Anadabwa ndi Zimene Anawona
CHILIMWE chathachi kumbali zambiri za Kum’maŵa kwa Yuropu limodzinso ndi Kazakhstan wakutali ndiponso Siberia, Mboni za Yehova zinawonedwa m’njira zosiyana ndi kalelonse. Nzika zakumaloko ndi alendo obwera kumisonkhano m’malowo anachita chidwi, inde, ngakhale kudabwa, ndi zimene anawona.
Nthumwi za ku Zagreb zinauzidwa mobwerezabwereza kuti: “Sitinalingalire kuti mudzabwera!” Alendo ambiri ochezera maiko anapha maulendo awo—koma Mboni za Yehova sizinatero. The Times ya London inasimba za msonkhanowo kuti: “Kwenikweni, ndiwo woyamba kulinganizidwa ndi Mboni za Yehova m’dziko limene liri pankhondo.”
Apolisi anazizwa kwambiri. Wina ku Zagreb anati: “Kukakhala bwino kusonyeza pawailesi yakanema zimene zikuchitika m’bwalo lamaseŵerali, kunoko, kumene tikuwona nzika za ku Serbia, Croatia, Slovenia, Montenegro, ndi ena atakhala pamodzi mumtendere.”
Ku Budapest wapolisi wina anafunsidwa kuyerekezera Mboni zosonkhana m’bwalo lalikulu lamaseŵeralo ndi makamu anthaŵi zonse openyerera mpira wachitanyu. Iye anamwetulira, nayang’ana m’mwamba, nati: “Kusiyana kwake kuli ngati kumene kuli pakati pa thambo ndi dziko lapansi.”
“Kodi mukutanthauzanji?”
Iye anayankha nati: “Eya, tangowonani. Palibe amene akusuta, kulibe zinyalala kulikonse, ndipo anthu ali aulemu. Amachita zimene uwapempha.”
Ku Kiev, likulu la Ukraine, 14,654 anasonkhana m’bwalo lamaseŵera la Dynamo. Mboni ina inafunsa mkulu wina wa apolisi ngati antchito ake adafunikira kugwira ntchito zolimba pamsonkhanowo. “Ayi, nthaŵi yotsatira tidzakutumizirani apolisi aŵiri okha.”
“Chifukwa ninji aŵiri?” anafunsidwa motero.
“Pamene mmodzi agona tulo, winayo adzamsamalira,” anayankha moseka.
Anthu Onse Anazizwa
Pesti Hírlap, nyuzipepala ya ku Budapest, inasimba kuti: “Oposa 40,000 anathera mapeto a mlungu uno ku Népstadion. Panalibe kachidutswa kapepala, nyenyeswa ya mkate, ngakhale kafodya komwe kanasiidwa.” Fehérvár Hírlap, pepala lina la mzindawo, linati: “Amene mwamwaŵi analoŵa mu Népstadion pakati pa July 26 ndi 28 anadabwadi. . . . Iwo anawona chitsanzo chopezeka mwakamodzikamodzi cha khalidwe Lachikristu ndi njira ya moyo.”
Mvula yamvumbi inagwa m’Budapest kumapeto a mlunguwo; yoposa masentimita asanu. Koma sinaletse Mbonizo. “Nzodabwitsa! Zothetsa nzeru!” wapolisi wina anamvedwa akunena tero. “Iwo akubwerabe ndi kubwerabe . . . Palibe chimene chingawaletse.” Pa Lolemba nyuzipepala ina inasonyeza mutu wake wankhani uwu “Pemphero Mvula Iri Mkati” nigwira mawu a nthumwi kuti: “Tangosambitsidwa chabe ndi mvulayi, osati kupitikitsidwa!”
Ku Lvov, kumene 17,531 anasonkhana mu bwalo lamaseŵera la Central Ukraine, ofisala wina wapolisi anauza Mboni ina kuti: “Pachochitika wamba chirichonse chopezekapo anthu ochuluka, tikafunikira apolisi mazanamazana. Pamsonkhano wanu tinali nawo khumi, ndipo sanafunikiredi.”
Kenako, akunena mmene anachitira chidwi ndi msonkhanowo, ofisalayo anati: “Mumapambana m’kuphunzitsa ena chabwino, mumalankhula za Mulungu, ndipo simuchita chiwawa. Timakambirana chifukwa chake tinkakuzunzani, ndipo tinapeza kuti sitinamvetsere kwa inu ndipo sitinadziŵe kalikonse ponena za inuyo.”
Atachezera msonkhano ku Usolye-Sibirskoye, Siberia, mkazi amene ndimtola nkhani wa nyuzipepala ya Soviet Union yotchedwa Leninskiy Put’ analemba kuti: “Zinali zodabwitsa kuwona ulemu, limodzinso ndi luso lakuzindikira ndi kuchitapo kanthu pazosoŵa za ena, zimene atumiki a Yehova anasonyeza kwa wina ndi mnzake. Sindidzaiŵala konse mawu onenedwa pamsonkhanowo akuti: ‘Musamaba! Musamanena bodza! Osamwa [mopambanitsa]! Khalani okangalika! Thandizani mnansi wanu!’ Ndiiko komwe, aŵa ndimalamulo amakhalidwe abwino amene anthu onse ayenera kukalimira. Koma timawaiŵala kaŵirikaŵiri.
“Zochititsanso chidwi zinali mkhalidwe waubale wosonyezedwa kwa ena, kukhala wofunitsitsa kuthandiza. Mkazi wina anatipatsa nyuzipepala kotero kuti sitikafunikira kukhala pabenchi lafumbi. Pamene mvula inayamba kugwa, msungwana yemwe anakhala pafupi nane anandipatsa sumbulele yake apo nkuti akumwetulira, ndipo chapafupipo mwamuna wina anakokera mnyamata wovumbwa m’sumbulele yake. . . .
“Mkhalidwe weniweniwo pamsonkhanopo unachititsa munthu kupeza bwinopo mwa njira inayake, kusonyeza khalidwe labwinopo, kukhala waulemu koposa. Kunali kosatheka kusachitapo kanthu mwakumwetulira pakukoma mtima kosonyezedwa ndi anthu achilendo. . . . Tinachoka m’bwalo lamaseŵeralo tikudzimva oyeretsedwa, tikumalingalira kuti tinapeza kanthu kena kabwino.”
Ponena za msonkhano wochitikira ku Kiev, oposa 2,000 anachokera ku Moscow ndi pafupifupi 4,500 anachokera ku Caucasus. Desiki lachidziŵitso linakhazikitsidwa pabwalo landege, ndipo mabuku Abaibulo anasonyezedwa. Ambiri anafunsa mafunso amene anayankhidwa mokoma mtima. Madzulo ŵena mwamuna wina anafika pompo nati: “Ndakhala ndikukuwonani kwanthaŵi yaitali. Ndine wodabwa ndi kulankhula kwanu kwa anthu mokoma mtima ponena za Ufumu. Chonde ndiloleni ndikupatseni maluŵa awa monga mphatso kaamba ka ntchito yanu yabwino koposa.”
Mkati mwaubatizo pamsonkhano wa ku Usolye-Sibirskoye, mtola nkhani wina anachita chidwi pamene anawona nzika za Russia zingapo zikukupatira ndi kuyamikira munthu wobatizidwa chatsopano wa fuko la Buryat. Ngakhale kuti Siberia ali nthaŵi zonse womasuka ku tsankho laufuko, ubwenzi weniweni pakati pa nzika za Russia ndi anthu oterowo ngwakamodzikamodzi. “Kodi munakhoza motani kulaka zopinga zimenezi zautundu?” mtola nkhaniyo anafunsa motero.
“Mwakugwiritsira ntchito lamulo lamakhalidwe abwino Labaibulo lakuti ‘uzikonda mnzako monga udzikonda iwemwini,’” anauzidwa motero.
Ubale Wadziko Lonse
Chimene chinali chochititsa nthumanzi kwambiri pamisonkhano itatuyo yamitundu yonse chinali kulankhulana mwachikondi pakati panthumwi zochokera padziko lonse. Budapest anali ndi alendo ochokera kumaiko 35, ambiri anachokera ku Poland ndi Jeremani, koma nthumwi zingapo zinachokera kumalo ena ambiri, kuphatikizapo pafupifupi 500 zochokera ku Soviet Union. Prague anali ndi nthumwi zochokera kumaiko 39, kuphatikizapo zoposa 26,000 zochokera ku Jeremani, pafupifupi 13,000 zochokera ku Poland, zoposa 900 zochokera ku Italiya, 570 zochokera ku Netherlands, 746 zochokera ku Sweden, ndi 743 zochokera ku Japani. Zagreb anali ndi alendo ochokera kumaiko 15, mosasamala kanthu za chiwopsezo cha nkhondo yachiŵeniŵeni.
Pamsonkhano wamitundu yonse uliwonse, panamangidwa mapulatifomu atatu pabwalo loyang’anizana ndi mbali zosiyanasiyana za bwalo lamaseŵera. Programu yonse inaperekedwa nthaŵi imodzi pamapulatifomu ameneŵa m’zinenero zitatu. Ku Budapest kunali zinenero izi Chihangaliya, Chipolishi, ndi Chijeremani; ku Prague kunali Chicheki/Chisolovaki, Chipolishi, ndi Chijeremani; ndipo ku Zagreb kunali Chikorosiya/Chisebiya, Chisilovene, ndi Chitaliyana. Mkati mwa drama yozikidwa pa Baibulo yopatsa chidziŵitso, imene inazikidwa pazokumana nazo za Ezara ndi atsamwali ake, nthumwi zolankhula zinenero zosiyana zinawonerera chitsanzocho zitakhala m’chigawo chirichonse cha zigawo zitatuzo chimene zinasankha kukhala.
Nkhani zazikulu zambiri za misonkhanoyo zinakambidwa nthaŵi imodzi m’Chingelezi ndi ziŵalo zosiyanasiyana za Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Aliyense wa ameneŵa analankhulira pa imodzi ya mapulatifomu atatuwo. Ndithudi, nkhanizi zinamasuliridwa kotero kuti magulu atatuwo a zinenero zazikulu apindule, ndipo ku Budapest ndi Prague, zinamasuliridwa m’zinenero zinanso zambiri.
Omasulira osiyanasiyana a zinenero zimenezi anaima pabwalo pandunji pa gulu lolankhula chinenero chawo. Zokuzira mawu zoyang’anitsidwa kugulu lenilenilo la chinenerocho zinachititsa munthu kumva chinenero chake popanda kucheutsidwa kwenikweni ndi mamasuliridwe operekedwa m’zinenero zina m’zigawo zinazo. Mwachitsanzo, ku Budapest nkhani zokambidwa ndi ziŵalo za Bungwe Lolamulira zinamasuliridwa m’Chidatchi, Chifalansa, Chifinishi, Chigiriki, Chijapani, Chinowejani, Chispanya, Chiswidishi, ndi Chitaliyana, kuphatikiza pazinenero zazikulu za Chihangaliya, Chipolishi, ndi Chijeremani.
Pamsonkhano wamitundu yonse uliwonse, nkhani yomalizira yolimbikitsa inakambidwa ndi ziŵalo zitatu za Bungwe Lolamulira. Chitokoso chawo chinali kumaliza nkhani yawo mothekera panthaŵi imodzi. Pambuyo pake, mawu a nzika za maiko ochuluka anagwirizana m’kuimba nyimbo, ndipo potsirizira mitima inagwirizana m’pemphero lotsitsimula lakuthokoza Yehova Mulungu kaamba ka kudalitsa misonkhano yozizwitsayi ndi chipambano.
Pamene “Ameni!” wotsirizira ananenedwa, panalibe aliyense amene anafuna kupita. Misozi inagwa pankhope za zikwi zambiri. M’mabwalo amaseŵerawo, mahandikachifi, nduwira, ndi masumbulele anazunguzidwa chauku ndi chauko potsazikana ndi mabwenzi okondedwa amene anasunga umphumphu kwa Mulungu poyang’anizana ndi zaka zambiri za ziletso ndi kuponyedwa m’ndende. Ku Prague mabwenzi ambiri anatsalira kwanthaŵi yoposa ola limodzi, akumaimba ndi kucheza.
Chipambano chozizwitsa cha misonkhano imeneyi sichinadze popanda kuyesayesa. Kwenikweni Mboni za Yehova zinathera maola zikwi mazana ambiri osati popanga makonzedwe okapezekako okha komanso posamalira zinthu zambiri zofunikira kuchititsa misonkhanoyi kukhala yachipambano.
Kukonzekeretsa Malowo
Bwalo lamaseŵera lalikulu la Strahov ku Prague, limene silinagwiritsiridwe ntchito kuchitira msonkhano waukulu mkati mwa zaka zambiri, linanyonyotsoka moti linafunikira kukonzedwanso kwakukulu. Munali mipando yokhoza kugwiritsiridwa ntchito yokwanira 55,000 yokha, yosakwanira kukhalidwa ndi chiŵerengero cha anthu oyembekezeredwa pamsonkhano waukulu koposa m’chilimwecho Kum’maŵa kwa Yuropu. Chotero makina osalazira owonongeka anapezeka, kukonzedwa, ndi kugwiritsiridwa ntchito kumanga mabenchi oposa makilomita 18 okhalapo anthu owonjezereka pafupifupi 30,000.
Ndithudi, kupanga ndi kuika mabenchi inali kokha mbali ya ntchitoyo. Kupaka utoto, kuyeretsa, kuchotsa zitsamba, ndi kukonza izi ndi izi kunalinso kofunikira. Pomalizira pake, bwalo lamaseŵeralo linakongoletsedwa ndi zitini 8,300 zokhala ndi maluŵa 33,200 ndi mitengo yankungudza yokwanira 1,357. Nthaŵi zina panali kukhala ogwira ntchito okwanira chikwi chimodzi. Antchito odzifunira a Mboni za Yehova ochokera m’mipingo 260 anatha chiwonkhetso cha maola oposa 66,000.
Ntchito yofanana inachitidwa ku Budapest, Zagreb, ndi mizinda ina kukonzekeretsa mabwalo amaseŵerawo. Pafupifupi antchito odzifunira 4,000 anathera maola oposa 40,000 kugwira ntchito pamalo a msonkhano ku Lvov. Ntchito yawo ndiyo inakhala malipiro a lendi ya malowo. Mabenchi onse m’bwalomo anakonzedwa ndi kupakidwa utoto, ndipo zimbudzi zonse zinayeretsedwa ndi kukonzedwa. Ndiponso, nyumba yanjerwa yamamita makumi atatu mphambu atatu m’litali inamangidwa imene inali ndi zimbudzi zowonjezereka. Mofananamo, mu bwalo lamaseŵera la Khimik ku Usolye-Sibirskoye, munamangidwa zimbudzi 52 zowonjezereka zogwiritsira ntchito pamsonkhanopo.
Mwamuna wina amene ndiinjiniya wamkulu m’bwalo lamaseŵera ku Lvov anati: “Sindinawonepo anthu odabwitsa otere m’moyo wanga wonse. Mukugwira ntchito monga banja limodzi lalikulu. Sindikhoza kumvetsetsa, koma kugwira nanu ntchito nkwabwino kwabasi.” Oyendetsa ntchito pabwalo lamaseŵeralo analemba kalata mwa imene anayamikira Mbonizo “kaamba ka kudzipereka kwawo m’ntchito imene anaichita ndi mikhalidwe yawo yabwino ndi kukhala kwawo athayo.” Kalatayo inamaliza kuti: “Tikufunirani msonkhano wachipambano m’Lvov.”
Ku Kiev pansi pa chipinda pamene kafeteria inayenera kumangidwa panafunikira kukonza. Ntchitoyo inamalizidwa m’masiku aŵiri. Ogwira ntchito m’bwalo lamaseŵeralo aŵiri anabwera kudzawona “chozizŵitsacho,” mmodzi anati kwa winayo: “M’masiku aŵiri iwo anatsiriza ntchito imene imatengera anthu athu theka la chaka kuimaliza.” Presidenti wa kalabu lamaseŵera a m’madzi anauza woyang’anira msonkhano kuti: “Munasandutsa bwalo lamaseŵerali kwakuti sitikhozanso kulizindikira.”
Akuluakulu a bwalo lamaseŵera la ku Kiev analemba kalata yoyamikira kuti: “Mitima yathu njosangalala ndi kulinganiza msonkhano kwa Mboni za Yehova. . . . Monga momwe timifuleni tochokera pa akasupe timakumana kupanga mtsinje wosefukira, choteronso mtsinje wa Mboni za Yehova wochokera kwa ang’ono ndi akulu ukuyenda mogwirizana kupita kuphwando lawo. Zimenezi nzokhumbirika. Tikuziwona kwanthaŵi yoyamba. Tikuyamikani kuti mwatiphunzitsa kanthu kena ndi chitsanzo chanu.”
Kusamalira Nthumwi
Imodzi ya ntchito zazikulu inali kukonza malo ogona alendo zikwi zambirimbiri. Mboni zakumaloko zinalandira nthumwizo m’nyumba zawo. Mboni za ku Chekosolovakiya zinapereka malo ogona m’nyumba zawo kwa nthumwi zokwanira 6,280 za ku Poland pamsonkhano wa ku Prague. Ku Budapest, nthumwi zokwanira 2,203 zinakhala m’nyumba za abale. Ndipo Mboni za ku Kiev zokwanira 278 zinapereka malo ogona kwa alendo pafupifupi 750 mpaka 800.
Ndiponso, sukulu zambiri ndi maholo amaseŵera ku Budapest ndi Prague zinagwira ntchito monga zipinda zokhala. Sukulu zoposa 40 zinagwiritsiridwa ntchito monga malo ogona anthu 7,930 ku Budapest. Ku Prague, anthu 12,530 anagona m’sukulu zambiri ndi maholo amaseŵera. Mamatiresi zikwi zambiri obvutira mpweya anagulidwa kuti agwiritsiridwe ntchito m’maloŵa. Opezeka pamsonkhano ku Prague oposa 29,000 anakhala m’magoŵero a ophunzira ndi m’mahositelo a achichepere, ndipo zikwi zowonjezereka anali kugona m’mahotela.
Pamisonkhano ina, makonzedwe anapangidwa kuti nthumwi zizigona m’sitima zimene zinawabweretsa. Mboni pafupifupi zikwi ziŵiri zochokera ku Zakarpatskaya Oblast zinagwiritsira ntchito ngolo monga zipinda zawo zogona ku Kiev. Enanso ochokera ku Caucasus kubwera ku Kiev anachita chimodzimodzi. Mofananamo, Mboni za ku Lithuania zopita kumsonkhano ku Tallinn, Estonia, zinagona m’sitima zimene zinawabweretsa.
Ngakhale zitafika, nthumwizo zinasamaliridwa mwa njira zambiri ndi owachereza awo. Mwachitsanzo, makonzedwe anapangidwa ku Prague kugwiritsira ntchito mabasi 40 oti achirikize njira imene mwanthaŵi zonse imayenda basi imodzi yokha. Ndiponso, chifukwa cholipiriratu pasadakhale, nthumwizo zinakhoza kukwera zoyendera za onse mwaulere kupita kumsonkhano m’maŵa ndi m’madzulo popita kunyumba mwakungosonyeza mabaji awo amsonkhano. Ku Soviet Union, mabasi okwanira 11 opita kumsonkhano ku Usolye-Sibirskoye kuchokera ku Angarsk wapafupi anaperekezedwa ndi magalimoto aŵiri apolisi owatetezera, imodzi kutsogolo ndi inayo kumbuyo!
Zoyesayesa Zokapezekako
Makamaka nthumwi za misonkhano ina ya mu Soviet Union zinayenda mitunda yaitali mwakudzilipirira ndalama zochuluka. Ena anasunga ndalama chaka chonse zolipirira ulendo wawo. Nthumwi ina inachokera kudoko lakutali la Vladivostok ku Nyanja Yamchere ya Pacific, kuyenda mtunda wamakilomita 3,200 kupita ku Usolye-Sibirskoye. Nthumwi zina khumi ndi ziŵiri zinachokera kuchilumba cha Sakhalin m’Nyanja Yamchere ya Pacific kumpoto kwa Japani. Mmodzi anali wachichepere wazaka 20 amene anatsagana ndi achichepere ena atatu kwa amene amachititsa maphunziro Abaibulo.
Woyendetsa basi wochokera ku Sayanogorsk, amene anafuna kubatizidwa ku Usolye, anaumirira kupempha tchuthi chamasiku angapo kwa womlemba ntchito kuti akapezeke kumsonkhano, koma mkulu wantchitoyo sanafune kumlola kuti apite. Choncho mwamunayo anapita ndi galimoto kumzinda wa Abakan nakatenga kope la chikalata cha Soviet Union cha March 27 yapitayo chimene mwalamulo chimazindikiritsa Mboni za Yehova kukhala gulu lachipembedzo. Ngakhale kuti anawona chikalatacho, mkulu wantchito wake sanamlolebe kupita. M’maŵa patsiku lake lonyamuka, pambuyo papemphero lamphamphu, mwamunayo anachondereranso ndipo pomalizira pake analoledwa kupita.
Ubatizo ndi Zofalitsidwa Zatsopano
Ubatizo unali mbali yosangalatsa ya misonkhano yonse Kum’maŵa kwa Yuropu. Mwakachitidwe kophiphiritsira ka kumizidwa m’madzi, anthu 18,293 opezeka pamisonkhanoyi anapereka umboni pamaso pa mboni wakuti apereka kotheratu miyoyo yawo kwa Yehova Mulungu. Wachichepere wina wopita kuubatizo ku Prague, amene posachedwa anapatsidwa ntchito yapamwamba, anati: “Ndinalingalira kuti ndinayenera kupanga chosankha pakati pa mulungu wautatu wopangidwa ndi madola a United States, ndalama ya mark ya Jeremani, ndi shilling ya Austria kumbali imodzi ndi Yehova kumbali ina. Ndinasankha Yehova ndi kukana mphatsoyo.”
Ubatizo ku Tallinn unachitidwira m’dziŵe lakunja pafupi ndi Nyanja ya Baltic kumene linga lakale lomwe linagwiritsiridwapo ntchito monga ndende linali kuwoneka kumbuyo kwake. Kunoko nkumene Mboni za ku Estonia zambiri zinasungidwa zisanatumizidwe kumisasa yachibalo ku Russia kuchiyambi kwa ma 1950. Kunali kosangalatsa chotani nanga, makamaka kwa achikulire otero, kuwona okhulupirika atsopano okwanira 447 akuchitira chithunzi kudzipereka kwawo kwa Yehova m’dzoma lapoyera!
Mbali ina yokondweretsa ya misonkhanoyi inali kutulutsidwa kwa zofalitsidwa zatsopano. Anzathu a ku Lithuania osonkhana ku Tallinn analumphadi kuchoka pamipando yawo nalira atauzidwa kuti brosha ya “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano” iripo tsopano m’chinenero chawo. Mofananamo, mfundo yaikulu ya misonkhano ku Romania inali kutulutsidwa kwa bukhu la Revelation—Its Grand Climax At Hand! m’Chiromaniya, ndipo kwa nzika zolankhula Chicheki ndi Chisolovaki ku Prague, inali kulandira New World Translation of the Holy Scriptures m’zinenero zawo.
Komabe, pamisonkhano yambiri, kutulutsidwa kwa bukhu latsopano la The Greatest Man Who Ever Lived kunadzetsa chimwemwe chachikulu. Makope okwanira mamiliyoni khumi asindikizidwa kale m’zinenero 59.
Kugwiritsira Ntchito Bwino Ufuluwo
Lerolino, mabuku ofotokoza Baibulo amaloledwa Kum’maŵa kwa Yuropu, kuphatikizapo Soviet Union. Magalimoto aakulu odzala ndi Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! amachoka panyumba yosindikizira ya Mboni za Yehova ku Selters/Taunus, Jeremani, ndi kudutsa malire kuloŵa m’maiko a Kum’maŵa kwa Yuropu. Kuli kosiyana motani nanga ndi nthaŵi pamene, powopa kuponyedwa m’ndende, Mboni zinazembetsa mabuku kuwaloŵetsa m’maikoŵa!
Pochitira fanizo kusintha kodabwitsaku, kukambirana kotsatiraku kunachitika pakati pa nduna yowona za katundu woloŵa ndi kutuluka m’dziko ndi mkazi amene ndimmodzi wa Mboni za Yehova kutatsala pang’ono kuti msonkhano ku Tallinn uyambike:
“Kodi wanyamulanji m’bokosi laling’onolo?”
“Magazini.”
“Magazini otani? Kodi ndimagazini a Mulungu?”
“O, inde, ndithu.”
“Magazini a Yehova Mulungu?”
“Inde!
“Jaa’a, ziribwino. Ungapite.”
Pambuyo pamsonkhano wa ku Budapest, Arpad Goncz, prezidenti wa Hungary, anaitana Mboni imene inali mkaidi mnzake m’nthaŵi ya chitsenderezo Chachikomyunizimu kukamchezera. Bambo Goncz anathera ola limodzi pamodzi naye ndipo pambuyo pake anapempha yemwe kale anali mkaidi mnzake kupereka mafuno abwino kwa Mboni za Yehova. Okonda ufulu waumulungu kulikonse athokozadi kuti akuluakulu aboma amakono, onga Bambo Goncz, tsopano akupereka ufulu wakulambira Kum’maŵa kwa Yuropu.
Ikumasonyeza kuti anthu a Yehova akugwiritsira ntchito bwino ufulu wawo, The New York Times ya September wa chaka chatha inalongosola chochitika ku St. Petersburg (mzinda umene kale unali Leningrad), kuti: “Nyimbo yoimba pang’onopang’ono ya Gershwin yamutu wakuti ‘Summertime’ inamveka modutsa Mtsinje wa Neva . . . Nyimboyo inamvedwa ndi owothera dzuŵa okulupala, tiana tomathamangitsa agalu, amalonda omagulitsa mamapu a St. Petersburg wakale ndi Mboni za Yehova zomafunafuna anthu otembenuza.”
Inde, Mbonizo zikugwiritsira ntchito mwachangu ufulu wawo kulalikira mbiri yabwino! Kodi mungafune kudziŵa zochuluka ponena za uthenga wawo? Nyuzipepala ya Soviet Union yotchedwa Vostochno-Sibirskaya Pravda inati: “Chidziŵitso chatsatanetsatane chonena za zochita zawo chingapezeke pamalo ophunzirira Baibulo a Mboni za Yehova m’mzinda uliwonse.” Kulikonse kumene mungakhale m’dziko, osazengereza kuzifunafuna.
[Tchati patsamba 25]
MISONKHANO KUM’MAŴA KWA YUROPU NDI SOVIET UNION
Dziko Chiŵerengero Chapamwamba Obatizidwa
cha Opezekapo
Chekosolovakiya (Prague) 74,587 2,337
Hungary (Budapest) 40,601 1,134
Poland (mizinda 12) 131,554 4,250
Romania (mizinda 8) 34,808 2,260
Soviet Union (mizinda 7) 74,252 7,820
Yugoslavia (Zagreb) 14,684 492
Onse pamodzi pamisonkhano 30: 370,486 18,293
[Zithunzi pamasamba 20, 21]
Kulamanja: Kumasulirira magulu olankhula zinenero zosiyana ku Prague
Pansi: Bwalo lamaseŵera la Strahov ku Prague lodzala ndi nthumwi zoposa 74,000
[Zithunzi patsamba 22]
Pamwamba: Msonkhano ku Tallinn, Estonia
Msonkhano ku Budapest, kumene nthumwi 40,000 zinasangalala ndi programu yonse mosasamala kanthu za mvula kapena dzuŵa
[Zithunzi patsamba 27]
Pamwamba: Zina za zimbudzi zomangidwira kugwiritsira ntchito pamsonkhano ku Usolye-Sibirskoye, Siberia
Kupaka utoto bwalo lamaseŵera ndi kupanga mabenchi owonjezereka okhalapo ku Prague
[Zithunzi patsamba 28]
Drama yozikidwa pa Baibulo ndi ubatizo ku Zagreb
[Zithunzi patsamba 29]
Pamwamba: Kuperekedwa kwa Nyumba Yaufumu yoyamba m’June 1991 yomwe inamangidwa ndi Mboni m’Hungary
Pakati: Oposa 20,000 anagona m’sukulu ndi maholo amaseŵera ku Budapest ndi Prague
Pansi: Kugaŵira bukhu la “The Greatest Man Who Ever Lived” ku Usolye-Sibirskoye, Siberia