Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndikuvutikiranji Motere ndi Kupunduka?
“NDINALI ndi zaka zisanu,” akukumbukira motero Becky. “Mnzanga anandikwezeka panjinga yake pamene galimoto linatulukira pagulaye ndi kutigunda.” Ndiyeno chinachitika nchiyani? “Ndinatyoka mwendo ndi kuvulala kwambiri kumutu. Madokotala sanayembekezere kuti ndikakhala ndi moyo.” Komabe, Becky anakhala ndi moyo, ndipo lerolino ali mtsikana wa zaka 16 wosangalala. Ngakhale nditero, ngoziyo inasiya ziyambukiro zake. “Inandichititsa kukhala wofooka,” iye akutero.
Mnyamata wotchedwa Craig alinso wolemala, chifukwa cha nthenda yotchedwa CP (cerebral palsy). “CP imayambukira minofu ndi mitsempha yanga,” akufotokoza motero Craig. “Minofu yanga simagwirizana bwino ndi mauthenga otumizidwa ndi ubongo. Chotero, ndimakhala ndi vuto poyenda, polankhula, ndi kuti ndiimilire bwino. Ndikhoza kuchita zinthu zonsezi koma osati bwino kwambiri.”
Kodi nanunso muli wopunduka mwanjira iliyonse? Ziŵerengero zimasonyeza kuti podzafika chaka cha 2000, chiŵerengero cha achichepere opunduka chidzafika pafupifupi 59 miliyoni padziko lonse. (World Health, January/February 1985) Komabe, kudziŵa kuti anthu ambiri ali ndi vutolo kumakupatsani chitonthozo pang’ono pamene mulephera kuthamanga, kulumpha, ndi kuseŵera mmene achichepere ena amachitira.
Mavuto a Olemala
Kupunduka kwa thupi sikwatsopano. M’nthaŵi za m’Baibulo ena anali kuvutika ndi kupunduka (2 Samueli 4:4; 9:13), khungu (Marko 8:22), ndi kupuŵala (Mateyu 12:10). Olemala oterowo kaŵirikaŵiri anapeza vuto pochita zinthu zofunika kwambiri m’moyo.—Yerekezerani ndi Deuteronomo 28:29; Miyambo 26:7.
Koma inunso mungakhale ndi vuto lofananalo posakhala wokhoza kuchita zinthu zina. Kuvala, kudya, kapena kupita kusukulu kungakhale kovuta kwambiri—ndipo mungafunikire kuthandizidwa kwambiri ndi ena. “Sindikhoza kugwiritsira ntchito bwino dzanja langa lamanja,” akutero Becky. “Chotero ndinaphunzira kulemba ndi dzanja lamanzere. Kuyenda kunalinso kondivuta. Koma tsopano ndimayenda bwino, koma masiku ena ndimatsimphina kwambiri.” Kapena lingalirani mavuto a mnyamata wina wovutika ndi ukanjipiti. Iye moseketsa akuti: “Kufikira maswichi a magetsi pachipupa kumandikwiitsa. . . Nyumba zimalinganizidwira anthu aatali okha.”—How It Feels to Live With a Physical Disability, lolembedwa ndi Jill Krementz.
Komabe, mungapeze kuti mavuto anu osautsa kwambiri sindiwo athupi. Magazini ya Parents imafotokoza kuti: “Achichepere amawona kwambiri mmene ena amachitira, zimene zimapangitsa moyo wa achichepere okhala ndi zosoŵa zapadera kukhala wovutirapo kwambiri. . . . Iwo amaganiza zimene anthu ena amalingalira ponena za mawonekedwe awo ndipo kaŵirikaŵiri samakhulupirira mawu kapena zowachitira zaubwenzi, akumaziwona kukhala machitidwe owachitira chisoni.” Kuli kwachibadwa kufuna kukondedwa ndi kufunidwa ndi ena. Komabe, mungamve kukhala wopeŵedwa. Monga momwe wachichepere Michelle ananenera kuti: “Kwa moyo wanga wonse ndakhala wosiyana ndi aliyense. Chifukwa nchakuti ndilibe dzanja lakumanzere.”
Kukhala wosiyana ndi ena kungachititsenso ena kumakusekani. “Ndinapita kusukulu ya olemala kufikira m’giredi lachisanu,” akukumbukira motero Craig. “Koma m’giredi lachisanumo, ndinayamba kupita kusukulu yozoloŵereka. Ndinalibe mavuto ambiri kwenikweni kufikira tsiku lina pamene anyamata ena anayamba kundiseka. Anali kuseka mmene ndinali kuyendera.” Becky akukumbukiranso nkhanza zimene anzake a pasukulu anamchitira. Chifukwa chakuti opaleshoni yoyambirira inawononga ziŵalo zake zotulutsa mawu, liwu lake linalikumveka losasa. “Anzanga pasukulupo ankati ndili ndi liwu la chilombo,” iye akutero.
Achikulire nawonso angasonyeze machitidwe oipa. Ena angamapeŵe kuyang’anana nanu kumaso. Ena angapeŵe kulankhula nanu, akumalankhula kwa makolo anu kapena anzanu—monga ngati kuti ndinu wosawoneka kapena wogodomala. Amene angakhale okwiitsa koposa angakhale anthu osonyeza chifundo amene nthaŵi zonse angakhale akukuuzani mawu omvetsa chisoni, akumakuchititsani kumva ngati kuti ndinu chinthu chowonongeka.
Mmene Mulungu Amawonera Nkhaniyo
Komabe, kodi Mulungu amakuwonani motani? Kodi kulemala kwanu kuli chisonyezero cha kusakufunani kwake? Onani zimene Yesu ananena pamene anakumana ndi “munthu ali wosawona chibadwire.” Ophunzira ake anafunsa kuti: “Anachimwa ndani, ameneyo, kapena atate wake ndi amake, kuti anabadwa wosawona?” Yesu anayankha kuti: “Sanachimwa ameneyo, kapena atate wake ndi amake.” (Yohane 9:1-3) Inde, kusawonako sikunali kaamba ka tchimo lakutilakuti la munthu wosawonayo kapena la makolo ake. Mmalomwake, kunali chifukwa cha kupanda ungwiro kumene tonsefe tinalandira kwa Adamu. Mtumwi Paulo akufotokoza kuti: “Monga uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.”—Aroma 5:12.
Pamenepo, kulemala kwakuthupi sikumachititsidwa ndi Mulungu ndipo sikuli chilango chochokera kwa iye. Kwina kumachititsidwa ndi kusasamala. Pamenenso kwina kumangochititsidwa ndi ‘nthaŵi ndi zotigwera zosadziŵika.’ (Mlaliki 9:11) Ndipo pali achichepere amene akuvutika ndi kupunduka chifukwa cha nkhanza kapena kulekerera kwa makolo awo.
Mosasamala kanthu ndi chimene chinachititsa mavuto anu, simuyenera kulingalira kuti Mulungu amakuwonani monga chinthu chowonongeka. Mosiyana ndi zimenezo, iye amakuwonani monga wamtengo wapatali ndi wofunika, makamaka ngati mumawopa Mulungu. (Luka 12:7) Iye ‘amakusamalani’ mwanjira yaumwini kwambiri ndipo amafuna kwambiri kukugwiritsirani ntchito muutumiki wake. (1 Petro 5:7) Eya, mmodzi wa atumiki apadera a Mulungu achikhalire, mtumwi Paulo, mwachiwonekere anavutika mwakuthupi—ndi “munga m’thupi.” (2 Akorinto 12:7) Kuli kotonthoza chotani nanga kudziŵa kuti “munthu ayang’ana chowoneka ndi maso, koma Yehova ayang’ana mumtima.” (1 Samueli 16:7) Iye amazindikira bwino lomwe zomwe mukhoza kuchita ndipo amadziŵa zimene mudzakhala wokhoza kuchita pamene mudzabwezeretsedwa kuungwiro m’dziko lake latsopano.—Chivumbulutso 21:3, 4.
Kuchita ndi Ena
Mwatsoka, anzanu apasukulu ndi ena angakhale opanda lingaliro lapamwamba la Mulungu. Ndithudi, anthu nthaŵi zina amangokhala ankhanza popanda chifukwa. Chotero, musadabwe ngati anzanu ena ali opanda chifundo pakuvutika kwanu. Komabe, kaŵirikaŵiri anthu samakhala ndi cholinga chakuti akukwiyitseni kapena kukuchititsani manyazi; nthaŵi zina amangotaya m’kamwa. Pokhudzidwa ndi kuvutika kwanu kapena mosalingalira, iwo anganene kanthu kena kopusa kapena kokupwetekani.
Kodi mungachitenji? Nthaŵi zina mungapeŵe mikhalidwe yochititsa manyazi. Mwachitsanzo, mungathandize ena kumva bwino ngati muwona kuti akuvutika maganizo kapena akusoŵa chonena. Zindikirani kuti tonsefe timawopa chimene sitimadziŵa bwino. Thandizani ena kusawona kupunduka kwanu koma umunthu wanu weniweniwo. Pamene mkhalidwe ulola, mungayese kunena motere: “Kodi mukudabwa chimene ndikuyendera pampando wa magudumu?” Malinga nkunena kwa magazini a Parents, mphuzitsi wina, woduka miyendo, amakhutiritsa zikaikiro za ophunzira ake mwakuyamba kukambitsirana ndi mawu aŵa: “Ndidziŵa kuti mukudabwa zimene zinachitika. Kodi mufuna kudziŵa?”
Mosasamala kanthu za kuyesayesa kwanu zolimba, mungamakwiyebe panthaŵi zina. Becky wachichepereyo akuti: “Pamene ndinali mwana, ndinali kukwiya mowopsa pamene ena anandiseka; ndakhala ndi mtima wapachala m’moyo wanga wonse. Koma tsopano sindimalola kuti zindikwiitse. Nthaŵi zina ndimakhoza ngakhale kuseka zikachitika.” Inde, kukhala wansangala kungathandize kwambiri kuletsa kukwiya ndi mawu opweteka. Pali “mphindi yakuseka.” (Mlaliki 3:4) Mfumu Solomo anaperekanso uphungu wakuti: “Mawu onsetu onenedwa usawalabadire.” (Mlaliki 7:21) Nthaŵi zina njira yabwino koposa yochitira ndi mawu opusa ndiyo kungowanyalanyaza. “Musadandaule ndi zimene anthu amanena,” akutero Becky.
Chiyembekezo Chimakuthandizani Kupirira
Ndithudi, mtundu wonse wa anthu ngwopunduka. “Cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m’zoŵaŵa pamodzi kufikira tsopano,” limatero Baibulo. (Aroma 8:22) Koma mungathe kukhala ndi chiyembekezo chamtsogolo. Mwachitsanzo, lingalirani msungwana wina amene tidzamutcha Carol. Iye anabadwa ali wogontha. Ndiyeno ngozi yapanjinga inapangitsa kuti adulidwe mwendo. Carol anafuna kuti afe chabe. Koma anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo anaphunzira za dziko lotsopano lolungama m’mene “wokhalamo sadzanena, ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Ndithudi, iye anapeza chiyembekezo chakuti tsiku lina kupunduka kwake kudzachiritsidwa—mozizwitsa!—Yesaya 35:5, 6.
Kodi kuphunzira za Mulungu kunayambukira motani maganizo a Carol? Mabwenzi ake ena okondedwa Achikristu amati ponena za iye: “Nthaŵi zonse amakhala wansangala ndipo samalingalira za kulemala kwake.” Komabe, mokondweretsa iwo amatinso: “Mabwenzi ake ambiri samazindikira kuti ali ndi mwendo woikilira ndi kuti samamva kwambiri.” Chifukwa ninji? “Iye amamva mwakutsatira milomo ndi mwa zipangizo zothandizira kumva.” Ndithudi, Carol wachita zoposa kungokhala ndi chiyembekezo chamtsogolo. Iye wayesayesa kuchita zonse zimene angathe pakali pano. Mmene mungachitire zofananazo ndiyo idzakhala nkhani yotsatira ya mpambo uno.
[Chithunzi patsamba 14]
Ena amakuwona kukhala kothandiza kufotokoza mkhalidwe wawo kwa awo owoneka kukhala okayikira