Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 4/8 tsamba 26-29
  • “Ndinalira ndi Chimwemwe”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Ndinalira ndi Chimwemwe”
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Yehova Ngwachifundo Ndipo Amasamala Mwakuya”
  • “Ndikuwona Kuti Moyo Ngwamtengo Wake Tsopano”
  • “Ndamasulidwa Mwamaganizo”
  • “Mwadzidzidzi Ndakhalanso ndi Moyo!”
  • “Ena Angaiŵale, Ena Sangaiŵale”
  • Kuyang’anizana ndi Zenizeni
  • Kuchokera kwa Oyang’anira
  • ‘Nthaŵi ya Kuchira’
    Galamukani!—1991
  • Mabala Obisika a Kuchitira Nkhanza Ana
    Galamukani!—1991
  • Tizisonyeza Chikondi ndi Chilungamo M’dziko Loipali
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Chitetezo m’Nyumba
    Galamukani!—1993
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 4/8 tsamba 26-29

“Ndinalira ndi Chimwemwe”

Oŵerenga Asonyeza Chiyamikiro Chachikulu pa “Kupoletsa Mabala a Kuchitira Nkhanza Ana”

MPAMBO waposachedwapa wa nkhani za magazini a Galamukani! unachititsa oŵerenga ambiri kumbali zonse zadziko kufotokoza chiyamikiro chawo chamtima wonse kaamba ka mpambo wankhani yapachikuto wakuti “Kupoletsa Mabala a Kuchitira Nkhanza Ana” mu Galamukani! wa October 8, 1991. Makalata awo asonyeza kuti nkhani zokonzekeredwa mosamalitsa zimenezi zinakwaniritsa chifuno chake, chomwe chinali chambali zitatu: (1) kupatsa mikole chidziŵitso ndi chiyembekezo; (2) kuchenjeza makolo kotero kuti akhale amaso ponena za chisungiko cha ana awo; (3) kuthandiza akulu amene amathandiza mikole ya kuchitiridwa nkhanza kuti akhale odziŵa bwino kotero kuti apereke chithandizo chogwira mtima kwambiri.—Miyambo 21:13; yerekezerani ndi 27:23.

Mutu womwe unabwerezedwa ndi oŵerenga ambiri unafotokozedwa ndi ndemanga iyi: “Nthaŵi zonse ndimayamikira kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Komabe, chiyamikiro ndi chikondi changa pa Yehova ndi ‘kapolo [wake] wokhulupirika ndi wanzeru’ (Mateyu 24:45-47) chawonjezeredwa nthaŵi zana limodzi pambuyo poŵerenga kope la Galamukani! la October 8, 1991.”

“Yehova Ngwachifundo Ndipo Amasamala Mwakuya”

Ambiri anafotokoza chiyamikiro kaamba ka mbali yofunika koposa ya nkhanizo: kuti Mulungu amamvetsera, amasamalira, amadziŵa kuti mikole sinali ndi liŵongo, ndikuti akhoza kuwachiritsa. Woŵerenga wina wamkazi anati: “Ndikuthokozani ndi mtima wonse kaamba ka Galamukani! wa October 8. Nkhani zanu zinandithandiza mwakundisonyeza kuti Yehova ngwachifundodi ndipo amasamala mwakuya.”—Briteni.

Mkazi wina analemba kuti: “Miyezi ingapo yapitayo ndinafuna kukupemphani kulemba nkhani yakupoletsa mabala a kuchitira nkhanza ana. Sindinalembe koma mmalomwake ndinapemphera kwa Yehova. Pamenepo, mungayerekezere chisangalalo changa pamene ndinawona chikuto cha kope la October 8. Ndinalira, ndipo ndinathokoza Mulungu wathu wachikondi, Yehova, ndi mtima wanga wonse.”—Girisi.

Mkazi wina akuti: “Ndikalingalira zimene ndinapyolamo, ndimalira kwambiri. Nchifukwa chake ndinaŵerenga mosamalitsa nkhani zonena za ‘Kupoletsa Mabala a Kuchitira Nkhanza Ana,’ zomwe ndinazipeza kukhala zothandiza kwambiri. Zikusonyeza bwino lomwe kuti muli ndi chikondwerero chachikondi mwa anthu amene anavutika ndi zinthu zoterozo m’miyoyo yawo.”—Italiya.

Ambiri anafotokoza lingaliro ili: “Ndikuthokoza Yehova chifukwa chopereka chidziŵitsochi, nkhani zabwino koposa zomwe ndaŵerengapo pankhaniyi. Ndikupemphera kuti izi zidzathandiza osati mikole (opulumuka) yokha komanso amene amawopa kutchula nkhaniyi ndi kukupeza kovuta kuilankhula.”—United States.

“Ndikuwona Kuti Moyo Ngwamtengo Wake Tsopano”

Mkazi wina amene mwana wake wamkazi anachitiridwa nkhanza analephera kulaka vutolo mwamaganizo. “Koma nkhani zanu zinandisonyeza njira yoyenera,” anafotokoza motero. “Ndakhala ndikulandira uphungu kwa akatswiri a zamaganizo mlungu uliwonse kwa miyezi 11 chifukwa cha nkhaŵa, kugwidwa ndi mantha, ndi kuchita tondovi. Nkhani zimenezi zinandithandiza kwambiri kuposa njira zonse zochiritsira m’dziko! Ndikuwona kuti moyo ngwamtengo wake tsopano, pamene kuli kwakuti ndisanaŵerenge kopelo, ndinadzimvabe waliŵongo chifukwa cha chinachake chomwe sindinathe kuchiletsa.”—Briteni.

Ambiri anati chidziŵitsocho chinali posinthira zinthu m’miyoyo yawo: “Sindingathe kukuthokozani mokwanira kaamba ka nkhanizo. Zinafika pamene ndinali wosungulumwa kwenikweni. Nthaŵi zina ndinkafunya ndikuyamba kulira. Mothandizidwa ndi nkhanizi, zomwe ndaziŵerenga mobwerezabwereza, ndawona kuti kuvutika kwanga, ndi kuvutika kwa aliyense, kuli ndi tanthauzo kwa Yehova ndi gulu lake. Chidziŵitso chimenechi chandipatsa chisonkhezero chakupola. Ndayamba kale kudzimva woyandikana ndi Yehova kachiŵirinso.”—United States.

Koma kuchitira nkhanza ana sivuto la Kumadzulo kokha, monga momwe chitsanzo ichi chikusonyezera: “Pamene ndinalandira kope la October 8 lonena za kuchitira nkhanza ana, ndinaliŵerenga panthaŵi yomweyo. Zinanditengera nthaŵi yaikulu kuti ndiŵerenge nkhanizo chifukwa cholephera kuwona bwino mawu chifukwa cha misozi! Malingaliro anga ndi maganizo anafotokozedwa m’nkhanizo. Tsopano ndine wachimwemwe kuti munthu wina amadera nkhaŵa. Ndinalimbikitsidwa kuwona mmene Yehova amathandizira mokoma mtima anthu amene mavuto awo sawonedwa ndi ena. Ndine woyamikira kwambiri kuti munafalitsa nkhanizi. Kuti ndipoletse mabala anga, ndidzagwiritsira ntchito zimene zalembedwa m’nkhanizo. Landirani moni wanga wachikondi ndi chiyamikiro chachikulu.”—Japani.

Mkazi wina analemba kuti: “Ndakhala ndikulimbana ndi kusweka mtima kochititsidwa ndi kuchitira nkhanza ana moyo wanga wonse. Nditalandira magazini a October 8, ndinalingalira kuti Yehova amadziŵa zosoŵa zathu tisanazidziŵe nkomwe ndipo amatikondadi. Ndinalephera kuwona bwino chifukwa cha misozi, ndipo mtima wanga unachita ngati udzaphulika chifukwa cha chikondi ndi chiyamikiro kwa Atate wathu wakumwamba wachikondi. Kope limeneli la October 8 ali magazini amene ndidzawayamikira ‘kufikira zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kuloŵa mumtima.’ (Yesaya 65:17)—United States.

“Ndamasulidwa Mwamaganizo”

Mkazi wina wovutitsidwa kwambiri kwa moyo wake wonse analemba kuti: “Ndikuthokozani kaamba ka nkhani za kuchitira nkhanza ana. Pomalizira pake, pamsinkhu wa zaka 53 zakubadwa, ndamasulidwa mwamaganizo! Sentensi lomwe linandimasula linali limene linasonyeza kuti mikole yachichepere imeneyi ‘inalibe mphamvu yakudzichinjiriza pamene inawopsezedwa, chotero Mulungu samaiŵerengera kukhala yathayo.’” Kuŵerenga Galamukani! wa October 8 ndi kumvetsetsa monga momwe ananenera magaziniwo kuti, “SUNALI MLANDU WANU!” kunamthandiza kugwiritsira ntchito dipo la nsembe ya Yesu m’kuyamba dongosolo la kupola.—Briteni.

Mkazi wina anati: “Kuyambira nthaŵi imene ndinali wachichepere mpaka m’zaka zanga zoyamba za sukulu yapulaimale, ndinavutitsidwa mwakugonedwa mobwerezabwereza. Monga momwe nkhanizo zinasonyezera, ndinathaŵa mwamaganizo. Komabe, zikumbukiro zinkabwerabe. Nthaŵi zonse ndimaganiza kuti: ‘Ndine munthu wodetsedwa. Yehova sadzandilandira konse.’ Choncho pemphero langa kwa Mulungu nthaŵi zonse linali lakuti: ‘Simungandipatse malo m’Paradaiso, koma chonde ndiloleni kukhala m’gulu lanu kufikira imfa.’ Ndinalingalira motero chifukwa chakuti, mofanana ndi mikole ina yotchulidwa m’nkhanizo, ndinaganiza kuti ‘Sindiri woyera mokwanira kukhala mu Ufumu wa Mulungu’ ndikuti imfa yanga idzachitika pa Armagedo. Ndinamva ngati malingaliro a manyazi ndi kupanda chimwemwe anali kundipha. Choncho, nkhanizo, zomwe zinali zabwino ndi zokoma mtima, zinandithandiza kwambiri. Poŵerenga nkhanizo, ndinagwetsa misozi.”—Japani.

Mkazi wina anati: “Ndifuna kukuthokozani chifukwa cha nkhani zanu zokhudza moyo ndi zofufuzidwa bwino. Kwa zaka zambiri, kupweteka kwa kuchitiridwa nkhanza kunaswa malingaliro anga. Nkosavuta kwa ambiri kumva chisoni chifukwa cha nkhanza ndi chizunzo zimene nkhondo ndi chipwirikiti chandale zimachititsa. Timachitira chisoni mikole ya Chipululutso. Zoipa zochitidwa ndi alendo sizovuta kuziiŵala. Komabe, nchifukwa ninji ena samamvetsetsa pamene zichitidwa ndi atate athu, amayi, amalume, alongo, abale—amene anafunikira kupereka chitonthozo, kutilera, ndi kutichinjiriza? Ndawona zipsera zanga ndipo ndadziŵa kukhwethemula kwa kupanda chiyembekezo. M’kupola kwanga Atate wanga wauzimu, Yehova, ndiye amene kwanthaŵi ndi nthaŵi wandichilikiza.”—United States.

“Mwadzidzidzi Ndakhalanso ndi Moyo!”

Mkazi amene akuti kwa zaka 28 anadzimva ngati wataidwa analemba kuti: “Ndinaŵerenga nkhanizo madzulo omwe ndinalandira kopelo ndipo ndinakhetsa misozi chifukwa ndinakhudzidwa ndi kuthokoza kwambiri. Ndine wachimwemwe kuzindikira kuti Yehova amamvetsetsa bwino lomwe malingaliro anga. Ndikumva ngati kuti mwadzidzidzi ndakhalanso ndi moyo! Popeza kuti nkhanizo zinagogomezera kuti ana okhala m’mkhalidwe woterowo alibe liŵongo pa zomwe zinachitika, ndazindikira kuti palibe chifukwa chodzitonzera. Maganizo anga apumulitsidwadi.” Mtima wake unachira ndi Mawu a Mulungu.—Japani.

Kugwirira ana chigololo kulinso vuto m’maiko otukuka kumene, monga momwe zikusonyezedwera ndi kalata yofanana yochokera ku Afirika iyi: “Nkhanizo zinafika panthaŵi imene ndinazifuna koposa. Kunali kodzetsa mpumulo chotani nanga kuŵerenga ndemanga zonga, ‘khalani ndi chitsimikizo kuti chiyembekezo chiripo, kuti mungachire’ ndipo ‘SUNALI MLANDU WANU!’ Pamene ndinaŵerenga nkhanizo, ndinadzimva wachisungiko ndi wotonthozedwa kwanthaŵi yoyamba m’moyo mwanga. Zinabweretsa chitonthozo chenicheni m’maganizo mwanga, moyo, ndi thupi. Tsopano ndidzakhala ndi nyonga yakuyenda pamsewu womka ku kuchira.”—Nigeria.

Mkazi wina akulemba kuti: “Ndiribe mawu ofotokozera chiyamikiro changa ndi mmene ndinamverera nditaŵerenga Galamukani! wa October 8 wa kuchitira nkhanza ana. Misozi inadzaza maso anga pamene ndinaŵerenga ndime iliyonse, tsamba lirilonse, lemba lirilonse. Inalembedwa molingalira kwambiri, mwachifundo ndi mwachikondi. Monga mkole, ndakhala ndikulimbana ndi malingaliro ndi maganizo anga. Tsopano ndikumva kuti mtolo waukulu wa chisoni wachotsedwa. Mothandizidwa ndi nkhani zanu ndi bwenzi lokhulupirika, loleza mtima lomwe limamvetsera ndi kundichilikiza, ndingalole kupoletsako kuyamba.” Mulungu wa kukoma mtima konse, kupyolera mu utumiki waunsembe wa Mwana wake, ‘akukhazikitsa’ ndi ‘kulimbitsa’ mikole yambiri yoteroyo. (1 Petro 5:6-11)—United States.

Mkole wina wa kugonedwa ndi achibale anakwiya kwakuti anafuna kudzipha mwakuyatsa galaja ya galimoto iye ali mkatimo. Anapulumutsidwa ndipo anaperekedwa kuchipatala. Mwamsanga pamene kope la October 8 linatuluka, linaperekedwa kwa iye. Analira kwambiri ataliŵerenga, ndiyeno anabwerezanso kuŵerenga nkhanizo kaamba ka chichilikizo, kumthandiza kulaka zikhoterero zake zakufuna kudzipha. Bwenzi lake lomwe linamthandiza kwambiri linalemba kuti: “Nthaŵi zina ndimaganiza kuti Galamukani! ayenera kupatsidwanso dzina lakuti Lakani popeza kuti ndizo zimene akutithandiza kuchita.”—United States.

“Ena Angaiŵale, Ena Sangaiŵale”

Woŵerenga wina woyamikira anati: “Nkhani za kuchitira nkhanza ana nzosapendekera mbali imodzi. Ndinayamikira malemba ogwiritsiridwa ntchito. Nkhanizi zinalembedwanso bwino kwakuti ndikhoza kukuyamikirani pandime iliyonse. Ndine woyamikira kuti munasonyeza kuti ngakhale kuti ena angaiŵale, ena sangatero. Ndakhala ndikukumbukira zochitikazo kwa zaka zitatu ndi kupweteka kwakuthupi komwe chikumbukiro chirichonse chimadzetsa. Koma ndimapeza bwino mwakuphunzira kulaka zikumbukirozo. Ndikuthokozaninso chifukwa cha nkhani zolinganizika bwinozo.” (United States) Nkhani Zamalemba zimenezi zathandiza mkole ameneyu, ndi ena ambiri, kupezanso chimwemwe m’makonzedwe auzimu a Yehova.—Afilipi 4:4-9.

Mkazi wina analemba kuti: “Ndakhala ndikuŵerenga Galamukani! kwa zaka zambiri. Komabe, sindinayambukiridwepo kwambiri ndi nkhani ina iliyonse monga momwe ndinachitira ndi mpambo wa magazini a mutu wakuti ‘Kupoletsa Mabala a Kuchitira Nkhanza Ana.’ Nkhaniyo njovuta, koma munailemba mwaluso ndi mokoma mtima. Pokhala mwana wochitiridwa nkhanza, magaziniwo anandithandiza ndi kunditonthoza mokulira. Ndidzasunga magaziniwa kuti ndidziwaŵerenga mobwerezabwereza. Sindingathedi kukuthokozani kaamba ka nthaŵi, kuyesayesa, chidziŵitso, ndipo chofunika koposa chikondi chomwe mwasonyeza kwa amene akuvutika mwakachetechete.”—United States.

Kuyang’anizana ndi Zenizeni

Kwakhala kothandiza kwa mikole yomwe singaiŵale maupandu ochitidwa kwa iwo kulankhula ndi mkulu wachifundo, kuyang’anizana ndi vutolo mwachindunji, kuwona mmene Yehova amawonera nkhaniyo, ndikuchita nayo Mwamalemba kotero kuti kuchiritsa kwa mphamvu ya dipo la Yesu kuchitike. Polingalira zimenezi, mkazi wina anati:

“Sindingathe kufotokoza mmene nkhanizo zinaliri zapanthaŵi yake. Ndinalepheradi kukhulupirira kulongosoka kwa chidziŵitsocho. Ndakhala ndikuchita tondovi ndi kudya mopambanitsa kwa zaka 20, kufunafuna chithandizo ndi mayankho kulikonse: kwa akatswiri a nthenda zamisala, zamaganizo, adokotala, kulandira uphungu pa gulu, zipatala zothandiza kukhala wowonda—koma zosaphula kanthu kwa ine.

“Koma tsopano ndikupeza chithandizo m’chidziŵitso chopezeka m’kope la October 8. Nlofunika kwambiri. Sindingathe kukusimbirani malingaliro akupanda chiyembekezo omwe ndimakhala nawo nthaŵi zina, othetsa nzeru kwambiri kotero kuti imfa imawoneka kukhala yodzetsa mpumulo. Koma tsopano ndikuwona kuti zimene zinandichitikira ndiri mwana sizinali mlandu wanga, ndipo Mulungu samandiwona kukhala wodetsedwa. Ndinali mkole. Chifukwa cha chidziŵitso choterocho, ndikuwona kuti Yehova amasamala, kuti nditha kumdalira. Pambuyo pa kukhala ndi moyo kwa zaka 33, ndikuumva mzimu wa Yehova ukuyamba kumasula maunyolo aukapolo. Ndikuthokoza chifukwa chotikonda kwambiri mwakutaya nthaŵi yochuluka pokonza ngale yabwino koposa imeneyi ya Galamukani! Chonde pitirizani kufalitsa nkhani zoterozo ndi zina, popeza kuti nzofunika ku uzimu wathu.”

Kalata yotsatirayi inachokera kwa mwamuna wina yemwe akumveketsa malingaliro a ambiri. Iye wakhala wosweka mtima kwa zaka zoposa 50 chifukwa chochitiridwa nkhanza ali mwana. Iye akuti: “Chisamaliro chachikondi cha Yehova kupyolera m’gulu lake lapadziko lapansi sichidzaleka kutizizwitsa ndi kutisonkhezera kusonyeza kudzipereka kozama ndi kumkhulupira. Nditaphunzira mosamalitsa chidziŵitso cha mu Galamukani! wa October 8, 1991 wa kuchitira nkhanza ana, ndinalira ndi chimwemwe ndi kuimbira Yehova nyimbo zambiri, thanthwe ndi linga lathu, pothaŵirapo pathu. Abale, pitirizani kufalitsa nkhani zoterozo. Yehova akukugwiritsirani ntchito m’njira zimene simungazilingalire.”

Kuchokera kwa Oyang’anira

Kalata iyi yochokera kwa woyang’anira woyendayenda amene amayang’anira ntchito ya mipingo yambiri ya Mboni za Yehova njosangalatsa:

“Ndikuthokozani chifukwa cha Galamukani! wa October 8 pa ‘Kupoletsa Mabala a Kuchitira Nkhanza Ana.’ Chidziŵitso chabwino koposa chimene timafunikira chinaperekedwa. Nkhanizo zinali zolongosoka kwenikweni. Ndinawona kuti kwanthaŵi ndi nthaŵi mikole imavutika kwambiri kulankhula kwa Yehova monga Atate wachikondi. Nditawona vutoli, ndimawafunsa mochenjera kuti, ‘Kodi munachitiridwapo moipa pamene munali mwana?’ Kaŵirikaŵiri yankho limakhala inde! M’chochitika chirichonse pamene munthuyo anakhoza kuwona kugwirizana pakati pa nkhanzayo ndi mmene kuchita tondovi kwawo kapena kuvutika kukuwayambukirira, anayamba kuwongokera.”

Yofotokoza mwachidule mmene akulu ambiri akulingalira ndiyo ndemanga iyi yoperekedwa ndi mkulu wina: “Kope la October 8 la kuchitira nkhanza ana linali labwino koposa ndi lofunika. Monga akulu m’mipingo, tifunikira kudziŵa zambiri monga momwe tingathere ponena za mavuto ameneŵa kotero kuti tisonyeze nkhaŵa ndi kuleza mtima kumene mikole imafunikira. Pamene dongosololi likuipiraipira, mavuto amtundu umenewu akuwonjezereka. Ndikuthokozaninso chifukwa cha chithandizocho.”

Kulandira makalatawa kwatisangalatsa. Pozindikira kotheratu kuti ‘sunali mlandu wawo,’ ndiponso chifukwa cha mphamvu yosintha ya Mawu a Mulungu, mikole ya kuchitira nkhanza ana imalaka zikumbukiro zoipa. Amakondwera m’chiyembekezo chiri kutsogolo, achidaliro kuti m’dziko latsopano la Mulungu, “zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima.” (Yesaya 65:17; Aroma 12:12) Ngakhale tsopano, kupyolera m’mphamvu yochiritsa ya mwazi wa Yesu, ali ndi kaimidwe koyera ndi Mulungu. (Ahebri 9:14) Ndipo afunikira kutembenukira kwa akulu kaamba ka chithandizo. Akulu ameneŵa angachite monga “pobisalira mphepo” kwa ovutika, kulankhula motonthoza ndi kupemphera nawo. (Yesaya 32:2; 1 Atesalonika 5:14; Yakobo 5:14, 15) Chotero, mikole ya kuchitiridwa nkhanza ingathandizidwe kupita patsogolo ndi kupeza chisangalalo m’ntchito zonse za mpingo Wachikristu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena