Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 6/8 tsamba 9-15
  • Achichepere Amene Ali ndi “Ukulu Woposa Wamphamvu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Achichepere Amene Ali ndi “Ukulu Woposa Wamphamvu”
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Lenae Martinez
  • Crystal Moore
  • Lisa Kosack
  • Ernestine Gregory
  • Nzeru Zoposa Zaka Zake
    Galamukani!—1988
  • Yendani Monga Momwe Mwalangizidwa ndi Yehova
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kutetezera Ana Anu ku Mwazi
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Kupulumutsa Moyo ndi Mwazi—Motani?
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 6/8 tsamba 9-15

Achichepere Amene Ali ndi “Ukulu Woposa Wamphamvu”

NDIWE wamng’ono. Zaka 12 zokha. Uli ndi banja limene umakonda. Uli ndi anzako akusukulu amene umakonda. Umapita kukasangalala kugombe la nyanja ndi kumapiri. Umachita mantha pamene uyang’ana thambo lodzaza ndi nyenyezi usiku. Uli ndi moyo wako wonse kutsogolo.

Ndipo tsopano uli ndi kansa. Nkhani imeneyo imakhala tsoka pamene uli ndi zaka 60. Imakhala nkhani yoipa koposa pamene uli ndi zaka 12.

Lenae Martinez

Ndimo mmene zinaonekera kwa Lenae Martinez wazaka 12. Chiyembekezo chake chinali cha kukhala ndi moyo kosatha padziko lapansi la paradaiso. Chiyembekezo chimenechi chinakulitsidwa ndi maphunziro a Baibulo amene analandira kwa makolo ake, amene ali Mboni za Yehova. Kodi iyemwini sanaŵerenge yekha m’Baibulo kuti dziko lapansi lidzakhala kosatha, kuti linalengedwa kuti likhalidwe ndi anthu kosatha, ndi kuti ofatsa adzakhalamo kosatha?—Mlaliki 1:4; Yesaya 45:18; Mateyu 5:5.

Tsopano anali mu Valley Children’s Hospital mu Fresno, California, U.S.A. Iye anagonekedwa mmenemo kaamba ka amene anaonekera ngati matenda a impso. Komabe, kupima kunasonyeza kuti anali ndi leukemia. Madokotala amene anali kusamalira Lenae anaganiza kuti maselo ofiira a mwazi ndi ma platelet ayenera kuthiridwa ndi kuyamba kupereka chemotherapy panthaŵi yomweyo.

Lenae ananena kuti sanafune mwazi kapena zinthu zamwazi, kuti anaphunzitsidwa kuti Mulungu amaletsa zimenezo, monga kwasonyezedwa m’mabuku a Baibulo a Levitiko ndi Machitidwe. “Pakuti chinakomera Mzimu Woyera ndi ife, kuti tisasenzetse inu chothodwetsa chachikulu china choposa izi zoyenerazi; kuti musale nsembe za mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama.” (Machitidwe 15:28, 29) Makolo ake anamchirikiza pa kaimidwe kameneka, koma Lenae anagogomezera kuti chinali chosankha chake ndipo chinali chofunika kwambiri kwa iye.

Madokotalawo analankhula ndi Lenae ndi makolo ake nthaŵi zingapo. Ngakhale zinali choncho, iwo anabweranso masana ena. Lenae anati ponena za ulendo umenewu: “Ndinali wofooka kwambiri chifukwa cha ululu ndipo ndinali kusanza mwazi wambiri. Iwo anandifunsa mafunso amodzimodziwo, kokha kuti anafunsa m’njira yosiyana. Ndinawauzanso kuti: ‘Sindikufuna mwazi kapena zinthu zamwazi. Ndingalolere kufa, ngati kuli koyenera, kuposa kuswa lonjezo langa kwa Yehova Mulungu la kuchita chifuniro chake.’”

Lenae anapitiriza kuti: “Anabweranso m’maŵa wotsatira. Ma platelet anga anali kutsika, ndipo thupi langa linali lidakali lotentha kwambiri. Ndinaona kuti madokotalawo anandimvetsera kwambiri panthaŵiyi. Ngakhale kuti sanakonde kaimidwe kanga, iwo ananena kuti ndinali wazaka 12 wokhwima maganizo. Pambuyo pake dokotala wanga wodziŵa za matenda a ana anabwera nandiuza kuti anali wachisoni koma palibe china chimene chikanathandiza kusiyapo kokha chemotherapy ndi kuthiridwa mwazi. Anachoka nanena kuti abweranso pambuyo pake.

“Pamene anachoka, ndinayamba kulira kwambiri chifukwa chakuti anandisamalira moyo wanga wonse, ndipo tsopano ndinalingalira kuti anali kunditaya. Pamene anabwera pambuyo pake, ndinamuuza mmene anandichititsira kulingalira—kuti sanandisamalirenso. Zimenezi zinamdabwitsa, ndipo ananena kuti anali wachisoni. Analibe cholinga cha kundivulaza. Anandiyang’ana nati: ‘Chabwino, Lenae, ngati ndimo mmene zinthu ziyenera kukhalira, pamenepo ndidzakuona kumwamba.’ Anachotsa mandala ake ndipo, ali ndi misozi yambiri m’maso mwake, ananena kuti amandikonda ndipo anandikupatira mwamphamvu. Ndinamuthokoza ndipo ndinati: ‘Zikomo. Nanenso ndimakukondani, Dr. Gillespie, koma ndikuyembekezera kudzakhala padziko lapansi la paradaiso pa chiukiriro.’”

Ndiyeno madokotala aŵiri ndi loya anabwera, nauza makolo a Lenae kuti anafuna kulankhula naye ali yekha, napempha makolowo kutuluka, ndipo anatuluka. Mkati mwa kukambitsirana kumeneku, madokotalawo anali olingalira ndi okoma mtima ndipo anachita chidwi ndi kalankhulidwe kaluso ka Lenae ndi chikhulupiriro chake champhamvu.

Pamene anali naye ali yekha, anamuuza kuti adzafa ndi leukemia nati: “Koma kuthiridwa mwazi kudzatalikitsa moyo wako. Ngati ukana mwazi, udzafa m’masiku oŵerengeka.”

Lenae anafunsa kuti: “Ngati ndilandira mwazi, kodi udzatalikitsa moyo wanga kwa utali wotani?”

“Pafupifupi miyezi itatu mpaka isanu ndi umodzi,” iwo anayankha motero.

“Kodi ndingachitenji m’miyezi isanu ndi umodzi?” anafunsa motero.

“Udzakhala wamphamvu. Ungachite zinthu zambiri. Ukhoza kupita ku Disney World. Ungaone malo ena ambiri.”

Lenae analingalira kwa kanthaŵi, ndiyeno anayankha nati: “Ndatumikira Yehova moyo wanga wonse, zaka 12. Iye wandilonjeza moyo wosantha m’Paradaiso ngati ndimumvera. Sindingamfulatire tsopano kuti ndikhale ndi moyo kwa miyezi isanu ndi umodzi. Ndifuna kukhala wokhulupirika mpaka imfa. Pamenepo ndidziŵa kuti panthaŵi yake yoikika adzandiukitsa kwa akufa ndi kundipatsa moyo wosatha. Ndiyeno ndidzakhala ndi nthaŵi yochuluka ya kuchita zonse zimene ndifuna kuchita.”

Madokotalawo ndi loyayo mwachionekere anachita chidwi. Iwo anamuyamikira natuluka nauza makolo ake kuti amaganiza ndi kulankhula ngati wachikulire ndipo ali wokhoza kupanga zosankha zake. Iwo anauza bungwe la malamulo a makhalidwe pa Valley Children’s Hospital kuti Lenae alingaliridwe kukhala wachichepere wokhwima maganizo. Komiti imeneyi, yopangidwa ndi madokotala ndi antchito ena a zaumoyo, limodzi ndi profesa wa malamulo a makhalidwe wa ku Fresno State University, inapanga chigamulo cha kulola Lenae kupanga zosankha zake ponena za chithandizo chake chamankwhala. Iwo analingalira Lenae kukhala wachichepere wokhwima maganizo. Sanafune ulamuliro wa bwalo lamilandu.

Pambuyo pa usiku wautali, wovuta, pa 6:30 a.m., September 22, 1993, Lenae anagona tulo ta imfa m’manja mwa amayi ake. Ulemu ndi bata la usiku umenewo zinakhazikika m’maganizo mwa amene analipo. Panali 482 amene anafika pamaliro, kuphatikizapo madokotala, manesi, ndi aphunzitsi, omwe anachita chidwi ndi chikhulupiriro ndi kusunga umphumphu kwa Lenae.

Makolo ndi mabwenzi a Lenae anali oyamikira kwambiri kuti madokotala ndi manesi ndi akuluakulu a pa Valley Children’s Hospital anasonyeza luntha m’kuzindikira kukhwima maganizo kwa wachichepere ameneyu ndi kuti kutengera nkhaniyo ku bwalo lamilandu sikunafunikire kuti papangidwe chosankha chimenecho.

Crystal Moore

Kulingaliridwa koteroko sikunaperekedwe kwa Crystal Moore wazaka 17 pamene anagonekedwa mu Columbia Presbyterian Medical Center mu New York City. Anali kudwala matenda a kutupa matumbo. Pamene anagonekedwa m’chipatala, Crystal, limodzi ndi makolo ake, anagogomezera mobwerezabwereza kukana kwake kulandira mwazi. Iye sanafune kufa; mmalo mwake, anafuna chithandizo cha mankhwala choyenerana ndi lamulo la Baibulo la kusala mwazi.—Machitidwe 15:28, 29.

Gulu la ogwira ntchito yamankhwala limene linali kusamalira Crystal linali lotsimikiza kuti mkhalidwe wake unafunikira kuthiridwa mwazi. Dokotala wina ananena mosabisa mawu kuti: “Ngati Crystal sathiridwa mwazi kufikira Lachinayi, June 15, ndiye kuti pa Lachisanu, June 16, iye adzakhala atafa!” Pa June 16, Crystal anali asanafe, ndipo chipatalacho chinapempha Bwalo Lamilandu Lalikulu Koposa la Boma la New York ulamuliro wa kuumiriza kuthira mwazi.

Pa mlanduwo, umene unazengedwa mofulumira pachipatalapo m’maŵa umenewo, mmodzi wa madokotala anavomereza kuti Crystal anafunikira ma unit aŵiri a mwazi mofulumira ndipo angafune pafupifupi ma unit ena khumi owonjezereka. Iye anapitiriza kunena kuti ngati Crystal adzayesa kukana kuthiridwa mwaziko, adzammangirira kubedi manja ndi miyendo kuti apereke mankhwalawo. Crystal anauza madokotalawo kuti “adzakuwa ndi kufuula” ngati adzayesa kumuthira mwazi ndi kuti monga mmodzi wa Mboni za Yehova, anaona kukakamiziridwa mwazi kulikonse kukhala konyansa mofanana ndi kugwiriridwa chigololo.

Mosasamala kanthu za mapempho obwerezabwereza a loya wake pa mlanduwo, Crystal anakanizidwa mwaŵi wa kudzilankhulira yekha pamaso pa bwalo lamilandulo kusonyeza kukhoza kwake kupanga zosankha. Ngakhale kuti Crystal anali atangolandira kumene mphotho pa mpikisano wa Super Youth Program chifukwa cha nzeru zake pasukulu ndi utsogoleri pa sukulu yake yasekondale, woweruza wozenga mlanduyo anakana kumulola kudziperekera umboni m’bwalo lamilandu ponena za kukana kwake mwazi. Zimenezi zinamanitsa Crystal kuyenera kwake kwakuti mlandu uzengedwe mwalamulo lake, kudzisankhira zimene zingachitikire thupi lake, chinsinsi cha munthu mwini, ndi ufulu wachipembedzo.

Ngakhale kuti bwalo lozenga mlandulo silinalole Crystal kudzichitira umboni, abwalowo anaonana ndi Crystal ali yekha m’chipinda chake kwa pafupifupi mphindi 20. Pambuyo pa kuchezako woweruza wozenga mlanduyo anati Crystal anali “mwachionekere wanzeru kwambiri” ndi “waluso kwambiri” ndipo analongosola kuti Crystal “analidi wolama maganizo” ndi “wokhoza kulankhula momasuka kotheratu.” Mosasamala kanthu za ndemanga zimenezi, bwalo lozenga mlandulo linakana kwamtu wagalu kupatsa Crystal mwaŵi wakusankha chisamaliro chake cha mankhwala.

Pa Sande m’maŵa, June 18, Crystal anafunikira opaleshoni yofulumira, imene anavomera, koma anapitiriza kukana mwazi. Mwazi wokwanira pafupifupi 50-100 cubic centimeters wokha ndiwo unataika pa opaleshoniyo. Komabe, madokotalawo ananena kuti kuthiridwa mwazi kwa pambuyo pa opaleshoni kungafunikire. Dokotala wina anapereka umboni wakuti kuthiridwa mwazi sikunali kofunika. Iye anali atachiritsapo nthaŵi zonse matenda ofananawo popanda mwazi kwa zaka 13 zapita, ndipo kuthira mwazi kotsatirapo sikunafunikire konse.

Pa June 22, 1989, bwalo lozenga mlandulo linapatsa chipatalacho ulamuliro wa kuyang’anira Crystal kwakanthaŵi kaamba ka kuthira mwazi komwe kungaperekedwe kokha ngati “ukhala wofunikira kutetezera ndi kupulumutsa moyo wake.” Uyang’aniro umenewu unatha pamene Crystal anatulutsidwa m’chipatala. Crystal sanafunikire konse mwazi, ndipo palibe umene unagwiritsiridwa ntchito, koma zinali zowopsa kuona mmene bwalo lamilandulo linachitira ndi Crystal.

Kuyambira pamene anatulutsidwa m’chipatala, Crystal anamaliza maphunziro pa sukulu yasekondale atakhoza bwino koposa. Mwamsanga pambuyo pake, anakhala mtumiki wanthaŵi yonse monga mmodzi wa Mboni za Yehova. Anakhala woonetsa alendo malo pa Jersey City Assembly Hall ya Mboni za Yehova ndipo anadzipereka modzifunira monga chiŵalo cha gulu limene limamanga ndi kukonza Nyumba Zaufumu.

Komabe, madokotala a pa Columbia Presbyterian Medical Center ananena kuti ngati sathiridwa mwazi kufikira pa June 15, akafa pa June 16 ndi kuti ngati akakana kuthiridwa mwazi, akamangidwa manja ndi miyendo. Pamene madokotala amene akufuna lamulo la bwalo lamilandu kuti apereke mwazi anena mosabisa mawu kuti ngati woweruzayo savomereza mwamsanga, wodwalayo adzafa, akumbukiretu nkhani ya Crystal Moore.

Lisa Kosack

Usiku woyamba umene Lisa anakhala mu Sick Children’s Hospital ku Toronto unali woipa kuposa loto lowopsa. Iye analembetsedwa pa 4 koloko masana ndipo anapimidwa nthaŵi yomweyo. Iye sanafike m’chipinda chake cha m’chipatala mpaka pa 11:15 p.m. madzulo amenewo. Pakati pa usiku—eya, mulekeni Lisa anene zimene zinachitika. “Pakati pa usiku nesi anabwera nanena kuti: ‘Ndiyenera kukupatsa mwazi.’ Ndinafuula kuti: ‘Sindingalandire mwazi chifukwa ndine mmodzi wa Mboni za Yehova! Ndikhulupirira mukudziŵa zimenezo! Ndikhulupirira mukudziŵa zimenezo!’ ‘Ee, inde, ndikudziŵa,’ iye anatero, ndipo nthaŵi yomweyo anachotsa IV [chipangizo cholasira] yanga ndi kuisomeka mwamphamvu ku mwazi. Ndinali kulira mosatonthozeka.”

Kanali kachitidwe kouma mtima ndi kankhanza chotani nanga kochitidwa pa mtsikana wodwala wochita mantha wazaka 12 pakati pa usiku m’malo achilendo! Makolo a Lisa anapita naye ku Sick Children’s Hospital ku Toronto ndi cholinga chokapeza madokotala ogwirizanika. Mmalo mwake, mwana wawo anaumirizidwa kuthiridwa mwazi mwankhanza pakati pa usiku, mosasamala kanthu za kaimidwe ka Lisa ndi makolo ake kakuti mwazi kapena zinthu zamwazi zili kuswa lamulo la Mulungu ndipo siziyenera kugwiritsiridwa ntchito.—Machitidwe 15:28, 29.

Mmaŵa wotsatira chipatalacho chinafuna kupeza lamulo la ku bwalo lamilandu la kupereka mwazi. Mlanduwo unazengedwa masiku asanu, motsogoleredwa ndi Woweruza David R. Main. Unachitidwira m’chipinda cha m’chipatala, Lisa akumapezekapo masiku onse asanu. Lisa anali ndi acute myeloid leukemia, matenda amene kaŵirikaŵiri amapha, ngakhale kuti madokotalawo anapereka umboni kuti mlingo wa kuchiritsa nthendayo unali 30 peresenti. Iwo anati ayenera kupatsidwa mwazi wambiri ndi chemotherapy yamphamvu—mankhwala amene amachititsa ululu waukulu ndi zivulazo zoipa.

Patsiku lachinayi la mlanduwo, Lisa anapereka umboni. Funso limodzi limene anafunsidwa linali lonena za mmene kuikidwa mwazi kokakamiza kwa pakati pa usikuko anakuonera. Iye analongosola kuti kunamchititsa kudziona ngati galu amene akugwiritsiridwa ntchito m’kufufuza, kuti anamva ngati akugwiriridwa chigololo, ndi kuti kukhala wamng’ono kunachititsa anthu ena kuganiza kuti akhoza kuchita chilichonse kwa iye. Iye anada kuona mwazi wa munthu wina ukuloŵa mwa iye, akumakayikira ngati adzatenga AIDS kapena nthenda ya kutupa chiwindi kapena matenda ena oyambukira. Ndipo kwakukulukulu, iye anada nkhaŵa ndi zimene Yehova akalingalira za iye chifukwa cha kuswa lamulo lake loletsa kuloŵetsa mwazi wa munthu wina m’thupi mwake. Iye anati ngati zidzachitikanso, iye “adzalimbalimba ndi kukankha chitsulo chokolowekako IV ndi kusolola IV mosasamala kanthu kuti zidzapweteka motani, ndi kuboola botolo lamwazilo.”

Loya wake anafunsa kuti, “Kodi ukuganiza motani pamene Children’s Aid Society ikupempha kuti chisamaliro chako chichotsedwe kwa makolo ako ndi kuperekedwa kwa iwo?”

“Eya, zikundipangitsa kukhala wokwiya kwambiri; zikundipangitsa kuganiza kuti iwo ali ankhalwe chifukwa chakuti makolo anga sanayambe andimenya, iwo amandikonda ndipo nanenso ndimawakonda, ndipo pamene ndinadwala chifuwa kapena chimfine kapena matenda ena alionse, iwo anandisamalira. Moyo wawo wonse unazikidwa pa ine, ndipo tsopano kuti munthu wina adzandichotse kwa iwo, kokha chifukwa chakuti iwo sakuvomereza, ndiganiza kuti ndi nkhanza yaikulu kwambiri, ndipo zikundikwiyitsa kwambiri.”

“Kodi ukufuna kufa?”

“Ayi, sindiganiza kuti aliyense amafuna kufa, koma ngati ndifa sindikuchita mantha, chifukwa ndikudziŵa kuti ndili ndi chiyembekezo cha moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi.”

Panali ochepa omwe sanalire pamene Lisa analongosola molimba mtima za imfa yake yomayandikirayo, chikhulupiriro chake mwa Yehova, ndi chitsimikizo chake cha kukhala wokhulupirika ku lamulo lake la kupatulika kwa mwazi.

“Lisa,” loya wake anapitiriza, “kodi pangakhale kusiyana kulikonse kwa iwe kudziŵa kuti bwalo lamilandu lakulamulira kuti uthiridwe mwazi?”

“Ayi, chifukwa ndidzakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu wanga ndi kumvera malamulo ake, chifukwa Mulungu ali wamkulu kwambiri kuposa bwalo lamilandu lililonse kapena munthu aliyense.”

“Lisa, kodi ungakonde kuti woweruza agamule motani nkhaniyi?”

“Eya, zimene ndingakonde kuti woweruzayo achite pa nkhaniyi ndizo kungondibwezera kwa makolo anga ndi kuwalola kundiyang’aniranso kotero kuti ndikhale wachimwemwe, ndipo motero ndingapite kunyumba ndi kukhala m’malo osangalatsa.”

Ndipo zimenezo ndi zimene Woweruza Main anagamula. Mawu a m’chigamulo chake akutsatira pansipa.

“L. wauza bwalo lamilandu lino momvekera bwino ndi motsimikiza kuti, ngati kuyesayesa kulikonse kupangidwa kumuthira mwazi, iye adzalimbana ndi kuthiridwa mwazi kumeneko ndi nyonga zonse zimene angapeze. Iye wanena, ndipo ndikumkhulupirira, kuti adzakuwa ndi kulimbalimba ndi kuti adzachotsa chipangizo cholasilacho pamkono pake ndipo adzayesa kutayira mwaziwo pabedi pake. Ndakana kupereka lamulo limene likachititsa mwana ameneyu kukumana ndi vuto limeneli.”

Ponena za kuthiridwa mwazi kokakamiza kwa pakati pa usiku, iye anati:

“Ndiyenera kunena kuti analakwiridwa pa maziko a chipembedzo chake ndi msinkhu wake mogwirizana ndi s. 15(1). M’mikhalidwe imeneyi, pamene anapatsidwa mwazi, kuyenera kwake kwa kutetezera thupi lake mogwirizana ndi s. 7 kunaponderezedwa.”

Maganizo ake ponena za Lisa ali okondweretsa:

“L. ndi munthu wokongola, wanzeru koposa, waluntha, waulemu, womva zinthu ndipo, chofunika koposa, wolimba mtima. Iye ali ndi nzeru ndi uchikulire woposa kwambiri zaka zake ndipo ndiganiza kuti kungakhale koyenera kunena kuti ali ndi mikhalidwe yonse yabwino imene kholo lililonse lingafune mwa mwana. Iye ali ndi chikhulupiriro chachipembedzo cholingaliridwa bwino, cholimba ndi choonekera bwino. M’lingaliro langa, palibe kuchuluka kulikonse kwa uphungu wochokera ku magwero alionse kapena chitsenderezo chochokera kwa makolo ake kapena wina aliyense, kuphatikizapo lamulo la bwalo lamilanduli, kumene kungagwedeze kapena kusintha zikhulupiriro zake zachipembedzo. Ndikhulupirira kuti L. K. ayenera kupatsidwa mwaŵi wakulimbana ndi nthendayi mwaulemu ndi mtendere wa maganizo.”

“Pempho lakanidwa.”

Lisa ndi banja lake anachoka m’chipatala tsiku limenelo. Lisa analimbanadi ndi nthenda yake mwaulemu ndi mtendere wa maganizo. Iye anafa mwamtendere kunyumba, m’manja achikondi a amayi ndi atate wake. Mwakuchita zimenezo anagwirizana ndi magulu a Mboni za Yehova zachichepere zambiri zimene zimaika Mulungu poyamba. Monga chotulukapo chake, iye pamodzi ndi iwo, adzakondwera ndi kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Yesu lakuti: “Iye amene ataya moyo wake, chifukwa cha ine, adzaupeza.”—Mateyu 10:39.

Ernestine Gregory

Pa msinkhu wazaka 17, Ernestine anapimidwa kukhala akudwala leukemia. Pamene anagonekedwa m’chipatala, iye anakana kuvomereza kugwiritsira ntchito zinthu zamwazi kuchirikiza chemotherapy imene madokotala anafuna kupereka. Chifukwa cha kukana kwa Ernestine ndi chichirikizo cha amayi ake pa chosankha cha mankhwala osagwiritsira ntchito mwazi, chipatalacho chinapereka nkhaniyo kwa akuluakulu oyang’anira anthu ovutika mu Chicago, Illinois, U.S.A., amene anafuna lamulo la bwalo lamilandu la kugwiritsira ntchito mwazi. Mlandu unalinganizidwa, kumene bwalo lozenga milandulo linamva umboni kuchokera kwa Ernestine, dokotala wa mankhwala, dokotala wa matenda a maganizo, ndi loya, limodzinso ndi anthu ena oloŵetsedwamo.

Ernestine anauza dokotala wake kuti sanali kufuna mwazi. Kuti chinali chosankha chake cha iyemwini chozikidwa pa kuŵerenga kwake Baibulo. Kuti kuthiridwa mwazi mosadzifunira koperekedwa chifukwa cha lamulo la bwalo lamilandu kumasonyezabe kusalemekeza lamulo la Mulungu ndipo kuli kulakwa m’maso mwake, mosasamala kanthu za ukumu wa bwalo lamilandulo. Kuti iye sanali kutsutsa chithandizo cha mankhwala ndipo sanafune kufa. Kuti chosankha chake sichinali kulakalaka imfa, sichinali kudzipha; komabe, iye sanawope imfa.

Stanley Yachnin, M.D., anapereka umboni wakuti iye “anachita chidwi ndi kukhwima maganizo kwa Ernestine, kudziimira kwake,” ndi kuwona mtima kwa zikhulupiriro zake zachipembedzo. Iye ananenanso kuti Ernestine anazindikira mtundu ndi zotulukapo za nthenda yake. Chifukwa cha kumvetsetsa kwake, Dr. Yachnin sanaone kufunika kwa kuitana dokotala wa matenda a maganizo kapena katswiri wa maganizo ndi khalidwe.

Komabe, mmodzi anaitanidwa, Ner Littner, M.D., dokotala wa matenda a maganizo, amene pambuyo pa kulankhula ndi Ernestine anali ndi lingaliro lakuti iye anali wokhwima maganizo mofanana ndi munthu wazaka zapakati pa 18 ndi 21. Iye ananena kuti Ernestine anasonyeza kumvetsetsa zotulukapo za kuvomera kapena kukana kuthiridwa mwazi. Iye ananena kuti anavomera zimenezi, osati chifukwa chakuti anali pansi pa ulamuliro wa wina, koma chifukwa chakuti anakhulupirira zimenezi iyemwini. Dr. Littner anati Ernestine ayenera kuloledwa kupanga chosankha chake cha iyemwini pankhaniyi.

Jane McAtee, loya wa chipatalacho, anapereka umboni wakuti pambuyo pofunsa Ernestine, anakhulupirira kuti Ernestine anamvetsetsa mtundu wa nthenda yake ndi kuti iye “anaonekera kukhala wozindikira mokwanira chosankha chake ndi kuvomera zotulukapo zake.”

Khotilo nalonso linachita chidwi kwambiri ndi umboni wa Ernestine. Khotilo linapeza kuti Ernestine anali wazaka 17 wokhwima maganizo, wokhoza kupanga zosankha za mankhwala zodziŵitsidwa; komabe, modabwitsa, khotilo linapereka lamulo lolola kuthira mwazi. Pa chipatalapo madokotala aŵiri anali kuyembekezera, atakonzeratu chiwiya chothirira, ndipo mwamsanga pamene chosankha cha khoti chinafika, mwaziwo unathiridwa mokakamiza pa Ernestine mosasamala kanthu za kutsutsa kwake kwamphamvu. Lamulo la khotilo linachitiridwa apilo panthaŵi yomweyo koma osati panthaŵi yokwanira kuletsa kuthira mwazi kodudukira kwa chipatalacho.

Pofuna kuletsa kuthira mwazi kowonjezereka, lamulo la bwalo lozenga milandulo linachitiridwa apilo poyamba ku Bwalo Lamilandu la Apilo la ku Illinois. M’chigamulo cha aŵiri kwa mmodzi, Bwalo Lamilandu la Apilo linachirikiza kuti Ernestine sangakakamizidwe kugonjera kuti athiridwe mwazi motsutsana ndi chifuno chake. Bwalo lamilandulo linapereka chifukwa chakuti kuyenerera kwa Ernestine kwa First Amendment kwa ufulu wachipembedzo limodzi ndi kuyenerera kwake kwa lamulo kwa chinsinsi kunatetezera kuyenera kwake monga wachichepere wokhwima maganizo wokhoza kukana kuthiridwa mwazi pa zifukwa zachipembedzo.

Pamenepo akuluakulu a malo oyang’anira ana ovutika anachitanso apilo chigamulo cha Bwalo Lamilandu la Apilo ku Bwalo Lamilandu Lalikulu Koposa la ku Illinois. Bwalo Lamilandu Lalikulu Koposa la ku Illinois linachirikiza mwamphamvu chigamulocho, likumanena kuti ngakhale kuti Ernestine anali wachichepere, iye anali ndi kuyenera kwakukana chithandizo cha mankhwala chimene chinali choipa kwa iye. Bwalo lamilandu lalikulu koposalo linazika chigamulo chake pa kuyenera kwa lamulo la onse la kudzisankhira zinthu ndi lamulo la wachichepere wokhwima maganizo. Muyezo woyenera kugwiritsiridwa ntchito m’milandu ya achichepere ofikapo mu Illinois unalembedwa mwachidule ndi Bwalo Lamilandu Lalikulu Koposa la ku Illinois mu ndemanga yotsatirayi:

“Ngati umboni uli woonekeratu ndi wokhutiritsa kuti wachichepereyo ali wokhwima maganizo mokwanira kuzindikira zotulukapo za machitidwe ake, ndi kuti wachichepereyo ali wokhwima maganizo mokwanira kugwiritsira ntchito chiweruzo cha munthu wamkulu, pamenepo chikhulupiriro cha wachichepere wokhwima maganizoyo chimampatsa kuyenera kwa lamulo la onse la kuvomera kapena kukana chithandizo chamankhwala.”

Ernestine sanapatsidwe mwazi wowonjezereka, ndipo iye sanafe ndi leukemia yake. Ernestine anachirimika ndi kuika Mulungu poyamba, mofanana ndi anthu ena achichepere otchulidwa poyambapo. Aliyense analandira “ukulu woposa wamphamvu.”—2 Akorinto 4:7.

[Bokosi patsamba 13]

Maupandu A Kuthira Mwazi

The New England Journal of Medicine, kope la December 14, 1989, linasimba kuti unit imodzi ya mwazi ingakhale ndi tizilombo ta AIDS tokwanira kuchititsa matenda ofika ku 1.75 miliyoni!

Mu 1987, zitadziŵika kuti AIDS inali kupatsiridwa kudzera m’mwazi woperekedwa ndi odzifunira, buku lakuti Autologous and Directed Blood Programs linadandaula kuti: “Chimenechi chinali chochitika choipitsitsa cha zochitika zonse zoipa za mankhwala; kuti mphatso yamtengo wake yopatsa moyo ya mwazi ingasanduke kukhala chipangizo cha imfa.”

Dr. Charles Huggins, mtsogoleri wa ntchito za kuthira mwazi pa chipatala cha Massachusetts, U.S.A., anati: “Uli chinthu chowopsa kopambana chimene timagwiritsira ntchito m’mankhwala.”

Surgery Annual inamaliza kuti: “Mwachionekere, kuthira mwazi kotetezereka kopambana ndi kumene sikunaperekedwe.”

Chifukwa chakuti pali kuyambanso kokulira koposa kwa kansa pambuyo pa opaleshoni yogwiritsira ntchito mwazi, Dr. John S. Spratt ananena mu The American Journal of Surgery, kope la September 1986 kuti: “Dokotala wochita opaleshoni ya kansa angafunikire kukhala dokotala wochita opaleshoni yopanda mwazi.”

Magazini a Emergency Medicine anati: “Chokumana nacho chathu ndi Mboni za Yehova chingatanthauziridwe kuti sitifunikira kudalira pa kuthira mwazi, kokhala ndi zocholoŵana zambiri, koposa momwe tinaganizira.”

Magazini a Pathologist anatchula za kukana kulandira mwazi kwa Mboni za Yehova ndi kunena kuti: “Pali umboni wokulira wochirikiza kutsutsa kwawo, mosasamala kanthu za kusakondwa kwa osunga mwazi.”

Dr. Charles H. Baron, profesa wa lamulo pa Boston College Law School, ananena motere ponena za kukana kulandira mwazi kwa Mboni za Yehova: “Chitaganya chonse cha America chapindula. Osati Mboni za Yehova zokha, koma odwala onse, lerolino sali othekera kupatsidwa mwazi mosayenerera chifukwa cha ntchito ya Makomiti Ogwirizanitsa ndi Chipatala a Mboni.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena