Gawo 1
Sayansi Kufunafuna Chowonadi kwa Mtundu wa Anthu Komapitirizabe
“MUDZAZINDIKIRA chowonadi, ndipo chowonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:32) Mawu anzeru ameneŵa amene amagwidwa kaŵirikaŵiri analankhulidwa ndi mwamuna amene anthu mamiliyoni ambiri amamuyesa munthu wamkulu koposa amene anakhalako.a Ngakhale kuti wokambayo anali kunena za chowonadi cha chipembedzo, m’zinthu zina chowonadi m’mbali iliyonse ya moyo chingamasule anthu.
Mwachitsanzo, chowonadi cha sayansi chamasula anthu ku malingaliro ambiri olakwa, onga akuti dziko lapansi lili latyatyatya, dziko lapansi ndilo pakati pa chilengedwe chonse, kutentha ndiko madzi otchedwa caloric, mpweya woipa ndiwo umachititsa matenda, ndi kuti atomu ndiyo kachidutswa kakang’ono koposa ka zinthu. Kugwiritsidwa ntchito mwa njira yowoneka kwa zowonadi za sayansi m’maindasitale, kudzanso m’zakulankhulana ndi kayendedwe, kwamasula anthu ku mavuto osafunikira ndipo, kumlingo wakutiwakuti, ku kuchepekedwa ndi nthaŵi ndi kutalika kwa mtunda. Zowonadi za sayansi zogwiritsiridwa ntchito m’mankhwala akatemera ndi m’zipatala zathandizira kumasula anthu ku imfa yofulumiza kapena mantha aakulu a matenda.
Sayansi—Kodi Nchiyani?
Malinga ndi The World Book Encyclopedia, “sayansi imaphatikizapo mbali zosiyanasiyana za chidziŵitso cha anthu chonena za maumboni oikidwa pamodzi ndi miyezo (malamulo).” Chotero, pali mitundu yambiri ya sayansi. Buku la The Scientist limati: “M’mawu, pafupifupi mtundu uliwonse wa chidziŵitso ungachititsidwe kukhala wasayansi, pakuti malinga ndi malongosoledwe, mbali ya chidziŵitso imakhala sayansi pamene ifufuzidwa mwa kugwiritsira ntchito njira zasayansi.”
Zimenezi zimabutsa mavuto akutiakuti polongosola, motsimikiza, pamene sayansi ina imayambira ndi pamene ina imathera. Kunena zowona, malinga ndi The World Book Encyclopedia, “nthaŵi zina, masayansi amaloŵerana kwambiri kotero kuti pakhazikitsidwa magulu amene amaphunzitsa maluso angapo ophatikizapo mbali ziŵiri kapena zoposapo za masayansi.” Komabe, mabuku ambiri amaumboni amanena za zigawo zinayi zazikulu: masayansi a zinthu zopanda moyo, masayansi a zinthu zamoyo, masayansi a kakhalidwe ka anthu, ndi sayansi ya masamu ndi nzeru.
Kodi masamu angakhale sayansi? Inde, popanda njira zopimira zophatikizidwa pamodzi, njira zina zodziŵira ukulu, kapena ung’ono wa chinthu, kuchuluka, kapena kuchepa kwake, kutalika kwa mtunda, kapena kufupika kwake, kutentha kwa chinthu, kapena kuzizira kwake, kufufuza kopindulitsa kwasayansi kukanakhala kosatheka. Chifukwa chake, masamu atchedwa “Mfumu Yaikazi ndi Kapolo wa Masayansi.”
Ponena za masayansi a zinthu zopanda moyo, amaphatikizapo chemistry, physics, ndi astronomy. Masayansi aakulu a zinthu zamoyo ndiwo botany ndi zoology, pamene masayansi a kakhalidwe ka anthu amaphatikizapo anthropology, sociology, zachuma, sayansi ya zandale, ndi psychology. (Wonani bokosi patsamba 8.)
Kusiyana kuyenera kupangidwa pakati pa sayansi yachilengedwere ndi sayansi yogwira ntchito. Yoyambayo imachita kotheratu ndi maumboni asayansi ndi malamulo ake chabe; yotherayo, imachita ndi ntchito zake zochitidwa. Lerolino sayansi yogwira ntchito imatchedwa luso la zopangapanga.
Kuphunzira mwa Kuyesa Izi ndi Izi
Zonse ziŵiri chipembedzo ndi sayansi zili zitsanzo za chikhumbo cha mtundu wa anthu cha kufuna kudziŵa chowonadi. Koma pali kusiyana kwakukulu pakati pa magwero a chowonadi cha chipembedzo ndi magwero a chowonadi cha sayansi. Wofunafuna chowonadi cha chipembedzo mwinamwake amatembenukira ku Baibulo Loyera, Koran, Talmud, Vedas, kapena Tripitaka, zikumadalira ngati iye ali Mkristu, Msilamu, Myuda, Mhindu, kapena Mbuddha. Kumeneko amapeza zimene chipembedzo chake chimayesa kukhala vumbulutso la chowonadi cha chipembedzo, mwina chochokera kumagwero aumulungu ndipo motero chowonedwa monga ulamuliro wosatsutsika.
Komabe, wofunafuna chowonadi cha sayansi alibe ulamuliro wosatsutsika wotero umene angatembenukireko—kaya buku kapena munthu. Chowonadi cha sayansi sichimavumbulidwa; chimatulukiridwa. Zimenezi zimachititsa njira ya kuyesa izi ndi izi, wofunafuna chowonadi cha sayansiyo akumangopeza kuti kaŵirikaŵiri akuchita kuyesayesa kosaphula kanthu. Koma mwa kutsatira njira zinayi mwatsatanetsatane, iye amachita kufunafuna kopindulitsa. (Wonani bokosi la “Kupeza Chowonadi mwa Njira ya Sayansi.”) Chikhalirechobe, pamakhala zikondwerero za zipambano za sayansi pamene malingaliro a sayansi amene kale anali ovomerezedwa amasiidwa kulola atsopano owonedwa kukhala olondola kwambiri.
Mosasamala kanthu za njira ya kulasa pambali nchamuna chomwe imeneyi, asayansi akundika chidziŵitso chachikulu chodabwitsa cha sayansi m’zaka mazana ambiri. Ngakhale kuti amalakwa kaŵirikaŵiri, iwo akhoza kuwongolera zigamulo zambiri zosalondola ngozi yaikulu isanachitike. Kunena zowona, malinga ngati chidziŵitso cholakwika chikhalabe m’sayansi yachilengedwere, upandu wakuchititsa kuvulala kowopsa umakhala wocheperapo. Koma pamene kuyesayesa kuchitidwa kwa kusanduliza sayansi yachilengedwere yolakwika kowopsayo kukhala sayansi yogwira ntchito, zotsatirapo zingakhale zatsoka.
Mwachitsanzo, tatengani chidziŵitso cha sayansi chimene chinatheketsa kupangidwa kwa mankhwala opha tizilombo. Ameneŵa anali kuthokozedwa kwambiri kufikira pamene kufufuza kowonjezereka kwa sayansi kunavumbula kuti ena a iwo amasiya zotsala zoika nthanzi la anthu pachiswe. M’madera ena pafupi ndi nyanja ya Aral, imene ili ku Uzbekistan ndi Kazakhstan, pakhala kugwirizana pakati pa kugwiritsiridwa ntchito mofala kwa mankhwala opha tizilombowo ndi chiŵerengero cha kansa ya pammero choŵirikiza kasanu ndi kaŵiri kuposa avareji ya dzikolo.
Chifukwa cha phindu limene anapereka, mankhwala owaza anakhala omveka—kufikira pamene kufufuza kwa sayansi kunasonyeza kuti anali kuchititsa kuwonongedwa kofulumira kwambiri kwa muyalo wa ozone wotetezera dziko lapansi, ndipotu, kuposa zimene zinkalingaliridwa. Chotero, kufunafuna chowonadi cha sayansi kuli mchitidwe womapitiriza. Maŵa, “zowonadi” za sayansi za lero zingakhale malingaliro olakwa a dzulo, ndipo mwinamwake ngakhale zowopsa.
Chifukwa Chake Tiyenera Kuchita Chidwi ndi Sayansi
Sayansi ndi luso la zopangapanga yachita zambiri pakumanga dongosolo lathu lamakono. Frederick Seitz, yemwe kale anali prezidenti wa U.S. National Academy of Sciences, anati: “Sayansi, imene inayamba kwakukulu monga maseŵera osangalatsa maganizo, tsopano ikukhala imodzi ya mizati yaikulu ya kakhalidwe kathu.” Chotero, kufufuza kwa sayansi lerolino kumayendera limodzi ndi chitukuko. Aliyense wokaikira kupita patsogolo kwamakono kwa sayansi amadziika yekha pangozi ya kutchedwa “wotsutsa chitukuko.” Ndiiko komwe, zimene ena amati chitukuko cha sayansi ndizimene m’kuganiza kwawo zimasiyanitsa otsungula ndi osatsungula.
Pamenepa, nkosadabwitsa kuti wolemba ndakatulo wa ku Briteni wa m’zaka za zana la 20 W. H. Auden anati: “Amuna achangu zedi m’nthaŵi yathu, amene amasintha dziko, sali atsogoleri andale ndi nduna za boma, koma asayansi.”
Ndianthu oŵerengeka chabe amene angakane kuti dziko lifunikira kusintha. Koma kodi sayansi ikhoza kuchita zimenezo? Kodi ingathe kutulukira zowonadi za sayansi zofunikira kuchitira ndi mavuto apadera amene adzakhala m’zaka za zana la 21? Ndipo kodi zowonadi zimenezi zingaphunziridwe mofulumira kwambiri moti nkumasula anthu ku mantha a tsoka la padziko lonse likudzalo?
Linus Pauling, amene anapata kaŵiri mphotho ya Nobel, anati: “Aliyense amene amakhala m’dziko afunikira kukhala ndi chidziŵitso chakutichakuti cha mkhalidwe ndi ziyambukiro za sayansi.” Pofuna kugaŵira kwa oŵerenga athu china cha chidziŵitso chofunikira chimenechi tayamba mpambowu wakuti “Sayansi—Kufunafuna Chowonadi kwa Mtundu wa Anthu Komapitirizabe.” Tikukulimbikitsani kuŵerenga Gawo 2, m’kope lathu lotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Kristu Yesu. Wonani buku la The Greatest Man Who Ever Lived, lofalitsidwa mu 1991 ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 7]
KUPEZA CHOWONADI MWA NJIRA YA SAYANSI
1. Pendani zimene zimachitika.
2. Pamaziko a kupendako, pekani chiphunzitso ponena za chimene chingakhale chowona.
3. Pimani chiphunzitsocho mwa kupenda ndi kuyesa kowonjezereka.
4. Dikirani kuwona ngati kulosera kozikidwa pa chiphunzitsocho kukwaniritsidwa.
[Bokosi/Zithunzi patsamba 8]
MASAYANSI ALONGOSOLEDWA
ANTHROPOLOGY ndimaphunziro onena za anthu malinga ndi kawonedwe ka moyo, kakhalidwe, ndi miyambo.
ASTRONOMY ndimaphunziro openda nyenyezi, mapulaneti, ndi zolengedwa zina zakuthambo.
BIOLOGY ndimaphunziro openda mmene zamoyo zimagwirira ntchito ndi magulu a zomera ndi zinyama.
BOTANY, imodzi ya mbali ziŵiri zazikulu za biology, ndimaphunziro openda moyo wa zomera.
CHEMISTRY ndimaphunziro openda mikhalidwe ndi misanganizo ya zinthu ndi mmene zimachitirana china ndi chinzake.
MASAMU ndimaphunziro openda manambala, kuchuluka, mipangidwe, ndi kugwirizana kwa zinthu.
PHYSICS ndimaphunziro openda mphamvu ndi zinthu zonga kuunika, mawu, mphamvu yokanikiza, ndi mphamvu yokoka.
PSYCHOLOGY ndimaphunziro openda maganizo a anthu ndi zochititsa mkhalidwe wa anthu.
ZOOLOGY, mbali yachiŵiri yaikulu ya biology, ndimaphunziro openda moyo wa zinyama.