Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 8/8 tsamba 27-29
  • Kulaka Moyo Wachiwawa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulaka Moyo Wachiwawa
  • Galamukani!—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Wachiwawa Koposa Pambuyo Pakumasulidwa
  • Chiwawa Chiwonjezereka
  • Njira Yabwino Koposa
  • Njira Yatsopano ya Moyo
  • Baibulo Limasintha Anthu
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndisiye Kugwiritsa Ntchito Mankhwala Osokoneza Bongo?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
  • Ndinamasuka ku Mikwingwirima ya Paubwana Wanga
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kodi Tingapambane Pankhondo Yolimbana ndi Mankhwala Osokoneza Bongo?
    Galamukani!—1999
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 8/8 tsamba 27-29

Kulaka Moyo Wachiwawa

BWENZI langa ndi ine tinathamanga monga momwe tikanathera, ndipo pamene tinafika pamtsinje wapafupi ndi tauni yakwathu, tinagweramo. Pamene tinawonekera pamwamba pamadzipo, tinayamba kusambira mwachiwawa kulinga kutsidya lina.

Kodi umenewu unali mpangidwe wina wa maseŵera akuubwana? Kutalitali! Inali nkhani ya moyo ndi imfa. Pamene ndinayang’ana kumbuyo, ndinawona apolisi ndi zida zawo akunenekera pa ife. Ndinamiranso m’madzi kuti ndithaŵe zipolopolo ndipo ndinapitirizabe kusambira kulinga kutsidya lina. Ngakhale pansi pamadzipo, ndinakhoza kumva kulira kwamfuti.

Pamene tinafika kutsidya linalo, tinali achipambano kuthaŵa kundende, kumene tinatsekeredwa chifukwa cha kuba mwakuthyola nyumba ndi kuba galimoto.

Iyi inali imodzi ya nthaŵi zambiri zimene ndinakhala ndikufunidwa kapena kuthamangitsidwadi ndi apolisi chifukwa cha kachitidwe kaupandu. Ngakhale kuti ndinali ndi zaka 17 zokha panthaŵiyo, ndinali nditapanga kale mbiri yaitali ya kugwidwa ndi olamulira. Potsirizira pake, ine ndi bwenzi langalo tinagwidwa, ndipo kachiŵirinso ndinaweruzidwa kukhala m’ndende, panthaŵiyi kwa nyengo ya zaka ziŵiri ndi theka.

Ngakhale m’ndendemo ndinasonyeza mkhalidwe wachiwawa. Chifukwa cha kumenyana ndi akaidi anzanga mobwerezabwereza, ndinapatsidwa yunifomu yoyera. Ichi chinapangitsa ovutitsa enawo ndi ine kuwonekera bwino kwa alonda kaamba ka chisamaliro chapadera.

Wachiwawa Koposa Pambuyo Pakumasulidwa

Ndinamasulidwa kundende, koma sindinasinthe kukhala wabwinopo. Kwenikwenidi, ndinali wachiwawa koposerapo kuposa kale. Posakhalitsa ndinazindikiridwa monga wolamulira wa makwalala ambiri. Aliyense amene ananditokosa anapeza wolimbana naye wofunitsitsa.

Panthaŵi ina kagulu ka amuna achichepere kanandikwiitsa. Ndinawaukira, ndipo apolisi asanafike kudzaletsa ndewuyo, ndinali nditavulaza ambiri ngakhale kuti mkono wanga wakumanja unathyoka pandewu ina mlungu umodzi wapitawo.

Nthaŵi ina ine ndi mabwenzi anga aŵiri tinatokosa kagulu ka amuna a m’tauni yoyandikana nayo. Mtsogoleri wawo anabwera pafupi kukumana nane ali ndi mpikidzo wachitsulo. Ndinamulanda chidacho, koma anapudzumuka m’manja mwanga nathaŵa. Njira yokha yompangitsa kupitirizabe ndewuyo inali kumbwezera mpikidzo wake wachitsulowo, ndipo ndinatero. Iye anabwerera, ndipo ndinamlanda kachiŵirinso chidacho, panthaŵiyi ndikumatsimikizira kuti sanathaŵe kufikira nditam’menya kwabasi.

Usiku wina, kungofuna “kusanguluka,” ndinaima pangondya ya khwalala mu Harlem, New York City, ndipo ndinatokosa aliyense kuti timenyane. Anthu osiyanasiyana anavomereza kumenyana nane, ndipo nkhondozo zinali zambiri. Monga chotulukapo, kutchuka kwanga monga munthu wowopsa, ndi wachiwawa kunawonjezeka. M’nkhondo zosiyanasiyana zimenezi, ndinamenyedwa ndi mabotolo, ziwiya zosinthira magudumu agalimoto, ndi zibonga ndipo ndinapyozedwa ndi mipeni ndi zida zina. Koma zonsezi sizinachite kalikonse kundisintha ku njira zanga zachiwawa.

Chiwawa Chiwonjezereka

Posakhalitsa ndinatumba kuti ndingapange ndalama zambiri m’malonda a mankhwala ogodomalitsa. Pokhala wogwiritsira ntchito mankhwala ogodomalitsa, ndinali wozoloŵerana ndi chitaganya cha mankhwala ogodomalitsa. Pasanapite nthaŵi yaitali ndinali ndi anthu ondigulitsira mankhwala ogodomalitsa, ndipo ichi chinandipanga kukhala wachiwawa kwenikweni.

Nthaŵi ina tinalalira wogulitsa mankhwala ogodomalitsa wina, tikumayembekezera kumbera mankhwala ake. Tiri okonzekera ndi mfuti yakumanja ndi mpeni, tinaloŵa m’nyumba mwake ndikugwira amuna atatu ndi mkazi pamene tinkasanthulasanthula m’nyumbamo, kufunafuna mankhwala ogodomalitsa.

Panthaŵi ina ine ndi bwenzi langa, titanyamula mfuti za sabuleta ndipo titavala zophimba kumaso zosambira, tinalingalira zobera munthu wina wachuma kotero kuti tipeze ndalama zogulira mankhwala ogodomalitsa. Tinathyola nyumba yake, koma iye sanawonekere konse, choncho tinachokapo. Mosakaikira, ngati iye akanawonekera, tikanachita zofuna zathu.

Chotero, pamsinkhu wazaka 20 zokha, ndinadzipeza ndiri woloŵetsedwa mozama m’chiwawa, mankhwala ogodomalitsa, ndi maupandu owopsa. Mothekera kwenikweni, mtsogolo mwanga munali moyo wothera m’ndende—ndipo sindinali wosangalala.

Kaŵirikaŵiri ndinakaika kuti ndani ayenera kusankha chimene chiri chabwino ndi chimene chiri choipa. Ndinatsimikiza kuti anali aliyense amene anali ndi mphamvu yaikulu m’chitaganya. Ndinalingaliranso kuti popeza kuti anthu anali kudzisankhira chabwino ndi choipa, ndipo sindinalemekeze ulamuliro waumunthu uliwonse, ndinali ndi kuyenera kokulira kwakudziyankhira ndekha funso limenelo. Koma ndinayenera kupeza yankho labwinopo mwamsanga.

Njira Yabwino Koposa

Mlongo wanga, yemwe anakwatiwa ndi mmodzi wa mabwenzi anga omwe ndinali nawo m’ndende, anavomereza phunziro Labaibulo ndi Mboni za Yehova. Iye anagawana ndi aliyense wam’banja mwathu zinthu zimene anali kuphunzira m’Baibulo—kupatulapo ine. Banja langa linali kundiuza kuti ndidzimthaŵa mlongo wangayo. Chifukwa ninji? Iwo anati chifukwa chakuti zonse zimene amalankhula ndi za “chipembedzo chopenga” chija.

Ndinakopeka. Kodi iye anali kunenanji zomwe zinakwiitsa anthu kwambiri motero? Ndinafuna kudziŵa, koma mlongo wanga sanalankhule nane ponena za izo. Nchifukwa ninji sanatero? Iye anaganiza kuti ndinali woipitsitsa kwakuti sindingamvetsere chirichonse chonena za Baibulo.

Koma madzulo ena ndinapempha mlongo wanga ngati ndingapite kunyumba kwake kukadya chakudya chamadzulo. Ndinali khale ndikumadya ndi mlongo wanga ndi mwamuna wake, ndipo ndinanena kuti: “Tandiuzani ponena za chipembedzo chatsopanochi.” Iwo anatero—kwa maola asanu ndi limodzi! Zinamveka zanzeru kwa ine kotero kuti ndinabwererako madzulo otsatira kukamva zowonjezereka.

Pambuyo paulendo wachiŵiriwu, ndinakhutiritsidwa kuti ndinapeza chinachake chokhalira moyo, cholinga chenicheni cha moyo. Mwamsanga, ndinayamba kufika pamisonkhano pa Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova ndi kulankhulanso kwa mabwenzi anga ponena za zimene ndinali kuphunzira.

Njira yanga yamoyo sinasinthe kwa kanthaŵi. Koma ndinapitiriza kuphunzira ndi kudziŵa zimene Yehova Mulungu anayembekezera, ndipo ndinatsimikiza kuti ndisaphonye misonkhano pa Nyumba Yaufumu, kumene Baibulo linali kufotokozedwa. Mwanjirayi ndinapeza nyonga yauzimu yosinthira moyo wanga, chinthu chimodzi panthaŵi imodzi.

Choyamba, ndinaleka kugulitsa mankhwala ogodomalitsa. Ichi chinakwiitsa ena a awo amene ndinagwirizana nawo papitapo, koma ndinali ndidakali ndi mbiri yanga yachiwawa, imene inandipulumutsa ku chivulazo. Chotsatira, ndinaleka kugwiritsira ntchito mankhwala ogodomalitsa amphamvu ndipo ndinalekanso moyo wanga wachiŵereŵere. Chinthu chomalizira chomwe ndinaleka chinali chizoloŵezi changa cha fodya. M’miyezi isanu ndi itatu ndinapita patsogolo kufikira pa kuyeneretsedwa kaamba ka ubatizo, ndipo ndinabatizidwa mu 1970.

Pomalizira pake ndinafika pakuzindikira kotheratu yankho la funso langa lonena za amene amasankha chimene chiri chabwino ndi chimene chiri choipa. Yankho nlakuti: Yehova, Mpatsi wathu wa Moyo, ndiye ali ndi kuyenera kumeneko, ndipo iye alinso ndi kuyenera kwakuyembekezera zolengedwa zake kukhala ndi moyo mofananamo.

Kaŵirikaŵiri ndinalingalira mmene fanizo la pa Yesaya 65:25 linagwirira ntchito kwa ine mophiphiritsira. Ulosi umenewo umalankhula ponena za nthaŵi imene ikudzayo pamene mkhalidwe wachiwawa wa mkango udzasinthidwa kukhala wamtendere kufika pamlingo wakuti udzadya udzu ngati ng’ombe. Ndinalingalira kuti m’njira yofananayo, ndinasintha kuchoka pakukhala munthu wachiwawa kukhala munthu wokhala ndi mkhalidwe wamtendere ndi kawonedwe ka moyo kamtendere.

Komabe, ndinali ndi mbiri yoipa yofunikira kusinthidwa ndi khalidwe labwino. Mwachitsanzo, ndinali kufikira anthu mosalekeza kukhomo ndi khomo kukambitsirana nawo Baibulo. Pakhomo lina, mwamuna wachichepere yemwe anayankha anandizindikira ndipo anachita mantha, akumalingalira kuti ndabwera kudzamvulaza. Ndinafotokoza mofulumira uthenga wanga wamtendere wochokera m’Baibulo, ndikumamsiya wodabwa koma womasuka kwenikweni.

Pasanapite nthaŵi yaitali pambuyo pa ubatizo wanga, ndinakwatira mmodzi wa Mboni za Yehova. Nzovetsa chisoni kuti, mu 1974 mkazi wanga anasankha kuti sanafunenso kuchita chifuniro cha Mulungu. Iye anandipatsa chosankha ichi: kuleka kulambira kwanga kapena andisiye, kupita ndi ana athu aŵiri aang’ono. Imeneyo inali nthaŵi yovuta kwambiri m’moyo wanga. Koma sindikanasiya kulambira kwanga Mulungu, ndipo ndinapitiriza kuchita chifuniro chake.

Njira Yatsopano ya Moyo

Komabe, Yehova anandifupa chifukwa chakupitiriza kukhala wokhulupirika kwa iye. Mu 1977, ndinakumana ndi Mboni yabwino koposa, ndipo tinakwatirana. Iye anali ndi mwana wamwamuna wazaka zisanu zakubadwa. Posakhalitsa mkazi wanga ndi ine tinaloŵa utumiki wanthaŵi zonse, tikumadzipereka enife kuphunzitsa ena ponena za Mulungu ndi zifuno zake. Pamene mwana wathu anakula, nayenso analoŵa utumiki wanthaŵi zonse. Tsopano amathandiza ndi mathayo osiyanasiyana mumpingo wakumaloko.

Mkazi wanga ndi ine takhala ndi mwaŵi wakupita kumbali zambiri zadziko, kuchita ntchito yomanga yodzifunira. Ntchitoyi imaphatikizapo kuthandiza kumanga nthambi zatsopano m’maiko osiyanasiyana kuchilikiza ntchito yophunzitsa yapadziko lonse ya Mboni za Yehova.

Pamene tiri kunyumba, timakhala otanganitsidwa kumaloko, kuthandiza ena kuphunzira ponena za Baibulo ndi kuthandiza kumanga Nyumba Zaufumu zatsopano. Ndimatumikiranso mu Regional Building Committee kumbali yakum’mwera kwa United States. Ndipo mnzanga wakundende wakale—mwamuna wake wa mlongo wanga—ndi ine timatumikira monga akulu mumpingo umodzimodzi wa Mboni za Yehova.

Ndiyamikira Yehova chifukwa chondithandiza kulamulira moyo wanga ndi kuupatsa chitsogozo chatsopano kotheratu. Pamene ndimlola kundisonyeza chimene chiri chabwino ndi chimene chiri choipa, moyo wanga umakhala bwino koposerapo.—Yoperekedwa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena