Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 7/8 tsamba 15-17
  • Kupatsa Ulemu Akazi Mumpingo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupatsa Ulemu Akazi Mumpingo
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ali “Chotengera Chochepa Mphamvu” Motani?
  • Kodi Chofunikira Nchiyani Kuti Pakhale Kusintha?
  • “Chotengera Chofookerapo” Kodi Nkunyoza Akazi?
    Galamukani!—1994
  • Malangizo Anzeru kwa Okwatirana
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Kusonyeza Chikondi ndi Ulemu Monga Mwamuna
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Mwamuna ndi Mkazi Onse Ali ndi Udindo Wolemekezeka
    Nsanja ya Olonda—2007
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 7/8 tsamba 15-17

Kupatsa Ulemu Akazi Mumpingo

BAIBULO limakhazikitsira Akristu ndandanda yateokratiki ya umutu, kumene Kristu ali wogonjera kwa Mulungu, mwamuna ali wogonjera kwa Kristu, ndi mkazi ali wogonjera kwa mwamuna wake. (1 Akorinto 11:3) Komabe, kugonjera kumeneku sikumatanthauza kutsendereza ufulu. Umutu m’banja sumakhazikitsidwa ndi chiwawa, kaya chikhale kumenya, kuvutitsa maganizo, kapena kulalata. Ndiponso, umutu Wachikristu uli ndi malire ndipo sumatanthauza kuti mwamuna angakhale munthu wankhaza wodziyesa kukhala wosalakwa.a Kudziŵa njira ndi nthaŵi yonenera kuti “Pepani, munalondola” kukathandizira maukwati ambiri kukhala odzetsa mpumulo ndi okhalitsa. Komabe, ndimosavuta chotani nanga mmene wina angalepherere kunena mawu akudzichepetsa amenewo!—Akolose 3:12-14, 18.

Muuphungu wawo waukwati, atumwi Achikristu Paulo ndi Petro mosalekeza amatikumbutsa chitsanzo cha Kristu. Ulemu umapezedwa kupyolera mwa chitsanzo chotsitsimula cha mwamuna pamene atsanzira chitsanzo chimene Kristu anapereka, pakuti “mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Kristu ndiye mutu wa [mpingo, NW], ali yekha mpulumutsi wa thupilo.”—Aefeso 5:23.

Uphungu wa Petro kwa amuna ngwomvekera bwino: “Momwenso amuna inu, khalani nawo [akazi anu] monga mwa chidziŵitso.” (1 Petro 3:7) Matembenuzidwe amakono Achispanya amatchula mwachidule malingaliro ameneŵa, kuti: “Amuna inu: khalani aluso m’moyo wanu wabanja, mukumakomera mtima mkazi wanu.” Mawu ameneŵa amatanthauza zinthu zambiri, kuphatikizapo kuzindikira malingaliro muunansi wa ukwati. Mwamuna sayenera kuwona mkazi wake monga chiŵiya chokhutiritsira chikhumbo chake chakugonana. Mkazi wina wabanja amene anavutika maganizo chifukwa chogonedwa paubwana analemba kuti: “Ndimalakalaka kuti mukananena zochuluka ponena za chichirikizo chimene mwamuna ayenera kupereka kwa mkazi wake amene anachitiridwa zimenezi. Zimene ochuluka a akazi abanja timafuna kudziŵa nzakuti tikukondedwadi ndi kusamaliridwa, osati kuti kukhalira kokha kukhutiritsa zikhumbo zakuthupi kapena monga wosunga nyumba, popanda chikondi chenicheni.”b Ukwati unayambidwa ndi Mulungu kotero kuti amuna ndi akazi awo akakhale atsamwali ndi othandizana. Iri nkhani yochitira zinthu pamodzi ndi kulemekezana.—Genesis 2:18; Miyambo 31:28, 29.

Kodi Ali “Chotengera Chochepa Mphamvu” Motani?

Ndiponso Petro akupatsa amuna uphungu wakuchitira akazi awo ulemu “monga chotengera chochepa mphamvu.” (1 Petro 3:7) Kodi Petro anatanthauzanji mwakunena kuti mkazi ali “chotengera chochepa mphamvu”? Ndithudi, kumlingo wozoloŵereka, mkazi ngwochepa mphamvu mwakuthupi kuposa mwamuna. Kusiyana kwa kaumbidwe ka thupi ndi minofu kumachititsa zimenezo. Koma ngati tinena za nyonga yamkati yamakhalidwe, pamenepo mkazi saali konse wofookerapo kuposa mwamuna. Kwa zaka zambiri akazi apirira mikhalidwe imene mwina amuna ochuluka sakanapirira ngakhale mwakanthaŵi—kuphatikizapo nkhanza yochokera kwa mnzawo wamuukwati wachiwawa kapena chidakwa. Ndipo talingalirani zimene mkazi amapirira kuti abale mwana, kuphatikizapo maola ochuluka a zoŵaŵa za kubala! Mwamuna aliyense wachifundo amene anawonapo kubala kozizwitsa ayenera kusonkhezeredwa kukhala waulemu kwambiri kwa mkazi wake ndi kulimba mtima kwake.

Pankhani imeneyi yanyonga yamkati yamakhalidwe, Hannah Levy-Haas, mkaidi Wachiyuda m’ndende yachibalo Yachinazi ya Ravensbrück analemba m’dayali yake mu 1944 kuti: “Chinthu chimodzi chimandikwiitsa kwambiri muno, ndipo chimenecho ndicho kuwona kuti amuna ngofookerapo kwambiri ndi osakhoza kupirira mavuto kuposa akazi—mwakuthupi ndiponso kaŵirikaŵiri mwamakhalidwe. Pokhala osakhoza kudziletsa, amasonyeza kupanda mphamvu yamakhalidwe kotero kuti wina amangowamvera chisoni.”—Mothers in the Fatherland, yolembedwa ndi Claudia Koonz.

Chokumana nacho chimenechi chimasonyeza bwino lomwe kuti palibe maziko enieni okhalira watsankho kwa akazi kokha chifukwa chakuti angakhale ocheperapo mphamvu kuthupi. Edwin Reischauer analemba kuti: “M’nthaŵi zamakono, kukuvomerezedwa kaŵirikaŵiri kuti akazi ngotsimikiza mtima kwambiri ndipo ali ndi nyonga yaikulu yamaganizo kuposa amuna.” (The Japanese) Nyonga imeneyi ingathe kugwiritsiridwa ntchito mumpingo Wachikristu pamene akazi akulu msinkhu angakhoze kuthandiza akazi ena amene akuvutika ndi kupsinjika maganizo kwambiri. Ndithudi, m’mikhalidwe ina kumakhala kosavuta kwambiri kwa mkazi wochitiridwa nkhanza kutembenukira kwa mkazi mkulu msinkhu kaamba ka chitonthozo chamwamsanga kuposa kutembenukira kwa mwamuna. Ngati kungafunikire, mkulu Wachikristu angapemphedwe chitsogozo chowonjezereka.—1 Timoteo 5:9, 10; Yakobo 5:14, 15.

Kugamula kosalingalira kwakuti mayankhidwe asontho a mkazi amachititsidwa ndi “nyengo yakusamba” kumakwiitsa akazi ambiri. Betty, mkazi Wachikristu, ananena kuti: “Tidziŵa, monga momwe Petro analembera, kuti m’mbali zina ndife ‘chotengera chochepa mphamvu,’ mkazi wokhala ndi kaumbidwe ka thupi kofooka kwambiri. Koma zimenezo sizitanthuza kuti folomani kapena kapitawo ayenera kukhala woluluza kapena watsankho, akumalingalira kuti kachitidwe kalikonse ka akazi kali chifukwa cha nyengo yakusamba. Ndife aluntha ndipo timafuna kumvedwa mwalemu.”

Siakazi onse amene amachita zinthu motengeka maganizo, monga momwenso siamuna onse amene amachita zinthu mosatengeka maganizo. Munthu aliyense ayenera kutengedwa mosiyana. Betty, wogwidwa mawu poyamba, anauza mlembi wa Galamukani! kuti: “Sindimakonda kupatulidwa pamaziko akuti ndine mkazi. Ndawona amuna akulira amenenso ali amtima wapachala. Ndipo pali akazi ena ouma gwa. Chotero amuna atimvetseretu mosamalitsa popanda kulingalira za ukazi.”

Kodi Chofunikira Nchiyani Kuti Pakhale Kusintha?

Ngati pati pakhale kusinthira kumikhalidwe yabwinopo, ena amanena kuti sikokwanira kuti akazi achite mkupiti wofuna zoyenera zawo ndi kuchitiridwa chilungamo; ndiponso sikokwanira kuti amuna apange njira yachiphamaso yakuchitira akazi ulemu. M’chitaganya chirichonse ndi mkhalidwe, amuna ayenera kupenda mbali yawo m’nkhaniyi ndi kudzifunsa zimene angathe kuchita kudzetsa moyo wachimwemwe kwambiri ndi mpumulo wowonjezereka kwa akazi.—Mateyu 11:28, 29.

Wolemba nkhani ndi ndakatulo Katha Pollitt analemba m’magazini a Time kuti: “Ndithudi, amuna ochuluka samagwirira chigololo kapena kumenya kapena kupha. Koma zimenezo sizikutanthauza kuti, monga momwe unyinji wa iwo umawonekerera kukhala akulingalirira, sumachita chiwawa chirichonse kwa akazi. Aliyense wa ife m’moyo wathu watsiku ndi tsiku timathandizira kuumba zikhulupiriro zachitaganya ndi malingaliro zimene zimaika malire pa zinthu zololeka. . . . Ndikunena amuna amene amadzipenda mwamphamvu, kukaikira malingaliro awo atsankhu ndi maudindo, kuvomereza thayo lawo kaamba ka mkhalidwe woipa umene tirimo.”

Koma ngakhale ngati amuna padziko lonse angapange masinthidwe aakulu m’kaimidwe kawo kamaganizo kulinga kwa akazi, kutero sikudzakhala konse njira yeniyeni yothetsera chisalungamo chimene chakantha anthu. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti amuna sakuchitira akazi okha chisalungamo ndi nkhalwe komanso amuna anzawo. Nkhondo, chiwawa, mbanda, magulu akupha, ndi uchigaŵenga zikadali zofunga m’maiko ambiri. Chofunika ndicho dongosolo latsopano laulamuliro wa dziko lonse. Ndi maphunziro atsopano a anthu onse. Ndipo ndizo zimene Mulungu walonjeza kupyolera mu Ufumu wake wakumwamba wodzalamulira dziko lapansi. Ndipanthaŵi yomweyo basi pamene chiweruzo cholungama chowona ndi kulingana zidzakhalapo kaamba ka onse—amuna, akazi, ndi ana. Ndipanthaŵi yomweyo basi pamene kulemekezana pakati pa amuna ndi akazi kudzakhalapo. Baibulo limanena zimenezi motere pa Yesaya 54:13: “Ndipo ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.” Inde, maphunziro oyenera a malamulo amakhalidwe abwino olungama a Yehova adzathandizira kudzetsa dziko latsopano m’limene mudzakhala kulemekezana.

[Mawu a M’munsi]

a Wonani nkhani yakuti “Kodi Kugonjera Muukwati Kumatanthauzanji?” mu Nsanja ya Olonda, ya December 15, 1991, masamba 19-21.

b Wonani Galamukani! ya October 8, 1991, masamba 3-11; April 8, 1992, masamba 26-9.

[Chithunzi patsamba 16]

Kaŵirikaŵiri mkazi mkulu msinkhu angapereke uphungu wothandiza

[Chithunzi patsamba 17]

Kuthandizana ntchito zapanyumba ndiimodzi ya njira zimene mwamuna angalemekezere mkazi wake

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena