Dziko Laudongo Tikulifunadi
Ndi mlembi wa Galamukani! mu Britain
KODI mudadziŵa kuti oyendetsa matekisi a mu London ali ndi lamulo la kusunga matekisi awo kukhala audongo? Kulephera kutero kungatulukepo kuwaletsa kuyenda m’makwalala a mzindawo kwa nyengo yanthaŵi. Ngakhale pamene mikhalidwe ya msewu iri yoipa ndipo magalimoto ambiri amakhala akuda kwa masiku ambiri, tekisi ya ku London imakhala yaudongo kopambana. Mawonekedwe owala a galimotowo amadzutsa mwa woyendetsayo ndi okweramo ake malingaliro a kunyadira ndi chisangalalo.
Mofananamo, pamene nyumba yathu, zovala zathu, ndi zinthu zathu ziri zaudongo, zimachititsa mwa ife malingaliro a mkhalidwe wabwino. Zimaipira mnyamata wa sukulu amene amayi ake amuwona akuloŵa m’nyumba nasiya nkukuluzi ya matope a ku nsapato zake zakuda pakapeti!
Ndiiko komwe, umoyo wabwino umadalira kwakulukulu pa udongo waumwini. Matupi athu amafuna chisamaliro ndi kusamba kokhazikika kuchotsa litsiro limene lingaloŵerepo matenda. Makampani amalonda amapeza mapindu aakulu mwakugulitsa zoyeretsera, zochapira, polishi, sopo, shampuu, ndi zophera tizirombo zimene timagwiritsira ntchito kudzisunga ife eni ndi malo otizinga kukhala audongo. Ndithudi, anthu ambiri ali ozindikira za kufunika kwa udongo. Koma ngati mukukhala mumzinda, mukudziŵa kuti sizokhazi.
Ngozi—Kuipitsa
Okhala mumzinda amadziŵa bwino lomwe za kuipitsa ndi malo owazinga odetsedwa. Iwo amakuwona m’zinyatsi zosatoledwa, m’zinyalala zosiidwa mosasamala pamakwalala, ndi m’zolembalemba zodetsa pa nyumba zapoyera. Iwo amakununkhiza mu utsi wotsamwitsa wochokera ku magalimoto ochuluka ndi mpweya wautsi wonunkha umene umakuta mizinda ina.
Mwinamwake ndicho chifukwa chake ambiri okhala m’mizinda amayesa nthaŵi zina kukathera nthaŵi ku malo akumidzi. Iwo amasangalala kupumira m’mapapo awo mpweya waudongo, mwinamwake ngakhale kumwa madzi oyera mbee a mu mfuleni wochokera m’phiri. Ena amakonda kupita kugombe ndi kumapuma pa mchenga kapena kuziziritsa thupi mwakusamba kosangalatsa pa nyanja.
Ngakhale nditero, taimani pang’ono! Litsiro ndi kuipitsa zikubisala kumenekonso. Inu mungafunse kuti ‘zingatero motani?’ ‘Akuwoneka awudongo.’ Chabwino, tiyeni tiyang’anitsitse pang’ono pa mpweya “waudongowo” ndi madzi “oyerawo.”