Kodi Mumadana ndi Kulandira Chisulizo?
KODI mungakumbukire nthaŵi yomalizira imene munasulizidwa? Zimenezi zimachitika kwa aliyense kwa nthaŵi ndi nthaŵi kaamba ka zifukwa zosiyanasiyana.
Mwinamwake winawake anakusulizani kuti adzikweze yekha. Komabe, kaŵirikaŵiri chisulizo chimachokera kwa munthu amene amalingalira za ubwino wanu: Mwamuna wanu anawona kulakwika m’kaphikidwe kanu; mkazi wanu anati tayi yanu sikugwirizana ndi suti yanu; bwenzi linakusulizani chifukwa chosasamalira thanzi lanu. Kapena kusulizako kungakhale kunali chilango, monga ngati chochokera kwa wolemba ntchito kapena kholo (ngati ndinu wachichepere), kuwongolera chinachake chimene munanena kapena kuchita.
Mosasamala kanthu za momwe icho chingakhalire, kodi munachilandira chisulizocho? Kapena kodi munakwiyitsidwa, mwinamwake kufikira pakumuuza kusamalira zochita zake zokha?
Kwa ambiri, kulandira chisulizo nchokumana nacho chopweteka. Iwo amakwiya, ndi kuipidwa. Ena amataya chidaliro, akumatsimikiza kuti ‘Sindingathe kuchita chirichonse molondola’ ndipo amachita tondovi.
Kodi ndinu mmodzi wa awo amene amadana ndi kusulizidwa? Sindinu wachilendo; ambiri amalingalira mofananamo. Kodi mungaphunzire kulandira chisulizo mosawawidwa kwambiri, popanda kunyanyuka? Nkhani ino idzasanthula njira zisanu ndi imodzi zimene zingapangitse kusuliza kukhala kolandirika. Izo zingakuthandizeni kuchotsa, kapena kuchepetsako, ululu wa kusuliza.
1. Kulandireni Kusuliza
Kodi chimakuwonekerani chachilendo kuti anthu ena amafuna chisulizo, kuchitadi kuchifunafuna? Magazini a Bits and Pieces ananena kuti: “Atsogoleri ochenjera . . . amadziŵa kuti adzalakwa ndi peresenti yakutiyakuti ya nthaŵi. Chimenecho ndicho chifukwa chake amafuna malingaliro osemphana ndi awo—kuti achepetseko zophophonya zisanapangidwe, ndikuwongolera zolakwa zakumbuyo mofulumira monga mmene kungathekere.”
Mongadi momwe anthu ena angawonere mbali zina za kawonekedwe kathu zomwe sitingaziwone—kolala yopindika, tayi yokwinyika—moteronso angawone mbali za umunthu wathu zomwe sitingathe kuziwona. Ziwoneni zonena zawo kukhala zothandiza mmalo moziwona kukhala chiwopsezo. Landirani kusuliza kwawo monga mwaŵi wakuphunzira chinachake. Kupangeni kukhala chokumana nacho chowongolera.
2. Lamulirani Kusuliza Kwanu Koipitsitsa
Kodi mumadzisuliza mopambanitsa? Kodi mumakhalirira pa zophophonya zanu? Kapena ngati wina akudziŵitsani za chophophonya, kodi mumachiwonjezera icho ku ndandanda ya zifooko zolingana nacho m’maganizo mwanu?
Dr. Harold Bloomfield akusonyeza kuti: “Ngati ndife okanthidwa kale ndi kudzisuliza, tidzavutitsidwa kwenikweni pamene tilandira chisulizo kuchokera kwa ena. Ngakhale ngati winawake atitamanda ndipo ali ndi chinthu chimodzi chokha chaching’ono chotisuliza, kaŵirikaŵiri timasumika pa zophophonyazo kuposa pa zinthu zimene timachita bwino.”
Khalani wolingalira pamene mukudzisanthula. Kodi mungadziŵe bwanji zimene ziri zolingalirika? Tangolingalirani kuti bwenzi lanu lapamtima likulandira chisulizo chofananacho. Kodi ndichivomerezo chotani chimene mungafune kuchokera kwa iye? Kudzimvera chisoni? Kukwiya? Kukana uphunguwo monyada? Ayi, mwachidziŵikire mudzayembekezera kuti akamvetsera ku chisulizocho mosavutitsidwa kwenikweni, kuchisanthula mowona mtima, ndikuchigwiritsira ntchito kudziwongolera yekha.
Pamenepo, bwanji osachita zofananazo kwa inumwini?
3. Funsani Kaamba ka Tsatanetsatane
“Sindikonda zochita zanu!” Kodi mungakonde kuti winawake akuuzeni zimenezo? Ayi, ndemanga zoterozo zimakwiyitsa, kodi sitero?
Kafikiridwe kanu kabwino koposa panopa kangakhale kufunsa kaamba ka nsonga zakutizakuti zowonjezereka. M’bukhu lake lakuti Conversationally Speaking, Alan Garner akulongosola kuti: “Kusuliza kaŵirikaŵiri kumaperekedwa mwachisawawa . . . Kufunsa kaamba ka nsonga zakutizakuti kukakukhozetsani kupeza zenizeni zimene munthu winayo akutsutsa. . . . Mofanana ndi mtola nkhani, zonse zomwe mungachite ndikufunsa mafunso ofuna kupeza munthuyo, chinthucho, pomwe chinachitika, kumene chinachitikira, chifukwa chake, ndi mmene chinachitikira.”
Mwachitsanzo, mungayankhe mawu ofuulidwa pamwambawo motere: ‘Kodi ndimkhalidwe weniweni uti umene mumalingalira?’ Ngati iye sakunenabe mwachindunji, mungafunsenso kuti: ‘Kodi nchifukwa ninji uli woipa? Kodi mungandipatse chitsanzo cha pamene ndinachita chimenechi?’ Atasonkhezeredwa ndi chikhumbo chanu chakufuna kulankhulana osati kutokosa, mafunso onga ameneŵa angathandize wokusulizaniyo ndi inu kusumika pa nsonga zakutizakuti. Iwo angavumbule kaya kusulizako nkoyenerera kapena nkuchita zinthu mopambanitsa. Ndipo amakupatsani nthaŵi yowonjezereka kulingalira za nkhaniyo.
4. Tonthozani Wokusulizaniyo
Kodi bwanji ngati amene akukusulizaniyo wakwiya? Dr. David Burns akuyamikira kuti: “Kaya wokusulizaniyo ngolondola kapena wolakwa, poyamba pezani njira ina yovomerezana naye.” Kodi izi zimakupindulitsani motani? Chimapangitsa wokusulizaniyo kukhala wopanda mphamvu, kumutonthoza, ndikumpanga kukhala wolankhulika.
Kumbali ina, ngati inu nthaŵi yomweyo muyamba kudzichinjiriza—monga momwe zingakhalire ngati chinenezocho nchosalungama—mungawonjezere bwino lomwe ukali wa wokusulizaniyo. Monga momwe Dr. Burns akusonyezera: “Mudzapeza kuti ukulu wa kuukira kwa wokutsutsaniyo kumawonjezeka!” Pamenepo, chinthu chabwino koposa chomwe mungachite chingakhale kupeza mfundo yogwirizana musanayambe kukambitsirana mkanganowo.
5. Sumikani Maganizo pa Mfundo Zake, Osati Kakambidwe
Nakubala wina analandira dandaulo lonena za mkhalidwe wa mwana wake wamwamuna m’mudzi. Dandaulolo linakambidwa mwaukali ndiponso mumzimu wampikisano. Nakubalayo akanatsutsa ndemanga za mnansiyo kukhala zosalungamitsika kapena zabodza, ndipo adafunadi kuchita tero.
Mmalomwake, pambuyo potsimikizira kuti munali chowonadi china m’kusulizako, anamuuza mwana wakeyo kuti: “Sianthu omwe timakonda amene nthaŵi zonse amatiwonetsa zolakwa zathu, monga momwedi tingapindulire nazo. Tiyeni tigwiritsire ntchito uphunguwu monga mwaŵi wakuwongolera.”
Kodi alipo winawake amene anakudzudzulani mwaukali? Mwinamwake munthuyo ali ndi vuto la kusalingalira kapena ngakhale nsanje. Inu kapena winawake mungakhale ndi mwaŵi wakumthandiza pansongayo panthanŵi yoyenerera. Koma musakane zonena zake kokha chifukwa chakuti anazinena mwaukali. Sumikani maganizo pa mfundo zake za kusulizako. Kodi nzowona? Ngati nzowona, musadzimane nokha mwaŵi wa kukula umenewu.
6. Chepetsaniko Kupweteka Kwake
Izi zingakudabwitseni, koma mungathe kulamulira kuchuluka ndi kupweteka komwe mumalandira nako kusuliza. Lamulo lamakhalidwe abwino limeneli nlowona makamaka pankhani ya kusuliza kowongolera kochokera kwa anthu okhala ndi mathayo. Motani?
Nthaŵi zakale, zomera za maŵere zinali zotchuka m’Palestina. Koma mosiyana ndi zomera zina, sanali kupunthidwa ndi magudumu olemera kapena zopunthira zakuthwa. Mmalomwake, anapunthidwa ndi ndodo kapena chibonga. Kodi nchifukwa ninji panafunikira kusamalira kwaluso, kosamalako? Chifukwa cha kuchepa kwake, mbewu zazing’onozo sizinafunikire kupuntha kwamphamvu ndipo, kwenikweni, izo zikanawonongeka.
Bukhu la Baibulo la Yesaya limagwiritsira ntchito maŵere kuchitira fanizo kusiyanasiyana kwa chilango. Pamene munthu avomereza ku mtundu wopepuka wa chiwongolero, iye sadzafunikira kuchitiridwa mwaukali pankhani imodzimodziyo.—Yesaya 28:26, 27.
Chotero mungapeŵe chiwongolero chachikulu mwakuvomereza mofulumira kukusuliza m’mitundu yake yopepuka. Monga chitsanzo, kodi mukudziŵa kuti nthaŵi zambiri mumafika pantchito mochedwa? Wongolerani chizoloŵezicho tsopano lino, wokulembani ntchito asanalankhule nanu za icho. Kodi iye wakudziŵitsani kale za chimenecho? Vomerezani panthaŵi yomweyo mwakukhala wosunga nthaŵi, iye asanadzimve wokakamizika kuchita kanthu kakakulu.
Mungakulake
Kusulizidwa kungavulaze. Mungafune kuti anthu akusiyeni nokha, kuleka kukuweruzani, kuleka kupereka ‘malingaliro othandiza.’
Koma kulakalaka ndi kupeŵa sikudzaletsa kusuliza. Kukhala wosuliza ndiko mbali ya chibadwa cha anthu tsopano. Kuwonjezera apa, mulibe ulamuliro pa luso limene ena amagwiritsira ntchito m’kupereka uphungu wosapemphedwa.
Mmalo modandaula, gwirani mwaŵi wa zimene mungathe kulamulira: kayankhidwe kanu. Gwiritsirani ntchito ena a malingaliro omwe ali pamwambawo kulakira kusuliza ndikuchepetsako ululu wake. Mudzakondwera kuti munatero.
Kupereka Chisulizo
Ngati mumadana nkulandira chisulizo, mungakhalenso ndi vuto m’kuchipereka. Panopo pali zitsogozo zofunikira kukumbukira popereka chisulizo:
Gwiritsira ntchito mawu ochepa. Zoyesayesa zosalingaliridwa bwino zakupeŵa kuvulaza malingaliro a uyo amene mukusuliza kaŵirikaŵiri zimachokera ku kuchulukitsa mawu, omwe sangapereke uthenga womvekera.
Peŵani kusuliza chophophonya chaching’ono chirichonse chomwe mungachiwone mwa munthuyo. Izi zimakwiyitsa, ndipo anthu m’kupita kwa nthaŵi sadzawona malingaliro anu kukhala ofunika. Iwo angayambedi kukupeŵani. Aliyense ngopanda ungwiro ndipo ali ndi zophophonya. Sangagwirire ntchito pa zonsezo panthaŵi imodzi. Ngati chophophonya chimene mwachiwona nchaching’ono, chiloleni kungodutsa. Monga momwe Baibulo likunenera kuti: ‘Chikondano chikwirira unyinji wa machimo.’—1 Petro 4:8.