Lingaliro la Baibulo
Kodi Ndiliti Pamene Moyo wa Munthu Umayambika?
SEPTEMBER 21, 1989, linali tsiku lachilendo kwa Fifth Judicial District ya Boma la Tennessee, U.S.A. Patsiku limenelo khoti lakadera kakang’ono linapereka lingaliro lake lonena za mkangano wolimbanirana ulamuliro wa kusunga miluza isanu ndi iŵiri youmikidwa ndi madzi owundana ozizira. Khotilo linafunikira kugamulapo kuti ndi kholo liti la makolo osudzulanawo limene likakhala ndi ulamuliro. Komabe, nkhani ina inayenera kuthetsedwa choyamba: Kodi miluzayo iyenera kulingaliridwa kukhala katundu kapena anthu?
Profesa Jerome Lejeune wa ku Paris, katswiri wa magene wotchuka kwambiri padziko, anatsimikizira khotilo kuti munthu aliyense ali ndi chiyambi chapadera, chimene chimachitika panthaŵi yakutenga pathupi ndipo kuti “mwamsanga pathupi pake patatengedwa, mwamuna amakhala mwamuna.” Kunena kwina, kuyambira pa sitepe la kukhala ndi maselo atatu (zygote), miluzayo, monga momwe iye anauzira khotilo, “ndi tianthu tating’ono”!—Kanyenye ngwathu.
Pamene anafunsidwa kuti atsimikizire ngati zygote iyenera kusonyezedwa zoyenerera zofanana ndi za munthu wamkulu, Dr. Lejeune anayankha kuti: “Sinditha kukuuzani zimenezo chifukwa chakuti sindikudziŵa. Ndikukuuzani kuti, iye ndi munthu wamoyo, ndipo Woweruza ndiye amene adzakuuzani kaya ngati munthuyu ali ndi zoyenerera zofanana ndi za ena. . . . Koma monga katswiri wa magene mundifunse kaya ngati munthuyu alidi munthu, ndipo ndidzakuuzani kuti popeza kuti ngwamoyo, ndipo pokhala munthu wamoyo, iye ndi munthu.”
Mozikidwa kwakukulukulu pa umboni wosatsutsika wa Dr. Lejeune, zitsimikizo zitatu zogwira mtima za makotiwo ndi izi:
◻ “Kuyambira pa kugwirizana kwa ubwamuna ndi dzira la mkazi, maselo a mluza wa munthu amalekanitsidwa, amakhala apadera ndipo kumlingo waukulu aluso lapadera.”
◻ “Miluza ya anthu sikatundu.”
◻ “Moyo wamunthu umayamba pakutenga pathupi.”
Kodi izi zikugwirizana ndi zimene Baibulo limanena ponena za kuyambika kwa moyo wa munthu?
Moyo Umayambira pa Kutenga Pathupi
Yehova Mulungu ndiye ‘chitsime cha moyo’ ndipo “mwa Iye tikhala ndi moyo ndi kuyendayenda, ndi kupeza mkhalidwe wathu.” (Salmo 36:9; Machitidwe 17:28) Kodi Mlengiyo akuti moyo umayambika liti? Iye amauwona moyo wa mwana kukhala wamtengo wake ngakhale nthaŵi yoyambirira ya kuumbidwa kwake pambuyo pa kutenga pathupi. Zaka zoposa 3,000 lamulo la khoti liri pamwambalo lisanapangidwe, iye anauzira Davide, mneneri wake, kulemba tere:
‘Munandiumba ndisanabadwe ine. Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchowopsya ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu. Thupi langa silinabisikira inu popangidwa ine mobisika [mkati mwa chibaliro] poombedwa ine [kulozera ku mitsempha ndi minyewa, imene imalukidwalukidwa m’thupi ngati ulusi wokongola wa nsalu] monga m’munsi mwake mwa dziko lapansi [kalongosoledwe ka ndakatulo ka mdima wokhala m’chibaliro]. Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya, ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku mwanu.’—Salmo 139:13-16.
Kuyambira panthaŵi yakutenga pathupi, moyo womaumbidwawo umatsatira dongosolo latsatanetsatane monga ngati kuti likumvera malangizo olembedwa m’bukhu, bukhu lalikulu ndithu. “Unyinji wa chidziŵitso chimene chiri mkati mwa zygote,” akutero Dr. Lejeune, “chitalembedwa ndikuikidwa m’kompyuta ndikuiuza kompyutayo kuti iŵerenge zimene zidzachitika potsatira, unyinji umenewu wa chidziŵitso ngwaukulu kwakuti palibe munthu amene angathe kuchiŵerenga.”
Moyo wa Munthu Wosabadwa Ngwamtengo Wake
Motero, mwana wosabadwa womaumbika m’chibaliro ngwamtengo wake koposa kokha mulu wa minyewa. Ali ndi mtengo wapamwamba, ndipo chifukwa cha ichi, Mulungu wanena kuti munthu adzaŵerengera chifukwa chovulaza mwana wosabadwa. Lamulo lake pa Eksodo 21:22, 23 likuchenjeza kuti: ‘Akayambana amuna, nakakantha mkazi ali ndi pakati, kotero kuti abala, koma alibe kupwetekwa; alipe ndithu, monga momwe amtchulira mwamuna wa mkaziyo; apereke monga anena oweruza. Koma ngati kupwetekwa kukalipo, uzipereka moyo kulipa moyo.’
Mabaibulo ena amatembenuza mavesi apamwambawo kuwapanga kuwoneka ngati kuti chimene chimachitika kwa mkaziyo ndicho chimene lamulo likusumikapo. Komabe, lemba loyambirira Lachihebri limalunjikitsa chisamaliro ku kupwetekwa kaya kwa mayiyo kapena kwa mwanayo.a Chotero, kuchotsa dala mimba kokha kuti mupeŵe kukhala ndi mwana wakunja kwa ukwati ndiko kupha moyo wamunthu mwadala.
Anthu ena angatsutse kuti mluza wa munthu simoyo wa munthu chifukwa chakuti sungathe kudzichilikiza wokha pamene uli kunja kwa chibaliro. Uku ndi kulingalira kopusa. Palibe amene amakaikira konse kuti khanda lobadwa chatsopano—lamphindi zoŵerengeka zokha—ndimunthu wamoyo. Komabe, ngati mwana ameneyo anasiyidwa wamaliseche pabwalo, kodi mwanayo angakhale kwa utali wotani? Iye ngopanda thandizo lirilonse, ndipo mofanana ndi mluza kapena mwana wosabadwa, alibe nyonga ya kudzichilikiza. Khanda lobadwa chatsopano limafunikira pogona, kufunda, ndi chakudya—chilikizo, thandizo, ndikugwiriziza kumene munthu wachikulire yekha, monga mayi, angapereke.
Chotero, chosankha chalamulo chotchulidwa koyambiriracho chikugwirizana ndi lingaliro Labaibulo lakuti moyo wa munthu umayambira pa kutenga pathupi. Moyo wa munthu wosabadwa suli chinthu chaching’ono chofunikira kuchotsedwa modzifunira monga ngati kuti unali chinthu chachilendo chosafunika. Moyo wa munthu ngwopatulika osati kokha pamene uchoka m’chibaliro komanso ngakhale pamene udakali mkati mwa chibaliro.
[Mawu a M’munsi]
a Liwu lotchulira chinthu lakuti “kupwetekwa” (Chihebri, ʼa·sohnʹ) liribe kugwirizana kwachindunji ndi ‘mkazi wapakati’; chotero, kupwetekwako sikulekezera kwa mkazi yekhayo basi koma moyenerera kukaphatikizaponso ‘ana ake’ amene ali m’chibaliro.
[Mawu a Chithunzi patsamba 14]
Windsor Castle, Royal Library. © 1970 Her Majesty The Queen