Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 6/8 tsamba 30
  • Kalata ya Chiyamikiro

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kalata ya Chiyamikiro
  • Galamukani!—1991
  • Nkhani Yofanana
  • Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!—Magazini Apanthaŵi Yake a Chowonadi
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Gawirani Magazini mu Utumiki Wanu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Kodi Magaziniwo Mumawaŵerenga?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Sankhani Nkhani Zokopa Chidwi cha Anthu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 6/8 tsamba 30

Kalata ya Chiyamikiro

MIYEZI ingapo yapita magazini a Galamukani! analandira kalata kuchokera kwa wophunzira wina wachichepere m’mene analongosola zotsatirazi:

“Magazini anu ngopatsa chidziŵitso koposa, osavuta kuŵerenga ndi kuwamva, apanthaŵi yake, ndi olimbikitsa amene sindinaŵerengepo. Iwo ali ndi chowonadi cha Mawu a Mulungu mumpangidwe womvekera bwino. Amafotokoza zochitika zapanthaŵiyo ndi kupatsa chidziŵitso ndi chiyembekezo cha mtsogolo.

“Mawu ogwiritsidwa ntchito ngosavuta kwa munthu wachichepere kuŵerenga, osavuta kwambiri kuposa ndi magazini ena, mabuku anazonse, ndi mabuku a zilozero. Ndipo ngapanthaŵi yake. Kaŵirikaŵiri ndimazizwa za chinthu chinachake, ndiyeno ndimapeza yankho m’kope lotsatira.

“Pokhala wophunzira wa ku sekondale, ndiyenera kufufuza kwambiri popanga malipoti ndi maprojekiti osiyanasiyana, zimene zimafuna mabuku ambiri a zilozero. M’mbaliyi ndimmene magazini anu atsimikizira kukhala othandiza kwenikweni. Ndiri wokondwa kunena kuti chidziŵitso cha unyinji wa maprojekiti anga chachokera m’magaziniŵa. Nthaŵi zonse kumawonekera kuti pamene ndifuna mutu wa nkhani ya projekiti, umakhalamo m’magazini. Kapena pamene ndikuphunzira chinachake kusukulu, nkhani pa mutu umenewo irimo kundithandiza kuumvetsetsa.

“Mwachitsanzo, ndinafunikira mutu wankhani wa projekiti yasayansi kaamba ka Science Fair yomwe timafunidwa kukhalamo ndi phande. Inayenera kukhala ndi zithunzithunzi zomamatiza zitatu, lipoti, ndi fanizo. Chotero ndinasankha mutu wankhani imene anthu ambiri amazizwa nayo masiku ano: greenhouse effect [chiyambukiro cha kutentha kwa dziko]. Inafotokozedwa mu Awake! ya September 8, 1989. Ndinagwiritsira ntchito chithunzithunzi cha mkati mwa chikuto monga chithunzithunzi chomamatiza chimodzi ndi chithunzithunzi cha patsamba 7 kaamba ka china. Chithunzithunzi chomamatiza chachitatu chinali cha miyalo ya thambo. Ndinagwiritsiranso ntchito chidziŵitso m’nkhanizo m’lipoti langa. Aliyense anakonda projekiti yanga ndi njira yomwe ndinaiperekera, makamaka mphunzitsi wanga wa biology. Iye anandipatsa A, ndipo ndinalandira mphotho yoyamba m’gawo langa la Ecology and Conservation.

“Ndiyeno, mu March, ndinafunikira mutu wankhani kaamba ka ntchito yanga yogaŵiridwa ya First Aid. Mu Awake! ya March 22, 1990, ndinawona nkhani yonena za phumi ndi mankhwala ake. Ndinasankha kugwiritsira ntchito chithunzithunzi cha patsamba 17 kaamba ka chithunzithunzi chomamatiza ndi chidziŵitso kaamba ka lipoti. Ndinalandiranso A m’projekiti imeneyi.

“M’kalasi yathu ya History ya Amereka, tinaphunzira za kutsungula kwamakedzana, konga ngati kwa Amaya, Aztec, ndi Inca, ndipo mungafune kudziŵa, pamene ndinafika kunyumba madzulo ena, Awake! ya May 8, 1990, inali kundiyembekezera m’bokosi lamakalata. Ndinaitulutsa m’chikuto chake kuwona zamkati ndipo ndinafika pankhani ina patsamba 13, yofotokoza kutsungula kwa Amaya. Ndinakondwera kwabasi. Panthaŵi yomweyo ndinaŵerenga nkhaniyo ndipo ndinapatsa mphunzitsi wanga wa mbiri yakale kope limodzi.

“Zikomo kaamba ka chidziŵitso chapanthaŵi yake chonsechi, chimene chimapanga kuchita maprojekiti ameneŵa kukhala chokumana nacho chophunzitsa ndi chosangalatsa mmalo mwa chothodwetsa. Ndithudi, magaziniŵa ali ngati ngale zamtengo wapatali. Sindidzafuna kuŵasiya konse. Iwo alidi othandiza, makamaka kwa achichepere onga ine, amene angasokonezedwe mosavuta. Mwakuŵerenga magaziniŵa, kuphatikizapo nkhani za ‘Achichepere Akufunsa Kuti,’ timalimbikitsidwa ndi nyonga yoletsa zosokoneza ndi kusumika maso athu pa mphotho ya moyo wosatha. Zikomo kwambiri kaamba ka ntchito yanu yaikulu yokonzekera magazini ameneŵa kaamba ka kumvetsetsa kwathu ndi chisangalalo.”—Yoperekedwa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena