Lingaliro la Baibulo
Kodi Chikhululukiro cha Mulungu Nchotheratu Motani?
“Ndimalingalira kuti Mulungu sadzakhululukira konse machimo anga. Sadzandifunanso chifukwa cha zimene ndinachita.”—Gloria.
GLORIA sanapeze vuto pouza ena kuti Yehova akhoza kukhululukira machimo awo.a Koma pamene analingalira za zolakwa zake, Gloria anadziona kukhala wodetsedwa. Chikhululukiro cha Yehova chinaoneka kukhala chosatheka.
Kuzindikira mchitidwe woipa kapena njira yolakwa ya moyo kungavutitse chikumbumtima. “Ndinatopa ndi kulira tsiku lonse,” analemba motero Davide atachimwa. “Mphamvu yanga inatheratu.” (Salmo 32:3, 4, Today’s English Version; yerekezerani ndi Salmo 51:3.) Mokondweretsa, Yehova amasangalala ndi kukhululukira cholakwa. Iye ali wokonzekera ‘kukhululukira.’—Salmo 86:5; Ezekieli 33:11.
Komabe, Yehova amaona mtima. Chikhululukiro chake sichimadalira pa malingaliro wamba. (Eksodo 34:7; 1 Samuel 16:7) Wochimwayo ayenera kuvomereza poyera cholakwa chake, akumasonyeza chisoni chenicheni, ndi kuleka njira yake yoipa monga chinthu chonyansa ndi chodetsa mtima. (Salmo 32:5; Aroma 12:9; 2 Akorinto 7:11) Ndipokhapo pamene wochita cholakwa angakhululukiridwe ndi kukhala ndi “nyengo za kutsitsimutsa” zochokera kwa Yehova.—Machitidwe 3:19.
Koma ngakhale pambuyo pa kulapa, ena amadzimva kukhala odetsedwabe. Kodi ayenera kupitirizabe kukhala a liŵongo? Kodi ndichitonthozo chotani chimene chingapezedwe m’Baibulo kwa awo amene alapa machimo awo nawaleka, koma namavutikabe mtima?—Salmo 94:19.
Kuchotsa Mlandu
Atapsinjika mtima ndi zolakwa zake, Davide anapemphera kwa Yehova kuti: “Penyani mazunzo anga ndi zovuta zanga; ndipo khululukirani zolakwa zanga zonse.” (Salmo 25:18) Panopa Davide anapempha kuti Yehova achite zoposa kukhululukira. Anapempha kuti Yehova ‘akhululukire’ machimo ake, kuti achotse kapena kunyamula, kuchotsapo. Tchimo limakhala ndi zotsatirapo zoŵaŵa, ndipo mosakayikira zimenezi zinaphatikizapo mtolo wa chikumbumtima chosautsika pa Davide.
Chaka chilichonse Aisrayeli anakumbutsidwa moona ndi maso kuti Yehova anakhoza kuchotsa machimo a mtunduwo. Pa Tsiku Lachitetezo, mkulu wansembe anaika manja ake pamutu wa mbuzi, anaulula machimo a anthu pa iyo, ndiyeno anatumiza mbuziyo kutali m’chipululu. Aliyense wokhalapo anaona m’maganizo kuchotsedwa kwa machimo a mtunduwo.—Levitiko 16:20-22.
Motero, anthu olapa machimo awo angapeze chitonthozo mwa zimenezo. Zochitika za pa Tsiku Lachitetezo zinachitira chithunzi makonzedwe aakulu koposa ochotsera machimo—nsembe ya dipo ya Yesu Kristu. Yesaya analemba molosera ponena za Yesu kuti: “Ananyamula machimo a ambiri.” (Yesaya 53:12) Chifukwa chake, machimo akale safunikira kuvutitsa chikumbumtima. Koma kodi Yehova adzakumbukira machimo amenewo panthaŵi ina mtsogolo?
Kufafaniza Mangaŵa
M’pemphero lake lachitsanzo, Yesu anati: “Mutikhululukire mangaŵa athu.” (Mateyu 6:12) Liwu Lachigiriki lotembenuzidwa panopa kuti “mutikhululukire” ndilo mtundu wa verebu wotanthauza kuti “chotsani.” Motero, kukhululukira machimo kumafaniziridwa ndi kuchotsa, kapena kufafaniza, mangaŵa.—Yerekezerani ndi Mateyu 18:23-35.
Petro anakulitsa mfundo imeneyi pamene anati: “Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu.” (Machitidwe 3:19) “Kufafaniza” kumatanthauza kuwononga, kapena kusakaziratu. Kumapereka lingaliro la kufufuta chinthu cholembedwa, kufafaniza mangawa akale.—Yerekezerani ndi Akolose 2:13, 14.
Chifukwa chake, awo amene alapa safunikira kuwopa kuti Mulungu adzafuna malipiro a mangaŵa amene wawafafaniza kale. Iye akunena kuti: “Sindidzakumbukira machimo ako.” (Yesaya 43:25; Aroma 4:7, 8) Kodi zimenezi zimatanthauzanji kwa wochimwa wolapa?
Kuchotsa Banga
Kupyolera mwa mneneri Yesaya, Yehova anati: “Ngakhale zoipa zanu zili zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale zili zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbu.”—Yesaya 1:18.
Zoyesayesa za kuchotsa banga lothimbirira pa chovala kaŵirikaŵiri zimalephera. Molimbikira kwambiri, bangalo limatumbuluka koma limaonekerabe. Kuli kotonthoza chotani nanga kudziŵa kuti Yehova akhoza kusanduliza machimo ofiira kukhala oyera ngati matalala.—Yerekezerani ndi Salmo 51:7.
Chotero, wochimwa wolapa safunikira kumva kuti ali ndi banga kwa moyo wake wonse. Yehova samafafaniza pang’ono chabe zolakwa, akumachititsa wolapayo kukhala ndi manyazi osatha.—Yerekezerani ndi Machitidwe 22:16.
Chichirikizo Chochokera kwa Ena
Ngakhale kuti Yehova amachotsa mlanduwo, kufafaniza mangawa, ndi kuchotsa banga la uchimo, wolapayo panthaŵi zina angavutitsidwebe ndi chisoni. Paulo analemba ponena za wochimwa wolapa mumpingo wa ku Korinto amene anakhululukiridwa ndi Mulungu koma amene ‘akanamizidwa ndi chisoni [“kukhala wachisoni kwambiri kwakuti nkulekeratu,” TEV].’—2 Akorinto 2:7.
Kodi munthu wotere akanathandizidwa motani? Paulo akupitiriza kuti: “Mumtsimikizire ameneyo chikondi chanu.” (2 Akorinto 2:8) Liwu limene Paulo anamasulira kuti “mumtsimikizire” ndiliwu lalamulo lotanthauza “kuyeneretsa.” Inde, olapa amene ali ndi chikhululukiro cha Yehova amafunikiranso chiyenerero, kapena chivomerezo, chochokera kwa Akristu anzawo.
Momvekera bwino, zimenezi zingatenge nthaŵi. Munthu wolapayo ayenera kufafaniza chitonzo cha tchimo lake ndi kupanga mbiri yokhutiritsa ya chilungamo. Ayenera kupirira moleza mtima ndi malingaliro a anthu ena amene anakhudzidwa mwachindunji ndi zolakwa zake zakalezo. Pakali pano, ayenera kukhala ndi chidaliro m’chikhululukiro chotheratu cha Yehova, monga momwe anakhalira Davide amene anati: “Monga kummawa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo [Yehova] anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu.”—Salmo 103:12.
[Mawu a M’munsi]
a Dzina lasinthidwa.
[Mawu a Chithunzi patsamba 29]
Return of the Prodigal Son kojambulidwa ndi Rembrandt: Scala/Art Resource, N.Y.