Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Bwanji za Kutaya Nthaŵi Mwakucheza?
MAKONDE amavidiyo oseŵeretsa, marestiranti, mphambano za misewu, masitolo abwino a mmalowo—ponse paŵiri mmalo olemera ndi osauka—akhala malo osonkhanira kumene achichepere amatayira nthaŵi.
Masitolo ali malo enieni otchuka otayira nthaŵi mu United States. Kaŵirikaŵiri kumeneko magulu a achichepere amawonedwa akungoyendayenda kwa maola ochuluka. “Masitolo adzakhalabe malo oyenera kupitako,” anatero msungwana wachichepere wina, “chifukwa kumeneko kumakhala zambiri zochitika, ndipo kumakhala kanthu kena nthaŵi zonse kokukopani—monga anyamata!”
Kodi kulibe masitolo chapafupi? Pamenepo malo opanda kanthu kapena mphambano ya msewu ingayenerere. Tari wazaka 15 akuti: “Ine ndi anzanga timakwera galimoto kumka kumalo aakulu oika galimoto pafupi ndi paki, timakhala pa maboneti a galimoto zathu ndi kuyamba kukamba nkhani kwa maola ambiri.”—magazini a ’Teen, September 1990.
Ndithudi, palibe chatsopano ponena za kutaya nthaŵi. Baibulo limanena za anthu a m’nthaŵi zakale amene ankasonkhana pamabwalo ndipo “osachita kanthu kena koma kunena kapena kumva chatsopano.” (Machitidwe 17:21) Koma kodi nchifukwa ninji kucheza kotere kuli kofala pakati pa achichepere lerolino?
Malinga nkunena kwa buku la The Adolescent, lolembedwa ndi F. Philip Rice, achichepere “amafikira pakuzindikira zosoŵa zawo kuti zimapezeka ku kagulu kakutikakuti. Amafuna kukondedwa ndi anzawo achichepere.” Chotero, kutaya nthaŵi ndi mabwenzi kumawonekera kukhala kukudzetsa ubwenzi ndi chichirikizo.
Achichepere ena amakuwona kukhala njira yokha yothetsera kuipidwa. Michelle wachichepere akufotokoza kuti: “Kukhala panyumba madzulo kumatopetsa. Umafuna kupita koyenda ndi kusangalala chifukwa ngati supita sudzapeza tulo.” Ed wazaka 16 akunena kuti kucheza kuli “kanthu kena kokachita ndipo mwanjira ina yake kamakuchotsera mavuto.” Koma kodi kumaterodi?
Pamene Anthu Ataya Nthaŵi
Baibulo silimatsutsa kucheza ndi mabwenzi. Komabe, limachenjeza kuti: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzawo wa opusa adzaphwetekedwa.” (Miyambo 13:20) Tsopano, kodi ndi achichepere angati osoŵa chochita amene amangoima pamphambano pa misewu amene anganenedwe kukhala anthu anzeru—awo amene amalemekezadi malamulo a Baibulo? Iwo sangakhaledi ovutitsa, koma gulu lalikulu la achichepere lonyong’onyeka, losayang’aniridwa ndiponso lomangokhala lingayambitsedi mavuto.
Chifukwa cha chimenechi Baibulo silimavomereza kutaya nthaŵi pachabe. Lingalirani za nthaŵi imene mtumwi Paulo ndi Sila anachezera mzinda wa Tesalonika. Otsutsa uthenga Wachikristu ‘anatenga anthu ena oipa achabe a pabwalo, [“otaya nthaŵi pachabe,” Today’s English Version] nasonkhanitsa khamu la anthu, nachititsa phokoso m’mudzi.’ (Machitidwe 17:5) Malingana ndi Vine’s Expository Dictionary of Old and New Testament Words, anthu oipa achabe apabwalo ameneŵa anali anthu pawokha “okhala pamsika, ndipo chotero amangoyendayenda kusoŵa chochita.” Kodi nzomvekera bwino? Mwachiwonekere, oyendayenda ameneŵa analibe kapena anali ndi chikondwerero chochepa muuthenga wa Paulo, opanda chabwino chochita, akananyengedwa mosavuta kuchita chipolowe.
Kufuntha ndi Chiwawa
Tangoganizani tsopano, kusapeŵeka kwa vuto pamene gulu la achichepere losoŵa chochita likumana. Palibe amene amakonzekera kuchita chiwawa. “Palibe zambiri zimene zikuchitika,” anatero Ken wa zaka 16 amene amatayira nthaŵi pamalo oika galimoto za pasukulu. “Timakhala pa galimoto zathu ndi kuyamba nthabwala zopusa kapena kukamba za kupita koyenda ndi atsikana.” Inde, kukamba za maseŵero, nyimbo, anyamata ndi atsikana kungasangalatse aliyense. Komabe, kaŵirikaŵiri achichepere amanyansidwa ndi kumangocheza.
Ofufuza ena Mihaly Csikszentmihalyi ndi Reed Larson akusimba kuti: “Kaŵirikaŵiri, [achichepere] amanena za zochitika zimenezi [za kungotaya nthaŵi] kukhala ‘koipa m’makhalidwe,’ kukhala kwaphokoso, kowopsa, ndi kosalamulirika. . . . Pali kanthu kena ponena za kucheza kwa achichepere kamene kamachititsa khalidwe loipa, ngakhale kuti wachichepere aliyense payekha sanakhoterere ku zimenezo. . . . Machitachita a khalidwe loipa amaphatikizapo kukuwa pamene akuyendetsa galimoto, kutayira zitini zopanda kanthu panyumba za anthu, ndi kumenyana.” (Kanyenye ngwathu.)—Being Adolescent.
Ndithudi, simungakhale ndi chikhoterero chakuchita chinthu chopusa chifukwa chakuti mabwenzi anu akutero. Koma mungadziike pansi pa chitsenderezo chowopsa chakuchita choipa ngati muli pakati pa ochita zoipa. (1 Akorinto 15:33) Ndipo ngakhale ngati mutadziletsa kusachita khalidwe loipa, kukhala kwanu pakati pawo kukapereka kwa ena chithunzi choipa cha inu. Zimenezi nzimene zinachitika kwa msungwana wachichepere wotchedwa Dina, mwana wamkazi wa Yakobo, kholo Lachihebri.
Dina analeredwa kukhala wolambira wa Yehova Mulungu, ngakhale kuti banja lake linakhala m’dziko la Kanani—dziko lodzala ndi mphulupulu za kugonana ndi kulambira mafano. Motero, Atate wake Yakobo, anayesetsa kwambiri kuchepetsa kuyanjana kwake ndi Akanani achisembwerewo mwakumanga chihema chawo kunja kwa mzinda wa Sekemu ndi kupeza chitsime chawochawo. (Genesis 33:18; Yohane 4:12) Komabe, Dina “ananka kukawona akazi a kumeneko,” mwinamwake nthaŵi zonse. (Genesis 34:1) Dina analingalira kuti kucheza ndi Akanani kunali kosavulaza. Komatu akazi Achikanani anali ndi mbiri ya uchiwerewere. Chotero pamene mwamuna wa ku Kanani wotchedwa Sekemu anawona Dina akucheza ndi akazi otero, “anamtenga nagona ndi iye, namuipitsa.”—Genesis 34:2.
Mofananamo, kucheza ndi gulu loipa kungakuikeni m’mavuto. Mnyamata wotchedwa Leonard akukumbukira kuti mosasamala kanthu kuti analeredwa monga Mkristu, anayamba “kucheza ndi gulu lopandukira. Tinkapita koyenda ndi kumwa moŵa pamodzi—ngakhale kuti ndinali wamng’ono wosalolezedwa kutero. Pofika zaka 18, ndinayamba kusuta chamba.”
Kugwiritsira Ntchito Bwino Nthaŵi
Kufufuza kwina kunapeza kuti 44 peresenti ya achichepere amene anafunsidwa anathera maola atatu kufika ku asanu kapena oposerapo nthaŵi iliyonse imene anapita ku masitolo; 14 peresenti anathera maola asanu ndi limodzi. Koma mmalo mwakuwononga nthaŵi pachabe, wachichepere wanzeru ‘amapeza nthaŵi yoyenera, chifukwa masiku ali oipa’—Aefeso 5:15, 16, NW.
Kodi ntchito yanu yakusukulu ndi ntchito zapanyumba sizimachitidwa chifukwa cha nthaŵi imene mumathera mukucheza ndi achichepere anzanu? Bwanji ponena za ntchito zanu zauzimu—phunziro laumwini la Baibulo, misonkhano Yachikristu, ntchito yochitira umboni kwa ena? Kodi mukunyalanyaza mathayo ameneŵa? Pamene muli “akuchuluka muntchito ya Ambuye,” sikungakhale kotheka kwa inu kukhala ndi nthaŵi ya kusoŵa chochita.—1 Akorinto 15:58.
Njira Zothandiza
Kusanguluka kuli mbali ya moyo yofunika. (Mlaliki 3:4) Koma kutaya nthaŵi sindiko njira yokha yosangalalira. “Ndimasangalala kukhala ndekha,” akutero mkazi wina wachichepere wotchedwa Lucy. “Ndimakonda kuŵerenga, ndipo zimenezi zandithandiza kukulitsa chikondwerero m’mbiri ya maiko ena, makhalidwe, ndi chinenero. Ndimapita ku myuziyamu, kukawona zosemasema za miyala, ndimasoka ndi kuphika. Ndimakondanso kujambula ndi kulemba makalata, ndipo ndimayesa kulemba ndakatulo zazing’ono nthaŵi zina.” Iyayi, kukhala wekha sikuyenera kukhala kotopetsa.
Banja lanu lingakhalenso njira ina yosangulukira. Tsopano, musanakane lingaliro ili, mvetserani kwa mnyamata wotchedwa Jack. Iye akukumbukira kuti: “Makolo anga nthaŵi zonse analinganiza kanthu ka ife kuti tichite. Tinkapita ku ice-skating ndi roller-skating; tinali kupita ku mapaki, kukawona zinyama, ndi ku myuziyamu. Ngakhale kusesa panyumba kapena kupukuta m’nyumba kunali kosangalatsa kwambiri pamene tinakuchita pamodzi monga banja.” Mwinamwake banja lanu lalekeza kuchitira zinthu pamodzi monga banja. Ngati ndi choncho, kodi bwanji osalinganiza zopita kukayenda monga banja? Mungasangalale kwambiri koposa mmene mukuganizira!
Zimenezi sizikutanthauza kuti simungasangalale ndi anzanu achichepere—kuphatikizapo nthaŵi imene mumakhala mukukambitsirana kapena kupumula limodzi. Koma sankhani mabwenzi anu. Mnyamata wotchedwa Enrique akuti: “Ndinkatayira nthaŵi ndi achichepere akudziko, koma pamene ndinapatulira moyo wanga kutumikira Yehova, ndinayanjana ndi achichepere a mumpingo. Tinapita m’ntchito yolalikira limodzi, tinaseŵera mpira limodzi—ndinayesa kuchita zonse zimene ndikanatha limodzi nawo.”
Mofananamo Shelleace ankakonda kutayira nthaŵi ndi gulu loipa. Iye akukumbukira mabwenzi ake akalewo kuti: “Miyoyo yawo inalibe chifuno ndi chitsogozo. Kunatenga nthaŵi kwa ine kuti ndisiyane nawo, koma pamene ndinatero, ndinakhala ndi mabwenzi abwino. Pamenepo ndinayamba kupita patsogolo mwauzimu.”
Chotero pamene kuli kwakuti kutaya nthaŵi mwakucheza kungakhale kwabwino kapena ngakhale kosangalatsa panthaŵi zina, sikungakuthandizeni mwauzimu, ndipo kudzakuvulazani. Khalani ochenjera. Pezani njira zabwinopo zogwiritsira ntchito nthaŵi yanu.
[Chithunzi patsamba 14]
Kodi kutaya nthaŵi mwakucheza ndiko kugwiritsira ntchito bwino nthaŵi yanu?