Zosangulutsa Zosavulaza Kapena Paizoni ya Maganizo?
Pa konsati ya rock, mmodzi wa oimbawo anaika mkazi m’bokosi ndi kuyamba kuphwanya bokosilo ndi nkhwangwa. Mwazi wonamizira unathamukira mkamwa mwa woimbayo, ndipo anaulavulira kwa omvetsera.
Mu 1984 mnyamata wa zaka 19 zakubadwa anadziwombera mfuti. Makolo ake amanena kuti kudzipha kwake kunasonkhezeredwa ndi mawu a nyimbo ya rock yakuti “Suicide Solution.”
Magazini a achichepere anafalitsa nkhani za kugonana koipa kumene kumachitidwa ndi gulu la oimba m’chipinda chawo chosinthira zovala limodzinso ndi m’chipinda chojambulira nyimbozo pamene akuzijambulitsa. Lekodi ina ya nyimbo ya rock inali ndi chithunzi choipa chosonyeza mpheto yachimuna ndi yachikazi.
CHIWAWA, kudzipha, ndi kugonana kwankhalwe—zimenezi ndi zoŵerengeka zokha za nkhani zoipa zimene zimakhala pa malekodi, mavidiyo, ndi makonsati a nyimbo za rock. Pamene mikangano yonena za maprogramu oluluzika ameneŵa idzutsidwa ndipo ngakhale kupititsidwa ku bwalo lamilandu, oimbawo ndi makampani ojambula nyimbo amayesayesa kupereka zifukwa zolungamitsa zoipa zimenezi. Mwachitsanzo, tsopano chithunzi choipa chimanenedwa kukhala umboni wa ndemanga yonena za “kuipitsa maganizo kwa Chitaganya cha Amereka ndi mmene kukutisakazira.” Mofananamo, m’nyimbo zina, mawu ophiphiritsira onena za mpheto yachimuna (onga ngati mfuti kapena mipeni) tsopano amanenedwa kuti amatanthauza mfuti ndi mipeni yeniyeni.
Oimba ndi makampani ojambula nyimbo angathaŵe zilango zachiweruzo, koma kodi anthu akunyengedwadi? Kodi inuyo mukunyengedwa? Kodi mungakane kuti chiwawa, kugonana, ndi matsenga zili mbali zotchuka za nyimbo zoipa za rock zimene zimagulitsidwa masiku ano?
Heavy Metal ndi Rap
Mitundu yambiri ya nyimbo za rock yapangidwa mkati mwa zakazi. Pakali pano, mitundu iŵiri, heavy metal ndi rap ikusulizidwa chifukwa cha mawu otukwana ochititsa kakasi.
Heavy metal ndinyimbo zamphamvu, zokhala ndi mawu okuzidwa ndi ziwiya zamagetsi zokhala ndi kugunda kwamphamvu. Malinga nkunena kwa magazini a Time, “oimba nyimbo za metal amaimba zogwirizana ndi malingaliro aupandu a omvetsera achichepere aamuna makamaka achizungu, mwakudzisonyeza kukhala anthu ogwiritsidwa mwala ofulatira chitaganya choipa.” Nyimbo zambiri za heavy metal zinalinganizidwa kuchititsa mantha. Mawu ake ena sangatheke kulembedwa. Magazini azamankhwala a ku Texas ananena kuti mawu ambiri a nyimbo za heavy metal amathokoza “makhalidwe oipa onena za kugonana, chiwawa, chidani, ndi matsenga.”
Chiwawa chochititsidwa ndi nyimbo za heavy metal nchodetsa nkhaŵanso. Mwachitsanzo, pamene chiwonetsero china chinaimitsidwa chifukwa chakuti woimbayo anadwala, omvetserawo anachita chiwawa ndipo anawotcha bwalo lamaseŵeralo. Pakonsati ina achichepere atatu anapuyitsidwa kufikira anafa pamene ochemerera zikwi zambiri anathamangira papulatifomu, akumagwetsa anthu amene anali kutsogolo kwawo ndi kuwapondereza.
M’nyimbo za rap, zimene zimadziŵikanso monga hip-hop, woimba ndipakamwa mmodzi (kapena ochulukirapo) amalankhula mawu mogwirizana ndi kulira kwa zoimbira, kaŵirikaŵiri opangidwa ndi luso lamakono lakompyuta lodziŵika monga sampling. Nyimbo zambiri za rap zimapekedwa ndi oimba achikuda koma zimagulitsidwa kwa anthu akuda ndi azungu omwe. Mawu angapo a rap ngabwino, amatsutsa zinthu zonga kuchitira nkhanza ana ndi kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala oledzeretsa. Komabe, nyimbo zambiri za rap zimanena za kupandukira ulamuliro, chiwawa, kudana ndi akazi, ndi tsankho la fuko. Nyimbo zambiri zili ndi mawu otukwana ndi malongosoledwe onyansa akugonana.
Chiwawa chakhala vuto lalikulu pamakonsati ena a nyimbo za rap. Pakonsati ina, mamembala a kagulu okwanira 300 anaukira omvetsera, ndipo omvetserawo anabwezera mwakuponyerana mipando yachitsulo mpaka pamene apolisi anabwera ndi kuthetsa konsatiyo. Anthu 45 anavulala.
Chaka chatha, bungwe la New York State Sheriffs Association linaitanitsa kuchita sitalaka pa makampani onse a Time Warner, Inc., kufikira kampaniyo italeka kugulitsa nyimbo ya rap yakuti “Cop Killer.” Mkulu wa bungwelo, Peter Kehoe, anati: “Nyimbo imeneyi imasonkhezera chidani ndipo imalimbikitsa ndi kuthokoza kuphedwa kwa akuluakulu apolisi. Monga chotsatirapo chachindunji cha nyimbo imeneyi, apolisi adzaphedwa.” Pomalizira pake, analeka kuigulitsa.
Kodi Pali Ziyambukiro?
Pamene oimba aimba za zinthu zoipa kapena kuchita zoipazo papulatifomu, kodi zimakhala ndi chiyambukiro chotani kwa omvetsera ndi openyerera? Talingalirani ndemanga ndi zochitika zotsatirazi.
Dr. Carl Taylor, profesa wothandizira wa chiweruzo cha apandu pa Michigan State University, akunena kuti akatswiri oimba rock “akuchilikiza njira ya moyo. . . . Mamembala a gulu loimbalo amasonkhezera kwambiri achichepere.”
Mnyamata wina amene analephera kudzipha ananena kuti nyimbo zinamnyenga iye ndi bwenzi lake (limene linadzipha) kulingalira kuti “yankho la mavuto a moyo ndilo imfa.”
Mu 1988 achichepere atatu anapha bwenzi lawo kokha kuti adzisangalatse. Mmodzi wa iwo ananena kuti kusangalala ndi imfa kunayamba ndi nyimbo za heavy metal.
Pambuyo pa konsati ina ya rap, achichepere ena anapita kukaphwanya mazenera. Mkulu woyang’anira zachitetezo cha anthu wa ku Pittsburgh, Pennsylvania, anati: “Sindikukaikira konse kuti nyimbo za rap zimasonkhezera chiwawa.”
Kufufuza achichepere ndi magulu olambira Satana kunasonyeza kuti ambiri amene amadziloŵetsa m’kulambira Mdyerekezi amagwiritsira ntchito molakwa mankhwala oledzeretsa ndipo amamvetsera ku nyimbo za heavy metal, zimene zimathokoza kugwiritsira ntchito mankhwala oledzeretsa ndi kulimbikitsa chisembwere. Chotsatirapo nchakuti, achichepere amakopeka ndi magulu olambira Satana.
Ndithudi, pamene achichepere asonkhezeredwa kumwa mankhwala oledzeretsa, kuchita upandu, kapena kudzipha, pali chochititsa china chowonjezera pa nyimbo. Mosakaikira kusweka kwa moyo wabanja ndi chitaganya cha anthu kumachita mbali yaikulu. Koma nyimbozo zingasonkhezere, zili monga njira yolimbikitsira achichepere kuchita zinthu zimene sangazilingalire paokha. Kodi anthu amene ngosautsidwa kale ndi mavuto amoyo amafunikira nyimbo zimene zimawalimbikitsa kugonjera ku zikhoterero zosakaza?
Mfundo njakuti nyimbo zoipa zingatumikire monga paizoni yamaganizo kwa omvetsera. Kumbukirani kuti, mauthenga a m’nyimbo zoterozo amakhala amphamvu kwambiri chifukwa chakuti amachokera kwa akatswiri, ngwazi, zimene zimalambiridwa ndi ochemerera awo.
Bwanji Ponena za Inu?
Kodi ndinyimbo zotani zimene mumamvetsera? Mwinamwake ndinu wochenjera kale ponena za nyimbo zimene mumasankha, ndipo zimenezo nzoyamikirika. Komabe, ngati ndinu mmodzi wa amene amamvetsera nyimbo zoluluzika kapena zosayenera, kodi mwayambukiridwa moipa? Ngakhale ngati khalidwe lanu silinasinthe, kodi munganene mowona mtima kuti kulingalira kwanu sikunayambukiridwe kukhala koipa? Ndiiko komwe, kumvetsera nkhani zoipa mobwerezabwereza kungakupangitseni kuwona nkhanizo kukhala zabwino.
Talingalirani chitsanzo cha mwamuna wachichepere amene anayesa kuphatikiza moyo wake monga Mkristu ndi chizoloŵezi chakumvetsera nyimbo za heavy metal ndi rap. Iye sanasonkhezeredwe kuchita zinthu zonga mbanda, kudzipha, kapena kulambira Mdyerekezi. Koma tamverani mmene kulingalira kwake kunayambukiridwira. Iye anati: “Nyimbo zimenezi nzauchinyama kwambiri. Zinandilola kuchita zinthu mwabata ndi mofatsa pamene kuli kwakuti ndinali kulingalira za zinthu zoluluzika ndi zachiwawa kwenikweni. . . . Ndinali kulingalira maloto oyerekezera achidani. Palibe tsiku linapita osalingalira mwamphamvu za kudzipha.” Iye anasankha kupanga masinthidwe otheratu m’zizoloŵezi zake zakumvetsera nyimbo. Pamene anachita zimenezo, kulingalira kwake kunawongokera kwambiri.
Ochilikiza nyimbo zoluluzika adzaumirira kulungamitsa mbali zoipa za nyimbo za rock. Koma kodi mwasankhapo chiyani? Kodi munganyalanyaze kuwopsa kwa nkhaniyi? Kodi mungapite ku makonsati onga ofotokozedwa poyambawo osawopa kuti mungavulazidwe? Ndipo bwanji za kugwirizana kumene kulipo pakati pa nyimbo zimenezo ndi mkhalidwe wochititsa manyazi wa oimbawo ndi omvetsera?
Ngati mumasamala za thanzi lanu, mosakaikira mumapeŵa zakudya zimene zingakuvulazeni ngakhale ngati nzokoma. Nyimbo zoipa, kaya zikhale za rock kapena mtundu wina, zili chiwopsezo ku thanzi lanu lamaganizo. Kodi mukamvetsera zosangulutsa zoipitsa maganizo? Ndithudi ayi. Chotero, kodi mungachitenji kuti mukhale ndi kawonedwe kabwino, kachikatikati pankhaniyi? Chonde, tawonani mfundo zoperekedwa m’nkhani yotsatira.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 6]
Kodi Kulambira Mdyerekezi Nchiyani?
Kulambira Mdyerekezi, kumene kumalimbikitsidwa ndi mawu ena a nyimbo za heavy metal, sikuli chosangulutsa chosavulaza. Texas Medicine/The Journal inafotokoza kuti kulambira kumeneko kumaphatikizapo machitachita amene “amayamba monga opanda chivulazo mpaka kufika pa kumwa mwazi wamunthuwe mwakudzivulaza ndi wa nsembe zanyama.” Magulu olambira Satana amanena “kuti ali okhulupirika kwa mdyerekezi. Madzoma akutiakuti amachitidwa kuitanira mphamvu za Satana pa otsatirawo. . . . Chiphunzitso cha ufulu wakudzisankhira ndi kudzichitira zinthu chimatanthauza kuchita zilizonse zimene mukufuna osalingalira za Mulungu, osakhala waliŵongo, ndipo wopanda chikumbumtima.” Chotsatirapo nchakuti, ena amachita machitachita aupandu popanda kuchita manyazi.
[Chithunzi patsamba 5]
Simungadye zinthu zoipa. Kodi nkuziikiranji m’maganizo mwanu?
[Chithunzi patsamba 7]
Kodi muyenera kumva bwino kupezekapo pa zochitika zoterozo?