Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 10/8 tsamba 22
  • Sali Zotaidwa Wamba!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Sali Zotaidwa Wamba!
  • Galamukani!—1992
  • Nkhani Yofanana
  • Mafuta—Kodi Timawapeza Bwanji?
    Galamukani!—2003
  • Mafuta—Kodi Ndi Dalitso Komanso Tsoka?
    Galamukani!—2003
  • Mafuta—Mmene Amakukhudzirani
    Galamukani!—2003
  • Mafuta a Golide a ku Mediterranean
    Galamukani!—2008
Galamukani!—1992
g92 10/8 tsamba 22

Sali Zotaidwa Wamba!

PA LACHISANU, March 24, 1989, chombo chapamadzi chamafuta chotchedwa Exxon Valdez chinagunda mwala ku Prince William Sound mu Alaska. Monga chotulukapo, malitala okwanira 42 miliyoni a mafuta osayenga anatayikira m’madzi. Ngoziyo inadodometsa ntchito ya asodzi akumaloko, kuipitsa madzi ndi nthaka m’mphepete mwa gombe makilomitala ambiri, ndi kupha mazanamazana a mbalame ndi nyama zam’madzi.

Ngozi ya chombo cha Exxon Valdez ikupitiriza kudetsa nkhaŵa anthu osamalira malo adziko. Komabe, “kutayikira kwamafuta” kosazindikirika kwambiri kukuchitika tsiku ndi tsiku. Ndipo mwachiwonekere iko kukuchitika kumene mumakhala kwenikweniko!

Malinga ndi magazini akuti Consumer Reports, anthu amene amadzisinthira okha mafuta mu injini ya galimoto amataya mafuta otha ntchito pakati pamalitala 750 miliyoni ndi 1.5 ya mamiliyoni chikwi chimodzi chaka chirichonse. Malipoti amati, “10 peresenti kufika ku 14 peresenti yokha ya mafutawo ndiyo imatayidwa moyenera.” Peresenti yaing’ono yamafuta otha ntchito imeneyi imagwiritsidwanso ntchito, mwakupangira zinthu zina zothandiza. Koma kodi nchiyani chimachitika kwa mafuta ena onsewo? Mwachiwonekere, anthu amagalimoto amangowataya monga zotayidwa wamba.

Chaka chirichonse malitala mamiliyoni ambirimbiri amafuta otha ntchito amaloŵa m’nthaka, m’mifuleni, kapena m’madzi otayamo zonyansa. Pakafunikira kuŵirikiza mafuta otayikira pangozi ya Exxon Valdez kwanthaŵi 25 kuti tipeze mafuta ochuluka motero! Koma mafuta ogwiritsiridwa kale ntchito, limodzinso ndi zinthu zina zotayika kugalimoto, zonga ngati madzi a m’galimoto otchedwa antifreeze, brake fluid, ndi mafuta otchedwa transmission oil, sindizo zotayidwa wamba. Nzoipitsitsa.

Consumer Reports imanena kuti ngati mafutawo aloŵa “m’madzi akumwa, pangakhale zotulukapo zowopsa: [Litala] imodzi ya mafuta ogwiritsiridwa kale ntchito ikhoza kuipitsa mamiliyoni ambirimbiri [amalitala] amadzi akumwa ndi kukhala osayeneranso kumwedwa, ndipo [0.5 l] yokha ya mafuta ikhoza kupanga muyalo wa [0.4 ha] pamwamba pamadzi.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena