Aids Kodi Idzatha Motani?
“NDIRI wokhutira kotheratu kuti tidzatulukiradi katemera wake mkati mwa zaka khumi zino.”—Jorg Eichberg, mkulu wa ofufuza katemela pa Wyeth-Ayerst Research Center, Philadelphia, U.S.A.
Tangoyerekezerani ngati mankhwala ochiritsira, kapena ngakhale katemera wotetezera AIDS anapezeka. Kukakhala kwabwino chotani nanga! Kwa akatswiri a AIDS 9,000 amene anasonkhana mu Florence, Italiya, chaka chathachi akumalankhula pansi pa mutu wakuti “Sayansi Ipereka Chitokoso pa AIDS,” mosakayikira kufunafuna njira yochiritsira kumeneko kunali kwakukulu m’maganizo mwawo.
Tsopano pamene kuyambukiridwa kwatsopano 9 mwa 10 kuchitika m’maiko amene akutukuka, chitsenderezo cha kupeza njira yothetsera chikupitirizabe. Komabe, mogwirizana ndi magaziniwo New Scientist, ambiri amene anali pamsonkhano wa ku Florence anawonekera kukhala “atatayikiridwa ndi lingaliro lawo la kufulumira.” “Mwinamwake,” magaziniwo akuperekera lingaliro motero, tsokalo nlalikulu kwambiri kwakuti ochuluka “anangonyalanyaza kuvutika ndi vutolo.”
Chenicheni chomvetsa chisoni nchakuti asayansi akuchulukiridwa ndi mafunso koposa mayankho. New Scientist ikufotokoza kuti “pambuyo pa zaka 10 tiri mkati mwa mliriwo, mavuto amene akuyang’anizana ndi akatswiri ofufuza kachirombo ka nthendayi ndi akatswiri a dongosolo lodzitetezera la thupi akuwonekera kukhala aakulu koposa kale.” Dokotala wina wa AIDS wa ku Britain Ian Weller anachenjeza kuti: “Mankhwala amphamvu otetezera kachirombo kameneka sadzapezeka mwamsanga.”
Koma ngati katemera wa AIDS anapezeka, kodi adzafika motani kwa anthu? Dr. Dennis Sifris, dokotala amene anadziwonera yekha mwa kugwira ntchito mu Afirika, akufotokoza kuti: “Tiri ndi mankhwala amphamvu kwambiri a TB [kholozi] chotero mwa mawu chabe TB ikanayenera kukhala itachotsedwa [chomwechonso] chikuku ndi Kutupa Chiwindi B. Komabe nthenda zitatu zimenezi ziri . . . zakupha zazikulu mu Afirika lerolino. Chotero ngakhale ngati mankhwalawo apezedwa kuwafikitsa kwa anthu ndiko vuto lalikulu.”
Pokhala ndi chiyembekezo chochepa cha kuchiritsa, njira yokha yotsala imene Afirika angachite ndiyo kukakamiza anthu kusintha khalidwe lawo la kudzisungira. Koma funso nlakuti—motani?
Mlingo Waung’ono wa Kulabadira
Kulabadira kochepa kuthetsa AIDS mu Afirika ndiko kugaŵira makondomu, makondomu ochuluka, ambirimbiri. Oyendetsa malole a akatundu amapatsidwa mwaulere pamalire a maiko. Oyendetsa manyuzipepala amawagaŵira m’mainivulopu. Makiliniki ndi ogwira ntchito m’zipatala ali nawo m’ziŵerengero zofikira mamiliyoni ambiri.
Pamene kuli kwakuti njira zimenezo zingakhale ndi mlingo wochepa wotetezera pakuwanditsidwa kwa AIDS, iwo ali ndi mavuto ake—makamaka mu Afirika. Wantchito ya chipatala wina Stefan van der Borght wa ku Medecins Sans Frontieres mu Angola anafotokoza kuti ngati mugaŵira makondomu mamiliyoni atatu, zimawonekera kukhala zabwino. Komatu zimenezo zimatanthauza kuti amuna miliyoni imodzi ndi theka okha ndiwo amene angakhale ndi unansi wa kugonana kaŵiri makondomuwo asanathe.
Ndiponso, kuwonjezera pa zovuta za kulinganiza kugaŵiridwa kwake, kodi ndichiyambukiro chotani chimene kugaŵiridwa kosasankha kwa makondomu kumeneku kuli nako pakhalidwe lachiwerewere—magwero enieni a AIDS mu Afirika? Zisonyezero zonse nzakuti kupereka makondomu kumasonkhezera machitachita a kugonana koposa kuwachepetsa. Ngakhale akuluakulu aboma akuyamba kuzindikira chenicheni chimenechi. Dziko lina mu Afirika lalamula kale madongosolo ake ofalitsira nkhani Aboma kuleka kulengezedwa kwa makondomu, popeza kuti amalimbikitsa khalidwe lachiwerewere. Mlembiyo Keith Edelston akuwonjezera pang’ono m’bukhu lake AIDS—Countdown to Doomsday kuti: “Polingalira za maupandu ake . . . amene tiri nawo chifukwa cha kugwiritsiridwa ntchito kwa makondomu, nkwachiwonekere kuti kukwatirana ndi munthu mmodzi ndiko njira yokha yotetezereka kotheratu.”
Koma kodi kubwereranso kukhalidwe la kukhala ndi munthu mmodzi m’kakonzedwe ka ukwati kuli chosankha chotsimikizirika?
Kutha kwa Aids
“Ngati anthu analeka uchiwerewere,” akutero Purofesala Reuben Sher, katswiri wa AIDS mu Afirika, “kachiromboko kakanasoloka. Anthu amene ali nako akanafa ndipo kumeneko kukanakhala kutha kwake.” Mofananamo, nkhani ina mu The Star, nyuzipepala yofalitsidwa mu Johannesburg, South Africa, ikuti “kwa munthu amene sali wachiwerewere kapena kubwerekana jakisoni wobayira chamba kapena kupatsidwa magazi, nkovuta kuti agwidwe ndi [HIV].”
Pakali pano, Mboni za Yehova zoposa 450,000 mu Afirika zikupeŵa zinthu zenizeni zimenezo. Izo zimakhulupirira mwamphamvu kuti kudzisungira kozikidwa pa Baibulo nkoyenera. Lingalirani za mmene amaganizirira: Popeza kuti Mlengi, Yehova Mulungu, anapanga anthu, pamenepo lamulo lake la makhalidwe a kudzisungira kwa anthu mwachibadwa nloyenerera kwambiri kulisamalira. Lamulo la makhalidwe abwino lolembedwa pa Ahebri 13:4 liri chitsanzo chabwino: “Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, pogona pakhale posadetsedwa.” Mmalo mwa kulingalira kukhala omanidwa chisangalalo, awo amene agwiritsira ntchito malemba otero adzitetezera kumavuto ochuluka akuthupi ndi a malingaliro.—Yerekezerani ndi Machitidwe 15:29; 2 Akorinto 7:1; Aefeso 5:3-5.
Mokondweretsa, kaŵirikaŵiri madongosolo ofalitsira nkhani asimba moyanja makhalidwe abwino a Mboni za Yehova mu Afirika kuti: “[Izo] zadzisonyeza . . . kukhala nzika zolemekezeka, zolongosoka zokhala mogwirizana ndi lamulo la makhalidwe abwino lapamwamba,” inatero Daily Telegraph ya London, Mangalande. Inawonjezeranso kuti: “Machitachita achiwerewere ndi mitala ofala pakati pa chitaganya cha anthu a mu Afirika ngosalingalirika konse pakati pa Mboni.” Mofananamo, mlembi wa bukhulo Contemporary Transformations of Religion, Bryan Wilson, akunena kuti “m’chitaganya cha mu Afirika, Mboni . . . zimakhala anthu apadera” ndi kuti “chiyambukiro cha . . . lamulo [lawo] la makhalidwe abwino nchachiwonekere pakati pawo.”
Zimenezi sizitanthauza kuti Mboni za Yehova nzotchinjirizidwa kotheratu kumatenda a AIDS. Ena agwidwa nayo kupyolera mwa anzawo a muukwati amene samamatira kumalamulo a makhalidwe abwino Achikristu ofananawo kwa amene iwo amamamatira, ndipo ena anatenga nthendayo asanakhale Mboni. Ndiponso, oŵerengeka asankha kubwereranso m’njira zosadzisungira za dziko lamakono, ndipo chiŵerengero chaching’ono cha ameneŵa chagwidwa ndi AIDS monga mbali ya chotulukapo cha njira zawo. (Agalatiya 6:7) Komabe awo amene modzifunira amalondola njira ya moyo wachisembwere atayikiridwanso ndi mwaŵi wawo wa kukhalabe mumpingo Wachikristu. (1 Akorinto 5:13; 6:9, 10) Koma chiŵerengero chachikulu kwambiri cha Mboni za Yehova zoposa mamiliyoni anayi kuzungulira dziko lonse chimasangala ndi thanzi labwino lakuthupi, la malingaliro, ndi lauzimu limene limadza chifukwa cha kumamatira kumalamulo a makhalidwe abwino a Mlengi akudzisungira.
Mwachimwemwe, Baibulo limasonyeza kuti mankhwala okhalitsa a miliri yonga AIDS ali pafupi. (Chivumbulutso 21:1-4) Yehova Mulungu akulonjeza dziko latsopano m’limene nakatande yense wa nthenda zachisembwere monga AIDS adzachotsedwa kotheratu. Sipadzakhalanso mikhole yovutika yosalakwa, popeza kuti aliyense adzalondola njira za moyo wathanzi labwino, zowongoka zimene zimachirikiza chimwemwe chenicheni.—Yesaya 11:9; 2 Petro 3:13.
[Mawu Otsindika patsamba 9]
“Sitifunikira kuthera mabiliyoni a ndalama kufufuzira mankhwala ndi kupangidwa kwake . . . Tifunikira kubwerera kumakhalidwe abwino a kudzisungira.”—Dr. Mark Hendricks, katswiri wa ku South Africa wa kudzitetezera kwa thupi la munthu
[Chithunzi patsamba 9]
Kukhala ndi mmodzi wokwatirana naye ndinjira yofunika yopeŵera mliri wa AIDS
[Chithunzi patsamba 10]
Mulungu akulonjeza dziko latsopano lopandiratu matenda onga AIDS