Lingaliro la Baibulo
Kodi Tifunikiradi Ansembe?
“YAMIKANI kaamba ka mphatso ya Unsembe,” anatero John Paul II m’kalata yake yapachaka ya kwa ansembe pa “Lachinayi Lopatulika,” 1992. Akatolika kuphatikizaponso ena afika pakuzindikira momvetsa chisoni zolakwa zawo. Aona kufunika kwa munthu wina wovomerezedwa ndi Mulungu kuwauza chifuniro cha Mulungu, kupereka nsembe kwa Iye, ndi kukhala mtetezi wawo kwa Mulungu. Munthu wotero amatchedwa wansembe. Kodi tifunikiradi wansembe kutithandiza kupeza chikhululukiro cha Mulungu?
Lingaliro la ansembe ndi nsembe silinayambe ndi munthu koma linayamba ndi Mulungu. Ngati panalibe machimo ochimwira Mulungu, sipakanafunikira ansembe. Mu Edeni, munthu wangwiro Adamu sanafunikire wansembe. Analengedwa wopanda uchimo.—Genesis 2:7, 8; Mlaliki 7:29.
Kodi Ndani Anali Ansembe Oyambirira?
Tonsefe lerolino tinalandira choloŵa cha uchimo chifukwa Adamu anachimwa mwadala ndipo ndife ana ake. (Aroma 3:23) Abeli, mwana wa munthu woyambirira, Adamu, anazindikira zimenezi. Ponena za iye Baibulo limati: “Ndi chikhulupiriro Abeli anapereka kwa Mulungu nsembe.” (Ahebri 11:4) Ngakhale kuti Abeli ndi amuna ena achikhulupiriro amakedzana—onga Nowa, Abrahamu, ndi Yobu—sanatchedwe ansembe, iwo anapereka nsembe kwa Mulungu za iwo eni kapena mabanja awo. Mwachitsanzo, Baibulo limati ponena za Yobu ndi ana ake: “[Yobu] anafukiza nsembe zopsereza, monga mwa kuŵerenga kwa iwo onse; pakuti Yobu anati, Kapena anachimwa ana anga.” (Yobu 1:5) Koma, kodi ndimotani mmene ansembe ndi nsembe zinakhalira zofala m’zitaganya zambiri?
Talingalirani zochitika zokhudza kholo lamakedzana Nowa. Nowa ndi banja lake ndiwo anthu okha amene anapulumuka Chigumula cha padziko lonse. Pamene anatsikira padziko loyeretsedwa, Nowa anamanga guwa la nsembe napereka nsembe zoyamikira chifundo cha Yehova ndi dzanja lake lotetezera. Popeza kuti mitundu yonse ili mbadwa za Nowa, iwo mosakayikira anatsatira chitsanzo chake ndipo m’kupita kwa nthaŵi anayambitsa miyambo yamitundumitundu yogwirizana ndi atetezi ndi nsembe za machimo.—Genesis 10:32.
Patapita zaka zoposa zana limodzi, kupandukira Mulungu kunabuka mumzinda wa Babele. Mulungu anasokoneza chinenero cha anthu ndipo iwo anamwazikana. (Genesis 11:1-9) Ansembe ena, ochilikiza zikhulupiriro zopotoka ndi zoluluzika tsopano, anayambitsa madzoma oipa kumaiko kumene anapita. Chikhalirechobe, Mulungu anaona kufunika kwa kuphunzitsa olambira ake za kufunikira kwawo unsembe wowona wokhala ndi mkulu wa ansembe, ansembe aang’ono, ndi nsembe zovomerezedwa ndi iye.
Chifukwa Chake Mulungu Anaika Ansembe
M’kupita kwa nthaŵi Yehova anapatsa mtundu wa Israyeli ansembe amene anachita ntchito zazikulu ziŵiri. Choyamba, anaimira Mulungu pamaso pa anthu monga oweruza ndi alangizi a Chilamulo cha Mulungu. (Deuteronomo 17:8, 9; Malaki 2:7) Chachiŵiri, anaimira anthu pamaso pa Mulungu mwakupereka nsembe kwa iye mmalo mwa anthu. Kalata ya Paulo kwa Akristu Achihebri imafotokoza kuti: “Pakuti mkulu wa ansembe aliyense, wotengedwa mwa anthu, amaikika chifukwa cha anthu m’zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke mitulo, ndiponso nsembe, chifukwa cha machimo. . . . Palibe munthu adzitengera ulemuwo mwini wake, komatu iye amene aitanidwa ndi Mulungu.”—Ahebri 5:1, 4.
Paulo akupitiriza kufotokoza kuti unsembe wa Israyeli sunali njira yomalizira ya Mulungu yoyanjanitsira anthu kwa Iyemwini. Ntchito za ansembe zinali zifaniziro zosonya ku zinthu zabwino koposa, “zakumwamba.” (Ahebri 8:5) Pamene zinthu zakumwamba zimenezo zinafika, zifaniziro sizinalinso zofunikira. Mwachitsanzo: Mungasunge chilengezo chosatsa malonda a chinthu chimene mukufuna kwambiri, koma kodi simungachitaye mutagula chinthucho?
Kalekale mtundu wa Israyeli usanakhaleko, Mulungu analinganiza unsembe umene ukatumikira kudalitsa, osati Israyeli yekha, koma mtundu wonse wa anthu. Poyamba, Israyeli anapatsidwa mwaŵi wakupereka ziŵalo za unsembe umenewo. Pamene mtunduwo unapangidwa, Yehova anauza Israyeli kuti: “Ngati mudzamvera mawu anga ndithu, . . . ndidzakuyesani ufumu wanga wa ansembe, ndi mtundu wopatulika.” (Eksodo 19:5, 6; yerekezerani ndi Genesis 22:18.) Momvetsa chisoni, mtunduwo nthaŵi zambiri sunamvere mawu a Mulungu. Chotero, Yesu anauza ansembe ndi Afarisi kuti: “Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu, nudzapatsidwa kwa anthu akupatsa zipatso zake.” Kodi ndani tsopano amene adzatumikira monga ansembe kaamba ka madalitso a mtundu wa anthu?—Mateyu 21:43.
Kodi Akristu Amafunikira Unsembe Wotani?
Chifukwa chakuti tinalandira choloŵa cha uchimo kwa Adamu, chipulumutso cha kumoyo wosatha chili chotheka kupyolera m’nsembe yangwiro yoperekedwa ndi Yesu yokha. (1 Yohane 2:2) Yesu iye mwini amatitetezera monga Mkulu wa Ansembe, monga momwe anachitiridwa chithunzi ndi unsembe wa Israyeli. Pa Ahebri 9:24 pamati: “Kristu sanaloŵa m’malo opatulika omangika ndi manja, akutsanza owonawo; komatu m’mwamba momwe, kuonekera tsopano pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.” Chotero, ukulu woposa waunsembe wa Kristu umathetsa kufunikira kwa ansembe aumunthu kukhala atetezi. Komabe, mautumiki a ansembe aang’ono afunikirabe. Mwanjira yotani?
Ansembe ayenera “kupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Kristu.” (1 Petro 2:5) Ponena za mtundu wa nsembe zimenezi, Paulo analemba kuti: “Tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo.” (Ahebri 13:15) Chotero, awo amene adzapanga unsembe wachifumu, pamene akali padziko lapansi, amaimira Mulungu pamaso pa anthu monga Mboni zake, osati monga atetezi. Pambuyo pake, ali kumwamba ndi Yesu Kristu, amaimira anthu pamaso pa Mulungu, akumasamalira mapindu a nsembe ya Kristu ndi kuchiritsa matenda onse.—Yerekezerani ndi Marko 2:9-12.
Pamene kuli kwakuti okhulupirira onse ayenera kuchitira umboni, ali oŵerengeka okha amene adzatumikira mu “ufumu wa ansembe” wakumwamba. Yesu anati: “Musawopa, kagulu ka nkhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani ufumu.” (Luka 12:32; Chivumbulutso 14:1) Ameneŵa adzaukitsidwira kumwamba ndipo “adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Kristu, nadzachita ufumu pamodzi ndi iye zaka chikwizo.”—Chivumbulutso 20:6.
Mulungu walinganiza kuti ansembe akumwamba ameneŵa achite zinthu ponse paŵiri m’lingaliro lauzimu ndi lakuthupi zimene ansembe ena onse sanachitepo. Posachedwapa, pamene adzakhala akugwiritsira ntchito mapindu a nsembe ya dipo ya Yesu, adzakhoza kukhala ndi phande m’kubwezeretsa mtundu wa anthu okhulupirira ku ungwiro waumunthu. Pamenepo, lemba la Yesaya 33:24 lidzakwaniritsidwa bwino kwambiri. Limati: “Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala; anthu okhala m’menemo, adzakhululukidwa mphulupulu zawo.”
[Mawu a Chithunzi patsamba 22]
“Kudalitsa Tirigu ku Artois” 1857, ndi Jules Breton: France / Giraudon/Art Resource, N.Y.