Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 9/8 tsamba 24-27
  • Ndinasunga Lonjezo Langa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndinasunga Lonjezo Langa
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kukumana Kwamwaŵi
  • Kusintha kwa Mikhalidwe
  • Ndipereka Lonjezo
  • Ndithandizidwa Kusunga Lonjezo Langa
  • Kuphunzitsa Ana Athu
  • Madalitso Aumwini
  • Khalani mu Gulu la Ana a Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Yehova Anadalitsa Kutsimikiza Mtima Kwanga
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Chidaliro Changa mwa Yehova Chinandichirikiza
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Yehova Akutichinjiriza Ife
    Nsanja ya Olonda—1987
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 9/8 tsamba 24-27

Ndinasunga Lonjezo Langa

NDINABADWIRA ku Rio de Janeiro paphwando la Carnival Sunday, mu 1930. Panali ziŵalo za gulu lapamwamba la mu Rio—madokotala, akuluakulu a asirikali, ndi eni mabizinesi achuma. Mwamwambo, onsewo anaponyera mphete zagolide ndi zadiamondi m’madzi anga osamba oyamba, akumakhulupirira kuti zimenezo zikathandiza mwana wamwamunayo kukhala wolemera ndi wotchuka. Patapita pafupifupi chaka chimodzi ndi theka, ndinalandira mfupo chifukwa chokhala mwana wokongola koposa m’Rio mumpikisano wochirikizidwa ndi magazini ena.

Mwamsanga pambuyo pake amayi anadwala kwambiri. Pamene madokotala anataya chiyembekezo cha kuchira kwawo, atate anasiya amayiwo ndi anafe. Atatewo anandigwiritsira ntchito monga malipiro othetsera ngongole, ndipo motero ndinayamba kukhala ndi banja lolemera ku Guarujá, pachilumba cha Santo Amaro, m’dera la São Paulo. Kumeneko ndinakula popanda kukumbukira banja langa loyamba. Komabe, patchuthi cha sukulu chomwe ndinakathera ku Rio de Janeiro—pafupifupi makilomitala 450 kuchokera kumene ndinkakhala ku Guarujá—kanthu kena kanachita kamene kanasintha moyo wanga.

Kukumana Kwamwaŵi

Ndinali kuseŵera ndi anyamata amsinkhu wanga m’chigawo cha Rio chotchedwa Jardim da Glória. Popeza kuti makolo anga ondilera ankandipatsa ndalama zochuluka, ndinali kugulira kagulu konse aisikirimu, choncho ndinali wotchuka. Mmodzi wa anyamatawo, Alberto, anandifunsa kumene ndinkachokera. Nditamuuza, anati: “Ndiri ndi mng’ono wanga amene nayenso amakhala kudera la São Paulo, koma sindinafike pakumdziŵa. Dzina lake ndi Cézar. Atate wanga anampereka kubanja lina kumeneko, ndipo tsopano amayi amalira masiku onse popeza sakuyembekezera kumuwonanso.”

Iye anawonjezera nati: “Ngati udzakumana ndi mnyamata wazaka zakubadwa pafupifupi 10 ku São Paulo wotchedwa Cézar, ukamuuze kuti unakumana ndi mchimwene wake ndi kuti amayi ake afuna kumuwona.”

“Sindidzaiŵala zimenezo,” ndinalonjeza motero. “Ndiiko komwe, iye ndimnzanga wa dzina.”

Kusintha kwa Mikhalidwe

Alberto anauza amayi ake za kukambitsirana kwathu, ndipo iwo anafuna kuwonana nane. Pamene Alberto ndi ine tinakumananso ku Jardim da Glória pa Sabata lotsatira, iye anati: “Amayi afuna kuwonana nawe. Ndiganiza afuna kukutumiza uthenga kwa mng’ono wanga ku São Paulo.”

Mosataya nthaŵi Alberto ananditengera kwa amayi ake, amene analikhale pabenchi m’paki. Iwo anandiyang’anitsitsa. Ndiyeno anandikupatira nayamba kulira. “Kodi makolo ako ndani?” anafunsa motero.

“Garibaldi Benzi ndi Nair,” ndinayankha motero. “Ndipo dzina langa ndi Cézar Benzi.”

Iwo anapempha kukumana ndi amayi, amene anatsala pang’ono kukomoka nditawauza zimene zinachitika. Pambuyo pake anakubala aŵiriwo anakumana nalankhula za ine kwanthaŵi yaitali. Zimenezo zitatha Alberto anati kwa ine: “Amayi anga ndiwo amayi ako enieni, ndipo ndiwe mphwanga!”

Amayi anali atachira nthenda yawo ndipo, mwa iwo okha, anali kulera mchimwene wanga wamkulu ndi mchemwali. Nditatsimikizira kuti ndapezadi banja langa lenileni, ndinapempha kukhala nalo, zimene zinagwiritsa mwala kwambiri amayi ondilera. Komabe, ndinafunitsitsa kukhala ndi mchimwene ndi mchemwali wanga. Ndinamveranso chisoni amayi, amene anavutika, chifukwa chosadziŵa ngati ndinali wakufa kapena wamoyo. Choncho ndinachirimika pachosankha changa ngakhale kuti chinatanthauza kusiya nyumba yamataya ku Guarujá kupita kunyumba ya m’chigawo chosauka cha Rio de Janeiro. Kunali kusintha kotani nanga! Tsopano ndinafunikira kupita ndi kukagwira ntchito zolimba nditaweruka kusukulu, chifukwa banja langa linadalira malipiro anga kuti lipeze zofunika zamoyo.

Ndipereka Lonjezo

Nditakula, ndinaphunzira kupanga ndipo, pambuyo pake, kulinganiza majuwelo. Gulu lomwe ndinagwira nalo ntchito linkagulitsanso zinthu zoitanitsidwa kunja—zimene zambiri za izo zinali katundu wosaloledwa—amene anabweretsadi ndalama. Chifukwa cha ndalama zosavuta kupeza, ndinayamba kupita kumapate, kwa asungwana, ndi michezo. Ndiyeno, pamene ndinali ndi zaka 22, ndinakwatira Dalva, tsamwali langa kuyambira kusukulu. Ine kwenikweni sindinamuyenerere. Anali mkazi ndi nakubala wabwino, wophunzira, waulemu, ndi wodzisungira bwino mwamakhalidwe.

Usiku wina, pambuyo pokwatirana kwa zaka zisanu ndi ziŵiri, ndinali kupita kunyumba kuchokera ku phwando lina lopambanitsa pamene ndinayamba kulingalira mwamphamvu. Ndinalingalira kuti ndi moyo umene ndinali nawo, sindikakhoza kuphunzitsa ana athu atatu omakula makhalidwe abwino. Choncho ndinasankha kusintha. Nditafika panyumba, ndinadzutsa Dalva kuti ndimuuze chosankha changa.

“Kodi undiuza kuti wandidzutsa m’maŵamaŵa muno pa 2 koloko kuti undiuze zachabechabe zimenezo?” Iye anali ndi zifukwa zambiri zosandikhulupiririra. Koma ndinalonjeza kuti: “Tsopano ndikunena zenizeni. Ndipo choyamba, ndidzasamutsira shopu yanga pafupi ndi nyumba yathu kotero kuti tikhale ndi nthaŵi yochuluka monga banja.” Tinagona Dalva akukaikirabe.

Tsiku lotsatira ndinapeza nyumba ya zipinda ziŵiri zosanja ndi kupanga mapulani akuika nyumba yathu pachipinda cha pamwamba ndi shopu yanga chapansi. Ndiyeno ndinapita kwa mabwenzi anga akale ndi kuwatsazika. Ndinatsimikizira kusunga lonjezo langa. Kwanthaŵi yoyamba, Dalva ndi ine tinayamba kusangalala ndi moyo pamodzi ndi ana athu.

Ndithandizidwa Kusunga Lonjezo Langa

Patapita pafupifupi miyezi itatu, Fabiano Lisowski anandichezera. Iye anandidziŵa kwa nthaŵi yaitali. Chotero pamene ndinati ndifuna kuti iye awone mkazi wanga, anati: “Mkazi wako walamulo kodi?”

Ataloŵa Dalva, ndinadziŵikitsa mwamunayo kwa iye monga “wansembe wa chipembedzo china cha Baibulo.” Mwamunayo anaseka nafotokoza kuti anali mmodzi wa Mboni za Yehova. Sindinafune chipembedzo, koma Dalva anakonda Baibulo. Iyeyo ndi Dalva anayamba kulankhula, koma ine ndinakhala chete, pakuti sindinazindikire chirichonse chomwe anali kulankhula.

Fabiano anatiitanira kumsonkhano pa Sabata lotsatira. Iye anadabwa nditalonjeza kupita. Dalva anakondwera kwambiri. Anadziŵa kuti ndinali mwamuna wosunga malonjezo ndi kuti ngati ndanena kuti ndidzamka kumsonkhano, iye akayembekezera zimenezo. Ndaphunzira zinthu ziŵiri m’malonda a katundu wosaloledwa: Unasunga lonjezo lako ndipo sunachedwepo kupangano.

Nthaŵi zonse ndinkanyamula kamfuti palamba langa, koma popita kumsonkhano, ndinasiya mfutiyo kunyumba. Anthu anali aubwenzi ndi odzisungira bwino mwamakhalidwe, choncho ndinalonjeza kupitanso pa Sabata lotsatira. Kuyambira pompo mpaka leroli tafika pamisonkhano mokhazikika pa Nyumba Yaufumu, ndipo sindinanyamulenso mfuti yanga.

Fabiano analinganiza kudzatichezetsa Lachitatu lirilonse madzulo, pamodzi ndi mkazi wake ndi apongozi. Pokhala wodziŵa kuti ndinali wosakhulupirira kukhalako kwa Mulungu, iye analankhula kwakukulukulu ndi Dalva. Podzimva wonyalanyazidwa, ndinayamba kulankhula naye zinthu zina, ndipo mwaulemu anayamba kupereka chisamaliro chachikulu kwa ine. Ndinawona kuti anali ndi bukhu la “Mulungu Akhale Wowona,” koma anali kuzengereza kundipatsa. Potsirizira, ndinafunsa kuti: “Kodi bukhulo nlanji?”

Modabwa, iye anayankha nati: “Nlophunzira.”

“Ngati nlophunzira,” ndinayankha tero, “tandipatsani ndiwone zimene limanena.”

Aliyense anadabwa ndipo sanadziŵe konse zimene zikatsatira. Komabe, phunziro linayambika, ndipo ndinamvetsera mosamalitsa. Dalva anakondwera, ndipo ngakhale ana atatuwo anakonda malongosoledwe a Fabiano.

Paphunziropo, mkazi wa Fabiano anawona kuti ndinali kusuta mosalekeza, ndipo anati: “Inu mumasuta kwambiri.”

“Ndakhala ndikusuta kuyambira pasukulu,” ndinafotokoza motero. “Ndipo popenda malinganizidwe a majuwelo, ndimasuta mosalekeza.”

Mwaluso, anati: “Anthu ambiri amayesa kusiya kusuta koma samasiya.”

“Ndingasiye panthaŵi iriyonse imene ndifuna,” ndinayankha mwa nchinyulira.

“Nzimene muganiza zimenezo,” anayankha motero.

“Kokha kuti ndikusonyezeni, ndikusiya leroli,” ndinamuuza tero. Ndinaterodi, ndipo sindinasuteponso chiyambire.

M’miyezi yoŵerengeka yoyambirira ya phunziro lathu, zinthu zinali zovuta. Mabwenzi anga akale anabwera kwa ine ndi kundisonyeza mapulani a bizinesi yosayenera, ndipo akazi amene ndinkapita nawo kumapate anabwera kunyumba kudzandifunafuna. Koma ndinali wotsimikiza kusintha moyo wanga, ndipo mwa kukoma mtima kwapadera kwa Yehova, ndinakhoza kutero. Bizinesi yanga inagwa poyamba, ndipo tinasintha kakhalidwe kathu. Koma mwachimwemwe, Dalva anali magwero osatha a chilimbikitso.

Titaphunzira Baibulo kwa miyezi isanu, zikaikiro zanga zonse zinatha. Ndinatsimikizira kuti Yehova ndiye Mulungu wowona ndi kuti Baibulo ndilo Mawu ake olembedwa. Chotero pa January 12, 1962, Dalva ndi ine tinali pakati pa anthu 1,269 obatizidwa pamsonkhano waukulu woyamba ku São Paulo, wochitidwira mu Ibirapuera Park. Kunali kodabwitsa chotani nanga kuwona anthu ofikapo pafupifupi 48,000!

Kuphunzitsa Ana Athu

Msonkhanowo unathandizira kukhomereza mwa ine thayo la kulangiza ndi kuphunzitsa ana athu. Chotero mosataya nthaŵi tinalinganiza phunziro la Baibulo labanja pa Lachitatu usiku. Ngakhale leroli, Lachitatu likupitirizabe kukhala usiku wathu wa phunziro labanja. Komabe, Dalva ndi ine timaphunzira tokha tsopano, pakuti ana onse ngokwatira.

Phunziro lathu ndi ana linaphatikizapo kukambitsirana mavuto ofala kwa achichepere m’tsiku lathu, onga ngati masitayelo a kavalidwe ndi kapesedwe ndi kudzisungira kwabwino kwa anyamata ndi asungwana. Ndiponso, ngati mmodzi wa ana anali ndi nkhani m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki, ikayesezedwa pa Lachitatu usiku.

Ndiponso, tinasonyeza anawo kukongola kwa chilengedwe cha Yehova mwa kuwatengera kumalo owonetsera zinyama ndi malo ena. Tinali kuwathandiza kuzindikira kuti zinyama ndi mbalame zinalengedwa ndi Yehova kuti zikondweretse munthu ndi kuti posachedwapa tidzasangalala kuziwona, osati m’zikwere kapena m’makola azitsulo, koma pabwalo, pamene zidzasisitidwa ndi kuyangatidwa.

Pamene anawo anali aang’ono kwambiri, tinamamatiza m’likole lathu programu ya kuŵerenga magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndi mabukhu ena a Watch Tower Society. Onse anachita zomwe anatha kutsatira programuyo kuti akatiuze zimene anaphunzira. Tinganenedi kuti kulangiza ana athu mwanjirayi kunatidzetsera mfupo yaikulu. Aliyense wa ana atatuwo anabatizidwa asanakule kwambiri.

Cézar, mwana wathu wamng’ono koposa, anali woyamba kusonyeza chikhumbo cha uminisitala wanthaŵi yonse. Pamene anali ndi zaka zisanu ndi zinayi, anaitanidwa kupulatifomu ndi woyang’anira woyendayenda popanda kuuzidwa pasadakhale, nafunsidwa amene anafuna kukhala atakula. “Chiŵalo cha Beteli, woyang’anira dera, kapena mmishonale,” anayankha motero Cézar.

Pausinkhu wazaka 17, Cézar anakhala minisitala waupaniya wanthaŵi yonse. M’nthaŵi yonseyo anayamba kosi ya kusindikiza, mwakutero kukonzekera kukagwira ntchito paofesi ya nthambi ya Watch Tower Society m’Brazil. Mwamsanga pambuyo pake anaitanidwa ku Beteli, ndipo anatumikira konko kwa zaka zinayi. Ndiyeno anakwatira, ndipo iye ndi mkazi wake anakhala apainiya apadera; anapitirizabe kutero mpaka pamene mwana wawo wamwamuna anabadwa. Tsopano Cézar akutumikira monga mkulu Wachikristu, ndipo mkazi wake ndimpainiya wokhazikika. Mwana wawo anabatizidwa mu 1990, pamene anali ndi zaka zakubadwa 11.

Sandra, mmodzi wa asungwana athu, anayamba utumiki waupainiya mu 1981. Chaka chotsatira anakwatidwa kwa Sílvio Chagas, chiŵalo cha banja la Beteli. Iwo anatumikira pamodzi kwa zaka zisanu ndi zitatu monga apainiya apadera ndipo tsopano ali m’ntchito ya dera, kuchezetsa mipingo ya Mboni za Yehova. Mchemwali wake wamapasa wa Sandra, Solange, ndi mwamuna wake anatumikira kwa zaka zitatu monga apainiya apadera. Mwana wawo wamwamuna, Hornan, anabatizidwa posachedwapa. Mwamuna wa Solange ndimkulu Wachikristu.

Dalva ndi ine tikhulupirira kuti kukula kwauzimu kwa ana athu kunachititsidwa kwakukulukulu ndi phunziro lathu labanja lokhazikika pa Lachitatu usiku, limene linayamba pafupifupi zaka 30 zapitazo. China chimene chinathandizira kuwalera chinali kuitanira kunyumba kwathu nthaŵi zonse oyang’anira oyendayenda ndi aminisitala ena anthaŵi yonse. Abale ndi alongo Achikristu ameneŵa anathandiza anawo kukulitsa chonulirapo cha uminisitala wanthaŵi yonse.

Madalitso Aumwini

Dalva ndi ine tapambana m’zochitika zambiri zosintha miyoyo yathu chiyambire chochitika chachikulu mu 1962, pamene tinabatizidwa. Panthaŵi ina ndinatumikira monga woyang’anira dera wogwirira malo, ndipo tinali ndi mwaŵi wa kuchezetsa mipingo ya Mboni za Yehova. Ndinakhalanso ndi phande m’ntchito yomanga Nyumba yathu Yamsonkhano ku Duque de Caxias, ntchito imene inatenga zaka zisanu. Ndipo kaŵirikaŵiri ndapita kwa akuluakulu a boma, zipatala, ndi asirikali, kuphatikizapo wachiŵiri kwa bwanamkubwa wa deralo. Chifuno chopitira kwa ameneŵa chinali kukapempha masitediyamu ochitira misonkhano yathu ndi kukafotokoza kaimidwe kathu ka uchete, limodzi ndi chifukwa chimene Mboni za Yehova sizimavomerezera kuthiridwa mwazi.

Ndikayang’ana m’mbuyo ndi kulingalira madalitso onse odabwitsa amene ndalandira kuyambira pa usiku wapadera uja umene ndinadzutsapo Dalva kumuuza za lonjezo langa, ndinganenedi mowona mtima kuti dalitso lalikulu loposa onse ndilo kukhala wofalitsa mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu. Dalva ndi ine tiri otsimikiza kuti njira imene Yehova Mulungu akutitsogolera nayo kupyolera m’gulu lake iridi “Njirayo” yotsogolera kumoyo wachimwemwe tsopano lino ndi potsirizira kumoyo wamuyaya m’dziko latsopano la Mulungu. (Machitidwe 9:2; 19:9)—Monga momwe yasimbidwira ndi Cézar A. Guimarães.

[Chithunzi patsamba 27]

Cézar Guimarães ndi banja lake lerolino

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena