Nkhaŵa Zachuma Kodi Zidzatha Liti?
Gawo 6: Kukhupuka ndi Kugwa kwa Dongosolo Lamalonda
MALINGA ngati malonda aumbombo apitiriza kulamulira unyinji wa anthu, nkhaŵa zachuma zidzapitirizabe. Imeneyi ndi mbiri yoipa. Mbiri yabwino njakuti ulamuliro wake udzaswedwa posachedwapa, kuthetseratu nkhaŵa zonse zachuma. Pakali pano, Mboni za Yehova zoposa mamiliyoni anayi zikudziŵikitsa mbiri yabwino imeneyi kwa ena kuzungulira dziko lonse.—Onani bokosi patsamba 14.
Chiŵiya Chogwira Mtima Kwambiri
Cholinga cha kusatsa malonda—pamene tifika ku zachuma—ndicho kugulitsa zinthu kapena mautumiki. Pofuna kuchilikiza malonda, anthu ayenera kusonkhezeredwa kuti agule. Zikwangwani, manyuzipepala, magazini, wailesi, ndi wailesi yakanema zimafuna kukwaniritsa chimenechi.
Kusatsa malonda kwapamwamba kwa wailesi yakanema yamakono kuli kosiyana kotheratu ndi olengeza poyera a m’Girisi wamakedzana. Koma cholinga cha kusatsa malonda—kusonkhezera anthu—sichinasinthe. Kupangidwa kwa makina osindikizira onyamulika opangidwa ndi Johannes Gutenberg kunatsegula njira zatsopano zosatsira malonda poyera kotero kuti pofika 1758, katswiri wolemba nkhani Wachingelezi Samuel Johnson analemba kuti: “Kusatsa malonda kuli kochuluka kwambiri tsopano kotero kuti kumaŵerengedwa mosasamala, ndipo chotero nkoyenera kuti osatsawo akoke chidwi mwakupanga malonjezo aakulu ndi kufotokoza mokometsera ndipo nthaŵi zina mosangalatsa ndipo nthaŵi zina mwachisoni.”
Kusatsa malonda kunapatsidwa mphamvu yatsopano ndi kusintha kwa maindasitale. Unyinji wa katundu watsopano yemwe anapezeka anafuna ogula, omwe tsopano anafikiridwa ndi lukanelukane womakulakula wa manyuzipepala ndi magazini. M’kupita kwanthaŵi, wailesi ndi wailesi yakanema zinakoka khamu lalikulu. Kusatsa malonda kunakhala bizinezi pa iko kokha. Nthambi zosatsa malonda zinapangidwa kalelo mu 1812, pamene nthambi ya Reynell and Son inatsegulidwa mu London.
Ngati kusatsa malonda kulidi kowona, kutidziŵitsa za katundu kapena mautumiki omwe alipo okhutiritsa zosoŵa zenizeni, kumatumikira cholinga chabwino. Komabe, sikumatero pamene kupitirira malire oyenerera, kutinyengerera kugula zimene sitizifunikira ndi kutiloŵetsa m’ngongole zambiri chifukwa chofuna kudzisangalatsa panthaŵi yomweyo. Wolemba wina anakufotokoza motere: “Kumanyengerera, kumachonderera, kumapereka zifukwa, kumafuula.” Nawonjezera kuti: “Modziŵa kapena mosadziŵa, tonsefe tayambukiridwa, mwanjira yabwino kapena yoipa, ndi kusatsa malonda.”
Kaŵirikaŵiri oyembekezeredwa kukhala ogula amapambutsidwa ndi zinthu zomwe siziri zofunika konse. Osatsa malonda amafikira maganizo; amasumika zolinga zawo pamalingaliro. Angatchule zinthu zomwe siziri zowona kwenikweni. Choipitsitsa nchakuti, angabise mbali yoipa kapena yaupandu ya katundu wawo, mwakutero kusonyeza kupanda nkhaŵa kwakukulu kaamba ka ubwino wa ena—zonsezi zimachitidwa chifukwa cha mpikisano wazachuma.
Kodi Mpikisano wa Zachuma Ngwoyenerera?
Monga mmene amachitira ambiri, mungalingalire kuti mpikisano uli wofunika kuti pakhale chitukuko. Ndipo makamaka pakali pano, mpikisano wa zachuma wochitidwa mowona mtima ungachinjirize ogula mwanjira zina. Koma bukhu lophunzirira la Psychology and Life likukaikira ngati mpikisano uli “mbali yoyenera ya chibadwa cha anthu,” likumafunsa kuti: “Kodi tiyenera kupondereza ogonjetsedwa kuti tikhale achimwemwe?”
Likumasonyeza kuti anthu okulira m’chitaganya chopikisana “amachitapo kanthu pa chitokoso chakulaka munthu wina,” bukhu lophunzirirali likutsimikizabe kuti kupikisana sikuli mkhalidwe wachibadwa. Kwenikweni, pomalizira pake, kupikisana kumakhala ndi zotulukapo zoipa. Kupenda kwavumbula kuti “kumachititsa mkhalidwe wa kupambana pamtengo uliwonse womwe kaŵirikaŵiri sumayenerera pa ntchito yamtundu wabwino koposa.”
Mwachitsanzo, mpikisano ungachititse mantha a kulephera. Koma mantha, kaya kukhale kusukulu, kuntchito, kapena kwina kulikonse, sali abwino pofuna kuchita bwino zinthu. Ndiponso, mpikisano ungachititse kusawona mtima kapena kunama. Pofuna kupeza magiredi abwino ophunzira opikisana kwambiri angaphonye cholinga chenicheni cha kuphunzira: kuwakonzekeretsa kukhala mamembala a chitaganya abwino ndi ogwira bwino ntchito.
Panthaŵi imene bukhu la Psychology and Life linkalembedwa m’ma 1930, linatchula Samoa kukhala chitsanzo cha chitaganya chosapikisana. “Anthu amagwira ntchito ndipo amasunga zokolola zawo m’nkhokwe imodzi m’mene onse angatengemo malinga ndi zosoŵa zawo,” likulongosola motero, niliwonjezera kuti: “Akatswiri a makhalidwe a anthu akusimba kuti anthu oterowo amakhala achimwemwe kotheratu monga momwe aliri anthu anzawo odziimira paokha m’mbali zina zadziko.”
Chotero, dongosolo lachuma lopindulitsa ndi lachipambano silifunikira kukhala lozikidwa pa mpikisano. Munthu wabizinezi wotchuka ananenetsa kuti pamene kuli kwakuti mpikisano ungakhale wofunikira kusonkhezera anthu achibwana, anthu ofikapo sayenera kukhala ndi vuto lakupeza chisonkhezero m’ntchito yeniyeniyo. Chimwemwe chimapezeka m’kuphunzira, kukhala ndi luso lakuchita zinthu, kusangalatsa ena, kuwongolera ndi kupeza maluso atsopano.
Pamenepo, nkosadabwitsa kuti uphungu wanzeru wa Baibulo umati: ‘Tisakhale odzikuza, outsana, akuchitirana njiru.’—Agalatiya 5:26; Mlaliki 4:4.
Wonjokani Kuti Mupeze Chinachake Chabwinopo!
Kuli kowonekeratu kuti Satana akugwiritsira ntchito malonda aumbombo monga chida polondola zofuna zake. Mwakuyambitsa nkhaŵa zachuma, iye akulamulira mwamphamvu anthu. Nkhaŵa yakukhutiritsa zikhumbo zakuthupi imakwirira zosoŵa zauzimu zofunika. Lingaliro lakuti katundu ayenera kugwiritsiridwa ntchito ndi kutaidwa lochilikizidwa ndi malonda limayambukira moipa malo. Mkhalidwe wake wakuti mukhale nazo zonse ndipo panthaŵi imodzi umawononga chikhutiro ndi chimwemwe. Kwenikweni, ngati zikondwerero zabwino zachuma sizogwirizana ndi malamulo amakhalidwe abwino a Mulungu, zimasinthiratu kukhala dyera, ndipo pambuyo pake, kukhala umbombo.
Komabe, umbombo ndi dyera zopambanitsa zili mitundu ya kulambira mafano, komwe sikukondweretsa Mulungu. (Akolose 3:5) Anthu amene amalola maumunthu awo kuumbidwa moipa ndi malonda, mofanana ndi ochilikiza chipembedzo chonyenga ndi opititsa patsogolo ulamuliro wa anthu, ali paupandu. Ali pangozi yakukhala minkhole ya kusayanjidwa ndi Mulungu. Yesu anachenjeza kuti: ‘Mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno [kuphatikizapo nkhaŵa zachuma], ndi kuti tsiku ilo [la chiweruzo cha Yehova] lingafikire inu modzidzimutsa.’—Luka 21:34.
Amene akufuna kukhala Akristu ayenera kuwonjoka m’manja mwa madongosolo opanda ungwiro azachuma mwakukana mzimu umene amasonkhezera ndi mwakutsutsa zonulirapo zadyera zachuma. Maumunthu ayenera kuumbidwa ndi Mlengi wamphamvuyonse, osati ndi chisonkhezero champhamvu cha ndalama. Nthaŵi zonse tiyenera kukalimira kukhala owona mtima. Chikhutiro chiyenera kupezedwa m’zimene munthu ali nazo, osati m’kufunafuna kosalekeza zinthu zowonjezereka.—Aefeso 5:5; 1 Timoteo 6:6-11; Ahebri 13:18.
Pofuna kukhazikitsa zinthu zoyambirira, Akristu ayenera kusanthula kwanthaŵi ndi nthaŵi zonulirapo zawo m’moyo. (Afilipi 1:9, 10) Izi zimasonyezedwa m’mtundu wa ntchito ndi maphunziro amene amasankhira ana awo. Iwo amakumbukira kuti ‘chirichonse cha m’dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi. Ndipo dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi yonse.’ Amadzikumbutsa mosalekeza kuti pamene dziko lipita, malonda adziko adzakumana ndi ‘Kugwa Kotheratu,’ kugwa komwe malondawo ndi achilikizi ake sadzathanso kudzuka.—1 Yohane 2:16, 17.
[Bokosi patsamba 14]
Mu Ufumu wa Mulungu Simudzakhala Nkhaŵa Zachuma
Sikudzakhala mitengo yokwera chifukwa cha kupereŵera kwa chakudya: ‘Dziko lapansi lapereka zipatso zake: Mulungu, Mulungu wathu, adzatidalitsa.’ ‘M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri.’—Salmo 67:6; 72:16.
Sikudzakhala ngongole zosalipiridwa za adokotala: “Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” ‘Maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzaimba.’—Yesaya 33:24; 35:5, 6.
Sipadzakhala malipiro okwera a lendi kapena ogulira nyumba: ‘Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzaoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzaoka, ndi wina kudya.’—Yesaya 65:21, 22.
Sipadzakhala magulu a olemera ndi osauka: ‘Iye adzaweruza mwa mitundu yambiri ya anthu, nadzadzudzula amitundu amphamvu ali kutali; . . . Koma adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena.’—Mika 4:3, 4.
Sipadzakhalanso zosoŵa zosakwaniritsidwa zamtundu uliwonse: ‘Iwo akufuna Yehova sadzasoŵa kanthu kabwino.’ ‘Muoloŵetsa dzanja lanu, nimukwaniritsa zamoyo zonse chokhumba chawo.’—Salmo 34:10; 145:16.
[Chithunzi patsamba 15]
Mu Ufumu wa Mulungu nkhaŵa zachuma zidzatheratu