Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 3/8 tsamba 29-31
  • Kulinganiza Banja—Lingaliro Lachikristu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulinganiza Banja—Lingaliro Lachikristu
  • Galamukani!—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Thayo Lopatsidwa ndi Mulungu
  • Njira Zopewera Kutenga Mimba
  • Kodi Ndani Ayenera Kusankha za Ukulu wa Banja?
    Galamukani!—1996
  • Makolo Ayenera Kuphunzitsa Ana Awo Kukonda Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Thayo Lobala Ana mu Nthaŵi Ino ya Mapeto
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kodi N’chifukwa Chiyani Alibe Ana?
    Nsanja ya Olonda—2000
Onani Zambiri
Galamukani!—1993
g93 3/8 tsamba 29-31

Kulinganiza Banja—Lingaliro Lachikristu

PA MSONKHANO woyamba wokambitsirana za Chiŵerengero cha Anthu cha Padziko, mu 1974, maiko 140 amene anasonkhana analengeza kuti okwatirana onse “ali ndi kuyenera kwakukulu kwa kudzisankhira momasuka ndi mwathayo chiŵerengero ndi kutalikitsa nthaŵi ya kubala ana awo ndi kupeza chidziŵitso, maphunziro, ndi njira zochitira motero.”

Ambiri amalingalira chilengezocho kukhala chabwino. Ndithudi, Mulungu anauza Adamu ndi Hava, ndipo pambuyo pake banja la Nowa, ‘kubalana, kuchuluka, kudzaza dziko lapansi.’ Palibe lamulo lotero limene linaperekedwa kwa Akristu. (Genesis 1:28; 9:1) Malemba samalimbikitsa okwatirana Achikristu kukhala ndi ana kapena kuwauza kusakhala nawo. Okwatirana angadzisankhire kuti kaya akufuna kukhala ndi ana kapena ayi ndi, ngati alinganiza kukhala ndi ana, kuti adzakhala ndi angati ndipo nthaŵi pamene adzakhala nawo.

Thayo Lopatsidwa ndi Mulungu

Komabe, kodi mwawona, kuti mawu a Msonkhano wokambitsirana za Chiŵerengero cha Anthu cha Padziko ananena kuti okwatirana ayenera kusankha momasuka ndi “mwathayo chiŵerengero ndi kutalikitsa nthaŵi ya kubala ana awo”? Lamulo lamakhalidwe abwino la kusenza thayo limeneli lirinso logwirizana ndi Baibulo. Makolo Achikristu amadziŵa kuti pamene kuli kwakuti ana ali mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Mulungu, mphatso imadzera limodzi ndi thayo lalikulu.

Choyamba, pali thayo la kusamalira ana mwakuthupi. Baibulo limati: ‘Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira.’—1 Timoteo 5:8.

Kugaŵira banja la munthuwe kumaphatikizapo zambiri koposa kupereka chakudya pathebulo ndi kulipilira ngongole, ngakhale kuti zimenezi kaŵirikaŵiri mwa izo zokha ziri ntchito yaikulu. Okwatirana Achikristu athayo, polinganiza ukulu wa mabanja awo, amalingalira thanzi la amayi limodzi ndi mkhalidwe wawo wamaganizo, wamalingaliro, ndi wauzimu. Kusamalira mwana kumatenga nthaŵi yaitalli, ndipo pamene ana atsatizana mofulumilirapo, azimayiwo, kaŵirikaŵiri amalephera kukhala osati kokha ndi nthaŵi yakupuma, kusanguluka, kupita patsogolo kwaumwini ndi kuphatikizidwa m’ntchito Zachikristu komanso thanzi lawo lakuthupi ndi lauzimu.

Makolo Achikristu athayo amalingaliranso zosowa za ana awo. Bukhulo The State of the World’s Population 1991 limati: “Ana obadwa m’mabanja aakulu, otsatizana mofulumilirapo kwambiri amafunikira kugawana ndi abale ndi alongo awo, chakudya, zovala ndi chikondi chamakolo. Amafulumiranso kuyambukiridwa ndi matenda. Ngati ana amenewa apulumuka zaka zawo zaubwana zosatetezerekazo, kukula kwawo mwachiwonekere kwambiri kudzapinimbiritsidwa ndipo kukula kwawo kwamaganizo kudzadodometsedwa. Ziyembekezo za ana ameneŵa m’moyo wa uchikulire zimachepa kwambiri.” Ndithudi, zimenezi, siziri choncho m’mabanja onse aakulu, koma ndizo kanthu kena kamene okwatirana Achikristu ayenera kukalingalira polinganiza chiŵerengero cha ana amene adzakhala nawo.

Makolo Achikristu ali ndi thayo la kusamalira ana awo mwauzimu, monga momwe Baibulo limalamulira kuti: ‘Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muŵalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.’—Aefeso 6:4.

Emeka, Mkristu amene amaphunzitsa za lamulo mu Nigeria, wakhala wokwatira kwachaka chimodzi ndipo sakufulumilira kukhala atate wa banja lalikulu. “Mkazi wanga ndi ine takambitsirana za chiŵerengero cha ana amene tidzakhala nawo. Tinalingalira za kukhala ndi asanu koma tinadzasankha kukhala ndi atatu. Pambuyo pake tinagamula kuti kukhala ndi aŵiri kungakhale bwinopo. Nkovuta kulera ana mogwirizana ndi malamulo amakhalidwe abwino Abaibulo. Ndilo thayo lalikulu.”

Okwatirana ena Achikristu asankha kusakhala ndi ana kotero kuti athere nthaŵi yawo yonse kutumikira Mulungu. Mmishonale wina mu Afirika amene anavomerezana ndi mwamuna wake kukhala opanda mwana anafotokoza kuti: “Sindikulingalira kuti ndataikiridwa ndi kanthu mwa kusabala ana. Ngakhale kuti mwamuna wanga ndi ine sitinakhalepo ndi chisangalalo cha ukholo, miyoyo yathu yadzala ndi zisangalalo zina. Mwa kuphatikizidwa m’kuthandiza ena kuphunzira chowonadi cha Baibulo, tiri nawo ana auzimu m’mbali zambiri za dziko. Timaŵakonda ndipo amatikonda. Pali chomangira chapadera pakati pathu. Moyenerera, mtumwi Paulo anadziyerekezera ndi mayi woyamwitsa chifukwa cha chikondi chake chachikulu pa awo amene iye anathandiza mwauzimu.”—1 Atesalonika 2:7, 8.

Njira Zopewera Kutenga Mimba

Kodi Baibulo limatsutsa njira zopewera kutenga mimba? Ayi, silimatero. Chosankhacho chikusiyidwira aŵiriwo. Ngati aŵiri okwatirana asankha kusakhala ndi ana, kusankha kwawo njira zopewera kutenga mimba ndiko nkhani ya iwo okha. Komabe, njira yopewera kutenga mimba imene aŵiri Achikristu asankha iyenera kugwirizana ndi kulemekeza kupatulika kwa moyo. Popeza kuti Baibulo limasonyeza kuti moyo wa munthu umayambira pa kukhaliridwa pakati, Akristu akapewa njira zopewera kutenga mimba zimene zimachotsa, kapena kuthetsa, moyo wa mwana womakulayo.—Salmo 139:16; yerekezerani ndi Eksodo 21:22, 23; Yeremiya 1:5.

Chotero okwatirana moyenerera angapange zosankha zosiyana ponena za kulinganiza banja. Ena angafune kuchepetsa chiŵerengero cha ana amene adzakhala nawo. Enabe, mogwiritsira ntchito njira ina yopewera kutenga mimba, angasankhe kusakhala konse ndi ana. Njira zambiri zopewera kutenga mimba ziri zopezeka, iriyonse ikumakhala ndi mapindu ndi zopinga zake. Posankha njira imene iri yabwino kopambana kwa iwo, okwatiranawo ayenera kukumbukira kuti njira zina ziri zogwira mtima kwambiri koposa zina. Ayeneranso kufunsa za ziyambukiro zina zothekera. Madokotala ndi makiliniki olinganiza mabanja ali okonzekera kupereka uphungu wonena za njira zopewera kubala ndi kuthandiza okwatiranawo kusankha imene idzatumikira bwino kwambiri zosowa zawo.

Chosankha chimene okwatirana akupanga cha kukhala ndi ana ambiri, ochepa, kapena kupanda ncha iwo okha. Chirinso chosankha chofunika chokhala ndi ziyambukiro zanthaŵi yaitali. Aŵiri okwatirana angachite mwanzeru kupenda nkhaniyo mosamalitsa ndi mwapemphero.

[Bokosi pamasamba 30, 31]

Njira Zofala Zopewera Kutenga Mimba

Sterilization

Mwa amuna: Mchitidwe wosavuta wa opareshoni umene kucheka chende pang’ono kumachitidwa ndipo misempha yonyamula ubwamuna imadulidwa.

Mwa akazi: Mchitidwe wa kuchita opareshoni mmene Matumbo otengera dzira kuchibaliro amamangidwa kapena kudulidwa kuti dzira lisadzere m’chibaliro.

Mapindu: Mwa njira zonse zopewera kubala, kufula ndiyo njira yogwira mtima koposa.

Zopinga: Kungakhale kwachikhalire. Ponse paŵiri mwa amuna ndi akazi, maopareshoni abwezeretsa kukhoza kubala, koma zimenezi sizingatsimikiziridwe.a

Mibulu Yopewetsa Kutenga Mimba

Imeneyi imaphatikizapo timibulu ta progestin chabe. Imagwira ntchito kudodometsa milingo ya mahomone anthaŵi zonse a mkazi kuti idodometse kukula kwa dzira ndi kutulutsidwa kwake.b

Mapindu: Njogwira mtima kopambana m’kupewa mimba.

Zopinga: Pali ziyambukiro zina zenizeni zovulaza, koma zimenezi nzocheperapo kwa athanzi labwino osasuta fodya azaka zosafikira 40.

Diaphragm ndi Spermicide

Diaphragm ndiko kachikho kampira kobulungika kotamulidwira mumkombero wowolowa. Pambuyo pa kudzola mankhwala kapena mafuta opha ubwamuna (spermicide) m’kachikho, kachikhoko kamavekedwa kumpheto ya mkazi kuti kayenerere m’mbali mwamphetoyo.

Mapindu: Ndimtundu wotetezereka, wodalirika kwambiri wopewera kutenga mimba utagwiritsiridwa ntchito moyenerera.

Zopinga: Uyenera kugwiritsiridwa ntchito nthaŵi iriyonse pamene aŵiriwo akugonana. Luso nlofunika kuika chipangizocho moyenerera, ndipo chiyenera kuikidwa musanayambe kugonana ndi kusiyidwako kwa maola asanu ndi limodzi kufikira asanu ndi atatu pambuyo pake.

Kachivimbo ka Kumpheto

Kachipangizo konga chikho kaplastiki kapena kampira kamene kali kakang’ono koposa diaphragm. Mofanana ndi diaphragm, kamaikidwa kumpheto ya mkazi koma kamayenerera bwinopo ndipo kamafunikira mafuta kapena mankhwala opha ubwamuna ocheperapo.

Mapindu: Kachivimboka nkofanana ndi diaphragm m’kudalirika, ndipo kangakhale pamalo ake kwamaola 48. Mankhwala opha ubwamuna safunikira kudzoledwanso pa kugonana kobwerezedwa.

Zopinga: Kali kovutirapo kukaika koposa diaphragm, ndipo kataikidwa kumphetoko kayenera kupendedwa musanayambe kugonana ndi pambuyo pa kugonana kulikonse. Kuyambukiridwa ndi nthenda kwa chibaliro kapena mpheto ya mkazi ndizo maupandu othekera. Kachivimboko kayenera kuvalidwa kokha ndi akazi opimidwa kukhala alibe zizindikiro za kansa.

Chinkhupule

Chinkhupule cha polyurethane chokhala ndi mankhwala opha ubwamuna chimene chimaloŵetsedwa kumpheto ya mkazi ndi kuphimba mpheto yachikazi, chotero chimapanga chopinga chenicheni ndi mankhwala. Chimataidwa pambuyo pa kugwiritsiridwa ntchito.

Mapindu: Chinkhupule chingasiidwe kumpheto kwamaola 24 ndipo nchogwira mtima ngati kugonana kobwerezedwa mkati mwanthaŵiyo.

Zopinga: Zisonyezero za kuyambukiridwa moipa ndi zochitika zingapo za zisonyezero zovulaza zasimbidwa.

Chipangizo cha Intrauterine

Chotchedwanso IUD, chingwe, kapena nkhata ndicho chipangizo chamkuwa kapena chaplastiki choloŵetsedwa m’chibaliro. Pamene kuli kwakuti pali zikaikiro za mmene chimagwiriradi ntchito, madokotala amakhulupirira kuti chimadodometsa kubala m’njira zingapo. Imodzi ya njira zimenezi mwinamwake ndiyo kuletsa dzira litalandira ubwamuna kuti lisaphatikike kuphambo la chibaliro.

Mapindu: Njira yodalirika yopewera kutenga mimba.

Zopinga: Nthaŵi zina imapangitsa kukha mwazi kapena kupweteka, ndipo nthaŵi zina ingagwire ntchito ngati kuti ikutayitsa mimba.c

Makondomu

Chimake chimene chimavekedwa mpheto ya mwamuna kutetezera ubwamuna kuloŵa kumpheto ya mkazi.

Mapindu: Njira yotetezereka, yogwira mtima ya kupewa kutenga mimba. Imachepetsa kuthekera kwa kuyambukiridwa ndi nthenda zopatsirana mwakugonana kuphatikizapo AIDS.

Zopinga: Siimakondedwa ndi ena chifukwa chakuti kugwira ntchito kwake kumafunikiritsa kudodometsa mchitidwe wakugonana.

Kutulutsa

Kutulutsa mpheto ya mwamuna m’mpheto ya mkazi mwamsanga asanatulutse ubwamuna.

Mapindu: Sikumafunikira ndalama, kukonzekera, kapena chipangizo chakunja.

Zopinga: Sikumakhutiritsa m’zakugonana, kumafunikiritsa kudziletsa kwakukulu ndipo nkosadalirika kwambiri.

Njira ya Nthaŵi ya Kuleka

Aŵiriwo amaleka kugonana m’nthaŵi imene ali pafupi kupita kumsambo mkazi pamene iye ali ndi kuthekera kwakukulu kwa kutenga mimba.

Mapindu: Yotetezereka, yopanda ziyambukiro zovulaza, yosafunikira mchitidwe uliwonse panthaŵi yakugonana.

Zopinga: Siiri njira yachipambano kwambiri yotetezera kutenga mimba kusiyapo ngati aŵiriwo ali otsimikiza kwambiri ndipo akuumirira mwathithithi kumalangizo a mchitidwewo.

Kuikidwa Mahomoni

Njira yatsopano kopambana ya yopewera kutenga mimba, mpambo wa timasilinda tasilikoni tating’ono kwambiri timalowetsedwa m’khungu la mkono wa mkazi. Kwazaka zofikira ku zisanu, timeneti timaloŵetsa mlingo wochepetsetsa wa mahomoni mumsempha wamwazi. Mkati mwanthaŵiyi mkazi amatetezeredwa kukutenga mimba.

Mapindu: Iri yogwira mtima kwambiri. Kubalanso kungabwezeretsedwe mwa kuchotsa zoikidwazo.

Zopinga: Nzochepa. Njofanana ndi mbulu wopewera kutenga mimba wa progestin yokha (mbulu waung’ono). Pamene progestin yokha iikidwa ndi kugwiritsiridwa ntchito, mimba mothekera imapewedwa mwa kuchotsa mimba.d

[Mawu a M’munsi]

a Makambitsirano a mmene mibulu yopewera kutenga mimba imagwirira ntchito akupezeka mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 1989, tsamba 29.

b Makambitsirano akuti kaya kufula kuli kogwirizana ndi malamulo amakhalidwe abwino Achikristu kapena ayi akupezeka mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 1985, tsamba 31.

c Makambitsirano a mmene mibulu yoletsa kubala imapewetsera kubala akupezeka mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 1989, tsamba 29.

d Makambitsirano akuti kaya IUD iri yogwirizana ndi malamulo amakhalidwe abwino Achikristu kapena ayi akupezeka mu Nsanja ya Olonda (Yachingelezi) ya May 15, 1979, tsamba 30-1.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena