Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 7/8 tsamba 24-25
  • Kodi Dzikoli Lifunikira “Kulalikiridwa Kwatsopano”?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Dzikoli Lifunikira “Kulalikiridwa Kwatsopano”?
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Kwatsopano” m’Lingaliro Lotani?
  • Chifukwa Chake Pali Kugwiritsidwa Mwala
  • Kulalikira—Njira ya Baibulo
  • Tchalitchi cha Chikatolika mu Spanya—Kodi Nchifukwa Ninji Vutolo?
    Galamukani!—1990
  • Tchalitchi cha Katolika mu Afirika
    Galamukani!—1995
  • Tchalitchi cha Anglican cha ku Australia Nyumba Yogaŵanika
    Galamukani!—1993
  • Kodi Nchifukwa Ninji tchalitchi Chikutha Mphamvu?
    Galamukani!—1996
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 7/8 tsamba 24-25

Lingaliro la Baibulo

Kodi Dzikoli Lifunikira “Kulalikiridwa Kwatsopano”?

Ndi mlembi wa Galamukani! mu Italy

ZIKHOTERERO zamphamvu za kusintha m’ndale zadziko zimene zakhala zikuchitika Kummaŵa kwa Ulaya konse zamkira limodzi ndi kuyambitsidwanso kwa chipembedzo. Kuti upindule ndi mpata umenewu wauzimu, Msonkhano Wapadera wa Sinodi ya ku Ulaya ya Mabishopu unachitika ku Vatican kuyambira November 28 kufikira December 14, 1991. “Abambo a Sinodi” 137, amene ali patsogolo m’kuchirikiza ulamuliro wa Chikatolika cha ku Ulaya, anasonkhana ncholinga cha “kulalikiridwa kwatsopano.”

Kuyambira panthaŵi imene sinodiyo inalengezedwa pa April 22, 1990 ku Velehrad, Czechoslovakia, inalengezedwa monga chochitika chapadera m’mbiri. Komabe, nkovuta kuganiza za sinodiyo kukhala ya chipambano chosonkhezera mtima, popeza kuti RAI, nyumba ya wailesi yakanema ya dziko la Italy, inalengeza pa December 14, 1991 kuti: “Sinodi yogwiritsa mwala ija yatha.”

Kodi nchifukwa ninji sinodiyo inali yogwiritsa mwala? Ndipo kodi Ulaya, kapena dziko lonseli, lifunikira “kulalikiridwa kwatsopano”?

“Kwatsopano” m’Lingaliro Lotani?

Ulamuliro Wachikatolika umaganiza kuti kulalikiridwa kwatsopano nkoyenerera chifukwa chakuti zochitika za chipembedzo nzatsopano. Potsegulira msonkhanowo, kadinala Camillo Ruini anafotokoza mwachidule mmene akuwonera zochitika za mu Ulaya. Iye anati Kummaŵa “mamiliyoni ambiri sanabatizidwebe ndipo amanyalanyaza chowonadi choyambirira koposa cha chikhulupiriro Chachikristu.” Kaamba ka chifukwa chimenechi “kugwa kwa maulamuliro Achikomyunisti kukutsegula mipata yambiri ya kulalikiridwa kwa Tchalitchi.” Kumbali ina, zochitikazo ku Ulaya Wakumadzulo zikusonyezedwa ndi chimene iye akutcha kuti “kusakhulupirira Mulungu kotheratu.” Liwu la Tchalitchi cha Katolika silikulandiridwanso monga chowonadi chochokera kwa Mulungu.

Kuyambitsidwanso kwachipembedzo mwa iko kokha kumadzetsa chitokoso china kwa mabishopu. M’njira yotani? Ponse paŵiri mabishopu a ku Ulaya ndi a ku Latin America akuvutika maganizo ndi kuwonjezeka kwa timagulu tina tachipembedzo. Chifukwa ninji? Mwachiwonekere chifukwa chakuti tchalitchi chatayikiridwa ndi mwaŵi wambiri wa malo antchito umene kale chinali nawo, ndipo tsopano chimadziwona kukhala “chikuwopsezedwa ndi adani aupandu.” Magazini yotuluka panthaŵi ndi nthaŵi ya Jesuit La Civiltà Cattolica inasonya Mboni za Yehova kukhala amodzi a adaniwo chifukwa cha “chiŵerengero chachikulu cha Akatolika ndi Aprotesitanti amene zimawakopa.”

Mawu a mu “Chilengezo” chomalizira cha sinodi amanena kuti kulalikiridwa kwatsopano ndiko chitsitsimulo ku “kupezedwanso kwa chiyambi cha Chikristu cha munthuwe.” Kodi nchifukwa ninji nzika za Ulaya zifunikira kupezanso ‘chiyambi chawo Chachikristu’? Mabishopuwo ananena kuti miyambo Yachikristu sikulingaliridwanso kukhala yogwira ntchito. “Kwa nzika za Ulaya zambiri zimene zikubatizidwa,” inatero La Civiltà Cattolica, chipembedzo “ncha achibwana, nthano yoseketsa ya ana chimene ndithudi achikulire sangachilingalire mwamphamvu, monga ngati kuti chinali kanthu kena kamene kangayambukire miyoyo yawo. . . . Nzika zina za Ulaya zimawona chipembedzo Chachikristu kokha monga miyambo wamba ya anthu, chifukwa cha chimenecho choyembekezeredwa kuzimiririka pamene kutsungula kukupita patsogolo . . . Ndiponso nzika zina za Ulaya zimalingalira chipembedzo Chachikristu kukhala chaupandu.”

Kaamba ka zifukwa zimenezi mabishopuwo akuwona kufunika kwa “kulalikiridwa kwatsopano.”

Chifukwa Chake Pali Kugwiritsidwa Mwala

Kuti apambane mu “kulalikiridwa kwatsopano” kumeneko kwa Dziko Lakale, gulu lalikulu la antchito likakhala lofunika. Komabe, limodzi la mavuto aakulu limene lakhala likuyambukira tchalitchi mu Ulaya ndilo kuchepa kwa ansembe. Mmodzi wa mabishopu ananena kuti m’zaka 13 zathazi, malinga ndi kuyerekezera ziŵerengero kwaposachedwapa kwa ku Ulaya, atsogoleri achipembedzo atsikira m’chiŵerengero ndi 9 peresenti.

Ambiri analingalira sinodi imeneyi kukhala yogwiritsa mwala chifukwa chakuti panali mfundo zogwira ntchito zoŵerengeka zokha ponena za mmene angachititsire “kuyambitsidwanso kwa Chikristu” kugwira ntchito mu Ulaya. Bishopu wa ku Falansa Joseph Duval analimbikitsa msonkhano wa sinodiyo kuti: “Tiyenera kupeŵa nkhani zosathandiza pakulalikira . . . Tonsefe timangolongolola monga akatswiri achilamulo. Uthenga wathu ukhalensotu ulaliki wosacholoŵana ndi womveka bwino.”

Ndimabishopu oŵerengeka chabe amene anatchulapo njira ya atumwi yolalikirira anthu. Mwachitsanzo, Bishopu František Tondra wa ku Spiš, Lipabuliki la Chitaganya cha Czech ndi Slovak, anati: “Kaamba ka kulalikiridwa kwatsopano kwa Ulaya, tiyenera kubwerera kumpangidwe woyamba wakulalikira. . . . Akristu oyamba, mwamsanga atangobatizidwa, analiwona kukhala thayo lawo kufalitsa Uthenga Wabwino.”

Kulalikira—Njira ya Baibulo

Kodi Akristu onse a m’zaka za zana loyamba anali alaliki? Inde! Bukhulo Evangelism in the Early Church, lolembedwa ndi Michael Green, Oxford, England, limati: “Imodzi ya mbali zochititsa chidwi m’kulalikira m’masiku oyambirira inali ya anthu amene analoŵetsedwamo. . . . Kulalikira kunali lamulo ndi thayo la chiŵalo chirichonse cha Tchalitchi. . . . Kwakukulukulu Chikristu chinali kagulu kachipembedzo ka anthu wamba, kofalitsidwa ndi amishonale wamba.”

Liwulo “mlaliki” limatanthauza “wolalikira mbiri yabwino,” ndipo zimene Yesu Kristu ananena ponena za kulalikira zinali kudzagwira ntchito kwa otsatira ake onse: “Mbiri yabwino imeneyi [uthenga wabwino] ya ufumu idzalengezedwa kudziko lonse monga umboni kumitundu. Ndipo pamenepo mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14, The New Jerusalem Bible) Motero, ntchito yolalikira yaikulu koposa yonse imene inachitidwa kale iyenera kuchitidwa mu “nthaŵi ya chimaliziro.”—Danieli 12:4.

Chaka chatha, Mboni za Yehova, zoposa mamiliyoni anayi zinathera pafupifupi maola biliyoni imodzi m’ntchito ya kulalikira m’maiko 211, kuphatikizapo mu Ulaya Wakummaŵa. Kodi ndimbiri yabwino yotani imene akhala akulalikira? Mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu ndi chipulumutso mwa kukhulupirira Yesu Kristu. (2 Timoteo 1:9, 10) Umenewu ndiwo uthenga umene dzikoli likufuna tsopano—mapeto asanafike.—Mateyu 24:3, 14.

[Mawu a Chithunzi patsamba 24]

Yesu Akulalikira pa Nyanya ya Galileya, chojambulidwa ndi Gustave Doré

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena