Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 6/8 tsamba 3-8
  • ‘Anakumbukira Mlengi Wake Masiku a Unyamata Wake’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Anakumbukira Mlengi Wake Masiku a Unyamata Wake’
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Anali Wosagonjera—Anakana Mwazi!
  • Mu Bwalo Lamilandu Lalikulu Koposa la Newfoundland
  • “Chonde Lemekezani Ine ndi Zofuna Zanga”
  • Chigamulo—Adrian ndi Wachichepere Wokhwima Maganizo
  • Uthenga wa Adrian kwa Woweruza Wells
  • Asanaphunzire ndi Ataphunzira Mfundo za m’Baibulo Zinamusintha
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Yendani Monga Momwe Mwalangizidwa ndi Yehova
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kupulumutsa Moyo ndi Mwazi—Motani?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Mwazi
    Kukambitsirana za m’Malemba
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 6/8 tsamba 3-8

‘Anakumbukira Mlengi Wake Masiku a Unyamata Wake’

“NTHAŴI zonse Adrian anali kukopa chidwi cha makolo choposa gawo lake,” anatero bambo wake. “Pa msinkhu wa zaka zinayi anagunditsa kumtengo galimoto la banja, akumachititsa aliyense kuchedwa ku msonkhano wampingo. Pamene anali ndi zaka zisanu anasonkhanitsa achule ambirimbiri nawabweretsa m’nyumba. Kunatenga masiku ambiri kuchotsa zinthu zimenezo. Tinadziona ngati banja la Aaigupto m’nthaŵi ya mliri wa achule a m’Baibulo.

“Pamene anali ndi zaka 11, anapeza ma raccoon atatu aang’ono m’mphepete mwa msewu ndipo anapita nawo kusukulu m’chola chake cha mabuku. Pamene mphunzitsi analoŵa m’kalasi, anapeza muli phokoso—ana atawunjikana mozinga chola cha mabuku cha Adrian, akumalankhula mokondwa. Mphunzitsiyo anayang’ana, naona ma raccoon, ndipo anamtenga pa galimoto limodzi ndi ziŵeto zake kupita kumalo kumene kunali kusungidwa zinyama zamasiye. Adrian analira pamene analingalira za kusiyana ndi ana akewo, koma pambuyo poyendera malowo ndi kuona ana a nkhandwe ndi zinyama zina zamasiye zikusamaliridwa bwino, anasiya ma raccoon akewo kumeneko.”

Bambo wake anapitiriza kuti: “Adrian sanali mnyamata woipa. Anali kokha wotanganidwa kwambiri. Malingaliro aumoyo amene anachititsa moyo kukhala wosangalatsa.”

Amayi ake a Adrian anasonyeza mbali yake ina—wokonda banja, wokonda kukhala panyumba, mnyamata wachikondi kwambiri. Iwo akusimba kuti: “Ana a sukulu anamufotokoza kukhala munthu amene sakanavulaza aliyense. Mtsikana wina wa m’kalasi mwake anali ndi nzeru zochepa ngakhale kuti sanali wolemala maganizo. Anali kukwera basi ya sukulu ndi Adrian. Ana ena anali kumseka, koma amayi ake anatiuza kuti nthaŵi zonse Adrian anachitira mwana wawo wamkazi mwaulemu ndi chifundo chapadera. Anali ndi mbali yake yamphamvu—mnyamata wolingalira kwambiri wokhala ndi malingaliro ozama amene sanawafotokoze kaŵirikaŵiri. Koma pamene anatero, anatidabwitsa ndi ndemanga zofika pa phata penipeni pa nkhani.”

Iwo anamaliza kufotokoza za mwana wawo kuti: “Matenda ake anamchititsa kukula mofulumira ndi kukulitsa mkhalidwe wauzimu wakuya mwa iye.”

Anali Wosagonjera—Anakana Mwazi!

Matenda ake? Inde. Anayamba mu March 1993, pamene Adrian anali ndi zaka 14. Chotupa chokula mofulumira chinapezedwa m’mimba mwake. Madokotala anafuna kuchita biopsy koma anaopa kuti angakhe mwazi wochuluka ndipo anati angafunikire kuthiridwa mwazi. Adrian anakana. Iye anali wosagonjera. Misozi ili m’maso, iye anati: “Sindingadzilemekeze ngati ndipatsidwa mwazi.” Iye ndi banja lake anali Mboni za Yehova, zimene zimakana kuthiridwa mwazi pa maziko a Baibulo olembedwa pa Levitiko 17:10-12 ndi Machitidwe 15:28, 29.

Pamene anali mu Dr. Charles A. Janeway Child Health Centre mu St. John’s, Newfoundland, akudikirira biopsy—yoti ichitidwe popanda mwazi—Adrian anafunsidwa ndi katswiri wa zotupa Dr. Lawrence Jardine kufotokoza malingaliro ake pa nkhani ya mwazi.

Adrian anati, “Taonani, sizikananunkha kanthu kuti kaya makolo anga anali Mboni za Yehova kapena ayi. Sindikanalandirabe mwazi.”

Dr. Jardine anafunsa kuti, “Kodi ukudziŵa kuti ukhoza kufa ngati suvomera kuthiridwa mwazi?”

“Inde.”

“Ndipo uli wokonzekera kuchita zimenezo?”

“Ngati ndizo zimene ziti zichitike.”

Amayi ake, omwe analipo, anafunsa kuti, “Kodi nchifukwa ninji ukutenga kaimidwe kotero?”

Adrian anayankha nati: “Amayi, sichinthu chabwino. Kusamvera Mulungu ndi kutalikitsa moyo wanga ndi zaka zoŵerengeka tsopano ndiyeno chifukwa cha kusamvera kwanga Mulungu kutaya mwaŵi wa kuukitsidwa ndi kukhala ndi moyo kosatha m’dziko lake lapansi la paradaiso—nzopanda nzeru zimenezo!”—Salmo 37:10, 11; Miyambo 2:21, 22.

Biopsy inachitidwa pa March 18. Inasonyeza kuti Adrian anali ndi chotupa chachikulu cha lymphoma. Biopsy ya mafuta a m’fupa yotsatirapo inatsimikizira nkhaŵa yakuti anali ndi leukemia. Tsopano Dr. Jardine analongosola kuti programu yamphamvu kwambiri ya chemotherapy yotsagana ndi kuthiridwa mwazi inali njira yokha imene Adrian mwinamwake angakhalire ndi moyo. Komabe, Adrian, anakana kuthiridwa mwazi. Chemotherapy inayambidwa, popanda kuthira mwazi.

Komabe tsopano, anali ndi nkhaŵa yakuti chifukwa cha mankhwala amphamvu amene anali kuperekedwawo, Child Welfare Department ingaloŵererepo ndi kupatsidwa mphamvu ndi bwalo lamilandu ya kuyang’anira ndi ya ulamuliro wa kuthira mwazi. Lamulo limalola aliyense wa zaka 16 kapena kuposa pamenepo kupanga chosankha chake cha mankhwala. Njira yokha imene aliyense wosafika zaka 16 angakhalire ndi kuyenera kumeneko ndiyo kuikidwa m’gulu la achichepere okhwima maganizo.

Mu Bwalo Lamilandu Lalikulu Koposa la Newfoundland

Chotero pa Sande m’maŵa, July 18, mkulu wogwirizira wa Child Welfare anakasuma nkhaniyo ku bwalo lamilandu kuti apeze mphamvu ya kuyang’anira. Mofulumira, loya wotchuka ndi wolemekezedwa kwambiri, David C. Day, Q.C., wa ku St. John’s, Newfoundland, analembedwa ntchito kuimira Adrian. Masana amodzimodziwo pa 3:30, Bwalo Lamilandu Lalikulu Koposa la Newfoundland linakomana, Woweruza Robert Wells akumatsogolera.

Mkati mwa chigawo cha masanacho, Dr. Jardine anauza woweruzayo momvekera bwino kwambiri kuti analingalira Adrian kukhala wachichepere wokhwima maganizo amene anali ndi chitsimikizo champhamvu chotsutsa kugwiritsira ntchito mwazi ndi kuti iye, Dr. Jardine, anali atalonjeza Adrian kuti sadzaphatikiza kuthira mwazi m’mankhwala alionse. Woweruza Wells anafunsa dokotalayo kuti ngati bwalo lamilandu linalamula kuti athire mwazi, kodi akauthira? Dr. Jardine anayankha kuti: “Ayi, ine mwinine sindingatero.” Iye ananena kuti Adrian analingalira kuti chiyembekezo chake cha Baibulo cha moyo wamuyaya chikaikidwa paupandu. Umboni woona mtima wa dokotala wapadera ameneyu unali wodabwitsa ndi wotonthoza mtima ndipo unadzetsa misozi ya chisangalalo kwa makolo a Adrian.

“Chonde Lemekezani Ine ndi Zofuna Zanga”

Pamene bwalo lamilandulo linakumananso pa Lolemba, July 19, David Day anapereka makope a lumbiro lolembedwa limene Adrian—wodwala kwambiri kosakhoza kufika kubwalo lamilandu—analemba ndi kusaina akumanena za zofuna zake ponena za mankhwala a kansa yake popanda mwazi kapena zinthu zamwazi. Mu ilo Adrian anati:

“Ukamadwala umaganiza kwambiri za zinthu, ndipo ngati ukudwala kansa, umadziŵa kuti ukhoza kufa ndipo umaganiza za zimenezo. . . . Sindidzavomera kuthiridwa mwazi kapena kulola kuti ugwiritsiridwe ntchito; kutalitali. Ndidziŵa kuti ndikhoza kufa ngati mwazi sugwiritsiridwa ntchito. Koma chimenecho ndicho chosankha changa. Palibe amene anandiumiriza kuchita zimenezo. Ndimadalira kwambiri Dr. Jardine. Ndikhulupirira kuti ndi munthu amene amasunga lonjezo lake. Iye anati adzandipatsa mankhwala amphamvu popanda kugwiritsira ntchito konse mwazi. Anandiuza maupandu ake. Ndikudziŵa zimenezo. Ndikudziŵa za zoipa zimene zingachitike. . . . Ndikuganiza kuti ngati ndipatsidwa mwazi uliwonse kuteroko kudzakhala ngati kundigwirira chigololo, kuipitsa thupi langa. Sindikufunanso thupi langa ngati zimenezo zichitika. Sindingathe kupirira zimenezo. Sindikufuna mankhwala alionse ngati mwazi udzagwiritsiridwa ntchito, ngakhale kuthekera kwake. Ndikukana kugwiritsira ntchito mwazi.” Lumbiro lolembedwa la Adrian linatha ndi dandaulo ili: “Chonde lemekezani ine ndi zofuna zanga.”

Nthaŵi yonse ya kuzenga mlanduko Adrian anabindikiritsidwa m’chipinda chake cha m’chipatala, ndipo Woweruza Wells mokoma mtima kwambiri anabwera kudzamuona kumeneko, ali ndi David Day. Posimba za tsatanetsatane wa kufunsana kumeneko, a Day analankhula za kukopa ndi ndemanga zogwira mtima za Adrian kwa woweruzayo pa nkhani imodzimodziyi, kwakukulukulu akumati: “Ndidziŵa kuti ndikudwala kwambiri, ndipo ndidziŵa kuti ndikhoza kufa. Anthu ena ogwira ntchito za mankhwala akunena kuti mwazi udzathandiza. Sindikuganiza choncho, polingalira za maupandu onse amene ndaŵerenga ponena za uwo. Kaya umathandiza kapena ayi, chikhulupiriro changa chimatsutsa mwazi. Lemekezani chikhulupiriro changa ndipo mudzandilemekeza. Ngati simulemekeza chikhulupiriro changa, ndidzadzimva kukhala wolakwiridwa. Ngati mulemekeza chikhulupiriro changa, ndingayang’anizane ndi matenda anga mwaulemu. Chikhulupiriro ndicho chokha chimene ndili nacho, ndipo tsopano ndi chinthu chofunika kwambiri chimene ndikufunikira kuti chindithandize kulimbana ndi nthendayi.”

A Day anali ndi ndemanga zina za iwo okha ponena za Adrian: “Iye anali munthu wokhoza kuchita ndi matenda ake owopsawo moleza mtima, mwamphamvu, ndi molimba mtima. M’maso mwake munali kutsimikiza mtima; liwu lake linali lachidaliro chotheratu; kachitidwe kake kanali kopanda mantha. Koposa zonse, kalankhulidwe ndi kachitidwe kake zinandiuza kuti ali ndi chikhulupiriro champhamvu. Chitsimikiziritso chake chinali chikhulupiriro. Matenda osachiritsika anamfunikiritsa kulunzanitsa maloto aunyamata ndi moyo wauchikulire. Chikhulupiriro chinamthandiza kuchita zimenezo. . . . Iye mosazengereza anali woona mtima ndipo, m’maganizo mwanga, anali wonena zoona. . . . Ndinadziŵa kuti mwina makolo ake [anamuumiriza] kukana kwawo kugwiritsira ntchito mwazi pompatsa chithandizo cha mankhwala. . . . Ndinali wokhutira [kuti] anasonyeza maganizo ake mwa kulongosola chikhumbo chake cha chithandizo cha mankhwala opanda mwazi.”

Panthaŵi ina a Day ananena za zikhulupiriro za Adrian “zimene zinali za pamtima kwa iye kuposa moyo weniweniwo” ndiyeno anawonjezera kuti: “Mnyamata wochirimika ameneyu, poyang’anizana ndi mavuto oterowo, amandichititsa kulingalira kuti mavuto onse a moyo wanga si kanthu. Iye adzakhala m’maganizo mwanga kosatha. Iye ali wachichepere wokhwima maganizo wokhala ndi kulimba mtima kwakukulu, chidziŵitso, ndi nzeru.”

Chigamulo—Adrian ndi Wachichepere Wokhwima Maganizo

Pa Lolemba, July 19, mlanduwo unatha, ndipo Woweruza Wells anapereka chigamulo chake, chimene chinafalitsidwa pambuyo pake mu Human Rights Law Journal, September 30, 1993. Zigawo zake zikutsatira pansipa:

“Pa zifukwa zotsatirazi, mapempho a Mkulu wa Child Welfare akanidwa; mwanayo sakufunikira chitetezo; kugwiritsira ntchito mwazi kapena zinthu zamwazi kaamba ka kuthira mwazi kapena jekeseni sikunasonyezedwe kukhala kofunikira, ndipo m’mikhalidwe yapadera ya nkhani imeneyi, kungakhale kovulaza.

“Kusiyapo kokha ngati kusintha kwa mikhalidwe kukafunikiritsa kupereka lamulo lina, kugwiritsira ntchito mwazi kapena zinthu zamwazi m’mankhwala ake kwaletsedwa: ndipo mnyamatayo walengezedwa kukhala wachichepere wokhwima maganizo amene chikhumbo chake cha kulandira chithandizo cha mankhwala popanda mwazi kapena zinthu zamwazi chiyenera kulemekezedwa. . . .

“Palibe chikayikiro chakuti ‘munthu wachichepere’ ameneyu ndi wolimba mtima kwambiri. Ndiganiza kuti ali ndi chichirikizo cha banja lachikondi ndi losamalira, ndipo ndiganiza kuti akuyang’anizana ndi nthenda yake molimba mtima kwambiri. Mbali ina ya chikhulupiriro chake chachipembedzo n’njakuti nkolakwa kwa iye kugwiritsira ntchito zinthu zamwazi mwa kuziloŵetsa m’thupi mwake, mosasamala kanthu za zolinga zake . . . Ndinali ndi mwaŵi wakuŵerenga lumbiro lolembedwa limene linapangidwa ndi A. dzulo, ndipo ndinali ndi mwaŵi wakumvetsera kwa amayi ake, amene anapereka umboni, ndi kulankhula ndi A. mwiniyo.

“Ndili wokhutira kuti amakhulupirira ndi mtima wake wonse kuti kutenga mwazi kukakhala kulakwa ndi kuti kukakamizidwa kutenga mwazi m’nkhani imene tikulankhulayi kukakhala kuloŵerera thupi lake, kumloŵerera mseri, ndi kumloŵerera iye monga munthu payekha, kwakuti kukakhala ndi chiyambukiro choipa kwambiri pa nyonga yake ndi mphamvu ya kulimbana ndi vuto lowopsa lomwe ayenera kulipyola, mosasamala kanthu za zotsatirapo zake.

“Ndikuvomereza kuti dokotalayo ananena zanzeru kwambiri pamene ananena kuti wodwala ayenera kukhala wogwirizanika ndi woganiza bwino polandira chemotherapy ndi mankhwala ena a kansa kuti pakhale chiyembekezo chilichonse, chiyembekezo chotsimikizirika chilichonse, cha chipambano, ndi kuti wodwala amene akukakamizidwa kanthu kena mosemphana ndi zikhulupiriro zake zamphamvu adzakhala wodwala amene kuyenerera kwake mankhwalawo kudzachepetsedwa kwambiri. . . .

“Ndikuganiza kuti zimene zachitika kwa A. zamkhwimitsa ku ukulu wosalingalirika kukhala wa munthu wazaka 15 amene sakuyang’anizana ndi kukhala ndi zimene akukumana nazo ndi amene ayenera kuyang’anizana ndi zimene akukumana nazo. Ndiganiza kuti chokumana nacho chake nchoipa kwambiri chomwe ndingalingalire, ndipo ndikulingalira kuti chikhulupiriro chawo ndi chinthu chimodzi chimene chikuchirikiza iye ndi banja lake. Ndiganiza kuti zimene zachitika zachititsa A. kukhala wokhwima maganizo kuposa zoyembekezeredwa zilizonse zachibadwa kapena kukhwima maganizo kwa wazaka 15. Ndiganiza kuti mnyamata amene ndinalankhula naye m’maŵa uno ali wosiyana kotheratu ndi wazaka 15 wamba, chifukwa cha chokumana nacho chatsoka chimenechi.

“Ndiganiza kuti ali wokhwima maganizo mokwanira kupereka lingaliro lokhutiritsa, ndipo walipereka kwa ine . . . ndilinso wokhutira kuti nkoyenera . . . kwa ine kulingalira zofuna zake, ndipo ndikufuna kutero. Zofuna zake nzakuti zinthu za mwazi zisaperekedwe, ndipo ndili wokhutiranso kuti ngati zofuna zimenezi zitsutsidwa mwa njira ina ndi Mkuluyo pansi pa lamulo la Bwalo Lamilanduli, ndiye kuti kwenikweni zofuna zake zabwino mwachionekere zikayambukiridwa moipa . . . Ndiponso, ngati—ndipo zimenezi zikhoza kutheka—angafe ndi nthendayi, adzachita zimenezo mu mkhalidwe wamaganizo umene, polingalira za zikhulupiriro zake zachipembedzo, udzakhala womvetsa chisoni kwambiri, woipitsitsa, ndipo wosakhumbika konse. Ndikulingalira zinthu zonsezi. . . .

“M’zochitika zonsezi, ndikulingalira kuti nkoyenera kwa ine kukana pempho lakuti zinthu zamwazi zigwiritsiridwe ntchito m’mankhwala a A.”

Uthenga wa Adrian kwa Woweruza Wells

Unali uthenga wolingaliridwa bwino kwambiri umene mnyamata ameneyu, amene anadziŵa kuti akufa, anatumiza kwa Woweruza Robert Wells, umene unaperekedwa ndi a David Day, motere: “Ndiganiza kuti ndingakhale wosasamala ngati sindinakuthokozeni m’malo mwa yemwe ndikumuimira, kuchokera pansi pa mtima wake, umene uli woyamikira kwambiri, amene ndinalankhula naye mwachidule mutangochoka kuchipatala lero, chifukwa chochita ndi nkhaniyi mofulumira ndi mwaluso ndi moyenerera kwambiri. Iye ali woyamikira kwambiri kwa inu, Mbuyanga, ndipo ndifuna kuti zolembedwa zisonyeze zimenezo. Zikomo.”

Amayi ake a Adrian akusimba zochitika zomalizira za nkhaniyo.

“Pambuyo pa mlanduwo Adrian anafunsa Dr. Jardine kuti, ‘Kodi ndidzakhala kwa utali wotani?’ Dokotalayo anayankha kuti: ‘Mlungu umodzi kapena iŵiri.’ Ndinaona mwana wanga akukhetsa msozi, womwe unatuluka m’zikope atatsinzina. Ndinapita kukamkupatira, ndipo anati: ‘Ndilekeni, Amayi. Ndikupemphera.’ Pambuyo pa mphindi zingapo, ndinafunsa kuti, ‘Kodi ukulingalira bwanji za zimenezi, Adrian?’ ‘Amayi, ndidzakhalabe ndi moyo, ngakhale nditafa. Ndipo ngati ndatsala ndi milungu iŵiri yokha yokhala ndi moyo, ndikufuna kusangalala nayo. Chotero muyenera kukhala wosangalala.’

“Iye anafuna kukaona nthambi ya Watch Tower ku Georgetown, Canada. Anachita zimenezo. Anasambira m’dziŵe lakumeneko ndi mmodzi wa mabwenzi ake. Iye anapita ku maseŵera a timu ya baseball ya Blue Jays ndipo anajambulitsa chithunzi ndi ena a oseŵerawo. Chofunika kwambiri, anali atadzipatulira mumtima mwake kutumikira Yehova Mulungu, ndipo tsopano anafuna kusonyeza zimenezo mwa kumizidwa m’madzi. Panthaŵiyi nkuti mkhalidwe wake utaipirapo, ndipo anali atabwereranso m’chipatala ndipo sakanatulukamonso. Chotero mokoma mtima manesi analinganiza kuti agwiritsire ntchito limodzi la matanki achitsulo limene linali m’chipinda cha physiotherapy. Anabatizidwa mmenemo pa September 12; anamwalira tsiku lotsatira, pa September 13.

“Maliro ake anali aakulu kwambiri amene sanachitikepo pa nyumba yamaliro—manesi, madokotala, makolo a odwala, anzake akusukulu, anansi, ndi abale ndi alongo ake ambiri auzimu a mumpingo wake ndi mipingo ina. Monga makolo, sitinazindikire konse mikhalidwe yabwino kwambiri imene inaonekera mwa mwana wathu pamene anapirira ziyeso zake zambiri kapena chifundo ndi kulingalira kumene kunali mbali ya kukulitsa kwake umunthu Wachikristu. Wamasalmo wouziridwa anati: ‘Ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova.’ Ndithudi mwanayu anali wotero, ndipo tiyembekezera kudzamuona m’dziko latsopano lolungama la Yehova, lomwe lidzakhazikitsidwa posachedwapa m’dziko lapansi la paradaiso.”—Salmo 127:3; Yakobo 1:2, 3.

Tiyeni tiyembekezere kuti lonjezo la Yesu pa Yohane 5:28, 29 lidzakwaniritsidwe kwa Adrian lakuti: “Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira, amene adachita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa kukuuka kwa kuweruza.”

Mwa kukana kuthiridwa mwazi kumene mwinamwake kukanatalikitsa moyo wake panthaŵi ino, Adrian Yeatts anadzisonyeza kukhala mmodzi wa achichepere ambiri amene aika Mulungu poyamba.

[Bokosi patsamba 5]

‘Moyo Uli M’mwazi’

Mwazi Uli Wocholoŵana Kwambiri, Ukumafika M’selo Lililonse M’thupi. Mkati Mwa Dontho Limodzi, Maselo Ofiira A Mwazi 250,000,000 Amanyamula Okosijeni Ndi Kuchotsa Carbon Dioxide; Maselo Oyera 400,000 Amafunafuna Ndi Kuwononga Zinthu Zoloŵerera Zosafunidwa; Ma Platelet 15,000,000 Amasonkhana Nthaŵi Yomweyo Pamalo Ochekeka Ndi Kuyamba Kuundana Kuti Atseke Potsegukapo. Zonsezi Zili M’madzi Oyera Motuwira Otchedwa Plasma, Imene Ili Yopangidwa Ndi Mazanamazana A Zinthu Zochita Mbali Zofunika Pandandanda Yaitali Ya Ntchito Za Mwazi. Asayansi Samvetsetsa Zonse Zimene Mwazi Umachita. Nzosadabwitsa Kuti Yehova Mulungu, Mlengi Wa Madzi Ozizwitsa Ameneŵa, Amalengeza Kuti ‘Moyo Uli M’mwazi.’—Levitiko 17:11, 14.

[Bokosi patsamba 7]

Kuikirira Mtima Popanda Mwazi

October Wathayu, Chandra Sharp Wazaka Zitatu Zakubadwa Anagonekedwa M’chipatala Mu Cleveland, Ohio, U.S.A., Ndi Vuto La Mtima Womwe Unali Waukulu Ndiponso Wosagwira Bwino Ntchito. Iye Anali Wowonda Chifukwa Cha Kusadya Mokwanira, Anali Wopinimbira, Ndipo Anali Kulemera Makilogalamu Asanu Ndi Anayi Okha, Ndipo Anafunikira Kuikiriridwa Mtima. Mkhalidwe Wake Unali Wowopsa. Anapatsidwa Milungu Yochepa Yokha Ya Kukhala Ndi Moyo. Makolo Ake Anavomera Kuikirira Mtimako Koma Anakana Kuthira Mwazi. Iwo Ndi Mboni Za Yehova.

Imeneyi Sinali Nkhani Yovuta Kwa Dokotala Wopanga Opaleshoniyo, Dr. Charles Fraser. The Flint Journal Ya Ku Michigan Inasimba Pa December 1, 1993 Kuti: “Fraser Ananena Kuti Cleveland Clinic Ndi Malo Ena A Zamankhwala Akukhala Aluso Pochita Maopaleshoni Ambiri—kuphatikizapo Kuikirira Ziŵalo—popanda Kupatsa Wodwalayo Mwazi Wa Anthu Ena. ‘Taphunzira Zambiri Za Mmene Tingasungire Mwazi, Ndi Mmene Tingayendetsere Makina A Mtima Ndi Mapapu Ndi Madzi Ena Osakhala Mwazi,’ Anatero Fraser.” Ndiyeno Anawonjezera Kuti: “Kwa Zaka Makumi Ambiri Zipatala Zina Zokhala Ndi Akatswiri Zakhala Zikuchita Maopaleshoni Aakulu A Mtima Ndi Mitsempha Ya Mwazi Popanda Kuthira Mwazi. . . . Nthaŵi Zonse Timayesa Kuchita Opaleshoni Popanda (kuthira) Mwazi.”

Pa October 29, Iye Anachita Opaleshoni Yoikirira Mtima Mwa Chandra Popanda Mwazi. Mwezi Umodzi Pambuyo Pake Chandra Anasimbidwa Kuti Anali Kuchira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena