakhoza kudzipatulira nokha kwa Yehova ndi mtima wonse.”—1 Atesalonika 5:21.
“Akuchita Mawu”
Komabe, tiyenera kukhala “akuchita mawu, osati akumva okha.” (Yakobo 1:22) Simungadzipereke ku ubatizo ndikukhala munthu amene ‘amabisa amene ali’ mwakubisa zolakwa zazikulu. (Salmo 26:4) Zolakwa zoterozo zikaphatikizapo chisembwere chakugonana, kuledzera, kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala ogodomalitsa, kapena lirilonse la machimo otchulidwa pa 1 Akorinto 6:9, 10. Ngati mwakhalapo ndi mavuto ponena za zimenezi, bwanji osapanga makonzedwe ndi makolo anu a kukambitsirana ndi akulu Achikristu? Khalani otsimikiziridwa kuti mudzapatsidwa thandizo lokoma mtima.—Yakobo 5:14, 15.
Zingakhalenso kuti mwina muyenera kupanga masinthidwe m’njira imene muchitira ndi makolo anu kapena mmene mumawonera uphungu wochokera kwa akulu Achikristu, ngakhale m’njira imene mumasankhira mabwenzi. (Miyambo 6:20; 13:20; 1 Akorinto 15:33; Ahebri 13:17) Sizingakhale zosavuta kupanga masinthidwe oterowo, koma Miyambo 11:19 ikutikumbutsa kuti: “Wolimbikira chilungamo alandira moyo; Koma wolondola zoipa adzipha yekha.”
Kodi Yehova amafuna kuti mukhale wangwiro? Kutalitali. Miyambo 20:9 ikufunsa kuti: “Ndani anganene, Ndasambitsa mtima wanga, Ndayera wopanda chimo?” Pokhala opanda ungwiro, tidakali okhoterera kupanga zophophonya. Koma chifukwa cha dipo la Kristu, tingakhalebe m’kaimidwe kabwino ndi Mulungu. (1 Yohane 2:1, 2) Mwachitsanzo, wachichepere amene akumenyera zolimba motsutsana ndi chizoloŵezi choipa, chonga ngati m’chitidwe woipa wa mphyotomphyoto, sayenera kulingalira kuti iye kwenikweni sali woyeneretsedwa kaamba ka ubatizo.b Ndithudi, mwakukaniza chisalungamo mowumiriza, munthu angakondweretse mtima wa Yehova!—Miyambo 27:11.
‘Kodi Ndapanga Mulungu Kukhala Bwenzi Langa?’
Ngakhale nditero, mwinamwake funso lovuta koposa limaloŵetsamo unansi wanu ndi Mulungu. Kumbukirani: Mudzipereka inu eni, osati ku ntchito kapena phindu, kapena ngakhale ku gulu, koma kwa Mulungu iyemwini. Kodi Mulungu akuwoneka kukhala wokaikirika, wokhala kutali? Kapena kodi mwamdziŵa ndi kumkonda monga Munthu? (Eksodo 34:6, 7) Ngati nditero, mudzapeza kuti mukulankhula kwa iye kaŵirikaŵiri, osati monga chizoloŵezi chabe, koma kuchokera mumtima.—Salmo 62:8.
Mudzadzipezanso kukhaladi wokakamizika kulankhula kwa ena ponena za Mulungu. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 5:14.) Miyambo 15:7 imati: “Milomo ya anzeru iwanditsa nzeru.” Kodi mukutero mwakulalikira kwa ena mokhazikika? Kapena kodi mukulola zosangulutsa, maseŵera, kapena ngakhale ulesi kukuletsani kuthandiza ena kumdziŵa Mulungu?—Miyambo 19:24.
Inde, kuti ubatizo ukhale watanthauzo, Mulungu ayenera kukhala bwenzi lanu lapamtima. (Yerekezerani ndi Yakobo 2:23.) Ngati siziri choncho tsopano, cholakwa si cha Mulungu, popeza iye mokoma mtima akuitana onse kumfunafuna. (Machitidwe 17:27) Ndipo mwakuumirira pa phunziro laumwini, pemphero, ndi kuyanjana ndi anthu ake, m’kupita kwa nthaŵi mudzadzimva woyandikira kwa Mulungu. (Aroma 12:12; 1 Timoteo 4:15; Ahebri 10:24, 25) Ubatizo udzakhala chotulukapo chachibadwa cha ‘kuyandikira kwa Mulungu’ koteroko.—Yakobo 4:8.
Lingalirani, mwachitsanzo, msungwana wachichepere wotchedwa Cindy. Iye akulemba kuti: “Pa msinkhu wa 14 ndinabatizidwa. Ndidziŵa mmene wina amakhalira wozengereza kuchita tero. Koma ine ndikuti chiri chinthu chabwino koposa chimene mungachite. Tangolingalirani, kudziŵa kuti Yehova wakuvomerezani ndikuti ‘sadzakusiyani konse kapena kukutayani’! (Ahebri 13:5) Ngati aliyense adati andifunse ngati anayenera kudzipatulira kwa Yehova, ndikadati inde! Koma musachite icho mwakufuna kukondweretsa winawake. Chitani icho chifukwa chakuti mukufuna kutero.”
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yapitayi yakuti “Kodi Ndibatizidwe?”
b Onani mitu 25, 26 ya bukhu la Questions Young People Ask—Answers That Work, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Chithunzi patsamba 16]
Achichepere ambiri amayeneretsedwa kaamba ka ubatizo. Kodi mwatero?