Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 11/8 tsamba 25-26
  • Chikhulupiriro cha Wyndham—Mmene Chayambukirira Ena

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chikhulupiriro cha Wyndham—Mmene Chayambukirira Ena
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chiyambukiro pa Achichepere Anzake
  • Yolimbikitsa Chikhulupiriro kwa Onse
  • Yehova Anandithandiza Kum’peza
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Kodi Umenewu Ndi Mtengodi?
    Galamukani!—2008
  • Chivomerezo cha Oŵerenga Bukhu la Young People Ask
    Galamukani!—1990
  • “Tiwonjezereni Chikhulupiriro”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 11/8 tsamba 25-26

Chikhulupiriro cha Wyndham—Mmene Chayambukirira Ena

MAGAZINI a Galamukani! a August 22, 1991, (Chingelezi), anafalitsa nkhani yonena za kukhulupirika kwa Wyndham Cook kulamulo la Mulungu limene limalamula Akristu kusala mwazi. (Machitidwe 15:20; 21:25) Wyndham anali ndi mitsempha yotupa ku mmero kwake, ndipo anali mumkhalidwe wakuchucha mwazi kosalalamulirika pang’ono. Nkhaniyo inachitira lipoti kuti anapulumuka zochitika zingapo zakuchucha magazi, panthaŵi imodzi mlingo wa magazi ake a hemoglobin unatsika kusafikira 2. Mwachisoni, pamene kope lotchulidwa pamwambapali linali kupita kukasindikizidwa, Wyndham anamwalira pambuyo pachochitika china cha kuchucha mwazi.

Chiyambukiro pa Achichepere Anzake

Achichepere ambiri mu United States analembera afalitsi a Galamukani! akumasonyeza chiyamikiro kaamba ka nkhaniyo ndi kufotokoza chiyambukiro chimene inali nacho pa iwo. Wina wa ku Clinton, Iowa, anati: “Pamene ndinawerenga mmene mnyamata wa zaka 15 zakubadwa ameneyu anaimiririra nji pamaso pa madokotala ndi kufotokoza moleza mtima kwa iwo chifukwa chake anakana mwazi, zinandichititsa kupenda chikhulupiriro changa ndi kudzifunsa zimene ndikanachita. Chikhulupiriro cha Wyndham ndi chipiriro zinandipangitsa kukhala wotsimikiza koposerapo kuposa ndi kale lonse kuti ngati ndinakhala mumkhalidwe wakayakaya, ndikanatenga kaimidwe kamene anatenga.”

Kalata yochokera kwa msungwana wa zaka 15 zakubadwa wa ku Maiden, North Carolina, inati: “Pambuyo pa kuwerenga kuvutika kwa Wyndham ndi kudalira kwake pa Yehova kufikira ngakhale imfa, ndinalira. Ndinadzifunsa funso lofufuza maganizo lakutilo, ‘Kodi ine nditakhala m’mikhalidwe yotere ndikaika moyo wanga m’manja mwa Mulungu ndi kuika chidaliro chotheratu mwa iye chakundikumbukira?’

“Ndawerenga mobwerezabwereza nkhaniyo nthaŵi zambiri, ndipo ndikulinganiza kuipendanso nthaŵi iriyonse imene ndimva chisoni chochititsidwa ndi dziko lotsendereza. Chikhulupiriro cha Wyndham chimapereka chilimbikitso. Ndikuyang’anira mtsogolo kukukomana naye m’dziko latsopano lolonjezedwa la Yehova.”

Wachichepere wina, wa ku Mzinda wa New York, analemba kuti: “Kaŵirikaŵiri ndimadziyerekezera kukhala mumkhalidwe wofanana ndi wa Wyndham Cook ndipo ndimadabwa zimene ndikananena ngati dokotala wanga anandiuza kuti ndikafa ngati sindinavomereze kuthiriridwa mwazi. Ine nthaŵi zonse ndimadzazidwa ndi kulimba mtima ndi kulimbikitsidwa mwa zitsanzo zamphamvu, zonga cha Wyndham, kuti ndichite changu mu utumiki kwa Yehova.”

Wachichepere wa ku Kent, Washington, anafotokoza kuti: “Ndinatenga magazini anga kuchokera ku positi ofesi dzuloli ndipo ndinaawerenga ndisanabwerere kunyumba. Ndinaitana mabwenzi ambiri amumpingo kuwalimbikitsa kuwerenga nkhaniyo. Pamenepo madzulo amenewo tinaiphunzira m’phunziro lathu labanja.” Akumatchula chiyambukiro chimene nkhaniyo inali nacho pa iye, msungwanayo anati: “Sikokha kuti inatsimikizira kukhala yochichiza ndi yolimbikitsa chikhulupiriro koma inandipangitsa, kudzifunsa ngati ndikakhoza kuima nji pa chiyeso chotero pa msinkhu wa 17.”

Wachichepere wina wa ku North Berwick, Maine, analemba kuti: “Ndinali wokhoza kumvetsetsa chochitika cha Wyndham chifukwa chakuti nanenso ndiri ndi zaka 15 zakubadwa. Sindingathe kunena mmene chipiriro chake ndi kulimba mtima zandisonkhezerera kuchita changu mu utumiki wa Yehova. Ngati iye anakhoza kuchita zambiri zotero kukondweretsa Mulungu ngakhale pamene anali mumkhalidwe wake wofooka, pamenepo kodi ine ndiri ndi chifukwa chotani chakulekera kuchita changu?

“Nditatha kuwerenga nkhani yolimbikitsayo, maso anga anadzala misozi ndinamva ngati kuti ndinadziŵana ndi Wyndham moyo wanga wonse. Bwenzi ndikanatero. Pamenepo ndinayang’ana pa chithunzithunzi chake ndi makolo ake ndipo ndinalingalira za mmene mwamsanga ndikawoneranso kumwetulira kwake kokongolako pambuyo pa chiukiriro pamene sakafunikiranso kuvutika.”

Wazaka 15 zakubadwa wina anafuna kuuza makolo a Wyndham mmene anayambukiridwira ndi nkhaniyo. Iye analemba kuti: “Kulimba mtima kwa Wyndham kunandithandiza kuwona kuti ndifunikira kukhala wokonzekera kuima nji kaamba ka zikhulupiriro zanga. Panthaŵi iriyonse ndikakhoza kukhala mumkhalidwe wofananawo. Ndikakonda kuti ngati nthaŵi yotero ikafika pamene ndikafunikira kutenga kaimidweko, ndidzakhala wolimba mtima ndi wotsimikiza monga momwe analiri Wyndham potsatira zimene Baibulo limanena.

“Sindinadziŵane konse ndi Wyndham, kumene mwa iko kokha kulidi kutaikiridwa, koma ndikuyang’anira mtsogolo kukumdziŵa pamene dziko latsopano lidzadza. Nkhani yake yandisonkhezera kuchita zonse zimene ndingathe mu utumiki wa Yehova ndi kuzichita kufikira mapeto.”

Yolimbikitsa Chikhulupiriro kwa Onse

Kholo lina la ku Newark, New Jersey, linafotokoza kuti: “Ndakhala mmodzi wa Mboni za Yehova kwa zaka 22 koma ndinafika pa misonkhano nthaŵiyo isanafike. Ndakhala ndikuwerenga magazini anga onse mokhazikika, koma sindinayambe ndawerenga nkhani imene inali yosonkhezera maganizo kwambiri ndi yolimbikitsa kuposa ya Wyndham Cook.

“Tsopano ndingathe kokha kupitirizabe kukwaniritsa ntchito yanga yoperekedwa ndi Mulungu monga kholo mwakuthandiza mwana wanga wamkazi wa zaka khumi kuima nji ndi kutetezera chikhulupiriro monga momwe anachitira Wyndham. Kaya ikhale nkhani ya mwazi, ya anamgoneka, kugonana, kapena machenjera aliwonse amene Satana amabweretsa pa ife tonse, makamaka achichepere athu, tiyenera kupitirizabe kuchirimika mwakulimbikitsa chikhulupiriro chathu.”

Mboni ina ya ku Cadiz, Kentucky, inatulutsa malingaliro ofananawo, ikumalemba kuti: “Imeneyi iri imodzi yankhani zosonkhezera maganizo koposa zimene ndawerenga. Wyndham anali chitsanzo chabwino koposa kwa achichepere onse chakuchitsatira. Ndinalira pamene ndinali kuwerenga zimene Mboni yabwino yachichepere imeneyi inakumana nazo. Ndinazindikira mmene tonsefe, achichepere ndi achikulire omwe, tiyenera kutsatirira kaimidwe kake kolimba mtima. Chitsanzo cha Wyndham chandipangitsa kudzipenda. Chinandipangitsa kuyesadi mwamphamvupo kugwirira ntchito Yehova mwaumoyo wonse, ndikumayesayesa nthaŵi zonse kupereka chitsanzo chabwino, mofanana ndi Wyndham, kuyeretsa dzina la Yehova.”

Mboni ina ya ku Palm Springs, California, inalemba kuti: “Nkhaniyi inakhudzadi mtima wanga. Ndiri ndi ana asanu, ndipo ndikhulupirira ndipo ndipemphera kuti ngati kukachitika kuti ayang’anizane ndi vuto lamtundu umenewu, akakhala ndi nyonga yachikhulupiriro imene Wyndham anali nayo. . . . Wyndham ali chitsanzo chabwino kwambiri kwa achichepere athu.”

Chikhulupiriro chowona ndicho chiyembekezo chotsimikiziridwa cha zinthu zoyembekezeredwa ngakhale kuti munthuwe sunaziwone kapena kukomana ndi zinthu zimenezi. (Ahebri 11:1) Wyndham anakhulupirira dziko latsopano la Mulungu ndi chiukiriro cha akufa chifukwa cha chidziŵitso cholongosoka cha malonjezo a Baibulo. (Machitidwe 24:15; 2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:3, 4) Chikhulupiriro chotero, chosonyezedwa ngakhale poyang’anizana ndi imfa, chiridi cholimbikitsa ku ubale wa padziko lonse.—1 Petro 5:9.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena