Lingaliro la Baibulo
Kodi Baibulo Limalola Kugwira Njoka?
MUMATCHALITCHI aang’ono, okhulupirika amasonkhana. Iwo amaliza magitala amagetsi ndi kuimba nyimbo zachipembedzo. Amapereka mapemphero a kuchiritsa. Amamvetsera ku maulaliki okhweka namabwebweta mokondwera m’zimene amatcha “zinenero zatsopano.” M’zonsezi, iwo saali osiyana kwenikweni ndi gulu lirilonse la Apentekoste kapena timagulu tachipembedzo m’Chikristu Chadziko. Ndiyeno amatenga ululu, moto, ndi njoka.
Kaŵirikaŵiri ululuwo umakhala strychnine, yosungunulidwa m’madzi. Moto ungakhale wa nsalu yoyaka yoviikidwa m’parafini kapena tochi ya acetylene, ndipo njoka zingakhale marattlesnake kapena zotchedwa copperhead, zosavuta kupeza mu Appalachian Mountains ku United States, kumene magulu ameneŵa ali owanda kwambiri. Atalingalira kuti awuzidwa ndi “mzimu” kutero, iwo adzamwa ululuwo ndikuika manja awo pamoto. Angagwirenso njoka, ndikuzikoloŵeka m’mikono ndi m’mapeŵa awo, kuziyandikitsa pafupi ndi matupi awo, nkumapatsirana. Nchifukwa ninji?
“Ndimagwira njoka chifukwa chakuti zinalembedwa m’Baibulo, monga lamulo,” akutero Dewey, mtsogoleri wa tchalitchi chaching’ono ku West Virginia.a Dewey akunena kuti analumidwa kwanthaŵi 106, ndipo ali ndi zipsera zotsimikizira nkhaniyo. Kodi Baibulo limalamuliradi kuchita zinthu zoterozo?
“Usamuyese Ambuye”
“Iye wosakonda samdziŵa Mulungu; chifukwa Mulungu ndiye chikondi,” limatero Baibulo pa 1 Yohane 4:8, King James Version. Kodi Mulungu wachikondi angafune kuti alambiri ake adzipweteke okha mosafunikira? “Kulumako kumapweteka,” akutero Dewey. “Ndikupweteka koŵirikiza pafupifupi nthaŵi 100 kuposa kuŵaŵa kwa dzino . . . Umamva ngati kuti uli pamoto.” Chinkana kuti ambiri olumidwa ndi njoka amapulumuka, imfa zambirimbiri zaikidwa m’cholembedwa, kuphatikizapo imfa ya mchemwali wa Dewey mu 1961.
Ndithudi, Akristu nthaŵi zonse akhala okonzekera kufera chikhulupiriro chawo, koma imfa zawo kaŵirikaŵiri zachititsidwa ndi anthu ena chifukwa chakukana kulolera molakwa malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo. Kumbali ina, pamene Satana anaitanira Yesu Kristu kuika moyo wake pachiswe mosafunikira ndipo mwadala mwakulumpha kuchoka pachimbuzi cha pakachisi m’Yerusalemu, “Yesu ananena naye, Ndiponso kwalembedwa, Usamuyese Ambuye Mulungu wako.” (Mateyu 4:7, KJ) Kodi sindiko kumuyesa Mulungu kuseŵera ndinjoka, moto, kapena ululu, kapena modzigangira kumtokosa? Kodi kuyesa koteroko sikumasonyeza kusoŵeka kwakukulu kwa chikhulupiriro kwa mlambiri, kuyesa kukakamiza Mulungu kuti atsimikiziritse kuwona kwa Mawu ake mwakuchita zinthu zodabwitsa?
Kodi Malemba Amalamuliranji?
Mamembala a timagulu togwira njoka amanena kuti zochita zawo nzolamuliridwa ndi Mawu a Mulungu, ndipo iwo amatchula Marko 16:17, 18 kukhala umboni. Malinga ndi King James Version, mavesi ameneŵa amati: “Ndipo zizindikiro izi zidzawatsata iwo akukhulupirira; M’dzina langa adzatulutsa ziŵanda; adzalankhula m’malirime atsopano; adzatola njoka; ndipo ngakhale akamwa kanthu kakufa nako, sikadzawapweteka; adzaika manja awo pa odwala, ndipo adzachira.”
Choyamba, muyenera kudziŵa kuti pafupifupi akatswiri onse Abaibulo amavomereza kuti mavesiŵa poyambirira sanali mbali ya Uthenga Wabwino wa Marko. “Kuwona kokaikiritsa kwa mavesi 9-20 kumachipangitsa kukhala kopanda nzeru kupanga chiphunzitso kapena kuwakhazikitsa maziko a chochitika (makamaka mave. 16-18),” akulongosola motero wothirira ndemanga wotchuka Charles Ryrie.
Komabe, omwe amagwira njoka m’kulambira kwawo nthaŵi zambiri samakondweretsedwa ndi zimene akatswiri Abaibulo amalingalira ponena za kuwona kwa Marko 16:9-20. Mavesiŵa ali m’Baibulo la King James, Baibulo lokha lomwe ambiri a iwo amakhulupirira, ndipo kwa iwo zonse zithera pamenepo.
Koma ngakhale ngati mavesiŵa anali owona, iwo samalamulira kugwira njoka kapena kumwa ululu, ndipo samalankhula kalikonse ponena zamoto. Chotero iwo sangaŵerengedwe kukhala chiyeneretso chakulambira. Kwenikweni, mtumwi Paulo anakumana ndi njoka pa chisumbu cha Melita koma zinali mwangozi chifukwa chakuti inali mumtolo wankhuni zomwe anali kusonkherera moto. Chinkana kuti Paulo analumidwa ndipo anachinjirizidwa mwamphamvu ya Mulungu kusapwetekedwa, iye sanapatsire ena njokayo kuti aigwire. Mmalomwake, iye ‘anakutumulira chilombocho kumoto.’ Mosiyana kwambiri ndikumva kupweteka komyula mtima komwe ogwira njoka amakono amakumva, iye “sanamve kupweteka.”—Machitidwe 28:3-6, KJ.
Kodi Nchiyeso cha Chikhulupiriro?
Mogwirizana ndi The Encyclopaedia of American Religions, kugwira njoka kuli kwenikweni chochitika chaposachedwapa. Iyo ikuti: “Mu 1909, George Went Hensley, nzika yachichepere ya kumalo akumudzi a Grasshopper Valley, Tennessee, anakhutiritsidwa kuti zilozero za Marko 16:17-18 ku njoka ndi ululu zinali, lamulo kwenikweni. Iye anagwira njoka yotchedwa rattlesnake ndipo masiku oŵerengeka pambuyo pake pa Sale Creek yapafupi, mkati mwa utumiki wakulambira, anatulutsa njokayo kuti otengamo mbali aigwire monga chiyeso cha chikhulupiriro chawo.” Koma palibe umboni wa m’Malemba kapena mu mbiri yakale, wakuti Akristu oyambirira anafunikira ‘chiyeso cha chikhulupiriro chawo’ choterocho.
Kuwonjezerapo, talingalirani izi: Paulo anagwiritsiridwa ntchito ndi Mulungu kuukitsa akufa; chikhalirechobe anadzichenjerera mwanzeru kaamba ka thanzi lake ndi la anzake. (1 Timoteo 5:23; 2 Timoteo 4:13) Paulo sanayeseyese kupeza mwaŵi woukitsa akufa.
Chotero, mmalo mwakuchititsa matupi kupweteka ndi mabala a kulumidwa ndi njoka, Akristu amalimbikitsidwa “kupereka matupi awo nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwawo koyenera.” (Aroma 12:1, KJ) Mmalo molamulira Akristu kuyesa chikhulupiriro chawo ndi zochita zaupandu, uphungu wanzeru wa mtumwiyo ngwakuti: “Dzisanthuleni nokha, kaya ngati muli m’chikhulupiriro; dzitsimikizireni nokha.” (2 Akorinto 13:5, KJ) Yesani zikhulupiriro zanu moyerekezera ndi Mawu a Mulungu. Kudzipenda kowona mtima kwaumwini, kuziyerekezera zikhulupiriro zanu ndi Malemba, kudzakuthandizani kutsimikizira kaya ngati chikhulupiriro chanu chidzapambana chiyeso chofunika koposa cha chivomerezo cha Mulungu.
[Mawu a M’munsi]
a Kope la magazini a People, a May 1, 1989.