Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 2/8 tsamba 27-29
  • Kulanditsidwa kwa Dziko Lapansi Kuli Pafupi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulanditsidwa kwa Dziko Lapansi Kuli Pafupi
  • Galamukani!—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Nkhaŵa ya Yehova kaamba ka Dziko Lapansi
  • Kuwonongedwa kwa Iwo Akuwononga Dziko
  • Kodi Dziko Lapansi Lidzathera m’Moto?
    Galamukani!—1997
  • Kupulumutsa Dziko Lapansi ku Kuwonongedwa
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Moyo Uli ndi Chifuno Chachikulu
    Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?
  • Kodi Dzikoli Lidzatha?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Onani Zambiri
Galamukani!—1993
g93 2/8 tsamba 27-29

Kulanditsidwa kwa Dziko Lapansi Kuli Pafupi

STEPHEN M. WOLF, tcheyamani ndi ofisala wamkulu wa United Airlines, anati m’nkhani ya mkonzi: “Kaya munthu akhale wochirikiza kusungitsa zamoyo kapena sali wotero, sikungakanidwe kuti chiyembekezo chowopsa cha zinyama zakutchire ndi nkhalango chikutanthauza tsoka ku dziko lonse lapansi—ndipo kwakukulukulu, chikuwopseza kukhalapo kwa zamoyo za mitundu yonse, kuphatikizapo anthu. Malinga ndi zimene zanenedwa, ‘Ife sitinaluke ukonde wa moyo; ife tiri nkhosi yake basi. Chirichonse chimene tingachite ndi ukondewo, timadzichitira ife eni.’” Iye ananena zowona.

Iye anatinso m’nkhani ya mkonziyo: “Ndife oyambitsa mavutowo. Ndipo ndife tokha amene tingawathetse.” M’mawu ameneŵa iye sanalondole kotheratu. Ndife oyambitsa mavutowo; sindife owathetsa. Sitikusonyeza umboni uliwonse wa kukhala otero. Chipambano chimakhalapo, koma nchochepa kwambiri poyerekezera ndi kusakaza kumene kukupitirizabe padziko lonse lapansi.

Chaka chatha Al Gore analemba bukhu lakuti Earth in the Balance—Ecology and the Human Spirit. Ndilo bukhu limene limachenjeza za tsoka lomakulakula la padziko lonse la malo okhala, ndipo m’menemo analembamo ndemanga yofunika iyi: “Pamene ndimafufuza mozana kwambiri magwero a tsoka la padziko lonse la malo okhala, mpamenenso ndimakhutiritsidwa kwambiri kuti liri umboni wakunja wa tsoka la mkati limene, chifukwa cha kusoŵa liwu labwino, ndingatche lauzimu.”

Liridi tsoka la mpangidwe wauzimu. Ndiko kunyonyotsoka kwa mzimu waumunthu. Ndiko kufunitsitsa kupindulira pakuwononga kukongola kwachilengedwe kwa dziko lapansi ndi chuma chake, miyoyo ya zomera ndi zinyama zikwi zambiri, ndipo ngakhale thanzi ndi miyoyo ya anthu. Ndiponso, ndiko kunyalanyaza kotheratu ana ndi adzukulu amene ayenera kukhala movutikira padziko lapansi losakazidwa limene asiidwira. Kulinso kunyalanyaza kwaliuma ndi kosayamika Uyo amene analenga dziko lapansi nalilinganiza kukhala kwawo kwa anthu.

Yesaya 45:18 amadziŵikitsa Yehova kukhala ‘amene analenga kumwamba, Iye ndiye Mulungu amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; Iye analikhazikitsa, sanalilenga mwachabe; iye analiumba akhalemo anthu.’ Pachiyambi iye anaika munthu padziko lapansi kuti aliyang’anire: “Yehova Mulungu anatenga munthuyo, namuika iye m’munda wa Edene kuti aulime nauyang’anire.” (Genesis 2:15) Ngakhale kuti analengedwa wangwiro, Adamu anataya ungwiro pofuna kutsatira njira yakeyake. Anasiya ntchito yake ya ‘kuyang’anira dziko lapansi.’

Kulephera kumeneko kwapitirizabe kufikira m’nthaŵi yathu, ndipo kuwonongedwa kwa dziko lapansi kwamakono kwakhala kowopsa. ‘Mulungu analenga anthu owongoka mtima; koma iwowo afunafuna malongosoledwe a mitundumitundu.’ (Mlaliki 7:29) ‘Anamchitira zovunda; sindiwo ana ake, chilema nchawo; iwo ndiwo mbadwo wopulukira ndi wokhotakhota.’ (Deuteronomo 32:5) Komabe, dziko lapansi lidzapitirizabe kukhalidwa ndi anthu, koma osati ndi mbadwo wopulukira ndi wokhotakhota. Wamasalmo ananena kuti panthaŵi yoyenera ya Mulungu, ‘olungama okha adzalilandira.’—Salmo 37:29.

Nkhaŵa ya Yehova kaamba ka Dziko Lapansi

Pamene Yehova anatsiriza ntchito yake yolenga dziko lapansi, iye ‘anaziwona zonse zimene adazipanga, ndipo, tawonani, zinali zabwino ndithu.’ Iye anafuna kuti lipitirize kukhala lotero. Iye anabzala munda wokongola mu Edene ndipo anaika munthuyo m’menemo kuti auyang’anire. Zomera za m’menemo sizinali chakudya cha munthu yekha. Mulungu anati: ‘Ndapatsa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi mbalame zonse za m’mlengalenga, ndi zakukwaŵa zonse za dziko lapansi m’mene muli moyo, therere laliŵisi lonse likhale chakudya.’—Genesis 1:30, 31.

Pamene Chilamulo cha Mose chinapatsidwa kwa Aisrayeli pambuyo pake, chinapereka malangizo osamalirira nthaka. Chaka chirichonse chachisanu ndi chiŵiri chinali “sabata lakupumula la dziko.” Zimene zinamera zokha m’nthaŵi imeneyo sizinayenera kututidwa koma kusiidwira osauka ndi “ng’ombe zako, ndi nyama ziri m’dziko lako.”—Levitiko 25:4-7.

Nkhaŵa ya Yehova ya kusungitsa mitundu ya zamoyo inasonyezedwa ndi kuchititsa kwake nyama zamoyo ziŵiriziŵiri kuloŵetsedwa m’chingalawa panthaŵi ya Chigumula cha m’tsiku la Nowa. Nkhaŵa imeneyo inasonyezedwanso m’pangano Lachilamulo. Mwachitsanzo, ng’ombe imene inali kupuntha dzinthu sinayenera kupunamizidwa. Inali ndi ufulu wa kudya zina za dzinthuzo. Ng’ombe ndi bulu sizinayenera kumangidwa m’goli limodzi polima. Kuteroko sikukakhalira bwino nyama yaing’ono, yamphamvu zocheperapo. Bulu wa mnansi anayenera kuthandizidwa ngati anali m’vuto, ngakhale ngati mwini wake anali mdani wa munthuyo ndipo ngakhale ngati kunatanthauza kugwira ntchito pa Sabata. (Eksodo 23:4, 5; Deuteronomo 22:1, 2, 10; 25:4; Luka 14:5) Mazira kapena ana a mbalame akatengedwa m’chisa chake, koma osati mayi wake. Iye anayenera kusiidwa kuti apitirize kubala mtundu umenewo. Ndipo Yesu ananena kuti ngakhale kuti mpheta inali yochepa mtengo, ‘imodzi ya izo siigwa pansi popanda Mulungu kudziŵa.’—Mateyu 10:29; Deuteronomo 22:6, 7.

Wamasalmo wouziridwa anati: “Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova; koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.” (Salmo 115:16) Yesu anati pa Mateyu 5:5: ‘Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi.’ Kodi muganiza kuti choloŵa chimenechi chochokera kwa Yehova chidzakhala dziko lapansi loipitsidwa? Ngati muli ndi nyumba yokongola imene mudzasiira ana anu, kodi mungalole ochita lendi amene akuwononga nyumbayo ndi bwalo lake kupitiriza kukhalamo? Mmalo mwake, kodi simungawachotsemo ndiyeno kuikonza musanaisiire ana anu?

Yehova anachita zimenezo asanaloŵetse Aisrayeli m’dziko limene adawalonjeza. Akanani, mwa makhalidwe awo oluluzika, anaipitsa dzikolo, ndipo chotero Yehova anawachotsamo. Panthaŵi imodzimodziyo, iye anachenjeza Aisrayeli kuti ngati akaipitsa dziko monga momwe anachitira Akanani, nawonso akachotsedwa. Mawu ameneŵa alembedwa pa Levitiko 18:24-28:

‘Musamadzidetsa nacho chimodzi cha izi [kugonana kwa paubale, mathanyula, kugonana ndi zinyama, mbanda], pakuti amitundu amene ndiwapitikitsa pamaso panu amadetsedwa nazo zonsezi; dziko lomwe lidetsedwa; chifukwa chake ndililanga, ndi dzikoli lisanza okhala m’mwemo. Koma inu, muzisunga malemba anga ndi maweruzo anga, osachita chimodzi chonse cha zonyansa izi; ngakhale wa m’dziko ngakhale mlendo wakugonera pakati pa inu; (pakuti eni dziko okhalako, musanafike inu, anazichita zonyansa izi zonse, ndi dziko linadetsedwa) lingakusanzeni inunso dzikoli, polidetsa inu, monga linasanza mtundu wa anthu wokhalako musanafike inu.’

Komabe, Israyeli anadetsa dzikolo mwa kuchita zinthu zoipa zimodzimodzizo zimene Akanani anachita. Mogwirizana ndi mawu ake, Yehova anachotsa Aisrayeli mwa kutumiza Ababulo kuwatenga kupita nawo ku Babulo muukapolo. Kalelo zimenezi zisanachitike, chenjezo linaperekedwa kwa Aisrayeli ndi Yesaya mneneri wa Yehova: ‘Tawonani, Yehova apululutsa dziko, nalipasula, nalitembenuza dodolido, nabalalitsa okhalamo ake. Dzikonso laipitsidwa ndi okhalamo ake omwe, chifukwa iwo alakwa pamalamulo nasinthanitsa malemba, nathyola chipangano cha nthaŵi zonse. Chifukwa chake chitemberero chadya dziko, ndi amene akhala m’menemo apezedwa ochimwa, chifukwa chake okhalamo a padziko atenthedwa, ndipo anthu oŵerengeka atsala.’—Yesaya 24:1, 5, 6.

Kuwonongedwa kwa Iwo Akuwononga Dziko

Lerolino tiri mumkhalidwe wofanana. Mabuku, magazini, manyuzipepala, wailesi ya kanema, mavidiyo, ndi zoulutsira nkhani zonse zimasonyeza chitaganya choluluzika m’zakugonana, chankhanza yosalamulirika, ndi chosalungama m’ndale zake zadziko. Zigwirizano zamalonda zaumbombo zimaipitsa malo a dziko, ngakhale kutumizira maiko osatukuka amene alibe njira zachitetezo zonga za kwawo, zinthu zoletsedwa zimene ziri zaupandu ku thanzi m’maiko awo otukuka. Akristu amachenjezedwa kupeŵa kachitidwe kameneka:

‘Pamenepo ndinena ichi, ndipo ndichita umboni mwa Ambuye, kuti simuyendanso inu monganso amitundu angoyenda, m’chitsiru cha mtima wawo, odetsedwa m’nzeru zawo, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu, chifukwa cha chipulukiro chiri mwa iwo, chifukwa cha kuumitsa kwa mitima yawo; amenewo popeza sazindikiranso kanthu konse, anadzipereka okha kuti akhumbe zonyansa, kuti achite chidetso chonse mu umbombo.’—Aefeso 4:17-19; 2 Timoteo 3:1-5.

Mzimu waumunthu ndi malo okhala omwe nzoipitsidwa. Dziko lapansi liri ndi njira zakezake zachilengedwe zoletsera ndi kulinganiza zinthu zirizonse. Chifukwa cha kuchimwa kwa munthu, chikumbumtima chaumunthu, mphamvu yake yomletsa yachibadwa, chakhala chodetsedwa, chikumachititsa kuipitsidwa kwa dziko lapansi. Tsopano, ndi Mulungu yekha amene akhoza kuletsa munthu. Mulungu yekha angalanditse dziko lapansi. Timapeza chitsimikizo chakuti iye adzatero pa Chivumbulutso 11:18, pamene Yehova akulonjeza ‘kuwononga iwo akuwononga dziko.’

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena