Mmene Ena Aphunzirira Kulaka Kupsinjika Mtima
NTHAŴI zina aliyense amapsinjika mtima. Chifukwa cha mavuto aakulu, onga matenda owopsa, ukalamba, kapena imfa ya okondedwa, ena angakhale opsinjika mtima kwambiri kotero kuti moyo wawo ungayambukiridwe moipa.
Komabe, ngakhale pakati pa anthu opsinjika mtima kwambiri, pali awo amene aphunzira kulamulira kukhudzidwa mtima kwawo kotero kuti angapitirize mwachipambano ndi zochita zawo za tsiku ndi tsiku. Otsatirawa ali zitsanzo za oterowo, amene anafunsidwa ndi mtola nkhani wa magazini a Galamukani!
Janis amalandira mankhwala a nthenda imene imayambukira mkhalidwe wa mtima wake. Komabe, iye ananena kuti: “Ndinapeza kuti njira yothandiza yochitira ndi vutolo ndiyo kulamulira malingaliro anga. Ndimachita zimenezi mwakuchitira ena zinthu, zonga kupanga makeke ndi kusoka. Ndiponso ndimayesayesa zolimba kusumika maganizo anga pazikumbukiro zabwino ndi zochitika zamtsogolo zimene ndimayembekezera. Chifukwa cha nthenda yanga, zonsezi nzovuta. Nthaŵi zina kungakhale kosavuta kugonja ndi kuipidwa. Koma zotulukapo zabwino zimafunikira kuyesayesako.”
Pambuyo pa ukwati wazaka 45, mwamuna wa Ethel anamwalira. Ngakhale kuti akali wachisoni, Ethel amalamuliradi mkhalidwe wa mtima wake. Iye analongosola kuti: “Ndimadzitanganitsa ndi kuchitira ena zinthu. Mwachitsanzo, ndimakonda kuphunzitsa ena zifuno za Mulungu zopezeka m’Baibulo. Mkazi wina wachichepere anakondweretsedwa kwambiri ndi zinthu zabwino zimene anali kuphunzira kotero kuti chiyamikiro chake chinandithandiza kukhala wachimwemwe kwambiri. Pamene ndisumika maganizo pazinthu zabwino za m’Baibulo zophunzitsa ena, kumandithandiza kuchotsa malingaliro akuipidwa m’maganizo mwanga. Ndiponso, asungwana amabwera kwa ine kuti ndiwathandize pamavuto awo osiyanasiyana, ndipo kulankhula zinthu zabwino zimene angachite m’moyo wawo kumandithandizanso kulaka kupsinjika mtima.”
Kwazaka zambiri Arthur anali ndi moyo wotanganidwa ndi wokangalika. Ndiyeno, chifukwa cha matenda aakulu, anasiya ntchito namachitira zinthu zonse panyumba. Kwa miyezi yambiri Arthur anadzimva kukhala wopanda pake ndi wochita tondovi. Kodi ndimotani mmene anachitira ndi mikhalidwe imeneyi yopsinja mtima? “Ndinasiya kuumirira pazinthu zimene sindingachitenso. Mmalo mwake, ndinasumika maganizo pazimene ndingachite kuthandiza anthu ena kuwongokera ndi kuwalimbikitsa pamene achita tondovi. Pokhala wobindikiritsidwa panyumba panga, ndimagwiritsira ntchito foni kwambiri. Pamene ndinakhala wotanganidwa kuthandiza ndi kulimbikitsa ena, ndinalibe nthaŵi yochuluka yakudzimvera chisoni.”
Pambuyo pa masoka otsatizanatsatizana, kuphatikizapo imfa ya mwamuna wake, Nita mwachiwonekere anachita chisoni ndi tondovi kwambiri. Mkupita kwa nthaŵi, anaphunzira kulamulira mikhalidwe imeneyo yopsinja mtima akumati: “Pamene ndichita chisoni, ndimafuna njira yothandiza yochokera mumkhalidwewo. Ndimadzikakamiza kukawongola miyendo, kulizira foni bwenzi lokoma mtima, kumvetsera nyimbo, kapena kuchita kalikonse kamene, malinga ndi zokumana nazo zakale, ndidziŵa kuti kadzachepetsa tondovi. Ndimadzichitira mokoma mtima monga momwe ndingachitire kwa bwenzi labwino.”
Mary wakhala ndi matenda aakulu kwa zaka 32. Pokhala wobindikiritsidwa pampando wamagudumu, iye amachoka panyumba popita kukawonana ndi dokotala basi. Kodi ndimotani mmene Mary amapeŵera kugonjetsedwa ndi kukhwethemulidwa? Iye anafotokoza kuti: “Mwamuna wanga wandichirikiza kwambiri. Ndiponso, ndimaŵerenga nkhani zomangirira kaŵirikaŵiri. Ndimalizira foni mabwenzi anga nthaŵi zonse, ndipo kaŵirikaŵiri ndimayamba kuwaitanira kunyumba kwanga. Ndimakondwa kucheza nawo ndipo sindimagwiritsira ntchito nthaŵi zimenezo kudandaula kapena kudzimvera chifundo. Sindimatayira nthaŵi kusinkhasinkha zinthu zopsinja mtima m’moyo wanga chifukwa ndiri ndi zinthu zambiri zokondweretsa zomwe ndimapeza bwino.”
Margaret mwachibadwa amatenga zinthu monga momwe ziliri. “Pamene ndipsinjika mtima,” iye anatero, “ndimafuna kuyanjana ndi munthu amene amatenga zinthu monga momwe ziliri—osati wotengeka maganizo—koma amene amandidziŵa bwino lomwe ndi amene adzandikumbutsa za zipambano zanga ndi kundilimbikitsa.”
Rose Marie anachitidwa maopaleshoni aakulu asanu pazaka zingapo, ndipo iye ndi mwamuna wake afedwa anthu asanu ndi aŵiri m’banja lawo m’nyengo yaposachedwapa pachaka chimodzi ndi theka. Ndithudi, kukula kwa vutoli kunachititsa kupsinjika mtima. Komabe, iwo sanaumirire kusinkhasinkha zinthu zimenezo. Pokhala Mboni za Yehova, iwo amachirikizidwa ndi chiyembekezo chotonthoza ndi chosangalatsa chimene Baibulo limapereka cha dziko latsopano lolungama limene liri pafupi m’mene Mulungu “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.” Ngakhale akufa adzaukitsidwa, monga momwe Yesu ananenera, “ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu [a Mwana wa Mulungu], nadzatulukira.”—Chivumbulutso 21:4; Yohane 5:28, 29.
[Chithunzi patsamba 9]
Janis amalamulira kukhudzidwa kwa mtima wake mwakuchitira ena zinthu, kusinkhasinkha zikumbukiro zosangalatsa, ndi kuyembekezera zochitika za mtsogolo