Aids mu Afirika Chenjezo Kudzikoli!
“Ngati muli ndi chibwenzi chimodzi pachaka kwa zaka 6, chomwechonso zibwenzi zonse, mudzakhala kwenikweni mutaphatikizidwa m’zakugonana ndi anthu 45 000.” Kuŵerengera kosavuta kumeneku kochitidwa ndi Dr. K. E. Sapire, kogwidwa m’magazini a mu South Africa otchedwa Continuing Medical Education kukufotokoza mwafanizo kuthekera kwakukulu kwa kuyambukiridwa ndi AIDS kumene kulipo kwa anthu achiwerewere.
Kodi nkusumikiranji maganizo pa Afirika?
Chifukwa chakuti zimene zikuchitika kumeneko ziri chenjezo kudziko lonse. Afirika sindiwo malo okha kumene chiwerewere chiri chofala. Chiri chothetsa nzeru chadziko lonse. “Potsirizira pake,” akutero katswiri wa AIDS Dr. Dennis Sifris, “munthu aliyense wokangalika m’zakugonana m’dzikoli wokhala ndi ogonana nawo oposa mmodzi mothekera ali paupandu.” Mofananamo, malinga nkunena kwa magazini otchedwa U.S.News & World Report, mogwirizana ndi miyezo ya masiku ano ngakhale “ukwati suli chotsimikizirira kuti mukugonana ndi munthu mmodzi—kapena kukhulupirika kwa mnzanu wamuukwati—ndipo ndicho chifukwa chake palibe chotetezerera AIDS changwiro.”
Motero, pali zifukwa zabwino, kuti magazini otchedwa African Affairs akuchenjeza kuti: “Mliriwo ukafalikira kwina kulikonse.” Zisonyezero zonse nzakuti vuto la Afirika liri kale pamlingo wa kuchitikanso m’maiko ena ambiri a dziko.
Mwachitsanzo, magazini a Newsweek akusimba kuti mu Brazil, “ziŵerengero zowonjezereka za ogonana mwachibadwa zatenga AIDS kwa mabwenzi awo okhala nayo.” Unduna wazaumoyo wa dziko limenelo umayerekezera kuti theka la miliyoni linapimidwa kukhala ndi HIV. “Ngati sipachitidwa chirichonse,” akutero Dr. Carlos Alberto Morais de Sá, mtsogoleri wa kufufuzidwa kwa AIDS pa Chipatala cha Yunivesite ya Rio de Janeiro cha Gaffrée e Guinle, “tidzakhala ndi tsoka paumoyo wa anthu onse.”
United States akuwopsezedwanso. “Pamene kuli kwakuti chiŵerengero pakati pa ogonana mwachibadwa nchocheperapo pang’ono,” akusimba motero magazini a Time, “chinadumpha kuchoka pa 40 peresenti chaka chatha [1990], mofulumirirapo kwambiri koposa kagulu kena kalikonse.” Mlungu umodzi pambuyo pa kudziŵika kuti katswiri wamaseŵera othamanga wotchukayo Magic Johnson anali atagwidwa ndi AIDS kupyolera mwa kugonana mwachibadwa, matelefoni anachulukiridwa ndi mauthenga a anthu othedwa nzeru ofunafuna chidziŵitso chowonjezereka chonena za nthendayo.
Asia nayenso akupereka machenjezo ofananawo a tsoka loyandikira. Mbali imeneyo ya dziko yakhala ndi chiwonjezeko cha anthu opimidwa kukhala ndi HIV kuyambira pafupifupi popanda mmodzi mu 1988 kufikira kwa oposa miliyoni lerolino! “Milingo ya Afirika ya kuyambukiridwako idzawonekera kukhala yocheperapo poyerekezeredwa nayo,” akuneneratu motero Dr. Jim McDermott, popereka lipoti pambuyo pa ulendo wake wokafufuza ku Asia. Iye akuwonjezera kuti: “Ndiri wokhutira kuti Asia adzakhala malo okhala mikhole yochuluka koposa ya mliri wapadziko lonse wa Aids.”
Kuyesa kuimba mlandu wa magwero ndi kuwanda kwa AIDS pakontinenti imodzi iriyonse kapena anthu a mtundu wakutiwakuti nkosapindulitsa ndi kopanda pake. Dr. June Osborn, mkulu wa School of Public Health pa Yunivesite ya Michigan, U.S.A., ananena mosabisa mawu kuti: “Sinkhani yakuti ndiwe yani koma zimene umachita.”
Kodi AIDS idzapitirizabe kuwononga paliponse? Kodi pali choithetsera, kapena kodi potsirizira pake AIDS idzapululutsa anthu m’madera aakulu a kontinenti ya Afirika ndi mbali zina za dziko?
[Chithunzi patsamba 8]
Chithunzithunzi cha WHO cha H. Anenden; chikuto: chithunzithunzi cha NASA