Zinthu Zimene Mkuntho wa Hurricane Andrew Sunakhoze Kuwononga
PALI mikuntho yambiri, koma mikuntho ina imasakaza kwambiri kuposa ina.a Ina iri kokha chimphepo, chobweretsa mvula yaikulu ndi kuzula mitengo. Ndiyeno panali mkuntho wa Hurricane Andrew kummwera kwa Florida (August 24, 1992) ndi ku Louisiana (August 26, 1992). Mkuntho wa Hurricane Iniki m’Kauai, Hawaii (September 12, 1992), ndi wa Typhoon Omar m’Guam (August 28, 1992).
Mikunthoyi inawonongetsa chuma chokwanira madola mamiliyoni zikwi zambirimbiri. Anthu makumi ambiri anafa m’Florida. Mabanja zikwi zambiri anasiyidwa opanda pokhala. Oimira makampani a inshuwalansi anayendayenda kuŵerengera mtengo wa nyumba zosakazidwazo kufunafuna eni ake ndi kulemba macheki.
Lipoti lochokera ku Komiti Yachithandizo ya Mboni za Yehova ya ku Fort Lauderdale linanena kuti nyumba 518 mwa zokwanira 1,033 za Mboni za Yehova m’chigawocho zinafunikira kukonzedwanso. Mutayerekezera ziŵerengerozi ndi nyumba za anthu onse, zimenezo zikatanthauza kuti yoposa 50 peresenti ya nyumba zonse kumene mkuntho wa Andrew unadutsa zinawonongedwa. Pambuyo pake, amwaŵi amene nyumba zawo zinali zokhoza kukhalidwabe anali kuyesa kuumitsa fanichala yawo ndi nsalu zotchinga ndi kuchapa njereza zochititsidwa ndi utoto wa kutsindwi umene unasungunulidwa ndi maliyambwe amene analoŵa m’matsindwi opasulidwawo. Ambiri anakupeza kukhala kovuta kuwona nyumba zawo zopasulidwa. Awo amene mwinamwake anataikiridwa kwambiri anali awo okhala m’nyumba zosalimbirapo za pamagudumu kapena matilela.
Mkuntho wa Hurricane Andrew Sunasiye Aliyense
Aŵiri okwatirana oterowo anali Leonard ndi Terry Kieffer. Pamene anabwerera kunyumba yawo ya pamagudumu mu Florida City, anafunikira kutulutsa chitupa pamalo osechera a asilikali kuti aloŵe m’deralo. Zimene anawona ndiyo nyumba ya pamagudumu imene inawonekera ngati inali itaphulitsidwa ndi mabomba amphamvu mazana ambiri—popanda kusiya chisonyezero chirichonse. Mitengo inazulidwa. Mikwamba ya aluminiyamu wotsupulidwa, yomwe kale inali makoma ndi matsindwi a nyumbazo, inazenengedwa kumitengo ndi kupachikidwa pamitengo mofanana ndi zokometsera phwando zoseketsa. Nsambo zamagetsi zinali mbwee kuli konse, mizati yamitengo inathyoledwa ngati timitengo tamacheso. Magalimoto anagubuduzidwa ndi kuphwanyidwa.
Bob van Dyk, yemwe nyumba yake yatsopano inalengezedwa kuti njosayenera kukhalamo munthu, anafotokoza zochitika panyumba pake motere: “Denga linagwera pansi ndi kutswanyika, kuphwanya zokhoza kuphwanyika, kuthifula zokhoza kuthifuka ndi kutiwopsa, okhoza kuwopsezedwa.”
Zinthu zaumwini, zidole, zovala, zithunzithunzi, mabukhu, zinangoti mbwee ponseponse monga zikumbutso zomvetsa chisoni za mmene kale tinaliri. Mphaka wakuda wosungulumwa anapupulikapupulika m’zinyalala. Modabwa mphakayo anayang’ana dwii kwa a Kieffer ndi mkazi wawo. Abuluzi aang’ono anayendayenda pa zimene kale zinali chuma chamtengo wapatali cha munthu wina. Kununkha kwa chakudya chomaola, kunatuluka m’mafiriji ophwanyidwa, kukumanunkhitsa mpweya. Kulikonse kunali zinthu zowonongedwa mowopsa—zonsezo zinachititsidwa ndi mphepo, mikuntho yamphamvu, yothamanga paliŵiro la makilomitala 260 paola.
Kunali koziziritsa nkhongono kwa eni ake ndi okhala m’nyumba zimenezi. Pambuyo pa zaka zambiri za kulera banja ndi kuchitira zinthu limodzi m’nyumba zawo, iwo anabwerera pambuyo pa mkunthowo ndi kupeza kuti kanthu kalikonse kaphwanyidwa ndi kubalalitsidwa. Banja la Kieffer linali litapulumutsa kale zina za zinthu zawo paulendo woyamba, koma kunali kovutitsa maganizo kwambiri kwa iwo kufufuza m’zinyalala za nyumba zimene zinasiyidwa. Komabe, anayamikira kuti anali amoyobe ndi okhoza kutumikira Mulungu.
Mkuntho wa Hurricane Andrew sunasiye kanthu. Zinthu za mkhonde mwa masitolo, mafakitale, mosungira zinthu—zonsezo zinakhala chandamale cha kukantha kwachigumuchire. Malamulo okhudza zomanga za munthu wosanunkha kanthu sanakhoze kuletsa kusakazako.
Mkhalidwe Wabwino Koposa ndi Woipitsitsa wa Munthu
Chithandizo chinayamba kufika chochuluka m’Florida kuchokera m’dziko lonselo pamene magulu opereka chithandizo osiyanasiyana analinganizidwa. Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova m’Brooklyn, New York, linachitapo kanthu mwamsanga nilinakhazikitsa komiti yachithandizo kuti igwire ntchito kuchokera pa Nyumba Yamsonkhano ya Fort Lauderdale. Linaperekanso chiŵerengero chachikulu cha ndalama zogulira zinthu, chakudya, ndi zinthu zina zofunika mwamsanga. Monga chotulukapo, Mbonizo zinali pakati pa oyamba kuchitapo kanthu kumkhalidwewo ndi kuyamba kuitanira odzipereka. Kunena zowona, ambiri anadza mosaitanidwa.
Antchito a Mboni anadza kuchokera ku California, North Carolina, Oregon, Washington State, Pennsylvania, Missouri, ndi mbali zina zambiri. Komiti Yomanga Yachigawo ya ku Virginia imene kaŵirikaŵiri imamanga Nyumba Zaufumu inatumiza kagulu ka Mboni 18 kukakonzanso matsindwi. Ulendowo unawatengera maola 18 pagalimoto. Ogwira ntchito yopereka chithandizo anatenga nthaŵi yatchuti kapena kupempha nthaŵi ya kusakhala pantchito nayenda pagalimoto kudutsa dzikolo, makilomitala mazana ambiri ndipo ngakhale zikwi, kukafikira Mboni zinzawo zokhala m’vuto.
Kothandiza koposa kanali kagulu kamene kanachokera kudera la Charleston m’South Carolina. Iwo anali atakumanapo ndi mkuntho wa Hurricane Hugo kalelo mu 1989. Iwo anadziŵa zoziyembekezera ndipo mwamsanga analinganiza zinthu zachithandizo, zophatikizapo majenareta amagetsi ndi milimo. Mkati mwa milungu iŵiri timagulu ta odzipereka tinali titaumika nyumba zokwanira 800 ndipo tinali titakonzanso matsindwi ambiri.
Anzawo a muukwati ambiri osakhala Mboni a Mboni ndi anansi ambiri anapindula ndi chithandizo choperekedwa ndi timagulu ta Mboni tokonza nyumba zogumuka. Ron Clarke wa ku West Homestead anasimba kuti: “Anzawo amuukwati osakhulupirira achititsidwadi chidwi ndi zonsezi. Agwetsa misozi, pochititsidwa kakasi ndi zimene Mbonizo zatowachitira kale.” Ponena za mwamuna wosakhulupirira wa mboni ina, Ron Clarke anawonjezera kuti: “Mwamunayo anakondwera kwambiri—Mbonizo ziri konko tsopano kumfolelera tsindwi lake.”
Mboni ina inasimba za anansi ake osakhala Mboni amene iyo inali kuzonda madzulo alionse. Iwo anati anali bwino. Patsiku lachisanu, mkazi sanakhozenso kudziletsa ndipo analira. “Tiribe mateŵera amwana. Tiri pafupifupi opandiratu chakudya chamwana. Tiribe chakudya chokwanira ndi madzi.” Mwamuna anafunikira malitala 20 a petulo koma sanali wokhoza kuwapeza kwina kulikonse. Patsiku limodzimodzilo, Mboniyo inawabweretsera zonse zimene anafunikira kuchokera ku malo osungira zinthu zachithandizo pa Nyumba Yaufumu. Mkazi analira moyamikira. Mwamunayo anathandiza mwa zopereka za ntchito yachithandizo.
Ntchito yofunika inachitidwa ndi akulu ndi atumiki otumikira ampingo amene anagwirira ntchito limodzi kulinganiza chithandizocho pa Nyumba Zaufumu zina zokonzedwanso m’dera losakazidwalo. Iwo anagwira ntchito mosatopa kupeza Mboni zonse ndi kudziŵa zosoŵa zawo. Mosiyana, mkulu wa Asilikali omenya nkhondo a Mumlengalenga anagwidwa mawu kukhala akumati ponena za zoyesayesa zachithandizo m’dera lina: “Mabwana onse akungofuna kukhala mabwana basi, koma palibe aliyense amene akufuna kuvala zilimbe ndi kuchitadi ntchito yadothi.”
Masoka angatulutse mikhalidwe yabwino ndi yoipa mwa anthu. Chitsanzo cha otsirizirawo chinali kuphanga. Banja lina la Mboni linasankha kuti likasunga firiji yawo ndi makina ochapira kuti agwiritsiridwe ntchito pamalo apakati pa Nyumba Yaufumu ya m’malowo. Anapita kuholoyo kukatenga galimoto. Asanabwerere, ophangawo anali ataba ziŵiya zonse ziŵirizo!
Mboni yowona ndi maso inasimba kuti: “Pamene tinayenda m’makwalala apululu, tinawona nyumba zokhala ndi zikwangwani zochenjeza ophanga kuti asafike pafupi. Zina za zikwangwanizo zinati, ‘Ophanga Ayenera Kufa’ ndi, ‘Ophanga Adzawomberedwa Mfuti.’ China chinati, ‘Ophanga aŵiri awomberedwa mfuti. Mmodzi anaphedwa.’ Masitolo ndi zinthu za m’khonde mwa masitolo zinafunkhidwa.” Malinga ndi kunena kwa mkulu wa Gulu la Ankhondo a Mumlengalenga la 82, pafupifupi wophanga mmodzi anagwidwa ndi kuphedwa ndi khamu la anthu.
Ambiri anamangidwa. Kukuwonekera ngati kuti m’chigumuchire chirichonse kagulu ka apandu kamakhala kokonzekera kutsomphola ngati miimba. Ndipo ngakhale anthu amene mwachibadwa siapandu amasonkhezeredwa kuphatikizidwa m’kuphangako. Chipembedzo, miyambo, ndi makhalidwe abwino zimawonekera kukhala zikuzimiririka pansi pa chiyeso cha kupeza chinthu chaulere.
Galamukani! anauzidwa kuti poyamba asilikali angapo anaberedwa ngakhale mfuti zawo zopanda zipolopolo ndi ophanga onyamula zida. Asilikali ena anamvedwa kukhala akunena kuti analingalira malo apakati achithandizo a Nyumba Yaufumu kukhala chitsime chamadzi m’chipululu “chifukwa chakuti,” monga momwe ananenera, “anthunu simumanyamula mfuti.”
“Musamangokhumata”
Kodi Mboni za Yehova zaphunziranji ku zokumana nazo zawo za chigumuchire? Kuyambiranso ntchito yauzimu mwamsanga monga momwe kungathekere. Ed Rumsey, woyang’anira mu Homestead, anauza Galamukani! kuti chimango china cha Nyumba Zaufumu ziŵiri chinali chokonzekeredwa kugwiritsiridwa ntchito kuchitira misonkhano pa Lachitatu mkunthowo utamenya pa Lolemba. Mbali zina za tsindwi zinali zitawonongeka, denga linali litagwa, ndipo madzi anali ataloŵa. Odzipereka anagwira ntchito mofulumira kuchititsa Nyumba Zaufumu kubwerera mumkhalidwe wabwino kuchitiramo misonkhano ndi kuzigwiritsira ntchito monga malo apakati otsogozera ntchito yachithandizo m’dera lawo lopululutsidwa. Makhitchini anakhazikitsidwa kotero kuti chakudya chikatha kuperekedwa kumikhole ndi kwa ogwira ntchito yachithandizo.
Fermín Pastrana, mkulu wa Mpingo wolankhula Chispanya wa ku Princeton, anasimba kuti mabanja asanu ndi aŵiri mumpingo wakwawo wa Mboni 80 anataikiridwa ndi nyumba zawo kotheratu. Kodi ndichothetsera vuto chotani chimene anavomereza kwa Mboni zinzake? “Lirani ngati mufunikira kulira. Komano musamangokhumata. Tanganitsidwani kuthandiza ena, ndipo, kumlingo wothekera, pitani muuminisitala. Musaphonye misonkhano yathu Yachikristu. Thetsani zimene zingathetsedwe, koma musawope zimene ziribe njira yothetsera.” Monga chotulukapo, Mbonizo mwamsanga zinali kulalikira ndi kupita ndi mabokosi achithandizo kunyumba ndi nyumba. Mkuntho wa Andrew sanazilalitse changu chawo.
‘Nthaŵi Yotsatira Tidzachoka!’
Sharon Castro, mkazi wazaka 37 zakubadwa wa ku Cutler Ridge anauza Galamukani! chokumana nacho chake kuti: “Atate anasankha kusachoka. Iwo analingalira kuti popeza kuti mkuntho wapapitapo unalambalala sunakanthe gombe la Florida, mkuntho wa Andrew ukachitanso chimodzimodzi. Sanali ngakhale kuika matabwa pa mazenera. Mwamwaŵi, mchimwene wanga anadza naumirira kuti mazenerawo atetezeredwe ndi matabwa a plaiwudu. Mosakaikira zochita zake zinapulumutsa miyoyo yathu. Mazenera athu akanaphwanyidwa, ndipo ife tikanadulidwa nthulinthuli.
“Pafupifupi pa 4:30 a.m., magetsi anazima. Mapokoso panjapo anali ochititsa mantha. Anali ngati mamvekedwe a tireni yanjanji yaikulu. Panali kuthetheka pamene mitengo ndi nyumba zinapasulidwa ndi kuthyoka. Pambuyo pake tinapeza kuti phokoso la kuthetheka lochititsa manthalo linali phokoso la misomali yaitali m’tsindwi lathu pamene inali kukhwethemuka yokha. Kachipinda kosanja kapamwamba kanaulutsidwa, ndipo mbali imodzi mwa zitatu ya tsindwi inachoka. Tonse pamodzi okwanira 12, kuphatikizapo amayi ofookawo, ndi agogo achikazi azaka 90, tinafunikira kubisala m’chipinda chapakati chopanda mazenera. Tinali otsimikizira kuti tinali kudzafera mmenemo.”
Kodi ndiphunziro lotani limene anaphunzira kuchochitikachi? “Nthaŵi yotsatira pamene atiuza kuchoka, tidzachoka—popanda kuwiringula. Tidzalabadira machenjezo. Ndaphunziranso kugaŵana ndi ena ndi kuchirira pa zochepa kwambiri. Ndipo ndidziŵa kuti palibe cholakwika ndi kulira, kudandaula, ndiyeno kuyang’anizana ndi zenizeni.”
Zochita za Manyuzipepala
Ngakhale zoulutsira mawu zinasimba mmene Mboni zinaliri zolinganizidwa bwino. Savannah Evening Press inali ndi mutu wankhani wakuti “Mboni za Yehova Zikupeza Kuti Zikulandiridwa Kummwera kwa Florida,” ndipo The Miami Herald inati: “Mboni Zimasamalirana—ndi Ena.” Inafotokoza kuti: “Palibe aliyense ku Homestead amene akutsekera kunja mwaukali Mboni za Yehova mlungu uno—ngakhale ngati adakali ndi zitseko zoti atseke. Mboni zodzipereka pafupifupi 3,000 zochokera m’dziko lonselo zasonkhana kudera lokanthidwalo, choyamba kudzathandiza Mboni zinzawo, ndiyeno kudzathandiza ena. . . . Gulu lankhondo lirilonse lingasirire dongosolo, kusunga mwambo ndi kukhoza kwa Mbonizo.”
Mboni zazoloŵera kulinganiza ntchito zodyetsa anthu ambirimbiri pamisonkhano yawo yadera ndi yachigawo. Ndiponso, zalinganiza Makomiti Omanga Achigawo mazana ambiri kuzungulira padziko lonse kuti amange Nyumba Zaufumu ndi Nyumba zazikulu Zamisonkhano. Chotero, izo zaphunzitsa antchito okonzekera kuchitapo kanthu atauzidwa m’maola ochepa chabe.
Komabe, pali mfundo ina—kaimidwe kawo kamaganizo. Lipoti limodzimodzilo linapitiriza kuti: “Palibe kagulu kolamulira ka antchito. Palibe kulimbana chifukwa cha kudzitukumula. Mmalo mwake, antchitowo akuwonekera kukhala osangalala ndi ogwirizanika kwambiri mosasamala kanthu kuti kukutentha motani, zivute zitani kapena kutopa.” Kodi chimachititsa zimenezo nchiyani? Mboni ina inayankha kuti: “Zimenezi zikuchokera muunansi ndi Mulungu umene umatisonkhezera kusonyeza chikondi chathu pa ena.” Chimenecho chinali kanthu kena kamene mkuntho wa Andrew sunakhoze kuchotsa, chikondi Chachikristu cha Mbonizo.—Yohane 13:34, 35.
Kuyerekezera kokondweretsa nkwakuti Mbonizo zinawonekera kukhala zitaphunzira ku mitengo. Mboni ina yowona ndi maso inakufotokoza motere: “Pamene ndinazungulira m’malowo, sindikanachitira mwina kusiyapo kuwona kuti mitengo yaikulu ya Ficus mazana ambiri inali itazulidwa ndi kugwetsedwera pansi. Kodi zimenezo zinali choncho chifukwa ninji? Inapereka chotetezera mphepo yolimba chifukwa cha ukulu wawo, ndipo inali ndi mizu yotambalala momwazikana koma inali yosazama. Kumbali ina, migwalangwa yambiri yokowama yaing’ono siinagwe. Inapindikira limodzi ndi mphepoyo, ina inayoyoka makhwatha, koma yambiri inazikabe mizu m’nthaka.”
Mbonizo zinali ndi mizu yakuya ya chikhulupiriro m’Mawu a Mulungu ndipo zinali zokhoza kusintha m’kachitidwe kawo. Chuma ndi nyumba sizinali zinthu zazikulu kwa iwo. Chachikulu nchakuti izo zinali zamoyo ndipo zikanatha kupitirizabe kutumikira Yehova mosasamala kanthu za chivuto. Moyo unali kanthu kena kamene mkuntho wa Andrew sunawatengere.
Kodi Kumachitidwa Motani?
Kampani ya Anheuser Busch inapereka lole yodzala ndi madzi akumwa. Itafika, woiyendetsayo anafunsa akulu aboma kumene anayenera kukatula madziwo. Iye anauzidwa kuti okha amene anali mumkhalidwe wolinganizidwa anali a Mboni. Kunena zowona, mkati mwa mlungu umodzi mkuntho wa Andrew utakantha, matirera a matalakitala a katundu pafupifupi 70 anali atafika ku Nyumba Yamsonkhano ya Mboni za Yehova ya ku Fort Lauderdale.
Wantchito wodzifunira kumeneko akusimba kuti: “Chotero tinalandira lole yodzala ndi madzi akumwa. Mwamsanga tinawaphatikiza pa zakudya zina zimene tinali kutumiza m’malo apakati ogaŵirira chithandizo pa Nyumba Zaufumu. Anagaŵiridwa kwa abale ndi anansi m’deralo amene anali osoŵa.” Kampani yopanga mapepala mu Washington State inathandiza mwa kupereka mbale zamapepala 250,000.
Pachiyambi, olamulira a mzinda anali kutumiza antchito odzifunira osakhala Mboni ku Nyumba Zaufumu, akumati, ‘Ndiwo okha amene ali olinganizidwa moyenerera.’ Potsirizira asilikali anafikanso nayamba kukhazikitsa malo apakati operekera chakudya ndi madzi ndi misasa yamahema.
Malo apakati operekera chithandizo oyambirira a Mboni anakhazikitsidwa ndi komiti yachithandizo pa Nyumba Yamsonkhano ya Fort Lauderdale, imene iri makilomitala 60 kumpoto kwa malo amene anakanthidwa kwambiri mozungulira Homestead. Kuchepetsa kuchuluka kwantchito, malo oyamba otulirako zinthu anakhazikitsidwa pa Nyumba ya Msonkhano ya Plant City pafupi ndi Orlando, makilomitala pafupifupi 400 kumpoto chakumadzulo kwa malo achigumuchire. Zinthu zachithandizo zambiri zinapititsidwa kumeneko kuti zilekanitsidwe ndi kupachiridwa. Komiti inaitanitsa zofunika zawo kuchokera ku Plant City pamlingo watsiku ndi tsiku, ndipo matilela amatirakitala aakulu anagwiritsiridwa ntchito kuyenda ulendo wamaola asanu kufika ku Fort Lauderdale.
Ndiponso malo apakati olekanitsira awa anapereka chakudya, milimo, madzi, majenaretala, ndi zofunika zina ku Nyumba Zaufumu zitatu zimene zinali zitakonzedwanso m’malo apakati a chigawo chachigumuchire. Kumeneko, Mboni zokhoza zinalinganiza timagulu tomanga ndi kuyeretsa kukacheza kunyumba mazana ambiri zimene zinafunikira chisamaliro. Makhitchini ndi malo operekera zakudya anatsegulidwanso pamalo a Nyumba Yaufumu, ndipo aliyense anali kulandiridwa kudzapatsidwa chithandizo. Ngakhale ena a asilikali anasangalala ndi chakudyacho ndipo pambuyo pake anawonedwa akumaponya zopereka m’mabokosi azopereka.
Pamene amuna anali otanganitsidwa kukonza nyumba zopasulidwa, akazi ena anali kuphika chakudya. Ena anali kukachezera anthu alionse amene anali okhoza kupeza kuti akagaŵane nawo zimene Baibulo limanena ponena za zigumuchire ndiponso kukapereka mabokosi a zinthu zachithandizo kwa ozifunikirawo. Mmodzi wa ameneŵa anali Teresa Pereda. Nyumba yake inagumulidwa, ndipo mazenera agalimoto yake anaswedwa—komabe galimotoyo inali yodzala mabokosi achithandizo ndi wokonzekera kuthandiza anansi ake. Mwamuna wake, Lazaro, anali wotanganitsidwa kugwira ntchito pa imodzi ya Nyumba Zaufumu.—Mlaliki 9:11; Luka 21:11, 25.
Kwa ambiri a opanda malo okhala, malo ogona anapezeka m’nyumba za Mboni zimene sizinakanthidwe ndi mkuntho wa Andrew. Ena anakhala m’matilela alendi kapena operekedwera chifuno chimenecho. Ena anasamukira kumahema okhazikitsidwa ndi asilikali. Ena anangosiya nyumba zawo kukhala kutaikiridwa nasamuka kukakhala ndi mabwenzi ndi achibale kumbali zina zadzikolo. Iwo analibe nyumba kapena ntchito. Kunalibe magetsi, kunalibe madzi, kunalibe zimbudzi zokwanira—chotero iwo anangoti ziwachoke.
Phunziro lina limene onsewo anaphunzira linafotokozedwa bwino lomwe ndi Mboni ina yolankhula Chispanya motere: “Tikuyamikira kwambiri phunziro limene taphunzira ponena za zonulirapo zathu m’moyo. Mudziŵa, ungagwire ntchito kwazaka 15 kapena 20 ukumamanga nyumba yako, kukundika zinthu zakuthupi, ndiyeno mu ola limodzi chabe, zonsezo zingathe kupita. Zimenezi zimatithandiza kuti tidziŵe zonulirapo zathu zauzimu, za kupanga moyo kukhala wofeŵa koposerapo ndi kulingaliradi za kutumikira Yehova.”
Kuli monga momwedi mtumwi Paulo anafotokozera kuti: “Komatu zonse zimene zinandipindulira, zomwezo ndinaziyesa chitayiko chifukwa cha Kristu. Komatu zenizeninso ndiyesa zonse zikhale chitayiko chifukwa cha mapambanidwe a chizindikiritso cha Kristu Yesu Ambuye wanga, chifukwa cha iyeyu ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadzionjezere Kristu.”—Afilipi 3:7, 8.
Zigumuchire zachilengedwe ndizo mbali ya moyo m’dziko lathu lamakonoli. Ngati tilabadira machenjezo a olamulira, tingapulumutsedi miyoyo yathu. Mwinamwake nyumba ndi chuma zidzatayika, koma unansi wa Mkristu ndi “Mulungu wachitonthozo” uyenera kulimbikitsidwa. Ngakhale ngati ena angafe m’chigumuchire, Yesu analonjeza chiukiriro chawo m’dziko latsopano la Mulungu padziko lapansi lobwezeretsedwanso—dziko limene silidzakhala nawo masoka ndi imfa zochititsidwa ndi zigumuchire zachilengedwe.—2 Akorinto 1:3, 4; Yesaya 11:9; Yohane 5:28, 29; Chivumbulutso 21:3, 4.
[Mawu a M’munsi]
a Mkunthowo ndiwo “kavumvulu wowopsa wa kumalo otentha wopangidwa cha Kumpoto kwa Nyanja ya Atlantic kumene mphepozo zimathamanga liŵilo loposa 75 mph (121 km/hr).” (The Concise Columbia Encyclopedia) Typhoon ndiwo “mkuntho wochitika kumadzulo kwa Pacific kapena kwa Nyanja ya China.”—The American Heritage Dictionary of the English Language.
[Bokosi patsamba 20]
Anazizwa Kotheratu
Kagulu ka Mboni zachizungu 11 kanachokera ku Tampa, Florida, kukathandiza m’ntchito yachithandizo. Iwo anapeza ziŵiya zogwiritsira ntchito nayamba kukonza tsindwi lopasuka la Mboni yachikuda. Pamene mdzukulu wake yemwe sali Mboni anafika, sanathe kukhulupirira zimene anawona—anazizwa kotheratu kupeza kuti kagulu ka Mboni zachizungu kanayamba kufika iye asanatero ndipo anali kukonza nyumba yogumuka ya amalume ake. Anachititsidwa chidwi kwambiri kotero kuti anathandiziranso m’ntchito yomangayo.
Iye ananena kuti m’nthaŵi yotsatira pamene Mboni zidzadza panyumba pake, adzaŵapempha phunziro Labaibulo. Pamene anali kulankhula ndi kagulu ka ku Tampa, kunali kwachiwonekere kuti iye anachokera kudera lakwawo. Mosataya nthaŵi mmodzi wa akulu m’kaguluko anapanga makonzedwe a phunziro Labaibulo mlungu wotsatira! Monga momwe Mboni ina inafotokozera, zimenezi zimatsimikizira kuti simutofunikira kugogoda pakhomo pokha kuti mupereke umboni—mungagogodenso pa matsindwi!
[Zithunzi patsamba 15]
Mkuntho wa Hurricane Andrew sunasiye kanthu, ndipo ndinyumba zochepa chabe zimene zinaima chiriri
Nyumba yatilela yabanja la a Kieffer—ndi zotsala zake
[Zithunzi patsamba 16]
Rebecca Pérez, ana ake aakazi, ndi ena 11 anapulumukira m’malo ochepa awa
Asilikali analoŵere- ra kuletsa ophanga (pamwamba kulamanja); masitolo ofunkhidwa (kulamanja)
Mkuntho wa “hurricane” unapasula matsindwi, ndipo magalimoto anagubuduzidwa
[Zithunzi patsamba 17]
Chithandizo chinalinganizidwira pa Nyumba Zaufumu
Nyumba zamagudumu zinazenengedwa m’mitengo; zidoli zamwana zangoti mbwee pamatilesi; mabukhu Abaibulo ali pakati pa zinyalala; Mboni, zonga Teresa Pereda, zinapereka mitokoma kwa anansi awo
Milimo yoperekedwa. Kusanthula zovala
[Zithunzi patsamba 18]
Antchito odzifunira ochokera ku United States yense anathandizira m’ntchito yachithandizo