Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 4/8 tsamba 9-11
  • Kodi Ndimotani Mmene Ndingasungire Nyimbo m’Malo Ake?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndimotani Mmene Ndingasungire Nyimbo m’Malo Ake?
  • Galamukani!—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nkumwerekera ndi Nyimbo?
  • Kusintha Zizoloŵezi Zanu Zakumvetsera
  • Kuphunzira Kuganiza Nokha
  • Kufutukula Nyimbo Zimene Mumakonda
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndisamangokhalira Kumvetsera Nyimbo?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Kodi Palibe Vuto Ngati Nditamangomvera Nyimbo Iliyonse?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Kodi Mumasankha Nyimbo Mwanzeru?
    Galamukani!—2011
  • Chenjerani ndi Nyimbo Zosayenera!
    Nsanja ya Olonda—1993
Onani Zambiri
Galamukani!—1993
g93 4/8 tsamba 9-11

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndimotani Mmene Ndingasungire Nyimbo m’Malo Ake?

WACHICHEPERE wotchedwa Jackie akutero kuti: “Ndiganiza kuti tinabadwa ndi chikhumbo chokonda nyimbo, popeza kuti zingafotokoze mmene ukumverera. Ndimbali yaikulu ya moyo wako pamene uli wachichepere.”

Jackie akunena zowona. Pamene kuli kwakuti achichepere amawoneka kukhala okokeredwa mwapadera ku nyimbo, kuthekera kwa kusangalala ndi maimbidwe ndi kugwirizana kumawoneka kukhala kwachibadwa mwa tonsefe. Ndipo mungofunikira kumva kuimba kosangalatsa kwa mbalame kapena kuthithima kwa mafunde amadzi kuti mudziŵe kuti nyimbo ndi mphatso yachikondi yochokera kwa Mlengi wathu wachimwemwe. (1 Timoteo 1:11; Yakobo 1:17) Chikhalirechobe, ndimphatso imene kaŵirikaŵiri imagwiritsidwa ntchito molakwa. Kwenikwenidi, ngati nyimbo siziikidwa m’malo ake, zingakuvulazeni m’malo mokuthandizani.

Kodi Nkumwerekera ndi Nyimbo?

Nyimbo zabwino zingakhale zothandiza, zopindulitsa. Komabe, ngakhale zinthu zabwino zochulukitsitsa zingakhale zoipa kwa inu. Mwambi wanzeru umachenjeza kuti: “Wapeza uchi kodi? Idyapo wokwanira, kuti ungakukole, nusanze.” (Miyambo 25:16) Uchi uli ndi mphamvu zochiritsa zodziŵika bwino kwambiri. Komabe, ‘kudya uchi wochulukitsitsa sikwabwino’ ndipo kungakuchititseni nseru. (Miyambo 25:27) Kodi mfundo njotani? Tiyenera kusangalala ndi zinthu zabwino mwachikatikati.

Komabe, nyimbo zimalamulira kotheratu miyoyo ya achichepere ena. Mwachitsanzo, mkazi wachichepere wotchedwa Jodie akuvomereza kuti pamene anali wazaka zapakati pa 13 ndi 19, “anali kumvetsera nyimbo nthaŵi zonse.” Kodi nanunso mumakhala mukumvetsera nyimbo mphindi iliyonse imene mumakhala m’maso? Pamenepo kumene mungakutche kuyamikira nyimbo kungatchedwe kumwerekera ndi nyimbo.

Wachichepere wotchedwa Steve akukumbukira kuti: “Ndinapita kusukulu ndi ana amene ankamvetsera nyimbo ngakhale m’kalasi.” Komabe, iye akuvomereza kuti: “Kuika [maheadphone] a Walkman m’makutu mwawo kunasokonezadi kuphunzira kwawo.” Mofananamo, kodi mumakhala mukuseŵera nyimbo zocheutsa ngakhale pamene mukuchita homuweki yanu? Ndipo bwanji ponena za nthaŵi zopatulidwa kaamba ka kuphunzira Baibulo kapena kukonzekera misonkhano Yachikristu? Kodi ndiyo nthaŵi yoseŵera nyimbo yanu yapamtima?

Talingaliraninso za mtengo umene zimakutengerani kugula nyimbo zatsopano zonse zotulutsidwa. Kodi ndi ochuluka motani a malipiro anu kapena ndalama zopatsidwa zimene pakali pano mukuthera pa marekodi, makaseti tepi, kapena compact discs? Kodi zina za ndalama zimenezo zingagwiritsiridwe bwino ntchito?

Kodi bwanji za maunansi abanja? Kodi mumaloŵetsedwamo m’kukambitsirana kwa banja, kupezekapo pa chakudya cha banja—kapena kodi mumakhala m’chipinda chanu kumvetsera nyimbo? Baibulo limachenjeza kuti: “Wopanduka afunafuna chifuniro chake, nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.”—Miyambo 18:1.

Kusintha Zizoloŵezi Zanu Zakumvetsera

Ngati nyimbo zikutenga nthaŵi yochuluka ya moyo wanu, mungachite bwino kulingalira mawu a pa Aefeso 5:15, 16 akuti: “Potero, penyani bwino umo muyendera, simonga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa.” Zimenezi zingaphatikizepo kudziikira malire ndi kukhala wachikatikati m’zizoloŵezi zanu zakumvetsera. (Yerekezerani ndi 1 Timoteo 3:2.) Mwachitsanzo, mungafunikire kuleka chizoloŵezi chotsegula nyimbo mphindi imene mufika kunyumba. Phunzirani kukhala ndi nyengo zabata.

Kwakukulukulu, kuchita tero kungakuthandizeni kuwongolera magiredi anu. Nyengo zabata nzabwino kuphunzira. Pakali pano, mungaganize kuti kuseŵera nyimbo kumakuthandizani kupumula. Koma bwanji osayesa kuphunzira popanda nyimbo, ndi kuwona ngati kusumika maganizo kwanu kuwongokera? “Mungakhoze kuphunzira [mukumvetsera nyimbo],” akutero Steve wachichepere, “koma mudzapindula kwambiri ngati muzima nyimboyo.”

Mungafunenso kupatula nthaŵi, kapena ndandanda, yoŵerenga ndi kuphunzira Baibulo ndi mabuku ofotokoza Baibulo. Nthaŵi zina Yesu Kristu anafuna malo abata, malo ‘achipululu’ kukapemphera ndi kusinkhasinkha. (Marko 1:35) Kodi malo anu ophunzirira ngabata ndi amtendere? Ngati ayi, mungapinimbiritse kukula kwanu kwauzimu.

Kuphunzira Kuganiza Nokha

Mwinamwake mbali yaikulu yodetsa nkhaŵa ndiyo mtundu wa nyimbo zimene mumamvetsera. Steve akufotokoza motere: “Kodi nchifukwa ninji nyimbo zonse zabwino zimakhala ndi mawu otukwana?” Nthaŵi za Baibulo, kunali nyimbo zomwe zinachilikiza kuledzera ndi dama. (Salmo 69:12; Yesaya 23:15, 16) Mofananamo, nyimbo zambiri zotchuka zamasiku ano zimachilikiza kumwerekera ndi mankhwala ogodomalitsa, kugonana ukwati usanakhale, ndi chiwawa.a

Ausinkhu wanu angaike chitsenderezo chachikulu kuti mumvetsere nyimbo zoterozo. Palinso chitsenderezo chochokera ku makampani anyimbo enieniwo. Mothandizidwa ndi wailesi ndi wailesi yakanema, nyimbo za rock zakhala indasitale yamphamvu, yopanga ndalama mamiliyoni zikwi zambiri. Akatswiri azamalonda amphamvu amaitanidwa kuwongolera—ndi kulamulira—nyimbo zimene mumakonda.

Koma pamene mulola ausinkhu wanu kapena ofalitsa nkhani kulamulira zimene mumamvetsera, mumataya mphamvu yanu yakusankha. Mumakhala kapolo wosaganiza. (Aroma 6:16) Baibulo limatilimbikitsa kuganiza tokha. Limatiuza ‘kuyesera chokondweretsa Ambuye nchiyani.’ (Aefeso 5:10) Ndithudi sitingayembekezere mpingo Wachikristu kusanthula nyimbo zikwi zambiri zimene zimatulutsidwa chaka chilichonse ndi kupereka ndandanda ya nyimbo zovomerezedwa kapena zoletsedwa. Ayi, muyenera kuphunzira “kuzoloŵeretsa zizindikiritso [zanu] kusiyanitsa chabwino ndi choipa.”—Ahebri 5:14.

Kodi mungachite motani zimenezo? Chabwino, talingalirani mfundo zotsatirazi:

Santhulani Chikuto: Kaŵirikaŵiri, kungoyang’ana kokha chikuto kapena mawu osatsira malonda kungakhale kokwanira. Zinthunzithunzi zosonyeza kugonana, chiwawa, kapena matsenga ziyenera kukhala chenjezo. Nyimbo zamkati mwake zingakhale zokaikiritsa mofananamo. Ngati nkotheka, ŵerengani mawu amene ali pachikutowo.

Fufuzani Zamkati Mwake: ‘Yesani mawu’ a nyimbo mwakulingalira mitu ndi mawu ake. (Yobu 12:11) Kodi mawu ake akunena za chiyani? Kodi mukufunadi kumvetsera kapena kubwereza malingaliro ameneŵa nthaŵi ndi nthaŵi? Kodi malingaliro ameneŵa ngogwirizana ndi makhalidwe anu abwino ndi malamulo amkhalidwe Achikristu?—Aefeso 5:3-5.

Onani Chiyambukiro Chake: Kodi chiyambukiro chake nchotani pa inu? Kodi nyimboyo imakupsinjitsani maganizo kapena kukusangulutsani mopambanitsa? Kodi mumakhala mukulingalira malingaliro oipa pambuyo poimva? Kodi mawu a m’makwalala ogwiritsiridwa ntchito m’nyimbo aloŵerera m’kalankhulidwe kanu?—1 Akorinto 15:33.

Lingalirani Ena: Kodi makolo anu amalingalira motani ponena za nyimbo zanu? Funsani lingaliro lawo. Ndiponso, lingalirani mmene Akristu anzanu amamverera ponena za nyimbo zanu. Kodi amavutika nazo maganizo?—Aroma 15:1, 2.

Kufutukula Nyimbo Zimene Mumakonda

Mwinamwake mungafunikire kupanga masinthidwe ena m’nyimbo zimene mumakonda. Koma popeza kuti kukonda zinthu kumachita kuphunziridwa, mukhoza kukusintha. Woimba wina wotchuka akunena kuti: “Achichepere ambiri sanamvepo chilichonse koposa nyimbo zimene zimasatsidwa malonda kwambiri ndi akatswiri azamalonda.” Kodi yankho nchiyani? Musamangomvetsera ku mtundu umodzi wokha wa nyimbo. Yesani kufutukula nyimbo zimene mumakonda.

Ndithudi, mukafunikirabe kukhala osankha. Koma mkati mwa mitundu ya folk, jazz, ndipo, ngakhale nyimbo za classic, pali nyimbo zabwino zambiri zimene mungaphunzire kusangalala nazo. Kwenikwenidi, mungakhale mukusangalala kale ndi nyimbo zoterozo mosazindikira. Mwachitsanzo, nyimbo za classic zingakhale zinagwiritsiridwa ntchito kusonyeza mkhalidwe wina wa chiwonetsero chanu chapamtima cha kanema kapena wailesi yakanema. Talingalirani mmene nyimbo zimenezo zingakhalire zosangalatsa mutazimva popanda zocheutsa.

Achichepere ena Achikristu ayamba kusintha kukonda nyimbo kwawo mwakumvetsera ku matepi a Kingdom Melodies opangidwa ndi Watch Tower Society. Nyimbo zimenezi, zodziŵika kwa Mboni zonse za Yehova, zimaphatikizapo mitundu yosiyanasiyana ya kaimbidwe. Pali mitundu ina yambiri ya nyimbo zabwino zimene mabwenzi angavomereze. “Bwenzi lina linandiphunzitsa kukonda nyimbo za orchestra—monga Beethoven,” akutero Michelle. Iye akuvomereza kuti: “Ndinkazida.”

Njira ina yofutukulira ndiyo kuphunzira kuimba chiŵiya choimbira inu mwini. Kuteroko sikukakhala kotokosa kokha ndi kokhutiritsa, koma kungakudziŵitseni mitundu ina ya nyimbo kuwonjezera pa rock. “Kuimba nyimbo nkwabwinodi,” akutero Jackie, “chifukwa umakhala ndi luso ndipo umaligwiritsira ntchito.” Mwakupanga kuyesayesa kochepa mukhoza kusangalatsa ena.

Nyimbo zilidi mphatso yochokera kwa Mulungu, koma muyenera kusamala kusaigwiritsira ntchito molakwa. Wachichepere wina akuvomereza kuti: “Ndili ndi nyimbo zimene ndikudziŵa kuti ndiyenera kuzitaya. Koma zimamveka bwino.” Komabe, talingalirani za chivulazo chimene wachichepere ameneyu amachita ku maganizo ndi mtima wake mwakumvetsera zinthu zoipa! Peŵani msampha umenewo. Musalole nyimbo kukuipitsani kapena kulamulira moyo wanu. Mamatirani ku miyezo yapamwamba Yachikristu m’nyimbo zanu. Pemphererani chitsogozo ndi chithandizo cha Mulungu posankha nyimbo zanu. Pezani mabwenzi amene ali ndi zikhulupiriro zanu.—Aroma 12:2, 12.

Nyimbo zingakuthandizeni kupumula. Zingachotse malingaliro a kusungulumwa pamene muli nokha. Koma pamene zileka, mavuto anu samachoka. Ndipo nyimbo sizimaloŵa m’malo mabwenzi enieni. Chotero musalole nyimbo kukhala chinthu chachikulu m’moyo wanu. Sangalalani nazo, koma zisungeni m’malo ake.

[Mawu a M’munsi]

a Onani makope a Galamukani! a February 8 ndi March 8, 1993.

[Chithunzi patsamba 11]

Kodi nyimbo zikusokoneza maphunziro anu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena