Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 10/8 tsamba 6
  • Malingaliro Olakwika Ofala

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malingaliro Olakwika Ofala
  • Galamukani!—1993
  • Nkhani Yofanana
  • Chitetezo m’Nyumba
    Galamukani!—1993
  • Tizisonyeza Chikondi ndi Chilungamo M’dziko Loipali
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Mabala Obisika a Kuchitira Nkhanza Ana
    Galamukani!—1991
  • ‘Nthaŵi ya Kuchira’
    Galamukani!—1991
Onani Zambiri
Galamukani!—1993
g93 10/8 tsamba 6

Malingaliro Olakwika Ofala

Lingaliro lolakwika: Kaŵirikaŵiri ogona ana amakhala anthu osadziŵika, anthu amisala amene amagwira ana ndi kugwiritsira ntchito mphamvu kuwagona.

M’zochitika zambiri—kuyambira 85 mpaka 90 peresenti malinga ndi kuyerekezera kwina—wogona mwana ndimunthu amene mwanayo amamdziŵa ndi kumkhulupirira. Mmalo mogwiritsira ntchito mphamvu, ogona ana nthaŵi zambiri amanyengerera mwana m’kugonana mwapang’onopang’ono, akumadyerera pachidziŵitso chochepa cha mwanayo ndi nzeru zake zochepa. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 13:11 ndi Miyambo 22:15.) Ogona ana ameneŵa sali anthu amisala amene samayanjana ndi ena. Ambiri ngopembedza kwambiri, olemekezeka, ndi okondedwa kwambiri m’chitaganya. Malinga nkunena kwa U.S. Federal Bureau of Investigation, “kulingalira kuti wina sali wokonda kugona ana kokha chifukwa chakuti ali munthu wabwino, amapita kutchalitchi, amagwira ntchito zolimba, ngwokoma mtima kwa zinyama, ndi zina zotero, nkopanda pake.” Kufufuza kwaposachedwapa kukusonyeza kuti kulinso kolakwika kulingalira kuti amene amagona ana ndiamuna okha kapena kuti onse amene amagonedwa ndiakazi okha.

Lingaliro lolakwika: Ana amangoyerekezera kapena kunama ponena za kugonedwa.

Mwachibadwa ana alibe chidziŵitso kapena luso lakugwiritsira ntchito chinyengo pankhani zakugonana zopekera mawu omveka a kugonedwa, ngakhale kuti ana ena aang’ono angasokonezeke ndi tsatanetsatane wake. Ngakhale ofufuza okayikira kwambiri amavomereza kuti zonena zambiri za kugonedwa nzenizeni. Talingalirani buku la Sex Abuse Hysteria—Salem Witch Trials Revisited, lozikidwa pa zonena zonama za nkhanza yogona ana.a Buku limeneli limavomereza kuti: “Nkhanza yeniyeni yogona ana ili yofala ndipo milandu yochuluka ya nkhanza yogona ana . . . iyenera kukhala yowona (mwinamwake ndi 95% kapena kuposapo).” Ana amakuona kukhala kovuta kwambiri kuulula kuti anagonedwa. Ngati anena bodza ponena za kugonedwa, kaŵirikaŵiri kumakhala kukana kuti kunachitika ngakhale kuti kunachitikadi.

Lingaliro lolakwika: Ana ali ndi mikhalidwe yokopa ndipo kaŵirikaŵiri amadzichititsa kugonedwa mwa mkhalidwe wawo.

Lingaliro limeneli nlopotoka kwambiri, popeza kuti, kwenikweni, limaimba mlandu wogonedwayo. Ana alibe ganizo lenileni la kugonana. Iwo sadziŵa zimene mchitidwe umenewo umatanthauza kapena mmene udzawasinthira. Chotero iwo ngosakhoza kuuvomereza mwanjira iliyonse yofunitsitsa. Ali wogona mwana yekha, iye yekhayo, amene ali ndi mlandu wa nkhanza yogona mwana.—Yerekezerani ndi Luka 11:11, 12.

Lingaliro lolakwika: Pamene ana aulula kuti agonedwa, makolo ayenera kuwaphunzitsa kusalankhula zimenezo ndi ‘kuziiŵala.’

Kodi amapindula kwambiri ndani ngati mwana akhala chete pankhani ya kugonedwa? Kodi sali wogona mwanayo? Kunena zowona, kufufuza kwasonyeza kuti kukana ndi kutsekereza kupsinjika mtima kungakhale njira yosathandiza konse yochitira ndi vuto la kugonedwa. Panjira zisanu ndi zinayi zopiririra zogwiritsiridwa ntchito ndi gulu la achikulire amene anagonedwapo paubwana lofufuzidwa ku Mangalande, amene anakana, kupeŵa, kapena kubisa nkhaniyo anakhala ndi vuto lalikulu la kusintha malingaliro ndi kupsinjika mtima kokulirapo atakula. Ngati muvulazidwa kowopsa, kodi mungakonde kuuzidwa kusanena kalikonse? Nkuuziranji mwana zimenezo? Kulola mwana kuchita mwachibadwa ndi chochitika choipa chimenecho, monga ngati kuchita chisoni, kukwiya, kulira, kudzampatsa mpata wakuchira nkhanza yakugonedwayo.

[Mawu a M’munsi]

a M’milandu ina ya chisudzulo, kwapezeka kuti mmodzi wa achikulire olimbanawo amaimba wina mlandu wa kugona ana kuugwiritsira ntchito monga chida.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena