Lingaliro la Baibulo
Imfa ya Mwana—Kodi Mulungu Amailoleranji?
MAKOLO ambiri oferedwa amatonthozedwa atadziŵa kuti Mulungu sanatenge mwana wawo paimfa, monga mmene zipembedzo zina zimaphunzitsira.a Komabe, pali mfundo yotonthoza yakuti: Mulungu ali nayo mphamvu yakuletsa imfa. Komabe, amailola kupitirizabe.
Chotero pamene mwana wamwalira, makolo angalire movutika mtima kuti, “Kodi nchifukwa ninji Mulungu anachilola kuchitika?” Imfa, kaya mwangozi, mwamatenda, kapena mwachiwawa, imawonekera kukhala pafupifupi kupanda chilungamo koipa. Imfa ya mwana imawonekeradi kwenikweni tero. M’manda ena mawu olembedwa pamanda a mwana anazokotedwa ndi ndakatulo yaukali iyi: “Wamng’ono tere, wapamtima tere, nafa mofulumira tere.”
Mlengi Amakulingalirani
Kodi Mulungu amakulola bwanji kupwetekaku? Ngati munaferedwa mwana posachedwapa, palibe mawu, kaya akhale olingalirika motani, omwe angathetse kupweteka kwa imfayo. M’nthaŵi za Baibulo, ngakhale amuna achikhulupiriro kwambiri anaipidwa ndi masoka oipa a moyo nafunsa Mulungu chifukwa chimene analolera zinthu zoterozo. (Yerekezerani ndi Habakuku 1:1-3.) Koma m’Baibulo muli mayankho amene m’kupita kwanthaŵi angatitonthoze.
Choyamba dziŵani kuti Mulungu sanafune kuti mwana wanu amwalire. Mulungu samakondwera ngakhale ndikuwonongeka kwa oipa, osati ngakhale imfa ya mwana. (Yerekezerani ndi 2 Petro 3:9.) Motsimikizirika, iye amaipidwa kwambiri mwana atamwalira. Ndiiko nkomwe, timakumva kupweteka kwa imfa kokha chifukwa chakuti tiri okhoza kukonda, kuchitira chisoni minkhole yake. Ndipo tiri okhoza kukonda kokha chifukwa chakuti tinapangidwa m’chifanefane cha Mulungu. Timasonyeza mphamvu zangwiro za Mulungu za kukonda, chinkana kuti ndife ofookadi. (Genesis 1:26; 1 Yohane 4:8) Baibulo limatsimikizira kuti Mulungu amadziŵa kulingalira kwathu kwamkati mwa mitima, amaŵerenga tsitsi lenilenilo la m’mutu mwathu, iye amadziŵa ngakhale pamene timba wagwa mumtengo. Chotero, iye akutchedwa “Atate wa zifundo.”—2 Akorinto 1:3; Mateyu 10:29-31.
Pamenepa, nkwachiwonekere kuti Mulungu samafuna kuti chirichonse cha zolengedwa zake zaluntha chife. Iye walinganiza kuthetsa imfa, kuimeza kosatha. (Yesaya 25:8) Koma ngati umu ndimmene amalingalirira, kodi nchifukwa ninji amailola imfa pakali pano, makamaka kwa ana?
Pamene Imfa Inayamba
Mulungu amawalola ana kufa kaamba ka chifukwa chofanana ndi chimene amalolera achikulire kufa. Imfa inali chosankha cha Adamu, osati cha Mulungu. Ngakhale Adamu ndi Hava asanapanduke motsutsana ndi Mlengi wawo mu Edene, iwo anadziŵa bwino kwambiri kuti Mulungu anaika chilango chauchimo kukhala imfa. Ngati iwo sanasankhe kukhala osakhulupirika kwa Mulungu, iwo akanakhalabe ndi moyo lerolino. Koma mopusa iwo anachitaya choloŵa chawo chamtengo wapatali chimene akanachipereka kwa ana awo—kuyenerera moyo wangwiro, wamuyaya pano padziko lapansi. Atachimwa, iwo sanalinso angwiro. Chinthu chokha chomwe anakhoza kupatsira kwa mbadwa zawo chinali uchimo ndi imfa.—Genesis 3:1-7; Aroma 5:12.
Koma inu mungadabwe kuti: ‘Popeza kuti mtengo unali waukulu kwambiri, kodi nchifukwa ninji Mulungu analola Adamu ndi Hava kuchimwa? Kapena kodi nchifukwa ninji sanachotsepo kupanduka kwawoko asanapatsire imfa ndi masoka kwa ana awo—ndi ana athu?’
Panaphatikizidwa Nkhani ya Chilengedwe Chonse
Mulungu anawalola makolo athu oyamba kusamvera chifukwa chakuti sanalingalirepo kupanga dziko la anthu oti nkuŵachitira zinthu, omwe akatumikira Mulungu kokha chifukwa chakuti adalinganizidwiratu kuchita tero. Mofanana ndi kholo lirilonse, Mulungu anafuna kuti ana ake aumunthu amumvere mwa kulingalira ndi kukonda, osati mokakamizidwa. Iye anapatsa Adamu ndi Hava zifukwa zokwanira kumkhulupirira ndi kumkonda, koma iwo sanamumvere nakana kulamulira kwake.—Genesis 1:28, 29; 2:15-17.
Kodi nchifukwa ninji Mulungu sanawaphe opandukawo pomwepo? Mulungu anali atanena kale chifuno chake kuti dziko lapansi tsiku lina likakhalidwa ndi mbadwa za Adamu ndi Hava. Iye samalephera kukwaniritsa zifuno zake. (Yesaya 55:10, 11) Koma chofunika kwambiri nchakuti, funso lalikulu linadzutsidwa mu Edene. Kodi Mulungu ali ndi kuyenerera kwa kulamulira anthu, ndipo kodi njira Yake njabwino koposa, kapena kodi anthu angadzilamulire okha bwino lomwe?
Njira yolungama yokha yoyankhira funsoli kamodzi kwatha inali ya kulola anthu kudzilamulira okha. Mbiri yakale yaliyankha mwachisoni funsoli. Zotulukapo zosakaza za kulamulira kwa anthu ziri ponseponse—dziko m’limene imfa ya ana opanda liŵongo njofala, pafupifupi lodzala ndi upandu wokhawokha. Ngati palibenso china, zaka zikwi zisanu ndi chimodzi za kulamulira kwa anthu zatsimikizira ichi: Lingaliro lakuti anthu angadzilamulire okha popanda Mulungu nloipa kwenikweni kuposa chinyengo chirichonse; ndibodza lamkunkhuniza. Malinga ngati anthu alamulira popanda Mulungu, anthu adzakhala ndi moyo nafa mowawitsa.
Yehova, Mulungu wachikondi, wolungama, ali ndi chosankha chanzeru. Mofanana ndi mmene kholo lingalolere mwana wokondedwa kukachitidwa opareshoni yopweteka kaamba ka mtsogolo mwachimwemwe ndi mwaumoyo wabwino mwa mwanayo, Mulungu walola anthu kupyola m’nsautso ya kudzilamulira kaamba ka mtsogolo mosatha mwa anthu. Ndipo monga mmene kuwawa kwa opareshoni sikumakhalirira, kulamulira kwa anthu ndi chisalungamo chake zidzatha posachedwapa.
Pamene Ufumu wa Mulungu udzalamulira popanda wotsutsa pano padziko lapansi, ana mamiliyoni ambiri adzaukitsidwa ndikulandiridwa kuchokera kwa akufa. Mofanana ndi makolo amene Yesu anawaukitsira ana awo m’zaka za zana loyamba C.E., anthu ambiri panthaŵiyo ‘adzadabwa kwakukulu.’ (Marko 5:42; Luka 8:56; Yohane 5:28, 29) Ndipo pamene anthu onse potsirizira pake abwezeretsedwa kumkhalidwe wangwiro umene Adamu ndi Hava anautaya, pamenepo palibe munthu amene adzamwaliranso—kuphatikizapo ana!—Chibvumbulutso 21:3, 4.
[Mawu a M’munsi]
a Onani “The Bible’s Viewpoint—‘Why Did God Take My Child?’” m’kope la Awake! la February 8, 1991.
[Mawu Otsindika patsamba 15]
Ana mamiliyoni ambiri adzaukitsidwa ndikulandiridwa kuchokera kwa akufa