Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 5/8 tsamba 11-12
  • Alendo—Kodi Mungawathandize Motani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Alendo—Kodi Mungawathandize Motani?
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Titengeni Mmene Tiriri
  • Chithandizo Chonunkha Kanthu
  • Kukhala ndi Wina Wake Womdalira
  • Alendo Kodi Angachite Motani?
    Galamukani!—1992
  • Alendo—Vuto la Dziko Lonse
    Galamukani!—1992
  • Kodi Nditsatire Chikhalidwe Chiti?
    Galamukani!—2007
  • Kodi Tingathandize Bwanji Ana a Anthu Ochokera M’mayiko Ena?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 5/8 tsamba 11-12

Alendo—Kodi Mungawathandize Motani?

MTOLA NKHANI Günter Wallraff ananamizira kukhala wantchito wochokera ku Turkey ndipo anagwira ntchito yaulebala m’kampani yosula zitsulo m’Jeremani. Pamene anaulula zimene anawona, mmene antchito akunja, kapena achilendo anachitidwira, zinadabwitsa ndi kukwiitsa anthu ambiri. Iye analemba nkhani zambiri za kuchita tsankho koipitsitsa kulinga kwa antchito ochokera kumaiko ena. Panthaŵi ina, anadziwonera pamene antchito ochokera ku Turkey analamulidwa kugwira ntchito m’malo owopsa mosasamala kanthu ndi kuimba kwa maalamu ndi kuchenima kwa nyali zofiira zopereka chenjezo. Pamene mwamuna wina anawopa ndi kufuna kuchokako kumalowo, anawopsezedwa kuchotsedwa ntchito.

Zokumana nazo za Wallraff zimasonyeza bwino lomwe mkhalidwe womvetsa chisoni wa alendo odzakhala m’dziko. Pamene nzika zachifundo zimadziŵa za mavuto oyang’anizana ndi alendo, zambiri zimalingalira zimene zingachite kuti zithandize wosamukira m’dzikoyo ndi banja lake.

Titengeni Mmene Tiriri

Peŵani tsankho. Tsankho ndichinthu chimene chimapangitsa mwamsanga kukaikirana kwakukulu ndi kusalolerana pakati pa nzika ndi alendo. “[Mwambo] umawononga kawonedwe kathu ka mmene anthu ena amachitira zinthu, makamaka pamene njira zawo zisiyana . . . ndi mikhalidwe yathu imene tiwona kukhala yabwino,” anatero wolemba nkhani Ben Levitas m’bukhu lake lakuti Tribal Life Today. Iye ananena kuti kusiyana kumeneku “kaŵirikaŵiri kumatipangitsa kusuliza mmene ena amachitira zinthu.” Helen, nzika ya ku Korea yosamukira ku Canada, akukumbukira bwino lomwe tsiku limene mphunzitsi wake anamzazira mwaukali pamene analephera kuchita zimene kalasi linauzidwa kuchita. “Mphunzitsi sanazindikire kuti sindinalikumva zimene ananena,” akutero Helen, amene zimenezo zidamvutitsa maganizo kwambiri panthaŵiyo.

Malingaliro olakwa ponena za anthu a mafuko ena kaŵirikaŵiri amazikidwa pa zopeka mmalo mwa zenizeni. M’bukhu lawo lakuti Cross-Cultural Learning & Self-Growth, Mildred Sikkema ndi Agnes Niyekawa-Howard anasimba za profesa wa ku Amereka amene anayesa ophunzira ake atsopano ochokera kumaiko ena mwakunena nthabwala kwa iwo. Ndiyeno ankawona mmene akachitira. Ngati sanaseke, pamenepo ophunzirawo akaperekedwa ku makalasi ophunzira Chingelezi. “Mwachiwonekere [profesayo] sanazindikire,” anatero olemba nkhaniwo, “kuti kumva nthabwala Yachimereka kumafuna kuzoloŵerana ndi miyambo Yachimereka ndi chinenero . . . Zimene anthu a miyambo ina angawone kukhala zoseketsa zingakhale zosaseketsa [kwa ena].” Machitidwe okhala ndi cholinga chabwino oterowo a nzika za dziko amavumbula kusoŵa kwawo luntha pochita ndi alendo.

Ngati mutenga mlendo mmene aliri, popanda kumlingalira molakwa, adzakuyamikirani kwambiri. Kachitidwe koteroko kamagwirizana ndi lamulo lamakhalidwe abwino loperekedwa ndi Yesu lakuti: “Uzikonda . . . mnansi wako monga iwe mwini.” (Luka 10:27) Yasushi Higashisawa, loya wa ku Tokyo, mu Japani, amene amachita kwambiri ndi alendo, akuvomereza kuti “kuyanjana ndi anthu ambiri a miyambo yosiyanasiyana ndiko mankhwala abwino koposa othetsera tsankho.” Mayanjano oterowo amakhozetsa wosamukira m’dziko kuthandizidwa mwa njira zina zambiri.

Chithandizo Chonunkha Kanthu

Pali zambiri zimene mlendo amafuna kudziŵa ponena za dziko latsopano—mmene angapezere nyumba, kuphunzira chinenero, kupezera ana sukulu, mmene angathandizidwire ndi mautumiki amene boma limapereka kwa anthu. Mukhoza kumthandiza kwambiri mwakumuuza zimene mumadziŵa.

Mwachitsanzo, kodi mungamthandize mlendo kupeza mabungwe amene adzamthandiza kuzoloŵera chinenero ndi miyambo ya dzikolo? Kapena kodi mungamperekeze mkazi wosamukira m’dziko pamaulendo ake oyambirira okagula zinthu kumthandiza kudziŵa zakudya ndi zinthu za m’nyumba? Bwanji ponena za kusonyeza banja losamukira m’dziko mmene angatsatirire njira zimene kaŵirikaŵiri zimakhala zocholoŵana, zopezera chilolezo chokhalira m’dziko, zopezera ntchito, kudzaza mafomu okhomera msonkho, ndi zina zotero?—Onani mawu amtsinde m’bokosi.

Kukhala ndi Wina Wake Womdalira

Kumakhala kothandiza nthaŵi zonse kudzifunsa kuti: ‘Ndikadakhala m’dziko lina, kodi ndikadakonda anthu kundichitira motani?’ ‘Zinthu ziri zonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero,’ anatero Yesu popereka Lamulo Lamakhalidwe Abwino. (Mateyu 7:12) Kukhala ndi bwenzi limene mumadalira m’zokunana nazo zovuta zakuyesa kusintha ndi kuzoloŵera mikhalidweyo kumakhala chithandizo chimene alendo angachiyamikire. Kuchezera koteroko kwa nzika za dzikolo kumadzetsa mapindu kwa onse. Lamulo lina lamakhalidwe abwino la Baibulo limanena kuti: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.”—Machitidwe 20:35.

Ngati ndinu mmodzi wa Mboni za Yehova, mphatso yabwino koposa imene mungapatse mlendo ndiyo chiyembekezo cha kupeza gulu la abale ogwirizana. Mwachiwonekere, mungapeze nkhani zolembedwa zomangirira zimene mungakambitsirane naye m’chinenero cha kwawo.

Ndithudi, kuti kusamukira m’dziko kukhale kwachipambano, zimadalira kwenikweni pa mlendoyo. Koma mutazilingalira pasadakhale, pamakhala zambiri zimene mungachite kumpangitsa kumva womasuka, mwakutero kuchititsa kusamuka kwake kukhala kosavutitsa maganizo kwambiri, ndipo ngakhale kokhutiritsa.

[Mawu Otsindika patsamba 11]

“Timalingalira kuti anthu a miyambo ina . . . amawona, kulingalira, ndi kuganiza monga ife. . . . Kulingalira ena molakwa kumachititsidwa ndi maganizo akuti mmene timachitira ndimmene anthu onse amachitira.”—Cross-Cultural Learning & Self-Growth

[Mawu Otsindika patsamba 12]

Wophunzira wina amene anakhalako pa chisumbu cha Guam anati: ‘Ndakhala wololera kwambiri njira zatsopano kapena zachilendo zochitira zinthu.’—Cross-Cultural Learning & Self-Growth

[Bokosi patsamba 12]

Mukhoza kuthandiza mlendo . . .

▶ kukhazikika mwakukhala mnansi wochereza kwa iye

▶ kudzaza mafomu okhomera msonkhoa

▶ kuwonana ndi akuluakulu aboma pamene akutenga chilolezo chokhalira m’dzikob

▶ kufunsira ku mabungwe amene amaphunzitsa miyambo yakumaloko ndi chinenero

▶ kupeza nyumba

▶ kumsonyeza zipatala ndi mautumiki ena aboma

▶ kupezera ana sukulu

▶ kukagula zinthu zofunika pamitengo yabwino

▶ kupeza ntchito

[Mawu a M’munsi]

a Maiko ena, monga Jeremani, ali ndi malamulo okhwima ponena za amene ayenera kupereka chithandizo pankhani za malamulo, kusamukira m’dziko, ndi zakukhoma msonkho. Chotero, muyenera kuzipenda zimenezi musanapereke chithandizo chirichonse kwa alendo chakupeza chilolezo chakukhala m’dziko.

b Maiko ena, monga Jeremani, ali ndi malamulo okhwima ponena za amene ayenera kupereka chithandizo pankhani za malamulo, kusamukira m’dziko, ndi zakukhoma msonkho. Chotero, muyenera kuzipenda zimenezi musanapereke chithandizo chirichonse kwa alendo chakupeza chilolezo chakukhala m’dziko.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena