“Mboni za Yehova Zochokera ku Ussr—Masiku Owala Ali Kutsogoloku”
UWO ndiwo unali mutu wankhani m’nyuzipepala yolembedwa m’chinenero cha Chingelezi yotchedwa The Warsaw Voice ya pa August 19, 1990, yofalitsidwa m’Poland. Woulemba, Anna Dubrawska, anathirira ndemanga pa Msonkhano wa “Chinenero Choyera” wa Mboni za Yehova wochitidwira mu Warsaw mu August 1990. Iye anafunsa Mboni zochokera ku Soviet Union, ena omwe anathera zaka 15 ali m’ndende ndi misasa yokhaulitsira chifukwa cha zikhulupiriro zawo zachipembedzo. Koma tsopano ankagogomezera masinthidwe abwino omwe akuchitika m’dziko lawo.
Grigor Goryachek, wantchito yomanga wochokera ku Crimea yemwe analeredwa monga Mboni, anali m’ndende kwa zaka 15 m’Siberia. Iye anati: “Tsopano tikuyembekzera kudza kwa nthaŵi zabwinopo.” Mboni ina, Anton Pohanich, inati: “Nthaŵi zabwino zafika kale. Tsopano ndingaufotokoze uthenga wathu mwaufulu kunyumba ndi nyumba, pamene kuli kwakuti kumbuyoku ichi chinali chosatheka.”
Dubrawska akugwira mawu Igor Cherny, Mboni ya zaka 17 zakubadwa yochokera ku Caucasus motere: “Kwa zaka 70 anthu, makamaka achichepere, anapatutsidwa kutalitali ndi Mulungu kwakuti tsopano akufuna kubwereranso chifupi kwambiri ndi Iye, kapenatu kumva za Iye poyamba.”
Nyuzipepala ya Chipolish yotchedwa Dziennik Wieczorny (Pepala Lamadzulo) linasimba, pansi pa mutu wakuti Radość braci (Chimwemwe cha Abale), kuti wantchito wa mbwalo lamaseŵera la Zawisza mumzinda wa Bydgoszcz anati: “Ndikukondwera nacho chinenero chaudongo chogwiritsiridwa ntchito ndi makhalidwe abwino osonyezedwa ndi achichepere.”
Polemba m’nyuzipepala ya Chipolish yotchedwa Trybuna pansi pa mutu wakuti Głosiciele Królestwa (Ofalitsa Aufumu), Zofia Uszynska ananena motere ponena za msonkhanowo: “M’nyengo ya mphindi 30 ndinapatsidwa masikono ndi kofi nthaŵi khumi. Kwanthaŵi zisanu anthu ena anafuna kundisiira pokhala. Kwa masiku otsatizana anayi anthu oposa 30,000 pa Bwalo Lamaseŵera la Dziesieciolecia mu Warsaw anagawanamo m’phwando [lachipembedzo]. Kunali akazi olemeratu ndi pathupi, mabanja okhala ndi ana aang’ono, achikulire ndi achichepere. Wachichepere kwambiri amene anabatizidwa anali wa zaka 11 zakubadwa, wokalambitsa anali pafupifupi wa zaka 80.”
Nkhaniyo inapitiriza motere: “Nzika za ku Russia zikwi zambiri [kwenikweni zoposa 16,000] zinabwera kumsonkhano wa chakachi. Chaka chatha panali 6,000 a iwo. Akuluakulu a m’malire a Russia anavomereza mabasi onse kudutsa popanda kufunikira kwa kuyembekezera kusechedwa pamzere wautali kwa makilomita ambirimbiri. Nthumwi zochokera m’Soviet Union monse zinabwera: zochokera ku Vladivostok, Khabarovsk, Vorkuta. Ena anatha masiku anayi kapena asanu ali paulendo wapasitima.”
Nyuzipepala imodzimodziyi ikugwira mawu Ivan M. Grevniak kukhala akunena kuti: “Ndinawona kupanda chilungamo m’zimene apapa ndi ansembe ankachita, ndipo ndinafunafuna komwe ndingapeze kuwona mtima.” Nkhaniyo ikupitiriza motere: “Iye anawona kuti panali kumvana pakati pa mawu ndi zochita mumkhalidwe wa Mboni za Yehova.” Kenaka Ivan anawonjezera kuti: “Ndithokoza Mulungu kuti anandilola ine kuphunzira chowonadi.”
Trybuna ikusimba kuti Ivan ndimkulu mumpingo wa ku Lvov, kumene “kuli mipingo 13 ndi akhulupiriri achipembedzo oposa 2,000. . . . ‘M’magulu onse achipembedzo kulikonse muli mzimu wa ukulu wautundu. Komabe, izi sizipezeka kwa amchipembedzo changa,” akutero Grevniak.”
Umodzi umenewu unasonyezedwa pamsonkhano wa Mboni za Yehova wa ku Warsaw kumene programu inaperekedwa panthaŵi imodzi m’Chipolish ndi m’Chirussia m’mbali zosiyanasiyana za bwalo lamaseŵeralo. Umu kunena mwantheradi munalibe kusamvana kwautundu.
Zofia Uszynska anasangalatsidwanso ndi kulinganizidwa kofunikira kupatsa kogona, chakudya, ndipo ngakhale kupatsa mankhwala anthu oposa 35,000 omwe anapezeka pamsonkhanopo. Iye akumaliza kuti: “Sindinapezekepo pamsonkhano wabwino kwambiri, ndi waubwenzi woterowo.”
Nyuzipepala Yachipolish yotchedwa Sztandar Młodych (Miyezo ya Achichepere) inathirira ndemanga pantchito yochitidwa kuti atheketse bwalo lamaseŵereralo kukhala loyenerera kukhalidwa ndi alendo ambirimbiri motere: “Monga ntchito yokomera aunyinji . . . atsatiri a Yehova anamanganso mabenchi, nakonzanso malikole ndi zimbudzi, nayeretsa kapinga. Iwo anathandizira zotaika pamsonkhanowo kuchokera m’matumba awo. Mboni za Yehova zinakonzekera pafupifupi nyumba zapambali zogonamo anthu 22,000 kaamba ka alendo, zinasamalira nyumba zogonamo nzika za ku Soviet, ndipo zinali ndi mankhwala awo.”
Motsimikizirikadi Mboni za Yehova zayamba kale kuwona “masiku owala” Kum’mawa kwa Yuropu ndipo zikupemphera kuti kaimidwe kawo kalamulo kopezedwa tsopanoko m’maiko onga ngati Romania, Hungary, ndi Poland posachedwapa kadzafutukulidwira ku Chekoslovakiya, Albania, Bulgaria, ndi Soviet Union.—2 Atesalonika 3:1; 1 Timoteo 2:1, 2.
[Zithunzi patsamba 31]
Mboni za ku Soviet pa Msonkhano wa “Chinenero Choyera” mu Warsaw, kuphatikizapo opita kuubatizo (chapamwaba ndi chithunzi chamkati), mlankhuli wa ku Russia, programu, ndi nthumwi za ku Soviet kutsogolo kwa mabasi awo