Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 7/8 tsamba 5-7
  • Ukwati—Chifukwa Chake Ambiri Amauthaŵa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ukwati—Chifukwa Chake Ambiri Amauthaŵa
  • Galamukani!—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nchiyani Chimachititsa Chisudzulo?
  • Kodi Ndicho Njira Yomkira ku Moyo Wachimwemwe Kwambiri?
  • Chisudzulo Chiridi ndi Minkhole
    Galamukani!—1991
  • Chisudzulo—Zotulukapo Zake Zoŵaŵa
    Galamukani!—1992
  • Mmene Kutha Kwa Banja Kumakhudzira Ana
    Mfundo Zothandiza Mabanja
  • Kuwonjezereka Kwakukulu kwa Zisudzulo
    Galamukani!—1992
Onani Zambiri
Galamukani!—1993
g93 7/8 tsamba 5-7

Ukwati—Chifukwa Chake Ambiri Amauthaŵa

POLANKHULA za chisudzulo m’Hong Kong, kumene miyambo ya Kum’maŵa ndi Kumadzulo imayendera limodzi, Asia Magazine inati: “Kusalankhulana, kusakhulupirika, mavuto a kugonana ndi kusagwirizana ndizinthu zimene kaŵirikaŵiri zimachititsa mkangano wa m’banja ponse paŵiri kwa okwatirana a ku China ndi a Kumadzulo.” Mkhalidwewo uli wofanana kwina kulikonse m’dziko.

Amuna ndi akazi omwe amene amakonda ntchito zawo amanyalanyaza mabanja awo mofulumira nayanja ntchito zawo. Motero, chotsatirapo nchakuti amatsekereza kulankhulana kwa m’banja. Atatopa ndi ntchito ya tsiku lonse, mwamuna amatengeka ndi kuŵerenga nyuzipepala. Junichi ndi mkazi wake anali ndi marestiranti atatu ndipo anagwira ntchito kuyambira 8 koloko m’maŵa mpaka 10 koloko usiku m’malo osiyanasiyana. Junichi akuvomereza kuti: “Panalibe kulankhulana kulikonse pakati pathu monga mwamuna ndi mkazi.” Kusalankhulana kumeneku kunachititsa mavuto aakulu a m’banja.

Mfundo ina imene imachititsa kusweka kwa zomangira zaukwati ndiyo mmene anthu amawonera kugonana ndi munthu wosakhala mnzawo wa muukwati. Kugonana kunja kwa ukwati tsopano kuli kofala kwakuti 20 peresenti ya amuna ndi 8 peresenti ya akazi amene anavomereza kufunsidwa m’Japan anavomereza kuti anagonana ndi anthu ena akunja kwa ukwati wawo mkati mwa chaka chapita. Yosadabwitsanso ndiyo nkhani ya mkazi wogwira ntchito wa ku Japan amene anagonana ndi amuna osiyanasiyana. Iye ankanyengana ndi amuna osiyanasiyana, namalingalira kuti, “Mwamuna wanga akatulukira nkhaniyi, ndidzangomsudzula.” Anthu amakono amanyalanyaza zinthu zimenezi.

Anthu omwewa amachilikiza mkhalidwe wamaganizo wakuti ine choyamba, kotero kuti mwamuna ndi mkazi yemwe amakhala adyera, limene limachititsa kusagwirizana, chochititsa china cha chisudzulo. “Kuyambira pachiyambi penipeni ukwati wathu unali ndi mavuto kwakuti tikanalekana nthaŵi iliyonse,” akutero Kiyoko. “Titangokwatirana kumene, mwamuna wanga anandiuza kuti ndidzivomereza zilizonse. Pamene zinthu zinamuyendera bwino, zonse zinayenda bwino, koma pamene zinthu zinavuta, anakana kuvomereza kulakwa kwake ndipo anaimba mlandu anthu ena. Nanenso ndinali ndi liŵongo, popeza kuti ndinakana kumvera ulamuliro. Ndinakupeza kukhala kovuta kumvera mwamuna wanga pamene anali kuchita zinthu mosalungama.”

Zifukwa zina zochititsa chisudzulo ndizo nkhanza ndi kuledzera, mavuto azachuma, kuvutana ndi achibale, ndi kuvutitsana maganizo.

Kodi Nchiyani Chimachititsa Chisudzulo?

Mosasamala kanthu kuti zifukwa zochititsa chisudzulo nzosiyanasiyana motani, pali kanthu kena kamene kakuchichititsa kukhala chofalikira padziko lonse. Ngakhale kuti maiko a Kum’maŵa amaimba mlandu chisonkhezero cha maiko a Kumadzulo chifukwa cha zovuta zake, chisudzulo chakhala chovomerezedwa kumaiko a Kumadzulo posachedwapa. Kwenikweni, mu United States zisudzulo zaŵirikiza katatu ndipo m’Britain zaŵirikiza kanayi m’zaka khumi zokha zapitazi. Andrew J. Cherlin wa bungwe la The Urban Institute (gulu lofufuza mavuto a kakhalidwe ndi a zachuma mu United States), ngakhale kuti akuvomereza kuti zochititsa kuwonjezeka kwa chisudzulo sizikudziŵika bwino, akundandalitsa “kudziimira m’zachuma kowonjezereka kwa akazi” ndi “kusintha kwa kulingalira kwa anthu” kukhala pakati pa zinthu zochititsa chikhotererochi.

Kwa akazi a mu United States, limodzinso ndi a m’maiko ena otukuka, kukwatiwa ndi kumagwira kwina ntchito sikulinso kwachilendo. Komabe, mbali ya ntchito zimene mwamuna amachita panyumba sinawonjezereke mofulumira. Nkosadabwitsa kuti akazi ena amadandaula kuti: “Zimene mkazi aliyense wogwira ntchito amafunitsitsa ndimunthu womchitira ntchito yake! ”

Pamene kuli kwakuti akazi amagwira ntchito zolimba kuchapa zovala, kusamalira m’nyumba, kuphika chakudya, ndi kusamalira ana, mu United States, “amuna ambiri amasangalala kuthera nthaŵi yawo ‘atangokhala,’” likutero buku lakuti The Changing American Family and Public Policy. Akatswiri a kakhalidwe ka anthu akunena kuti zimenezi zikuchitika padziko lonse. M’Japan sikwachilendo kuwona amuna akupita kocheza ataweruka kuntchito. Iwo amanena kuti kuteroko nkoyenera kaamba ka maunansi abwino kumalo awo antchito, pamene kuli kwakuti amanyalanyaza maunansi abwino panyumba. Popeza kuti amuna, malinga nkuganiza kwawo, ndiwo amene amapeza zofunika za banja, akazi ndi ana sayenera kudandaula. Komabe, pokhala ndi akazi ambiri ogwira ntchito, kulingalira koteroko kumawoneka kukhala chodzikhululukira chabe.

Mfundo ina yaikulu imene ikuchititsa kulephera kwa ukwati ndiyo “kusintha kwa mkhalidwe wamaganizo wa chitaganya” kapena, monga momwe Journal of Marriage and the Family inanenera, “kutsika kwa lingaliro la uchikhalire wa ukwati.” Kwa akwati ndi akwatibwi a m’ma 1990, lumbiro laukwati lamwambo lakuti “kufikira imfa” silimatanthauzanso zimenezo. Iwo amapitirizabe kufunafuna mnzawo wabwino kwambiri. Ngati mmenemo ndimo mmene okwatirana chatsopanowo amawonera ukwati wawo, kodi udzakhala wolimba motani?

Kusintha kwa makhalidwe kumeneku sikumadabwitsa konse ophunzira Baibulo. Buku louziridwa limeneli limavumbula kuti kuyambira 1914 takhala tili “m’masiku otsiriza,” amene ali “nthaŵi zowawitsa.” Anthu ali “odzikonda okha, . . . osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika.” (2 Timoteo 3:1-3) Chotero kwa anthu amene amadzikonda okha kwambiri kuposa anzawo, amene amakhala osayera mtima kwa anzawo amuukwati, ndi amene samayanjanitsika muukwati wawo, chisudzulo chimakhala njira yokha yothaŵira mavuto awo amuukwati.

Kodi Ndicho Njira Yomkira ku Moyo Wachimwemwe Kwambiri?

Nthaŵi zambiri, chisudzulo sichinakhale njira yomkira ku chimwemwe.a “Chisudzulo chimanyenga,” anatero wofufuza thanzi la maganizo Judith Wallerstein pambuyo pa kufufuza kwa zaka 15 pa amene anali okwatirana 60 osudzulana. “Mwalamulo ndichochitika chimodzi, koma mwamaganizo ndimpambo wa zochitika—nthaŵi zina mpambo wosalekeza—wa zochitika, kusintha malo ndi kusintha kwa maunansi kwakukulu kumene kumachitika kwa nyengo yaitali ya nthaŵi.” Kupenda kwake kunasonyeza kuti mkazi mmodzi mwa anayi ndi mwamuna mmodzi mwa asanu miyoyo yawo sinabwerere pa mkhalidwe wakale pambuyo pa zaka khumi za chisudzulo.

Makamaka ana a m’chisudzulo ndiwo amakhala paupandu waukulu. Kuchokera pakufufuza kumodzimodziko, Wallerstein anapeza kuti pafupifupi kwa ana onse oloŵetsedwamo, chisudzulo chinachititsa “ziyambukiro zamphamvu ndi zosayembekezereka kotheratu.” Ana ena amene amakana kuti alibe malingaliro alionse oipa ponena za kusudzulana kwa makolo awo mwadzidzidzi angakhale ndi malingaliro amenewo pambuyo pake m’moyo wawo pamene akufunafuna mnzawo wamuukwati.

Zimenezi sizikutanthauza kuti mikhole yonse ya chisudzulo sidzapeza konse chimwemwe, popeza kuti ena amachipeza. Kwa ameneŵa, umunthu watsopano umabuka, kaŵirikaŵiri kuchokera kuumunthu wakale. Mwachitsanzo, kuvutika maganizo ndi chisudzulo ndi chisoni chotsatirapo limodzi ndi kudziwona kukhala wopanda pake zitatha, munthu wopanda liŵongoyo angatuluke m’vutolo nakhala munthu wamphamvu kwambiri, wofunika.

Mkazi wina amene mwamuna wake anamsiya kumka kwa mkazi wina anafotokoza kuti pamene kupwetekedwa maganizo ndi mkwiyo ziyamba kutha, “umapeza kuti ndiwe munthu wina. Malingaliro ako asintha. Sungakhalenso ndi umunthu umene unali nawo papitapo.” Iye anapereka uphungu wakuti: “Patulani nthaŵi ya kuzidziŵa inu eni monga munthu kachiŵirinso. Muukwati kaŵirikaŵiri okwatiranawo amapondereza zokonda ndi zikhumbo zawo kuti zilingane ndi za mnzawo, koma pambuyo pa chisudzulo, muyenera kupeza nthaŵi ya kudziŵa zimene mumakonda ndi zimene simumakonda tsopano. Ngati mupondereza malingaliro anu, sadzatheratu. Tsiku lina adzabwerera, ndipo mudzafunikira kulimbana nawo. Chotero mungachite bwino kulimbana nawo ndi kuthana nawo.”

Chifukwa cha kudziŵa mowonjezereka mavuto amene chisudzulo chimachititsa, icho chikusiya kukhala chosankha chokopa. Magazini a Time akusimba kuti aphungu angapo owonjezereka tsopano akulimbikitsa okwatirana okhala ndi zovuta kuti: “Pitirizani kukhala pamodzi.” David Elkind wa ku Tufts University analemba kuti: “Kusudzulidwa nkofanana pang’ono ndi kuthyoka mwendo wanu pamaseŵera othamanga pa chipale chofeŵa: Mosasamala kuti ndi anthu ochuluka motani amene amathyoka miyendo yawo pamaseŵerawo, zimenezo sizimapangitsa mwendo wanu wothyokawo kusapweteka kwambiri.”

Chisudzulo sichili yankho lokhweka lothetsera mavuto amuukwati. Pamenepo, kodi ndiiti yomwe ili njira yabwino kwambiri yothetsera mavuto amuukwati?

[Mawu a M’munsi]

a Chisudzulo chalamulo kapena kulekana kwalamulo kungapereke chitetezo china kukuchitiridwa nkhanza kopambanitsa kapena kusachilikiza banja mwadala.

[Chithunzi patsamba 7]

Kaŵirikaŵiri okwatirana lerolino samalankhulana

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena