Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 11/8 tsamba 16-20
  • Kodi Yehova ndi Mulungu Wankhondo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Yehova ndi Mulungu Wankhondo?
  • Galamukani!—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ziweruzo Zakale
  • Nkhondo za Mulungu Zinali Zofunika Kaamba ka Mtendere
  • Miyezo ya Yehova Imachirikiza Mtendere
  • Zilango za Mulungu Kodi Zimasonyeza Kuti Ndi Wankhanza?
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Konzekerani Kaamba ka Chipulumutso Kuloŵa M’dziko Latsopano
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • N’chifukwa Chiyani Mulungu Anawononga Akanani?
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Galamukani!—1993
g93 11/8 tsamba 16-20

Lingaliro la Baibulo

Kodi Yehova ndi Mulungu Wankhondo?

OŴERENGA Baibulo ena aimba mlandu Yehova kwanthaŵi yaitali wa kukhala mulungu wankhondo, ndi wokondweretsedwa kukhetsa mwazi. Mwachitsanzo, George A. Dorsey, m’buku lake lakuti The Story of Civilization—Man’s Own Show, amanena kuti Mulungu wa Baibulo, Yehova, “ndiye Mulungu wa ofunkha, wa ozunza, wa anthu ankhondo, wa chigonjetso, wa chilakolako chilichonse chankhanza.” Wosuliza Baibulo Roland H. Bainton akunena mosapita m’mbali kuti: “Nkhondo imakhala yabwinopo ngati Mulungu apatulidwamo.”

Kodi Yehova ndi Mulungu wankhondodi? Kodi iye, monga momwe ena amanenera, amakondwereradi kupha anthu opanda chifukwa?

Ziweruzo Zakale

Zowonadi, Baibulo limasimba mosabisa za ziweruzo zazikulu zakale za Yehova Mulungu. Komabe, izo nthaŵi zonse zinali zolanga anthu osapembedza Mulungu. Mwachitsanzo, kunali kokha kufikira pamene dziko lapansi la m’tsiku la Nowa “linadzala ndi chiwawa” pamene Yehova anati: “Ine ndidzadzetsa chigumula cha madzi padziko lapansi, kuti chiwononge zamoyo zonse, mmene muli mpweya wa moyo.” (Genesis 6:11, 17) Ponena za chiweruzo china, chinachitika kokha chifukwa chakuti mizinda ya Sodomu ndi Gomora “idadzipereka kudama ndi kutsata zilakolako zonyansa” zimene zinachititsa Mulungu “kuvumbitsa sulfure ndi moto.”—Yuda 7, The New Berkeley Version; Genesis 19:24.

Kodi Mulungu anakondweretsedwa ndi kuwononga zamoyo m’nthaŵi ya Nowa? Kapena kodi iye anapeza chikondwerero chankhanza m’kuwononga nzika za Sodomu ndi Gomora? Kaamba ka yankho, tiyeni tiyang’ane pazochitika za m’tsiku la Chigumula cha Nowa. Litanena kuti Mulungu akawononga anthu oipa pankhope ya dziko kuti achotsere dziko lapansi chiwawa, Baibulo limati: “Yehova . . . anavutika m’mtima mwake.” Inde, kunamvetsa chisoni Mulungu kuti “ndingaliro zonse za maganizo a mitima yawo [anthuwo] zinali zoipabe zokhazokha.” Chifukwa chake, kuti apulumutse anthu ambiri monga momwe kukanathekera ku Chigumula chomayandikiracho, Mulungu anatuma Nowa, “mlaliki wa chilungamo,” kuti alengeze uthenga wachenjezo ndi kumanga chingalaŵa chopulumukiramo.—Genesis 6:5-18; 2 Petro 2:5.

Mofananamo, asanatumize angelo kukawononga Sodomu ndi Gomora, Mulungu anati: “Ndikulingalira kutsika ndi kukaona ngati achita zinthu zonse zimene zanenedwa m’kulira motsutsana nawo . . . ndatsimikiza kuti ndidziŵe.” (Genesis 18:20-32, The Jerusalem Bible) Yehova anatsimikizira Abrahamu (amene Loti mwana wa mbale wake anali kukhala mu Sodomu) kuti ngati Iye atafufuza napeza anthu khumi okha olungama, mizindayo sikawonongedwa. Kodi Mulungu amene amakondwera ndi kukhetsa mwazi akakhala ndi kudera nkhaŵa kwachifundo kotero? Mosiyana ndi zimenezo, kodi sitinganene kuti umodzi wa mikhalidwe yaikulu ya umunthu wa Yehova ndiwo chifundo? (Eksodo 34:6) Iye mwiniyo amati: “Sindikondwera nayo imfa ya woipa, koma kuti woipa aleke njira yake, nakhale ndi moyo.”—Ezekieli 33:11.

Ziweruzo zowopsa zochokera kwa Mulungu nthaŵi zonse zakhalapo chifukwa chakuti anthu oipa akana mouma khosi kuleka njira yoipa, osati chifukwa chakuti Yehova amakondwerera kupha anthu. Koma inu mungafunse kuti, ‘Kodi Yehova sanalimbikitse Aisrayeli kuchita nkhondo ndi Akanani ndi kuwawononga?’

Nkhondo za Mulungu Zinali Zofunika Kaamba ka Mtendere

Mbiri imasonyeza mkhalidwe wa moyo wosakondweretsa wa Akanani—iwo anali oipa kwambiri. Kulambira mizimu, kupereka nsembe za ana, chiwawa chauchiwanda, ndi mipangidwe yosiyanasiyana ya kulambira kugonana koluluzika zinali zinthu zofala. Monga Mulungu wa chiweruzo cholungama amene amafuna kudzipereka kotheratu, Yehova sakanalola michitidwe yonyansa imeneyi kudodometsa mtendere ndi chisungiko cha anthu opanda liŵongo, makamaka Israyeli. (Deuteronomo 5:9) Mwachitsanzo, tayerekezerani ngati m’chitaganya chimene mumakhala munalibe apolisi olemekezeka kapena asilikali osungitsa malamulo a dziko—kodi zimenezo sizikanachititsa kusalamulirika kwa zinthu ndi chiwawa choipa kwambiri? Mofananamo, Yehova anaumirizika kulanga Akanani chifukwa cha mkhalidwe wawo woluluzika ndi ngozi yeniyeni imene inalipo pakulambira koyera. Chifukwa chake, iye analamula kuti: “Dziko lomwe lidetsedwa; chifukwa chake ndililanga.”—Levitiko 18:25.

Chiweruzo cholungama cha Mulungu chinaperekedwa pamene magulu ankhondo akupha a Mulungu—magulu ankhondo a Israyeli—anawononga Akanani. Chenicheni chakuti Mulungu anasankha kugwiritsira ntchito anthu kupereka chilango chimenechi, mmalo mwa moto kapena chigumula, sichinachepetse chilangocho. Motero, pamene anali kumenyana ndi mitundu isanu ndi iŵiri ya Kanani, magulu ankhondo a Israyeli analamulidwa kuti: “Musasiyepo chamoyo chilichonse cha kupuma.”—Deuteronomo 20:16.

Komabe, monga wolemekeza moyo, Mulungu sanapereke chilango cha kupha mosasankha. Mwachitsanzo, pamene nzika za mumzinda wina wa Akanani, Gibeoni, zinapempha kuchitiridwa chifundo, Yehova anavomera. (Yoswa 9:3-27) Kodi mulungu wa nkhondo wankhanza akanachita zimenezi? Ayi, koma Mulungu amene amakonda mtendere ndi chiweruzo cholungama akatero.—Salmo 33:5; 37:28.

Miyezo ya Yehova Imachirikiza Mtendere

Mobwerezabwereza, Baibulo limagwirizanitsa madalitso a Mulungu ndi mtendere. Zimenezo zili chifukwa chakuti Yehova amakonda mtendere, osati nkhondo. (Numeri 6:24-26; Salmo 29:11; 147:12-14) Chifukwa chake, pamene Mfumu Davide analakalaka kumanga kachisi wolambiriramo Yehova, Mulungu anamuuza kuti: “Sudzamangira dzina langa nyumba, popeza wakhetsa pansi mwazi wambiri pamaso panga.”—1 Mbiri 22:8; Machitidwe 13:22.

Pamene anali padziko lapansi, Davide Wamkuluyo, Yesu Kristu, analankhula za nthaŵi pamene kukonda kwa Mulungu chiweruzo cholungama sikukamlola kulekerera kuipa kumene kulipoku kumene timaona. (Mateyu 24:3, 36-39) Monga momwe anachitira m’tsiku la Chigumula cha Nowa ndi pachiwonongeko cha Sodomu ndi Gomora, posachedwa Mulungu adzapereka chiweruzo cha kuchotsa anthu adyera, oipa, padziko lapansi, motero akumatsegulira njira mikhalidwe yamtendere kuti ikhalepo pansi pa ulamuliro wa Ufumu wake wakumwamba.—Salmo 37:10, 11, 29; Danieli 2:44.

Mwachionekere, Yehova sali mulungu wankhondo amene amafuna kuona mwazi. Komanso, samalekerera kupereka chilango cha chiŵeruzo cholungama pamene chili chofunika. Chikondi cha Mulungu cha ukoma chimafuna kuti achitepo kanthu kaamba ka awo amene amamkonda mwa kuwononga dongosolo loipa limene limawapondereza. Pamene achita motero, mtendere weniweni udzafalikira padziko lonse pamene ofatsa mowona mtima adzalambira mogwirizana Yehova, “Mulungu wamtendere.”—Afilipi 4:9.

[Mawu a Chithunzi patsamba 20]

Davide ndi Goliati/The Doré Bible Illustrations/Dover Publications, Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena