Kodi Ndidziko Lamtundu Wanji Limene Mumafuna?
NGATI mukanakhala ndi mphamvu, kodi mukanalenga dziko latsopano, dziko lopanda mavuto onse amene amasautsa anthu lerolino? Ngati mukanachita zimenezo, kodi sikwanzeru kuyembekezera kuti Mlengi wathu wachikondi, Yehova Mulungu, amene ali nayo mphamvuyo, adzalenga dziko latsopano la chilungamo?
Baibulo limati: “Yehova achitira chokoma onse; ndi nsoni zokoma zake zigwera ntchito zake zonse. Muwolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo.” (Salmo 145:9, 16) Kodi zina za zokhumba zanu nzotani? Kodi ndidziko lamtundu wanji limene mumakhumba?
M’buku lawo lakuti A Sane and Happy Life: A Family Guide, Abraham ndi Rose Franzblau analemba kuti: “Ngati tikanati tipende anthu onse m’dziko ndi kupeza lingaliro lawo ponena za mtundu wa dziko limene tonse tingakonde kukhalamo, nkothekera kwambiri kuti tonsefe tingagwirizane pazofunika zazikulu zakutizakuti.”
Tiyeni tipende zofunika zondandalikidwa ndi madokotala ameneŵa ndi kuona ngati zili zosafanana ndi zimene mukufuna. Pamene tikuchita zimenezi, tidzaonanso ngati Mlengi wathu walonjeza kupereka zinthu zimenezizi.
Chofunika Choyamba
Madokotalawo anandandalika choyamba “dziko lopanda nkhondo.” Anthu ambiri pokhala avutika ndi nkhondo zambiri zoipitsitsa, amalakalaka dziko mmene anthu sadzamenyananso ndi kuphana. Chiyembekezo chawo chimasonyezedwa m’mawu olembedwa pachipupa cha nyumba ya United Nations Plaza mu New York City, amene amati: ADZASULA MALUPANGA AWO KUKHALA ANANGWAPE. NDI MIKONDO YAWO KUKHALA ZOLIMIRA: MTUNDU SUDZANYAMULANSO LUPANGA KUMENYANA NDI MTUNDU WINA. NDIPO SADZAPHUNZIRANSO NKHONDO.
Kodi munali kudziŵa kuti mawuwo ali mbali ya lonjezo loperekedwa ndi Yehova Mulungu? Mawuwo alembedwa m’Baibulo Lopatulika pa Yesaya chaputala 2, vesi 4, mu King James Version. Mwakuŵerenganso Salmo 46:8, 9, mudzaona kuti chili chifuniro cha Mulungu kuwononga zida zonse ndi kuletsa “nkhondo kumalekezero a dziko lapansi.” M’dziko lamtendere, lopanda nkhondo lopangidwa ndi Mulungu, ulosi wosangalatsa wa Baibulo uwu udzakwaniritsidwa: “Adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwawopsa.”—Mika 4:4.
Kodi inu simukanalemba pampambo “dziko lopanda nkhondo” monga chofunika chachikulu cha mtundu wa dziko limene mumafuna? Ndipo tangolingalirani, Mlengi wathu Wamkulu walilonjeza!
Dziko la Mwana Alirenji
Kodi nchiyani chikakhala chofunika chanu chachiŵiri? Kodi chikakhala chofanana ndi chachiŵiri choperekedwachi, “dziko lopanda njala, mmene kupereŵera ndi kusoŵa zikachotsedwa kosatha”? Kodi sikukakhala kwabwino koposa ngati pakanakhala popanda konse mwana wovutika ndi njala? Ndithudi inu mungakonde kukhala m’dziko la mwana alirenji. Koma kodi ndani amene angapereke chitsimikiziro cha zimenezi?
Talingalirani zimene Mulungu akulonjeza: ‘Dziko lapansi lidzapereka zipatso zake.’ “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka.” (Salmo 67:6; 72:16) Inde, m’dziko latsopano la Mulungu, zakudya zabwino zidzakhala zochuluka. Baibulo likutitsimikiziritsa kuti Yehova “adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okhaokha.”—Yesaya 25:6.
Ngakhale kuti dziko lopanda njala nlosatheka kudzetsedwa ndi anthu, Mulungu sangalephere kulidzetsa. Mwana wake, Yesu Kristu, anachitira chitsanzo kusonyeza kuti kugaŵira chakudya anthu onse sikudzakhala vuto mu Ufumu wa Mulungu. Pamene Yesu anali padziko lapansi, anadyetsa zikwi za anthu mwakuchulukitsa mozizwitsa mitanda ya mikate yoŵerengeka ndi tinsomba tingapo.—Mateyu 14:14-21; 15:32-38.
Dziko Lopanda Matenda
Simukapeza munthu wodwala kulikonse m’dziko limene tonsefe timafuna. Chotero chofunika chachitatu sichodabwitsa. “Likakhala dziko lopanda matenda,” analemba motero madokotalawo, “dziko mmene onse akakhala ndi mwaŵi wa kukula mwathanzi ndi kukhala moyo wawo wonse popanda matenda okhoza kutetezeredwa ndi okhoza kuchiritsidwa.”
Talingalirani za mpumulowo ngati palibe aliyense amene akadwala chimfine kapena matenda ena aliwonse! Anthu sangachotse matenda, koma Yehova Mulungu akhoza kutero. Ndipo iye akulonjeza kuti m’dziko lake latsopano “wokhalamo sadzanena, ine ndidwala.” M’malomwake, “pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilume la wosalankhula lidzaimba.” (Yesaya 33:24; 35:5, 6) Inde, Mulungu “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa.”—Chivumbulutso 21:4.
Pamene Yesu Kristu anali padziko lapansi, anapereka chitsanzo cha zimene tingayembekezere pamlingo waukulu m’dziko latsopano la Mulungu. Iye anabwezeretsa kuona kwa akhungu, anatsegula makutu a ogontha, anamasula malilime a osalankhula, anatheketsa opunduka kuyenda, ndipo ngakhale kubwezeretsa akufa kumoyo.—Mateyu 15:30, 31; Luka 7:21, 22.
Ntchito Yokhutiritsa ndi Chiweruzo Cholungama kwa Onse
Mosakayikira konse, ntchito yokhutiritsa ndi chiweruzo cholungama kwa onse zidzakhalapo m’dziko limene inuyo ndi pafupifupi munthu aliyense angafune. Chotero madokotalawo analemba kuti: “Chachinayi, chikakhala dziko lokhala ndi ntchito kwa awo okhumba kupeza njira yopezera zofunika kwa iwo ndi mabanja awo.” Ndipo anawonjezera kuti: “Chachisanu, chikakhala dziko mmene munthu aliyense akasangalala ndi ufulu pansi pa lamulo, limodzi ndi chiweruzo cholungama kwa onse.”
Ulamuliro wa anthu sunakhozepo kukwaniritsa zofunika zimenezi za moyo wachimwemwe. Koma dziko latsopano la Mulungu lidzatero. Baibulo limalonjeza ponena za ntchito yopindulitsa imene anthu adzachita panthaŵiyo kuti: “Ndipo iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. . . . Osankhidwa anga adzasangalala nthaŵi zambiri ndi ntchito za manja awo. Iwo sadzagwira ntchito mwachabe.”—Yesaya 65:21-23.
Bwanji ponena za ufulu ndi chiweruzo cholungama kwa onse? Mosasamala kanthu za mmene olamulira aumunthu ayesayesera mwakhama, iwo alephera kupereka zimenezi kwa aliyense. Chisalungamo ndi chitsenderezo zikupitirizabe kukhalapo kuzungulira dziko lonse. Motero anthu sangathe kukwaniritsa chosoŵa chimenechi. Koma Mulungu Wamphamvuyonse akhoza kutero. Wolamulira wake woikidwayo ndiye Yesu Kristu woukitsidwayo, ndipo ponena za iye Yehova akuti: “Wosankhika wanga, amene moyo wanga ukondwera naye. . . . Iye adzatulutsira amitundu [chiweruzo cholungama, NW].”—Yesaya 42:1; Mateyu 12:18.
Inde, Baibulo limalonjeza kuti pansi pa Ufumu wa Mulungu “cholengedwa chomwe chidzamasulidwa kuukapolo wa chivundi, ndi kuloŵa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21) Ha, lidzakhala dziko latsopano lachisangalalo chotani nanga pamene kudzakhala ufulu ndi chiweruzo cholungama kaamba ka onse!
Mwaŵi ndi Kupumula
Ndithudi m’dziko limene mukafuna, nzika zonse zikasangalala ndi mwaŵi wolingana mosasamala kanthu za fuko kapena mtundu. Chifukwa chake, nzosadabwitsa kuti chofunika chachikulu chachisanu ndi chimodzi chondandalikidwa ndi madokotalawo nchakuti: “Likakhala dziko mmene munthu aliyense akakhala ndi mwaŵi wa kukulitsa maluntha ake ndi maluso mokwanira, ndi kufupidwa kaamba ka zoyesayesa zake, popanda tsankho.”
Anthu sanakhozepo konse kukhazikitsa dziko mmene anthu onse anachitiridwa mwachilungamo. Tsankho ndipo ngakhale kuzunzidwa kwa mafuko aang’ono kukupitirizabe mosaletsedwa. Komabe, Mfumu ya dziko latsopano la Mulungu, Yesu Kristu, idzatsanzira chitsanzo cha Yehova, Atate wake, amene ali “wosasamalira nkhope za anthu, kapena kulandira chokometsera mlandu.” (Deuteronomo 10:17; Aroma 2:11) Chimene chidzachititsa dziko latsopanolo kukhala labwino koposa nchakuti anthu onse sadzangophunzitsidwa kokha kutsanzira kupanda tsankho kwa Yehova Mulungu komanso adzaphunzitsidwa kukuchita.—Yesaya 54:13.
Kaŵirikaŵiri miyoyo ya anthu yakhala yotopetsedwa ndi ntchito zovuta zokhala ndi mpumulo wochepa kapena zopandiratu uliwonse. Chotero mudzavomerezadi chofunika chachikulu chotsatira: “Chachisanu ndi chiŵiri, likakhala dziko mmene anthu onse ali ndi nthaŵi yakupuma yokwanira yosangalala ndi zinthu zimene amaziona kukhala zabwino m’moyo.”
Podziŵa chofunika cha munthu cha kukhala ndi nthaŵi za kupumula ndi kusanguluka, Yehova Mulungu m’Chilamulo chake chakale analola tsiku la kupumula lamlungu ndi mlungu. (Eksodo 20:8-11) Chotero, tikhoza kukhala otsimikizira kuti m’dziko lake latsopano, Mulungu adzatsimikizira kuti chofunika chathu cha kupumula ndi mitundu yabwino ya kusanguluka chakwaniritsidwa.
Mtundu wa Nzika za Dzikolo
Chofunika chotsirizira choperekedwa ndi madokotalawo chimalongosola mikhalidwe yokhala ndi awo amene akakhala mu “dziko limene tonsefe tikakonda kukhalamo.” Tawonani ngati nanunso mukuona mikhalidwe imene iwo akundandalika kukhala yofunika: “Chachisanu ndi chitatu, likakhala dziko mmene kufunika kwakukulu kukaikidwa pamikhalidwe imene imasiyanitsa munthu ndi nyama, yonga ngati luntha ndi umisiri, ulemu ndi umphumphu, chikondi ndi kukhulupirika, kudzilemekeza ndi kupanda dyera, ndi kudera nkhaŵa anthu ena.”
Kodi simukakonda kukhala m’dziko limene nzika iliyonse imasonyeza mikhalidwe yabwino ya umphumphu, chikondi, kukhulupirika, kupanda dyera, ndi kudera nkhaŵa anthu anzake? Ndithudi ili ndilo dziko limene mukufuna! Palibe olamulira aumunthu amene angakhoze kutheketsa zimenezi. Yehova Mulungu yekha ndiye angatero. Ndipo iye adzaterodi chifukwa chakuti dziko lake latsopano silili loto chabe.—Salmo 85:10, 11.
Kodi Lidzadza Liti?
Monga momwe taonera m’nkhani yapitayo, bwenzi lapamtima la Yesu Kristu linalemba kuti: “Monga mwa lonjezano lake [Mulungu] tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano mmenemo mukhalitsa chilungamo.” (2 Petro 3:13) Nthaŵi ya kukwaniritsidwa kwa lonjezo limeneli idzakhala, monga momwe Yesu ananenera, “ [m’kulenganso, NW], pamene Mwana wa munthu adzakhala pachimpando cha ulemerero wake.”—Mateyu 19:28.
Mulungu poyamba analangiza Adamu ndi Hava, okwatirana oyambirira aumunthu, kufutukula munda wa Paradaiso mmene Iye anawaika. Iye anafuna kuti abale ana ndipo limodzi nawo kupanga dziko lonse lapansi kukhala munda wokongola wa Edene. (Genesis 1:26-28; 2:7-9, 15) Ngakhale kuti Adamu ndi Hava analephera kukwaniritsa chifuno chimenechi, padzakhala kubwezeretsedwa kwa Paradaiso wa padziko lapansi m’kulenganso, pamene Kristu adzakhala akulamulira mu Ufumuwo. M’kupita kwanthaŵi, mikhalidwe ya mu Edene idzafutukulidwira padziko lonse lapansi. Chotero Mlengi wathu wachikondi adzakwaniritsa chifuno chake choyambirira cha kukhala ndi dziko lamtendere, ndi lachilungamo. Koma kodi lidzadza liti?
Kodi mumaganiza mofanana ndi ambiri amene amati, ‘Aa, lidzafika mtsogolomu koma osati m’nthaŵi ya moyo wathu.’ Komabe, kodi mudziŵa bwanji? Kodi nthaŵi yathu ino yokhala ndi mavuto adziko oposa ndi kale lonse ingakhale chizindikiro chakuti dziko latsopano la Mulungu layandikira? Kodi tingadziŵe motani?
[Chithunzi patsamba 28]
M’dziko latsopano, mudzakhala mtendere, thanzi langwiro, ndi kulemerera
[Mawu a Chithunzi]
Misona: Mwakukoma mtima kwa Hartebeespoortdam Snake and Animal Park
[Chithunzi patsamba 29]
M’dziko latsopano, anthu adzasangalala ndi ntchito yopindulitsa
[Chithunzi patsamba 30]
M’dziko latsopano, mudzakhala nthaŵi ya machitachita a kupumula